N’chifukwa Chiyani Mulungu Sayankha Mapemphero Ena?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Sayankha Mapemphero Ena?

Yehova Mulungu, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba, amafuna komanso amasangalala kumva mapemphero athu ochokera pansi pa mtima. Koma pali zinthu zina zimene zingachititse kuti asayankhe mapemphero athu. Kodi zinthu zake ndi ziti, nanga tiyenera kukumbukira chiyani tikamapemphera? Mfundo za m’Baibulo zotsatirazi zingatithandize pa nkhaniyi.

“Popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza.”​—Mateyu 6:7.

Yehova safuna kuti tizingobwereza mapemphero amene taloweza kapena kuwawerenga kuchokera m’buku la mapemphero. Koma amafuna kuti tizilankhula kuchokera mumtima. Taganizirani mmene mungamvere ngati mnzanu atamalankhula nanu mongobwereza mawu omweomwewo tsiku lililonse. Anzanu apamtima sangachite zimenezi koma amamasuka nanu n’kumakuuzani zamumtima mwawo. Tikamapemphera kuchokera mumtima timasonyeza kuti timaona kuti Atate wathu wakumwamba ndi mnzathu.

“Mumapempha koma simulandira, chifukwa mukupempha ndi cholinga choipa.”​—Yakobo 4:3.

Sitingayembekezere kuti Mulungu ayankhe mapemphero athu ngati tapempha zinthu zimene tikudziwa kuti sasangalala nazo. Mwachitsanzo, Yehova amatichenjeza kuti tisamakhale ndi mtima wadyera kapena kukhulupirira mulungu wa Mwayi. (Yesaya 65:11; Luka 12:15) Ndiye ngati munthu wotchova juga atapempha Mulungu kuti achite mphumi, kodi Mulungu angayankhe pempherolo? N’zosachita kufunsa kuti sangayankhe pemphero loterolo. Koma kuti Mulungu ayankhe mapemphero athu, tiyenera kupempha zinthu zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena.

“Munthu amene amathawitsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake limakhala lonyansa.”​—Miyambo 28:9.

Kale, Mulungu sankayankha mapemphero a anthu amene sankamvera malamulo ake. (Yesaya 1:15, 16) Ndiye Mulungu sanasinthe. (Malaki 3:6) Ngati tikufuna kuti Mulungu aziyankha mapemphero athu, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tizimvera malamulo ake. Koma bwanji ngati m’mbuyomu tinachita zinthu zina zoipa? Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova sangamvetserenso mapemphero athu? Ayi. Mulungu adzatikhululukira tikasintha n’kumayesetsa kuchita zimene zimamusangalatsa.​—Machitidwe 3:19.