KODI DZIKOLI LIDZAKHALANSO BWINO?
Mpweya
TIMAFUNIKA mpweya, koma osati kuti tizingopuma basi. Mpweya umateteza dziko lathuli ku mphamvu yoipa yochokera ku dzuwa. Popanda mpweya, padzikoli pakhoza kuzizira kwambiri moti chilichonse chikhoza kuuma.
Mpweya Ukuwonongeka
Kuwonongeka kwa mpweya kukhoza kuchititsa kuti zamoyo zonse padzikoli zife. Mogwirizana ndi zimene Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linanena, munthu mmodzi pa anthu 100 alionse ndi amene akupuma mpweya wabwino padzikoli.
Kuwonongeka kwa mpweya kukhoza kuyambitsa matenda monga chifuwa, khansa ya m’mapapo komanso matenda a mtima. Kuwonongeka kwa mpweya kumachititsa kuti anthu pafupifupi 7 miliyoni azimwalira asanakule chaka chilichonse.
Dzikoli Linapangidwa M’njira Yoti Lizitha Kudzikonza Lokha
Dzikoli linapangidwa m’njira yoti lizitha kupereka mpweya wabwino kwa chamoyo chilichonse. Koma zimenezi zimatheka ngati anthu akuyesetsa kuti asawononge chilengedwechi. Taganizirani zitsanzo zotsatirazi:
-
Timadziwa bwino kuti mitengo ya m’nkhalango imakwanitsa kuchotsa mpweya woipa wa kaboni dayokisaidi. Koma anthu ambiri sadziwa kuti mitengo yopezeka m’mbali mwa nyanja, ikhoza kuchotsa bwino kwambiri mpweyawu. Mitengoyi imachotsa mpweya wa kaboni dayokisaidi wochuluka kuwirikiza maulendo 5 kuposa umene mitengo yonse ya m’nkhalango zikuluzikulu imachotsa.
-
Kafukufuku wina wa posachedwapa, anasonyeza kuti ndere zina zikuluzikulu zam’madzi zimachotsa mpweya woipa wa kaboni dayokisaidi mumlengalenga. Nderezi zomwe zimakhala ngati masamba, zili ndi timatumba ting’onoting’ono tomwe timadzaza ndi mpweya ndipo timathandiza kuti masambawa aziyandama kuchoka m’mbali mwa nyanja ndipo amakafika kutali kwambiri chapakati pa nyanja. Akafika kumeneko, timatumba tija timaphulika ndipo masamba omwe ali ndi mpweya wa kaboni dayokisaidi amayamba kumira n’kufika pansi pa nyanja. Zimaoneka kuti masambawo amakwiririka pansi pa nyanjapo kwa zaka mahandiredi ambirimbiri.
-
Mumlengalenga mumatha kudziyeretsa mokha ngati muli mpweya woipa. Zimenezi zinaonekera bwino pamene panaikidwa lamulo loti anthu asamayendeyende pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Mu 2020, pamene mafakitale ndi magalimoto zinasiya kutulutsa mpweya woipa, mpweya mumlengalenga unayamba kukhala wabwino kwambiri. Malinga ndi lipoti lina lomwe linatuluka mu 2020, mayiko oposa 80 peresenti mwa mayiko amene anaika lamulo loti anthu asamayendeyende, anafotokoza kuti anayamba kukhala ndi mpweya wabwino pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anakhazikitsa lamuloli.—2020 World Air Quality Report.
Zimene Anthu Akuchita Kuti Athetsa Vutoli
Maboma akupitiriza kulimbikitsa mafakitale kuti achepetse kuwononga mpweya. Komanso asayansi akupitirizabe kupeza njira zatsopano zothandiza kukonza zinthu zimene anthu aipitsa. Mwachitsanzo, pali njira inayake imene amagwiritsa ntchito mabakiteriya pochotsa zinthu zina zomwe zimakhala m’mankhwala oopsa. Komanso akatswiri ena akulimbikitsa anthu kuti aziyenda wapansi kapena kukwera njinga yakapalasa m’malo moyenda pagalimoto. Akulimbikitsanso anthu kuti asamagwiritse ntchito kwambiri magetsi komanso kuti azigwiritsa ntchito zophikira zamakono.
Koma zimenezi si zokwanira, ndipo zinaonekera bwino mu lipoti lina limene linalembedwa ndi mabungwe akuluakulu padziko lonse, kuphatikizapo Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse ndi World Bank.
Lipotili linanena kuti mu 2020, anthu pafupifupi 2.4 biliyoni padziko lonse ankagwiritsa ntchito njira zowononga mpweya pophika. M’madera ambiri, ndi anthu ochepa okha omwe angakwanitse kupeza zophikira zamakono kapena kumagwiritsa ntchito njira zina zophikira zosawononga chilengedwe.
Kodi Baibulo Limatipatsa Chiyembekezo Chotani?
“Mulungu woona Yehova, amene analenga kumwamba ndiponso . . . amene anapanga dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo, amene amapereka mpweya kwa anthu amene ali mmenemo.”—Yesaya 42:5.
Mulungu anapanga mpweya umene timapumawu komanso anakhazikitsa njira zachilengedwe zimene zimayeretsa mpweyawu ngati waipitsidwa ndipo zimenezi zimasonyeza kuti iye ali ndi mphamvu zopanda malire komanso amakonda kwambiri anthu. Ndiye kodi zingakhale zomveka kunena kuti iye sangakwanitse kukonza mpweya umene anthu awononga? Onani nkhani yakuti “Mulungu Akulonjeza Kuti Dzikoli Lidzakhalanso Bwino.”
GALAMUKANI!