Kudziwa munthu sikutanthauza kungomudziwa dzina kapena maonekedwe ake. Koma zimakhudza mbiri yomwe munthuyo ali nayo pa nkhani ya khalidwe lake, zimene amakhulupirira komanso mmene amachitira zinthu ndi ena.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Koma aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera ndi munthu wina.”—Agalatiya 6:4.
Zimene mumalephera: Kodi ndi zinthu ziti zomwe ndikufunika kuyesetsa kukonza? Kodi ndi nthawi iti imene ndimayesedwa kuti ndichite zoipa? Kodi ndiyenera kukhala wodziletsa kwambiri pa zinthu ziti?
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Tikanena kuti: ‘Tilibe uchimo,’ ndiye kuti tikudzinamiza ndipo mwa ife mulibe choonadi.”—1 Yohane 1:8.