Kodi Mungafufuze Bwanji? YAMBANI Kodi Mungafufuze Bwanji? Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu “Zinthu za m’chilengedwe zinangokhalapo zokha.”—Anatero akatswiri a sayansi Stephen Hawking ndi Leonard Mlodinow, mu 2010. “Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Limatero Baibulo pa Genesis 1:1. Kodi chilengedwechi komanso zamoyo, zinachita kulengedwa ndi Mulungu kapena zinangokhalapo zokha? Mawu ali pamwambawa a akatswiri awiri asayansi komanso mawu oyambirira a m’Baibulo, akusonyeza kuti funsoli lili ndi mayankho awiri osiyana kwambiri. Yankho lililonse lili ndi anthu amene amaliikira kumbuyo. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri sadziwa zimene ayenera kukhulupirira. Anthu akhala akupereka maganizo osiyanasiyana kudzera m’mabuku otchuka komanso mitsutso. N’kutheka kuti aphunzitsi anu anakutsimikizirani kuti zinthu zonse m’chilengedwechi, zinangokhalapo zokha ndipo sizinachite kulengedwa. Koma kodi aphunzitsi anuwo anaperekadi umboni wosonyeza kuti kulibe Mlengi? Komanso n’kutheka kuti munamvapo atsogoleri a chipembedzo akunena kuti kuli Mlengi, koma kodi anakupatsani umboni wa zimene ankanenazo? Kapena anangokuuzani kuti muzikhulupirira chifukwa chakuti ndi zimene amaphunzitsa? N’zosakayikitsa kuti munadzifunsapo funso limeneli ndipo mwina mumaona kuti palibe amene anganene motsimikiza kuti kuli Mlengi. N’kutheka kuti mumakhalanso ndi funso lina lakuti: Kodi kupeza yankho lake n’kofunikiradi? Magazini ya Galamukani! ino, ifotokoza zimene zachititsa anthu ambiri kukhulupirira kuti kuli Mlengi. Ifotokozanso chifukwa chake n’zofunika kudziwa yankho la funso lakuti, kodi moyo unayamba bwanji padziko lapansili? Yam'mbuyo Yotsatira Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO Kodi Mulungu Anasintha Zamoyo Zina Polenga Mitundu Inanso ya Zamoyo? Baibulo silitsutsa zimene asayansi amanena zoti mitundu ya zamoyo imatulutsanso zamoyo zina zofanana ndi zamtundu womwewo. ZOKHUDZA IFEYO Pemphani Kuti Tidzakuyendereni Mutha kukhala ndi mwayi wokambirana nkhani inayake ya m’Baibulo kapena kudziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova. Sindikizani Patsani ena Patsani ena Kodi Mungafufuze Bwanji? GALAMUKANI! Kodi Mungafufuze Bwanji Mfundo Zokuthandizani Kukhulupirira Ngati Kuli Mlengi? Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kodi Mungafufuze Bwanji Mfundo Zokuthandizani Kukhulupirira Ngati Kuli Mlengi? https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/102021083/univ/art/102021083_univ_sqr_xl.jpg g21.3