KODI DZIKOLI LIDZAKHALANSO BWINO?

Madzi Abwino

Madzi Abwino

PADZIKOLI sipangakhale zamoyo popanda madzi, makamaka madzi abwino. Ndipotu mu zinthu zonse zamoyo mumakhala madzi ndipo madziwo amakhala mbali yaikulu kwambiri. Anthu ndi nyama amapeza madzi akumwa komanso anthuwo amapeza madzi othirira mbewu zawo kuchokera m’nyanja, m’mitsinje, m’madambo ndi m’madzi a pansi pa nthaka.

Chifukwa Chake Sitikhala ndi Madzi Abwino Okwanira

Mbali yaikulu ya dzikoli ndi madzi. Komabe, bungwe lina linanena kuti “madzi abwino omwe amapezeka komanso kugwiritsidwa ntchito ndi okwana 0.5 peresenti yokha, omwe ndi ochepa kwambiri.” (World Meteorological Organization) Ngakhale kuti madzi abwinowa ndi ochepa chonchi, ndi okwanira kuti zamoyo zonse padzikoli zikhale ndi moyo. Komabe, mbali yaikulu ya madzi ochepawa imawonongedwa kapenanso sipezeka n’komwe chifukwa cha kuchuluka kwa anthu komanso chifukwa cha kusintha kwa nyengo. Akatswiri amanena kuti m’zaka 30 zikubwerazi, anthu okwana 5 biliyoni sadzatha kupeza madzi okwanira.

Dzikoli Linapangidwa M’njira Yoti Lizitha Kudzikonza Lokha

Dzikoli linapangidwa m’njira yakuti nthawi zonse lizikhala ndi madzi okwanira. Dothi, zinthu za m’madzi ndiponso dzuwa zimagwira ntchito limodzi kuti madzi azikhala abwino. Taonani ena mwa maumboni osonyeza kuti dzikoli linapangidwa kuti lizitha kudzikonza lokha.

  • Zimaoneka kuti dothi limathandiza kuchotsa zinthu zambiri zomwe zimawononga madzi. M’madambo, zomera zina zimachotsa m’dothi michere yosafunika komanso michere imene imapezeka mu mankhwala amene timathira mu mbewu zathu.

  • Asayansi anazindikira kuti dothi ndi miyala komanso tizilombo tinatake zimathandiza kukonza madzi oipa kuti akhale abwino. Madzi akamayenda, zoipa zimene zimakhala m’madziwo zimasungunuka ndipo tizilombo timawononga zoipazo.

  • Nkhono zam’madzi zimachotsa m’masiku ochepa chabe michere ina yosafunika yomwe imapezeka m’madzi. Ndipotu mwina nkhonozi zikhoza kusefa bwino madzi kuposa malo osefera madzi omwe anthu amapanga.

  • Chifukwa chakuti madzi amayenda kuchoka panthaka kupita kumwamba n’kubwereranso, dzikoli limakwanitsa kusunga madzi okwanira. Kayendedwe ka madzika limodzi ndi zinthu zimene zimachitika m’chilengedwechi, zimathandiza kuti madzi asathe padzikoli.

Zimene Anthu Akuchita Kuti Athetse Vutoli

Tikamakonza magalimoto athu ngati akudontha oilo komanso tikamataya moyenera mankhwala oopsa, timathandiza kuti madzi athu akhale abwino

Akatswiri amalimbikitsa kuti tizisamala madzi. Kuti tisamaipitse madzi, akatswiriwa amalimbikitsa kuti tizikonza magalimoto athu ngati akudontha oilo komanso tisamataye m’chimbudzi mankhwala amene sitikuwagwiritsa ntchito kapena mankhwala ena oopsa.

Pofuna kuti tikhale ndi madzi abwino ambiri, akatswiri enanso apeza njira zabwino zochotsera mchere m’madzi amchere.

Koma pakufunikabe zambiri. Njira imeneyi yochotsa mchere m’madzi siyodalirika kwenikweni chifukwa imafuna ndalama zambiri komanso magetsi ambiri. Lipoti lina lokhudza madzi la bungwe la United Nations la 2021 linanena kuti: “Padziko lonse, anthu akufunika kuchita zambiri kuposa zimene akuchita panopa pa nkhaniyi.”

Kodi Baibulo Limatipatsa Chiyembekezo Chotani?

“Mulungu . . . amakoka madontho a madzi. Madonthowo amasintha n’kukhala nkhungu imene imapanga mvula, kenako mitambo imagwetsa mvula, imagwetsera aliyense madzi.”—Yobu 36:​26-28.

Mulungu anakonza kuti zinthu m’chilengedwechi zizichitika mobwerezabwereza kuti madzi azisungika m’dzikoli.—Mlaliki 1:7.

Taganizirani izi: Ngati Mlengi anakonza kuti madzi azidziyeretsa okha, kodi sizingakhale zomveka kunena kuti iye ali ndi mphamvu komanso ndi wofunitsitsa kukonza zinthu zimene anthu awononga? Onani nkhani yakuti “Mulungu Akulonjeza Kuti Dzikoli Lidzakhalanso Bwino,” patsamba 15.