Zamoyo zimaoneka kuti zinachita kupangidwa. Zinthu zamoyo zinapangidwa ndi tinthu tina ting’onoting’ono totchedwa maselo. Selo lililonse limachita zinthu zambirimbiri kuti zinthu zamoyo zipitirizebe kukhala ndi moyo komanso kuti ziswane. Zimenezi zimachitika ngakhale ndi zamoyo zina zomwe ndi zazing’ono kwambiri. Mwachitsanzo, taganizirani za yisiti amene amagwiritsidwa ntchito mu zinthu ngati mandasi kuti afufume, yemwe ndi kanthu kakang’ono kwambiri. Selo la yisiti silogometsa kwambiri poyerekezera ndi selo limene limakhala m’thupi mwa munthu. Ngakhale zili choncho palokha limachita zinthu modabwitsa kwambiri. Mu selo lililonse, mumakhala DNA. Selo lililonse limagaya chakudya chimene chimathandiza kuti selolo lipitirizebe kukhala ndi moyo. Ngati chakudya chake chayamba kuchepa, selolo limasiya kuchita zinthu zina ndipo limakhala ngati lagona. N’chifukwa chake yisiti amatha kusungidwa kwa nthawi yaitali, n’kudzagwiritsidwanso ntchito bwinobwino.
Asayansi akhala akufufuza za maselo a yisiti kwa zaka zambiri n’cholinga choti adziwe zokhudza maselo a anthu. Komatu pali zambiri zimene sazimvetsa. Pulofesa wina dzina lake Ross King wa ku yunivesite ya Chalmers ku Sweden, ananena kuti: “Pali akatswiri ochepa omwe angamafufuze zinthu zonse zomwe timafunikira kuti tidziwe mmene zinthu ngati yisiti zimagwirira ntchito.”
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti selo la yisiti lizigwira ntchito mogometsa chonchi, kapena linachita kulengedwa?
Moyo umachokera ku zinthu zamoyo. DNA imapangidwa ndi timamolekyu ting’onoting’ono totchedwa manyukiliyotaidi. Selo lililonse la munthu lili ndi manyukiliyotaidi okwana 3.2 biliyoni. Timamolekyu timeneti, tinayalidwa mu ndondomeko yapadera kuti selo lizitha kupanga mapulotini komanso timadzi tinatake.
Zoona zake n’zakuti asayansi sanapangepo chinthu chamoyo kuchokera ku chinthu chopanda moyo.
Anthufe ndi apadera. Monga anthu, tili ndi makhalidwe amene amatithandiza kuti tizisangalala kwambiri ndi moyo kuposa chamoyo chilichonse. Tili ndi maluso osiyanasiyana, timakhala bwino ndi anthu ena komanso timasonyezana chikondi. Timatha kumva kakomedwe ka zakudya, fungo, timaphokoso komanso timatha kuona mitundu yosiyanasiyana ya zinthu. Timakonza mapulani a zinthu zam’tsogolo komanso timafufuza cholinga cha moyo.
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti tikhale ndi makhalidwe amenewa chifukwa chakuti ndi ofunika kuti tizitha kukhala ndi moyo komanso kuberekana? Kapena kodi zimasonyeza kuti moyo ndi mphatso yochokera kwa Mlengi wachikondi?