Mulungu akumvetsera. Baibulo limanena kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi . . . Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”—Salimo 145:18, 19.
Mulungu amafuna kuti muzipemphera kwa iye. Baibulo limatiuza kuti: “Pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.”—Afilipi 4:6.