NKHANI YOPHUNZIRA 16
NYIMBO NA. 64 Tizigwira Ntchito Yokolola Mosangalala
Zimene Tingachite Kuti Tizisangalala Kwambiri Tikamalalikira
“Tumikirani Yehova mokondwera.”—SAL. 100:2.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Nkhaniyi itithandiza kuona zimene tingachite kuti tizisangalala kwambiri tikamagwira ntchito yolalikira.
1. Kodi anthu ena amamva bwanji akaganizira zolalikira uthenga wabwino? (Onaninso chithunzi.)
MONGA anthu a Yehova, timalalikira chifukwa timakonda Atate wathu wakumwamba ndipo timafuna kuthandiza anzathu kuti amudziwe. Ofalitsa ambiri amakonda ntchito yolalikira. Koma ena sasangalala akamagwira ntchitoyi. Chifukwa chiyani? Ena amakhala ndi manyazi komanso amadzikayikira. Enanso zimawavuta kupita kunyumba za anthu asanaitanidwe. Ena amaopa kuti anthu sakawalandira ndipo enanso amaopa kuti zimene angalankhule zingakhumudwitse anzawo. Ngakhale kuti abale ndi alongowa amakonda kwambiri Yehova, zimawavuta kuyamba kulankhula ndi anthu za uthenga wabwino. Komabe, iwo nthawi zonse amagwira nawo ntchitoyi chifukwa amadziwa kuti ndi yofunika kwambiri. Yehovatu amasangalala kwambiri ndi zimenezi.
2. Ngati simukusangalala ndi ntchito yolalikira, n’chifukwa chiyani simuyenera kugwa ulesi?
2 Kodi inunso nthawi zina simumasangalala ndi ntchito yolalikira? Ngati ndi choncho, musataye mtima. Ngati mumadzikayikira, ndi umboni woti ndinu wodzichepetsa ndipo simumafuna kuti anthu aziganizira kwambiri za inuyo komanso simufuna kukangana ndi ena. Ndipotu palibe amene amafuna kukhumudwitsa ena makamaka pamene akuyesetsa kuwachitira zabwino. Atate wanu wakumwamba amadziwa bwino mavuto omwe mumakumana nawo ndipo amafunitsitsa kukuthandizani. (Yes. 41:13) Munkhaniyi tiona zinthu 5 zimene zingakuthandizeni kuthetsa mantha komanso zomwe mungachite kuti muzisangalala mu utumiki.
MUZILOLA KUTI MAWU A MULUNGU AZIKULIMBIKITSANI
3. N’chiyani chinathandiza mneneri Yeremiya kuti azilalikira?
3 Kuyambira kale, Mawu a Mulungu akhala akulimbikitsa atumiki ake kuti athe kugwira ntchito zovuta. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mneneri Yeremiya. Iye ankachita mantha Mulungu atamutuma kuti akalalikire. Yeremiya anati: “Ine sinditha kulankhula chifukwa ndine mwana.” (Yer. 1:6) Ndiye kodi iye anatani kuti asiye kudzikayikira? Anapeza mphamvu kuchokera m’Mawu a Mulungu. Iye anati: “Mawu ake anali ngati moto woyaka umene watsekeredwa mʼmafupa anga, ndipo ndinatopa ndi kudziletsa kuti ndisalankhule.” (Yer. 20:8, 9) Ngakhale kuti Yeremiya ankalalikira m’gawo lovuta, uthenga womwe ankalalikira unamupatsa mphamvu zoti agwirire ntchitoyo.
4. Kodi n’chiyani chimachitika tikamawerenga Mawu a Mulungu komanso kuwaganizira mozama? (Akolose 1:9, 10)
4 Akhristu amapeza mphamvu kuchokera m’Mawu a Mulungu. M’kalata imene analembera Akhristu a ku Kolose, mtumwi Paulo ananena kuti kudziwa zinthu molondola kungalimbikitse abale akewo kuti ‘akhale ndi khalidwe logwirizana ndi zimene Yehova amafuna’ ndiponso kuti ‘apitirize kubala zipatso pantchito iliyonse yabwino.’ (Werengani Akolose 1:9, 10.) Ntchito yabwino imeneyi ikuphatikizapo kulalikira uthenga wabwino. Choncho tikamawerenga Mawu a Mulungu komanso kuwaganizira mozama timayamba kukhulupirira kwambiri Yehova ndiponso timayamba kuona kuti kuuza ena uthenga wabwino n’kofunika kwambiri.
5. Kodi tingatani kuti tizipindula kwambiri tikamawerenga komanso kuphunzira Baibulo?
5 Kuti tizipindula kwambiri ndi Mawu a Mulungu, tiyenera kupewa kuthamanga powerenga, kuphunzira komanso kuganizira zimene tikuwerengazo. Tizidzipatsa nthawi yokwanira. Tikapeza lemba limene sitikulimvetsa, tisamangolidutsa. M’malomwake, tizigwiritsa ntchito Watch Tower Publications Index kapena Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani kuti tidziwe mmene afotokozera lembalo. Tikamakhala ndi nthawi yokwanira pophunzira, tidzayamba kukhulupirira kwambiri kuti Mawu a Mulungu ndi olondola. (1 Ates. 5:21) Ndipo tikamawakhulupirira kwambiri m’pamenenso timasangalala kuuza ena zomwe taphunzira.
MUZIKONZEKERA BWINO UTUMIKI
6. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera bwino zimene tinganene polalikira?
6 Tikakonzekera bwino utumiki zimakhala zosavuta kuti tilankhule ndi anthu. Yesu anathandiza ophunzira ake kuti akonzekere asanawatume kuti akalalikire. (Luka 10:1-11) Popeza anagwiritsa ntchito zimene Yesu anawaphunzitsa, ophunzirawo anasangalala kwambiri chifukwa cha zimene anakwanitsa kuchita.—Luka 10:17.
7. Kodi tingakonzekere bwanji zimene tingakanene mu utumiki? (Onaninso chithunzi.)
7 Kodi tingakonzekere bwanji utumiki? Tiyenera kuganizira mmene tingafotokozere mfundo za choonadi mogwira mtima m’mawu athuathu. Tingachitenso bwino kuganizira zinthu ziwiri kapena zitatu zimene anthu a m’gawo lathu amakonda kunena n’kukonzekera mmene tingawayankhire. Ndiyeno tikamalankhula ndi anthu mtima wathu ukhoza kukhala m’malo, tikhoza kumasekerera komanso kukhala aubwenzi.
8. Kodi Akhristu amafanana bwanji ndi ziwiya zadothi zomwe Paulo anatchula?
8 Mtumwi Paulo anafotokoza za udindo wathu pa ntchito yolalikira, pomwe anati: “Tili ndi chuma chimenechi mʼziwiya zadothi.” (2 Akor. 4:7) Kodi chuma chimenechi n’chiyani? Ndi ntchito yolalikira za Ufumu yomwe ndi yopulumutsa miyoyo. (2 Akor. 4:1) Nanga ziwiya zadothi n’chiyani? Zikuimira atumiki a Mulungu omwe amauza ena uthenga wabwino. M’nthawi ya Paulo, amalonda ankagwiritsa ntchito mitsuko yadothi ponyamula zinthu zofunika monga chakudya, vinyo komanso ndalama. Mofanana ndi zimenezi, Yehova watipatsa uthenga wabwino womwe ndi wamtengo wapatali. Mothandizidwa ndi Yehova, tingathe kupeza mphamvu zomwe timafunikira kuti tipitirize kulalikira uthenga wabwino mokhulupirika.
TIZIPEMPHERA KWA YEHOVA KUTI TIKHALE OLIMBA MTIMA
9. Kodi tingatani kuti tisamaope anthu kapenanso kuopa kuti samvetsera uthenga wathu? (Onaninso chithunzi.)
9 Nthawi zina tikhoza kumaopa anthu kapenanso kuopa kuti akana uthenga wathu. Kodi tingalimbane bwanji ndi vutoli? Taganizirani pemphero limene atumwi anapereka atalamulidwa kuti asiye kulalikira. M’malo mochita mantha n’kusiya, iwo anapempha Yehova kuti awathandize kuti ‘apitirize kulankhula mawu ake molimba mtima.’ Yehova anayankha pemphero lawo nthawi yomweyo. (Mac. 4:18, 29, 31) Ifenso nthawi zina tikayamba kuopa anthu, tiyenera kumapemphera kwa Yehova kuti atithandize. Muzimupempha kuti akuthandizeni kuti muzikonda kwambiri anthu n’cholinga choti musamaope kuwauza uthenga wabwino.
10. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kukwaniritsa udindo wathu monga Mboni zake? (Yesaya 43:10-12)
10 Yehova watisankha kuti tikhale Mboni zake ndipo watilonjeza kuti azitithandiza kukhala olimba mtima. (Werengani Yesaya 43:10-12.) Tiyeni tione njira 4 za mmene amatithandizira. Choyamba, Yesu amakhala nafe tikamalalikira uthenga wabwino. (Mat. 28:18-20) Chachiwiri, Yehova watuma angelo kuti azitithandiza. (Chiv. 14:6) Chachitatu, Yehova watipatsa mzimu woyera womwe umatithandiza kukumbukira zimene tinaphunzira. (Yoh. 14:25, 26) Cha 4, Yehova watipatsa abale ndi alongo omwe timalalikira nawo. Mothandizidwa ndi Yehova komanso abale ndi alongo athu, tili ndi chilichonse chomwe chingatithandize kugwira bwino ntchitoyi.
MUZIKHALA NDI MAGANIZO OYENERA KOMANSO OKONZEKA KUSINTHA
11. Kodi tingatani kuti tizipeza anthu ambiri mu utumiki? (Onaninso chithunzi.)
11 Kodi mumagwa ulesi mukakhala kuti simukupeza anthu m’makomo? Ngati ndi choncho, muzidzifunsa kuti: ‘Kodi panopa anthu ayenera kuti ali kuti?’ (Mac. 16:13) ‘Kodi ali kuntchito kapena kokagula zinthu?’ Zikatero, n’kutheka kuti mungapeze anthu ambiri polalikira mumsewu. M’bale wina dzina lake Joshua ananena kuti, “Ndimapeza mwayi wolalikira ndikamayenda m’mashopu komanso m’malo oimika magalimoto.” Iye ndi mkazi wake Bridget, amapezanso anthu ambiri ali panyumba akalowa mu utumiki chakumadzulo komanso Lamlungu masana.—Aef. 5:15, 16.
12. Kodi tingadziwe bwanji zimene anthu amakhulupirira komanso zomwe zikuwadetsa nkhawa?
12 Ngati anthu sakuchita chidwi ndi uthenga wathu, muziyesa kuganizira zimene amakhulupirira kapenanso zomwe zikuwadetsa nkhawa. Joshua ndi Bridget amakonda kugwiritsa ntchito funso lomwe limakhala patsamba loyamba la kapepala komwe akugawira. Mwachitsanzo, akamagawira kapepala kakuti Kodi Baibulo mumalikhulupirira? Iwo amanena kuti: “Anthu ena amaona kuti Baibulo ndi buku lochokera kwa Mulungu pomwe ena ayi. Inuyo maganizo anu ndi otani?” Zimenezi zimachititsa kuti ayambe kukambirana.
13. N’chifukwa chiyani tiyenera kumasangalalabe ngakhale anthu akane kumvetsera uthenga wathu? (Miyambo 27:11)
13 Sikuti anthu akamvetsera uthenga wathu m’pamene tinganene kuti zinthu zatiyendera bwino mu utumiki. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa timakhala titachita zimene Yehova komanso Mwana wake amafuna kuti tizichita, zomwe ndi kuchitira umboni. (Mac. 10:42) Ngakhale tisapeze anthu oti tiwalalikire kapena palibe amene wamvetsera uthenga wathu, timakhalabe osangalala chifukwa timadziwa kuti tasangalatsa Atate wathu wakumwamba.—Werengani Miyambo 27:11.
14. N’chifukwa chiyani timasangalala wofalitsa wina akapeza munthu wachidwi mu utumiki?
14 Tingasangalalenso wofalitsa wina akapeza munthu wachidwi mu utumiki. Nsanja ya Olonda ina inayerekezera ntchito yathu yolalikira ndi kufufuza mwana wotayika. Anthu ambiri angagwire nawo ntchito yomufufuza m’malo osiyanasiyana. Mwanayo akapezeka, anthu onsewo amasangalala osati munthu amene wamupeza yekhayo. Mofanana ndi zimenezi, nayonso ntchito yolalikira timaigwira ngati gulu. Aliyense mumpingo amagwira nawo ntchito yofufuza anthu ndipo aliyense amasangalala munthu mmodzi akayamba kusonkhana.
MUZIKONDA KWAMBIRI YEHOVA KOMANSO ANZANU
15. Kodi lemba la Mateyu 22:37-39, lingatithandize bwanji kuti tizikonda kwambiri ntchito yolalikira? (Onaninso chithunzi chapachikuto.)
15 Kukonda Yehova komanso anzathu kungatichititse kuti tizikonda kwambiri ntchito yolalikira. (Werengani Mateyu 22:37-39.) Tangoganizirani mmene Yehova amasangalalira akationa tikugwira ntchitoyi komanso mmene anthu amasangalalira akayamba kuphunzira Baibulo. Muzikumbukiranso kuti anthu amene amvetsera uthengawu n’kuyamba kutumikira Yehova, adzapulumuka.—Yoh. 6:40; 1 Tim. 4:16.
16. Kodi tingatani kuti tizisangalala ndi utumiki wathu ngakhale pamene sitikuchoka pakhomo? Perekani zitsanzo.
16 Kodi simungathe kuchoka pakhomo pazifukwa zina? Ngati ndi choncho, ganizirani zimene mungachite kuti musonyeze kuti mumakonda Yehova komanso anthu. Pa nthawi ya mliri wa COVID-19, Samuel ndi Dania sankachoka pakhomo. Pa nthawi yovuta yonseyi, iwo ankalalikira pogwiritsa ntchito telefoni, makalata ndiponso ankachititsa maphunziro a Baibulo pa Zoom. Samuel ankalalikiranso anthu omwe ankakumana nawo akapita kuchipatala komwe ankakalandira mankhwala a khansa. Iye anati: “Mavuto amachititsa kuti tizida nkhawa, tizitopa komanso chikhulupiriro chathu chizifooka. Choncho timafunika kuyesetsa kuti tizisangalala potumikira Yehova.” Pamene zimenezi zinkachitika, Dania anagwa n’kuvulala ndipo anakhala ali chigonere kwa miyezi itatu. Kenako kwa miyezi 6 ankayenda panjinga ya olumala. Iye anati: “Ndinkayesetsa kuchita zonse zomwe ndikanatha. Ndinkalalikira kwa nesi yemwe ankandithandiza komanso anthu osiyanasiyana omwe ankabweretsa zinthu kunyumba.” Ndinkalalikiranso pafoni kwa mayi wina yemwe ankagwira ntchito zachipatala.” Ngakhale kuti Samuel ndi Dania sankatha kuchita zambiri ngati kale, ankayesetsa kuchita zomwe angathe ndipo ankasangalala.
17. Kodi tingatani kuti tizipindula kwambiri ndi mfundo zimene takambirana munkhaniyi?
17 Mungachite bwino kugwiritsa ntchito mfundo zonse 5 zomwe takambirana mu nkhaniyi. Mfundo iliyonse ili ngati zinthu zimene timagwiritsa ntchito kuti tiphike chakudya. Zonse zikasakanizidwa bwino timaphika chakudya chokoma kwambiri. Choncho tikamagwiritsa ntchito mfundo zonsezi, tidzatha kulimbana ndi maganizo ofooketsa n’kumasangalala ndi ntchito yolalikira.
KODI ZINTHU ZOTSATIRAZI ZINGATHANDIZE BWANJI KUTI TIZISANGALALA NDI NTCHITO YOLALIKIRA?
-
Kukonzekera bwino
-
Kupemphera kuti tikhale olimba mtima
-
Kukonda kwambiri Yehova ndi anthu
NYIMBO NA. 80 “Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova Ndi Wabwino”
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA