M’banja limene mwamuna kapena mkazi ndi wosakhulupirika, akakumana ndi mavuto amangoti, ‘tinakumana okulakula.’ Ndipo zikatero amafunafuna njira zothetsera banjalo.
A Jean ananena kuti: “Anthu ambiri amalowa m’banja ali ndi maganizo akuti adzathetsa banjalo zinthu zikadzavuta. Munthu akalowa m’banja ali ndi maganizo amenewo zimakhala zovuta kuti akhale wokhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wake.”
ZIMENE MUNGACHITE
DZIFUNSENI KUTI
Tikasemphana maganizo . . .
Kodi ndimaona kuti ndinalakwitsa kukwatirana ndi mwamuna kapena mkazi wangayu?
Kodi ndimaganiza kuti nthawi ina ndikhoza kudzakwatirana ndi mwamuna kapena mkazi wina?