NKHANI YOPHUNZIRA 15

NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse

Muzikhulupirira Kwambiri Gulu la Yehova

Muzikhulupirira Kwambiri Gulu la Yehova

“Muzikumbukira amene akukutsogolerani. Amenewa anakuphunzitsani mawu a Mulungu.”​—AHEB. 13:7.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona zimene tingachite kuti nthawi zonse tizikhulupirira gulu la Yehova.

1. Kodi anthu a Yehova a munthawi ya atumwi ankachita bwanji zinthu?

 YEHOVA akapereka ntchito kwa anthu amayembekezera kuti aigwire mwadongosolo. (1 Akor. 14:33) Mwachitsanzo, Mulungu amafuna kuti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse lapansi kumene kuli anthu. (Mat. 24:14) Yehova anasankha Yesu kuti azitsogolera ntchito imeneyi. Ndipo Yesu akuonetsetsa kuti ntchitoyi izigwiridwa mwadongosolo. Mu nthawi ya atumwi pamene mipingo inkakhazikitsidwa, akulu ankaikidwa kuti azipereka malangizo komanso azitsogolera. (Mac. 14:23) Ku Yerusalemu kunali bungwe limene linapangidwa ndi atumwi ndi akulu ndipo linkapereka malangizo amene mipingo yonse inkayenera kutsatira. (Mac. 15:2; 16:4) Chifukwa chomvera malangizo amene ankapatsidwa, “anthu m’mipingo anapitiriza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndipo chiwerengero chinkawonjezeka tsiku ndi tsiku.”​—Mac. 16:5.

2. Kungoyambira mu 1919, kodi Yehova wakhala akutsogolera bwanji anthu ake komanso kuwapatsa chakudya chauzimu?

2 Masiku anonso Yehova akupitiriza kutsogolera anthu ake. Kuyambira mu 1919, Yesu wakhala akugwiritsa ntchito kagulu ka abale odzozedwa kuti azitsogolera ntchito yolalikira komanso kupereka chakudya chauzimu kwa otsatira ake. a (Luka 12:42) Ndipo zikuonekeratu kuti Yehova akudalitsa ntchito yawo.​—Yes. 60:22; 65:13, 14.

3-4. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza mmene timapindulira tikamachita zinthu mwadongosolo. (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Tikanakhala kuti sitichita zinthu mwadongosolo sitikanakwanitsa kugwira ntchito imene Yesu watipatsa. (Mat. 28:19, 20) Mwachitsanzo, zikanakhala kuti kulibe magawo, bwenzi aliyense akulalikira kulikonse kumene akufuna. Magawo ena bwenzi akulalikidwa mobwerezabwereza ndi ofalitsa osiyanasiyana pomwe ena akanangosiyidwa. Kodi mukuganiza kuti kuchita zinthu mwadongosolo kumatithandizanso m’njira ziti?

4 Yesu ali padzikoli ankathandiza otsatira ake kuchita zinthu mwadongosolo ndipo akupitirizabe kuchita zimenezi masiku ano. Munkhaniyi tikambirana chitsanzo cha Yesu komanso zimene gulu lathu limachita potengera chitsanzo chake. Tikambirananso mmene tingasonyezere kuti timakhulupirira gulu la Yehova.

GULU LATHU LIMATENGERA CHITSANZO CHA YESU

5. Kodi ndi njira imodzi iti yomwe timatsanzirira Yesu? (Yohane 8:28)

5 Yesu anaphunzira kwa Atate ake akumwamba zoyenera kuchita komanso kulankhula. Potengera chitsanzo cha Yesu, gulu la Yehova limagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pophunzitsa anthu kuti adziwe zoyenera ndi zosayenera komanso popereka malangizo. (Werengani Yohane 8:28; 2 Tim. 3:16, 17) Nthawi zonse timakumbutsidwa kuti tiziwerenga Mawu a Mulungu komanso kuwatsatira. Kodi kutsatira malangizo amenewa kumatithandiza bwanji?

6. Kodi timapindula m’njira yofunika iti tikamaphunzira Baibulo?

6 Timapindula kwambiri tikamaphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito mabuku athu. Mwachitsanzo, timatha kuyerekezera zimene Baibulo limaphunzitsa ndi malangizo amene gulu limatipatsa. Tikaona kuti malangizo amene timalandira ndi ochokera m’Malemba timayamba kukhulupirira kwambiri gulu la Yehova.​—Aroma 12:2.

7. Kodi Yesu ankalalikira uthenga wotani, nanga gulu la Yehova limamutsanzira bwanji?

7 Yesu ankalalikira “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:43, 44) Yesu analamulanso ophunzira ake kuti azilalikira za Ufumu wa Mulungu. (Luka 9:1, 2; 10:8, 9) Masiku ano, anthu onse amene ali m’gulu la Yehova amalalikira uthenga wa Ufumu posatengera kumene amakhala kapena udindo umene ali nawo m’gululi.

8. Kodi tapatsidwa mwayi wotani?

8 Timaona kuti ndi mwayi waukulu kuuza ena choonadi chokhudza Ufumu wa Mulungu. Koma si aliyense amene ali ndi mwayi wogwira ntchito imeneyi. Mwachitsanzo, Yesu ali padziko lapansi sanalole kuti mizimu yoipa izilalikira za iye. (Luka 4:41) Masiku ano, munthu asanayambe kulalikira ndi anthu a Yehova amafunika kukwaniritsa zinthu zofunikira. Timasonyeza kuti timayamikira mwayi umenewu tikamalalikira kulikonse komanso pa nthawi iliyonse. Mofanana ndi Yesu, cholinga chathu ndi kudzala ndi kuthirira mbewu za choonadi m’mitima ya anthu.​—Mat. 13:3, 23; 1 Akor. 3:6.

9. Kodi gulu la Yehova limathandiza bwanji anthu kuti adziwe dzina la Mulungu?

9 Yesu ankauza anthu za dzina la Mulungu. Popemphera kwa Atate ake akumwamba, Yesu anati: “Ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu.” (Yoh. 17:26) Potengera chitsanzo cha Yesu, gulu la Yehova limachita zonse zimene lingathe pothandiza anthu kuti adziwe dzina la Mulungu. Baibulo la Dziko Latsopano lathandiza kwambiri pa nkhaniyi pobwezeretsa dzina la Mulungu pamalo ake oyenera. Baibuloli, lonse kapena mbali yake, likupezeka m’zilankhulo zoposa 270. Mu Zakumapeto A4 ndi A5 m’Baibuloli, mudzapeza mfundo zokhudza kubwezeretsa dzina la Mulungu m’Baibulo. Zakumapeto C, m’Baibulo Lophunzirira la Chingelezi zikupereka umboni wakuti dzina la Mulungu liyenera kupezeka m’Malemba a Chigiriki a Chikhristu maulendo 237.

10. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene ananena mayi wina amene amakhala ku Myanmar?

10 Mofanana ndi Yesu, tikufuna kuyesetsa mmene tingathere kuphunzitsa anthu ambiri kuti adziwe dzina la Mulungu. Mayi wina wa zaka 67 ku Myanmar atamva dzina la Mulungu anagwetsa misozi n’kunena kuti: “Aka n’koyamba pa moyo wanga kumva kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. . . . Mwandiphunzitsa chinthu chofunika kwambiri.” Zimene zinachitikazi zikusonyeza kuti kuphunzira dzina la Mulungu kungathandize kwambiri anthu a mitima yabwino.

PITIRIZANI KUKHULUPIRIRA GULU LA YEHOVA

11. Kodi akulu angasonyeze bwanji kuti amakhulupirira gulu la Yehova? (Onaninso chithunzi.)

11 Kodi ndi njira imodzi iti imene akulu angasonyezere kuti amakhulupirira gulu la Mulungu? Akalandira malangizo, ayenera kuwawerenga mosamala n’kuyesetsa mmene angathere kuti awatsatire. Mwachitsanzo, kuwonjezera pa kupatsidwa malangizo a mmene angachititsire misonkhano komanso kupemphera, amapatsidwanso malangizo a mmene angasamalirire nkhosa za Khristu. Akulu amene amatsatira malangizo a gulu amathandiza kuti amene akuyang’aniridwawo azimva kuti ndi otetezeka komanso amakondedwa.

Akulu amatithandiza kuti tizikhulupirira malangizo amene gulu la Yehova limatipatsa (Onani ndime 11) b


12. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi anthu amene amatitsogolera? (Aheberi 13:7, 17) (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kumaona makhalidwe abwino a amene amatitsogolera?

12 Tikalandira malangizo ochokera kwa akulu tiyenera kuwatsatira ndi mtima wonse. Tikatero timathandiza akuluwo kuti azigwira bwino ntchito yawo. Baibulo limatilimbikitsa kuti tizimvera komanso kugonjera amene akutitsogolera. (Werengani Aheberi 13:7, 17.) N’chifukwa chiyani zimenezi zimakhala zovuta nthawi zina? Chifukwa chakuti abale amenewa si angwiro. Koma tikamaganizira kwambiri zimene amalakwitsa osati zimene amachita bwino, timakhala tikuthandiza adani athu. Kodi timawathandiza bwanji? Timayamba kukayikira gulu la Mulungu ndipo izi ndi zimene adani athu amafuna kuti tizichita. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizindikire komanso kukana njira zimene adani athu amagwiritsa ntchito?

MUSALOLE KUTI ENA AKULEPHERETSENI KUKHULUPIRIRA GULU LA YEHOVA

13. Kodi adani athu amayesa bwanji kuipitsa mbiri ya gulu la Mulungu?

13 Adani a Mulungu amafuna kuti zinthu zabwino zimene gulu la Mulungu limachita zizioneka ngati zoipa. Mwachitsanzo, timaphunzira kuchokera m’Malemba kuti Yehova amafuna kuti anthu amene amamulambira azikhala aukhondo, amakhalidwe abwino komanso azimulambira m’njira imene amavomereza. Iye amafuna kuti munthu amene amachita makhalidwe oipa ndipo salapa azichotsedwa mumpingo. (1 Akor. 5:11-13; 6:9, 10) Ifeyo timayesetsa kutsatira lamulo la m’Malemba limeneli. Koma adani athu amagwiritsa ntchito zimenezi pofuna kutinena kuti si ife ololera, timaweruza anzathu komanso tilibe chikondi.

14. Kodi ndi ndani amene amayambitsa nkhani zabodza zokhudza gulu la Mulungu?

14 Muzikumbukira kuti amene akutitsutsa ndi Satana. Satana Mdyerekezi ndi amene amayambitsa nkhani zabodza. Iye ndi “tate wake wa bodza.” (Yoh. 8:44; Gen. 3:1-5) Choncho tisamadabwe kuti Satana amagwiritsa ntchito anthu ake pofalitsa nkhani zabodza zokhudza gulu la Yehova. Zoterezi zinachitikanso mu nthawi ya Yesu.

15. Kodi atsogoleri a chipembedzo anamuchitira chiyani Yesu komanso ophunzira ake?

15 Mu nthawi ya Yesu, anthu otsutsa ankanena zinthu zabodza zokhudza Mwana wa Mulungu wangwiro amene ankachita zodabwitsa. Mwachitsanzo, atsogoleri achipembedzo ankauza anthu kuti mphamvu zimene Yesu ankagwiritsa ntchito potulutsa ziwanda anapatsidwa ndi “wolamulira ziwanda.” (Maliko 3:22) Pa nthawi imene ankaimbidwa mlandu, atsogoleri achipembedzo ankanena kuti Yesu ndi wonyoza Mulungu ndipo analimbikitsa anthu kuti iye aphedwe. (Mat. 27:20) Pambuyo pake, pamene otsatira a Khristu ankalalikira uthenga wabwino, anthu otsutsa “anauza zoipa anthu a mitundu ina nʼkuwasokoneza maganizo” kuti azizunza Akhristu. (Mac. 14:2, 19) Pofotokoza lemba la Machitidwe 14:2, Nsanja ya Olonda ya December 1, 1998, inanena kuti: “M’malo mongokana uthengawu, Ayuda otsutsawa anayamba kukopa anthu a mitundu ina kuti azidana ndi Akhristu.”

16. Kodi tizikumbukira chiyani tikamva nkhani zabodza?

16 Satana sanasiye kunena zabodza. Masiku ano, iye “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chiv. 12:9) Mukamva nkhani zoipa zokhudza gulu kapena abale amene akutsogolera, muzikumbukira mmene adani a Mulungu ankachitira ndi Yesu komanso ophunzira ake. Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, masiku anonso anthu a Yehova amazunzidwa komanso kuneneredwa zinthu zabodza. (Mat. 5:11, 12) Nkhani zabodza sizingatisocheretse ngati titazindikira amene akuziyambitsa n’kuchitapo kanthu mwamsanga. Kodi tiyenera kuchita chiyani?

17. Kodi tingatani kuti nkhani zabodza zisatisokoneze? (2 Timoteyo 1:13) (Onaninso bokosi lakuti “ Zimene Tingachite Tikamva Nkhani Zabodza.”)

17 Musamamvere nkhani zabodza. Mtumwi Paulo anafotokoza momveka bwino zimene tingachite ngati titamva nkhani zabodza. Iye anauza Timoteyo kuti ‘aletse anthu ena . . . kuti asamamvere nkhani zonama’ komanso kuti ‘azipewa nkhani zonama zosalemekeza Mulungu.’ (1 Tim. 1:3, 4; 4:7) Mwana akhoza kutola chinthu pansi n’kuika mkamwa. Koma munthu wamkulu, amene amazindikira kuopsa kwake sangachite zimenezo. Timakana nkhani zabodza chifukwa timadziwa amene amaziyambitsa. Choncho timagwiritsitsa “mawu olondola” a choonadi.​—Werengani 2 Timoteyo 1:13.

18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira gulu la Yehova?

18 Tangokambirana njira zitatu za mmene gulu la Mulungu limatsanzirira Yesu. Mukamaphunzira Baibulo, muziona njira zinanso za mmene gulu la Mulungu limamutsanzirira. Muzithandiza anthu ena mumpingo wanu kuti azikhulupirira gulu la Mulungu. Pitirizani kusonyeza kuti mumalikhulupirira potumikira Yehova mokhulupirika, komanso kukhalabe mbali ya gulu limene akuligwiritsa ntchito pokwaniritsa cholinga chake. (Sal. 37:28) Tiyeni tiziyamikira mwayi wokhala m’gulu la Yehova la anthu achikondi komanso okhulupirika.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi anthu a Mulungu amatsanzira Yesu m’njira ziti?

  • Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira gulu la Yehova?

  • Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tamva nkhani zabodza?

NYIMBO NA. 103 Abusa Ndi Mphatso za Amuna

b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pambuyo poti akulu akambirana mmene angachitire ulaliki wa pamalo opezeka anthu ambiri, woyang’anira kagulu akupereka malangizo kwa ofalitsa oti aziima ndi kashelefu kawo pafupi ndi khoma.