ACHINYAMATA

10: Kukhulupirika

10: Kukhulupirika

ZIMENE ZIMACHITIKA

Anthu amene ndi okhulupirika amakhala odalirika kwa makolo, anzawo komanso kwa mabwana awo. Amatsatira malamulo, amakwaniritsa zomwe alonjeza ndipo amalankhula zoona nthawi zonse.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUGANIZIRA NKHANIYI N’KOFUNIKA?

Nthawi zambiri anthu amene akhala okhulupirika kwa nthawi yaitali ndi amenenso amapatsidwa ufulu wambiri.

Sarahi ananena kuti: “Makolo amakudalira kwambiri ngati nthawi zonse umachita zinthu ngati munthu wamkulu komanso ngati umachita zinthu moganiza bwino ngakhale pa nthawi imene iwowo kulibe.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.”​—2 Akorinto 13:5.

ZIMENE MUNGACHITE

Ngati mukufuna kuti makolo anu azikukhulupirirani kapena ngati anasiya ndipo mukufuna ayambirenso, mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni.

Muzichita zinthu moona mtima. Anthu amasiya kukukhulupirirani ngati mumakonda kunama. Koma ngati mumavomereza moona mtima mukalakwitsa zinazake, m’pamene amakukhulupirirani kwambiri.

Caiman ananena kuti: “Zimakhala zosavuta kulankhula zoona zinthu zikamayenda bwino. Komabe ngakhale anthu ena atadana nawe chifukwa chochita zinthu mwachilungamo, ambiri amakuonabe kuti ndiwe wodalirika.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheberi 13:18.

Muzikhala odalirika. Pa kafukufuku wina amene anachitika ku United States, anapeza kuti mabwana 78 pa 100 alionse, amaona kuti munthu amafunika kukhala wodalirika kuti amulembe ntchito. Mukamayesetsa kukhala wodalirika panopa, zidzakuthandizani mukadzakula.

Sarah ananena kuti: “Makolo anga amasangalala kwambiri ndikayamba kugwira ntchito za pakhomo popanda wina kundikumbutsa. Ndikamachita zimenezi, amandidalira kwambiri.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Ndikukulembera kalatayi pokhulupirira kuti uchita zimenezi. Ndikudziwa kuti uchita ngakhale zoposa zimene ndanenazi.”​—Filimoni 21.

Muzikhala woleza mtima. Munthu akamakula, anthu amaona ndithu kuti akukula. Koma pamatenga nthawi kuti anthu aone kuti wayamba kuchita zinthu mwanzeru komanso moganiza bwino.

Brandon ananena kuti: “Sizingachitike lero ndi lero kuti makolo ako kapena anzako ayambe kukukhulupirira. Pamafunika kuleza mtima komanso nthawi yokwanira kuti zimenezi zitheke.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Valani . . . kuleza mtima.”​—Akolose 3:12.