GALAMUKANI! Na. 2 2018 | Mfundo 12 Zothandiza Kuti Banja Liziyenda Bwino

Mfundo 12 Zothandiza Kuti Banja Liziyenda Bwino

Nthawi zambiri timamva nkhani zosiyanasiyana zomwe zimasokoneza mabanja. Magaziniyi ikufotokoza zimene anthu ena achita kuti mabanja awo aziyenda bwino.

  • Zaka zapakati pa 1990 ndi 2015, ku United States, chiwerengero cha mabanja omwe anatha chinawirikiza kawiri kwa anthu a zaka zoposa 50 ndipo chinawirikiza katatu kwa anthu a zaka zoposa 65.

  • Makolo ambiri asokonezeka chifukwa akatswiri ena amawauza kuti nthawi zonse aziyamikira ana awo. Pomwe ena amawauza kuti mwana amafunika kumuikira malamulo okhwima.

  • Achinyamata ambiri akukula asanaphunzire luso lililonse lomwe lingadzawathandize m’tsogolo.

Komabe zoona ndi zakuti . . .

  • N’zotheka kukhala ndi banja losangalala komanso kwa moyo wonse.

  • Makolo angakwanitse kulangiza ana awo mwachikondi.

  • Achinyamata akhoza kuphunzira luso linalake lomwe lingadzawathandize akadzakula.

Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Werengani Galamukani! iyi kuti mupeze mfundo 12 zothandiza kuti banja liziyenda bwino.

 

1: Kukhulupirika

Werengani nkhaniyi kuti mupeze zinthu zitatu zomwe zingathandize mwamuna ndi mkazi wake kuti azikondana.

2: Kuchita Zinthu Mogwirizana

Kodi inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu mumangokhala ngati anthu okhalira limodzi basi?

3: Kulemekezana

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mawu abwino omwe mungalankhule komanso zinthu zomwe mungachite kuti mwamuna kapena mkazi wanu azidziwa kuti mumamulemekeza.

4: Kukhululukirana

Kodi mungatani kuti musamaganizire kwambiri zimene mwamuna kapena mkazi wanu amalakwitsa?

5: Kulankhulana

Werengani nkhaniyi kuti mupeze njira zitatu zomwe zingakuthandizeni kuti muzimasukirana ndi ana anu.

6: Kulangiza

Kodi kulangiza mwana kumamuchititsa kudziona ngati wosafunika?

7: Makhalidwe

Kodi muyenera kuphunzitsa ana anu makhalidwe otani?

8: Kupereka Chitsanzo

Kuti ana anu azitsatira zimene mumawaphunzitsa, zimene mumanena zizigwirizana ndi zimene mumachita.

9: Mbiri Yanu

Kodi achinyamata angatani kuti azilimba mtima kufotokoza zimene amakhulupirira?

10: Kukhulupirika

Ngati mumachita bwino zinthu ndipo makolo anu amakudalirani, zidzakuthandizani mukadzakula.

11: Kulimbikira Ntchito

Mukaphunzira kugwira ntchito mwakhama panopo, zinthu zidzakuyenderani bwino mukadzakhala panokha.

12: Kukhala ndi Zolinga

Mukakwaniritsa zolinga zanu, mumalimba mtima. Zimathandizanso kuti anzanu azikudalirani komanso mumakhala osangalala.

Mfundo Zina Zothandiza Mabanja

Mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kukhala ndi banja losangalala.