NKHANI YOPHUNZIRA 14
NYIMBO NA. 56 Inuyo Panokha Muzikonda Kwambiri Choonadi
‘Tiyesetse Mwakhama Kuti Tikhale Aakulu Mwauzimu’
“Tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale aakulu mwauzimu.”—AHEB. 6:1.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tiphunzira mmene Mkhristu wamkulu mwauzimu amaganizira komanso mmene amachitira zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna kuti azisankha zochita mwanzeru.
1. Kodi Yehova amafuna kuti tizichita chiyani?
KUBADWA kwa mwana kumakhala chimodzi mwa zinthu zosangalatsa kwambiri kwa makolo ake. Ngakhale kuti makolo amakonda kwambiri mwana wawo wakhanda, safuna kuti azingokhalabe choncho mpaka kalekale. Ndipotu angadandaule kwambiri ngati mwanayo sakukula. Mofanana ndi zimenezi, Yehova amasangalala tikayamba kutsatira Yesu, koma iye safuna kuti tizingokhala ana mwauzimu. (1 Akor. 3:1) M’malomwake amafuna kuti tikhale Akhristu aakulu mwauzimu.—1 Akor. 14:20.
2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
2 Kodi kukhala Mkhristu wamkulu mwauzimu kumatanthauza chiyani? Kodi tingatani kuti tikule mwauzimu? Kodi chakudya chotafuna ndi chofunika bwanji kuti tikule mwauzimu? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kudzidalira? Munkhaniyi tikambirana mayankho a mafunso amenewa.
KODI KUKHALA MKHRISTU WAMKULU MWAUZIMU KUMATANTHAUZA CHIYANI?
3. Kodi kukhala Mkhristu wolimba kumatanthauza chiyani?
3 M’Baibulo, mawu amene anamasuliridwa kuti anthu “akuluakulu,” angatanthauzenso anthu okhwima kapena “olimba mwauzimu.” a (1 Akor. 2:6) Mofanana ndi mwana amene amapitiriza kukula mpaka atakhala wamkulu, ifenso tiyenera kupitiriza kukula mwauzimu mpaka titakhala Akhristu olimba. Koma ngakhale titafika pamenepo sitiyenera kusiya kupita patsogolo. (1 Tim. 4:15) Mkhristu aliyense ngakhale wamng’ono akhoza kukhala wolimba mwauzimu. Koma kodi n’chiyani chimene chimasonyeza kuti Mkhristu ndi wolimba mwauzimu?
4. Kodi tingadziwe bwanji Mkhristu wolimba mwauzimu?
4 Mkhristu wolimba mwauzimu amatsatira mfundo zonse za Mulungu osati kusankha zina zimene akufuna kutsatira. N’zoona kuti monga munthu yemwe si wangwiro angamalakwitse zinthu zina. Koma tsiku lililonse amayesetsa kuti aziganiza komanso kuchita zinthu zimene Yehova amafuna. Iye amavala umunthu watsopano ndipo amayesetsa kuti maganizo ake azifanana kwambiri ndi maganizo a Mulungu. (Aef. 4:22-24) Amadziphunzitsa kuti azisankha zochita mwanzeru potsatira malamulo a Yehova ndi mfundo zake. Choncho samafunika malamulo ambirimbiri omuuza zochita. Akasankha zochita, amayesetsa kuti akwaniritse zimene wasankhazo.—1 Akor. 9:26, 27.
5. Kodi Mkhristu yemwe si wolimba mwauzimu angakumane ndi mavuto otani? (Aefeso 4:14, 15)
5 Koma munthu amene sakukula mwauzimu, akhoza kukhulupirira mosavuta zinthu zachinyengo zimene zimafalitsidwa komanso mabodza ndipo angapusitsidwenso ndi ampatuko. b (Werengani Aefeso 4:14, 15.) Iye akhoza kumachitira nsanje anthu ena, kukangana nawo, kapena kukwiya msanga ndipo nthawi zambiri akhoza kuchita zoipa ngati wayesedwa.—1 Akor. 3:3.
6. Kodi kukula mwauzimu tingakuyerekeze ndi chiyani? (Onaninso chithunzi.)
6 Monga tanenera kale, Malemba amayerekezera kukula mwauzimu ndi mmene mwana amakulira n’kukhala munthu wamkulu. Mwana sadziwa zinthu zambiri choncho amafunika munthu wamkulu kuti azimutsogolera komanso kumuteteza. Mwachitsanzo, mayi akhoza kugwira mkono wa mwana wake wamng’ono kuti adumphe msewu. Koma mwana uja akamakula, mayi akhoza kumulola kuti adutse yekha koma angamamukumbutse kuti aziyang’ana mbali zonse asanadutse. Ndiyeno mwanayo akakula amachita zinthu ngati zimenezi payekha. Mofanana ndi mwana amene amafunika munthu wamkulu kuti azimuthandiza kupewa zinthu zoopsa, Akhristu omwe si olimba mwauzimu amafunika Akhristu olimba mwauzimu kuti aziwathandiza kupewa zinthu zimene zingawononge ubwenzi wawo ndi Yehova komanso kuti azisankha zochita mwanzeru. Koma mosiyana ndi zimenezi, Mkhristu wolimba mwauzimu akafuna kusankha zochita, amaganizira mfundo za m’Baibulo kuti adziwe maganizo a Yehova pa nkhaniyo ndipo amachita zinthu zoyenera.
7. Kodi Akhristu olimba mwauzimu amafunika kuthandizidwa ndi ena?
7 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mkhristu wolimba mwauzimu samafunikira kuthandizidwa ndi wina aliyense? Ayi. Nthawi zina anthu olimba mwauzimu amafunikiranso kuthandizidwa. Kungoti munthu amene ndi mwana mwauzimu angayembekezere kuti anthu ena azimuuza kapena kumusankhira zochita pa nkhani zimene anafunika kusankha yekha. Pomwe Mkhristu wolimba mwauzimu akapempha anthu ena anzeru kapena odziwa zambiri kuti amuthandize, amadziwa kuti udindo wosankha zochita ndi wake chifukwa aliyense ayenera “kunyamula katundu wake.”—Agal. 6:5.
8. Kodi Akhristu olimba mwauzimu amasiyana m’njira ziti?
8 Anthu akuluakulu amaoneka mosiyana. Mofanana ndi zimenezi, Akhristu olimba mwauzimu amasiyananso pa nkhani ya makhalidwe monga nzeru, kulimba mtima, kupatsa komanso kuganizira ena. Kuwonjezera pamenepo, Akhristu awiri olimba mwauzimu akakumana ndi zinthu zofanana akhoza kusankha zinthu zosiyana koma zonse zili zogwirizana ndi mfundo za m’Malemba. Zimenezi zimachitika makamaka pa nkhani zokhudza chikumbumtima. Chifukwa chozindikira mfundo imeneyi, iwo saweruza ena akaona kuti asankha mosiyana. Chimene amafuna kwambiri n’kukhalabe ogwirizana.—Aroma 14:10; 1 Akor. 1:10.
KODI TINGATANI KUTI TIKHALE AAKULU MWAUZIMU?
9. Kodi kukula mwauzimu kumangochitika pakokha? Fotokozani.
9 Pakapita nthawi, mwana amakula n’kukhala munthu wamkulu koma kukula mwauzimu sikumachitika pakokha. Chitsanzo ndi zomwe zinachitikira abale a ku Korinto. Iwo analandira uthenga wabwino, anabatizidwa, analandira mzimu woyera ndipo anaphunzira zambiri kuchokera pa malangizo a mtumwi Paulo. (Mac. 18:8-11) Komabe ngakhale kuti panali patapita zaka zambiri kuchokera pamene anabatizidwa, ambiri anali adakali osalimba mwauzimu. (1 Akor. 3:2) Kodi tingatani kuti zangati zimenezi zisatichitikire?
10. Kodi tingatani kuti tikhale aakulu mwauzimu? (Yuda 20)
10 Kuti tifike pokhala aakulu mwauzimu, choyamba tiyenera kukhala ndi mtima wofuna kukhala olimba mwauzimu. Anthu amene amasankha kukhala “osadziwa zinthu” n’kumangokhalabe makanda mwauzimu, sapita patsogolo. (Miy. 1:22) Sitikufuna kukhala ngati anthu akuluakulu amene amadalirabe makolo awo kuti aziwasankhira zochita. M’malomwake timaonetsetsa kuti tikupitirizabe kukula mwauzimu. (Werengani Yuda 20.) Ngati mukuchita khama kuti mukule mwauzimu, muzipempha Yehova kuti akupatseni “mtima wofuna kuchita zinthu zimene iye amakonda komanso mphamvu zochitira zinthuzo.”—Afil. 2:13.
11. Kodi ndi zinthu ziti zimene Yehova watipatsa kuti zitithandize kukula mwauzimu? (Aefeso 4:11-13)
11 Yehova sayembekezera kuti tizikula tokha mwauzimu. Choncho watipatsa abusa ndi aphunzitsi mumpingo, omwe anaphunzitsidwa bwino kuti azithandiza munthu aliyense n’cholinga choti akhale ‘wachikulire’ mwauzimu n’kufika “pa msinkhu wa munthu wamkulu ngati mmene Khristu analili.” (Werengani Aefeso 4:11-13.) Yehova amatipatsanso mzimu woyera kuti uzitithandiza kukhala ndi “maganizo a Khristu.” (1 Akor. 2:14-16) Komanso Mulungu anauzira anthu kuti alembe mabuku 4 a Uthenga Wabwino kuti atisonyeze mmene Yesu ankachitira zinthu ali padziko lapansi, mmene ankaganizira komanso mmene ankalankhulira. Tikamatsanzira kaganizidwe ka Yesu komanso mmene ankachitira zinthu, tingakhale Akhristu olimba mwauzimu.
MMENE CHAKUDYA CHOTAFUNA CHINGATITHANDIZIRE
12. Kodi “mfundo zoyambirira zokhudza Khristu” ndi ziti?
12 Kuti tikule mwauzimu tiyenera kuphunzira zambiri osati chabe “mfundo zoyambirira zokhudza Khristu.” Chitsanzo cha mfundo zoyambirirazi ndi nkhani yokhudza kulapa, chikhulupiriro, ubatizo ndi kuuka kwa akufa. (Aheb. 6:1, 2) Zimenezi ndi zina mwa mfundo zoyambirira zimene Akhristu amazikhulupirira. N’chifukwa chake mtumwi Petulo anafotokoza mfundo zimenezi pamene ankalalikira gulu limene linasonkhana pa Pentekosite. (Mac. 2:32-35, 38) Tiyenera kuvomereza mfundo zoyambirira zimenezi kuti tikhale ophunzira a Khristu. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anachenjeza kuti munthu aliyense amene amakana chiphunzitso cha kuuka kwa akufa wakana zinthu zonse zimene Akhristu amakhulupirira. (1 Akor. 15:12-14) Koma sitiyenera kukhala okhutira ndi mfundo zoyambirira zokha za choonadi.
13. Kodi tingatani kuti tizipindula ndi chakudya chotafuna chotchulidwa pa Aheberi 5:14? (Onaninso chithunzi.)
13 Mosiyana ndi mfundo zoyambirira, chakudya chotafuna chimaphatikizapo malamulo a Yehova komanso mfundo zake zimene zimatithandiza kumvetsa maganizo ake. Kuti tipindule ndi chakudya chotafunachi, tiyenera kuphunzira Mawu a Mulungu, kuwaganizira mozama komanso kuwagwiritsira ntchito pa moyo wathu. Tikamachita zimenezi timaphunzira kusankha zinthu zimene zingasangalatse Yehova. c—Werengani Aheberi 5:14.
14. Kodi Paulo anathandiza bwanji Akhristu a ku Korinto kuti akule mwauzimu?
14 Akhristu osakhwima mwauzimu amavutika pakachitika nkhani imene ikufuna kuganizira mfundo za m’Baibulo n’kuzitsatira. Anthu ena amaganiza kuti ngati palibe lamulo la m’Baibulo pa nkhani inayake ndiye kuti akhoza kuchita zilizonse zimene akufuna. Ena amafuna kuti achite kupatsidwa lamulo pa nkhani zimene palibe lamulo. Mwachitsanzo, zikuoneka kuti Akhristu a ku Korinto ankafuna kuti Paulo awaikire lamulo pa nkhani ya chakudya chimene chaperekedwa ku mafano. M’malo mongowauza zochita, Paulo anawafotokozera kuti aliyense ali ndi ‘ufulu wosankha’ mogwirizana ndi chikumbumtima chake. Iye anakambirana nawo mfundo zimene zingathandize kuti chikumbumtima cha aliyense chisamamuvutitse komanso asamakhumudwitse ena. (1 Akor. 8:4, 7-9) Choncho Paulo anathandiza Akhristu a ku Korinto kuti akule mwauzimu n’cholinga choti azigwiritsa ntchito luso lawo la kuganiza m’malo modalira anthu ena kapena kumafuna kuti pa nkhani iliyonse pakhale lamulo.
15. Kodi Paulo anathandiza bwanji Akhristu a Chiheberi kuti akhale olimba mwauzimu?
15 Tikuphunziranso mfundo ina yofunika pa mawu amene Paulo analembera Akhristu a Chiheberi. Ena mwa Akhristuwa sanapitirize kukula mwauzimu. Iwo ‘anayambanso kufuna mkaka osati chakudya [chauzimu] chotafuna.’ (Aheb. 5:12) Iwo sanaphunzire komanso kuvomereza mfundo zatsopano zimene Yehova ankawaphunzitsa kudzera mumpingo. (Miy. 4:18) Mwachitsanzo, Akhristu ambiri a Chiyuda ankalimbikitsabe Chilamulo cha Mose ngakhale kuti chilamulocho chinali chitathetsedwa zaka 30 m’mbuyomo chifukwa cha nsembe ya Khristu. (Aroma 10:4; Tito 1:10) Zaka 30 zinali zokwanira kuti Akhristu amvetse mfundo yakuti sayeneranso kutsatira Chilamulo. Aliyense amene angawerenge kalata imene Paulo analembera Akhristu a Chiheberi akhoza kuvomereza kuti m’bukuli muli chakudya chauzimu chotafuna. Mfundozi ndi zimene iwo ankafunikira kuti azikhulupirira kuti njira yolambirira ya Akhristu ndi yapamwamba. Zikanawathandizanso kuti azilalikira molimba mtima ngakhale kuti ankatsutsidwa ndi Ayuda.—Aheb. 10:19-23.
MUZIPEWA KUDZIDALIRA
16. Kuwonjezera pa kukula mwauzimu kodi tiyeneranso kuchita chiyani?
16 Sikuti tizingoyesetsa kuti tikule mwauzimu koma tiziyesetsanso kuti tikhalebe aakulu mwauzimu. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kupewa kudzidalira. (1 Akor. 10:12) Tifunika “kupitiriza kudziyesa” kuti tione ngati tikupitabe patsogolo.—2 Akor. 13:5.
17. Kodi kalata imene Paulo analembera Akhristu a ku Kolose imasonyeza bwanji kufunika kopitirizabe kukhala olimba mwauzimu?
17 M’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Kolose, Paulo anatsindika kufunika kokhalabe olimba mwauzimu. Ngakhale kuti iwo anali aakulu kale mwauzimu, Paulo anawachenjeza kuti asapusitsidwe ndi nzeru za anthu. (Akol. 2:6-10) Epafura, yemwe zikuoneka kuti ankawadziwa bwino anthu a mumpingomo, ankawapempherera nthawi zonse kuti “apitirize kukhala olimba mwauzimu.” (Akol. 4:12) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Paulo ndi Epafura ankadziwa kuti pamafunika khama komanso kuthandizidwa ndi Mulungu kuti munthu akhalebe wolimba mwauzimu. Iwo ankafuna kuti Akhristu a ku Kolose akhalebe olimba mwauzimu ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto.
18. Kodi n’chiyani chingachitikire Mkhristu wolimba mwauzimu? (Onaninso chithunzi.)
18 Paulo anachenjeza Akhristu a Chiheberi kuti munthu wolimba mwauzimu akhoza kusokonezeratu ubwenzi wake ndi Mulungu. Ngati Mkhristuyo atakhala wamakani sangalape kuti Mulungu amukhululukire. Chosangalatsa n’chakuti Akhristu a Chiheberi sanafike pamenepo. (Aheb. 6:4-9) Nanga bwanji za anthu amene afooka masiku ano, kapena amene anachotsedwa koma kenako analapa? Kulapa kwawo komanso kudzichepetsa zimasonyeza kuti iwo sali ngati anthu amene Paulo anawafotokoza kuti angasokonezeretu ubwenzi wawo ndi Yehova. Komabe anthuwo akabwerera kwa Yehova amafunika kuthandizidwa. (Ezek. 34:15, 16) Akulu angakonze zoti Mkhristu wodziwa zambiri awathandize kuti apezenso mphamvu mwauzimu.
19. Kodi tiyenera kukhala ndi cholinga chotani?
19 Ngati mukuyesetsa kuti mukhale Mkhristu wolimba mwauzimu mukhoza kukwaniritsa zolinga zanuzo. Pitirizani kudya chakudya chotafuna komanso kuyesetsa kuti maganizo anu azifanana kwambiri ndi maganizo a Yehova. Ngati ndinu Mkhristu wolimba mwauzimu, yesetsani kuti mukhalebe choncho mpaka kalekale.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
-
Kodi kukula mwauzimu kumatanthauza chiyani?
-
Kodi tingatani kuti tikule mwauzimu?
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kudzidalira?
NYIMBO NA. 65 Pita Patsogolo
a Ngakhale kuti m’Malemba a Chiheberi mawu akuti “wolimba” kapena “wosalimba” sapezekamo, mfundo yake imapezekamo. Mwachitsanzo, buku la Miyambo limasiyanitsa munthu yemwe ndi wamng’ono ndiponso wosadziwa zinthu ndi munthu wanzeru yemwe ndi womvetsa zinthu.—Miy. 1:4, 5.
b Onani nkhani yakuti “Samalani Kuti Musamapusitsike ndi Nkhani Zabodza” pa gawo lakuti “Nkhani Zina” pa jw.org ndi pa JW Library.
c Onani nkhani yakuti “Zoti Ndiphunzire” m’magaziniyi.
d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akugwiritsa ntchito mfundo zimene waphunzira m’Mawu a Mulungu posankha zosangalatsa.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA