Zimene Anthu Amanena Zokhudza Kupemphera

Zimene Anthu Amanena Zokhudza Kupemphera

“Ndikamapemphera ndimamva ngati Mulungu ali pambali panga ndipo wandigwira dzanja n’kumanditsogolera ndikaona kuti ndasochera.”​—MARÍA.

“Mkazi wanga anamwalira atavutika ndi khansa kwa zaka 13. Ndikukumbukira kuti pa nthawiyo ndinkapemphera kwa Mulungu tsiku lililonse ndipo ndinkaona kuti akundimvetsera komanso kumvetsa mmene zinkandipwetekera. Ndikapemphera ndinkapeza mtendere wamumtima.”​—RAÚL.

“Pemphero ndi mphatso yabwino kwambiri imene Mulungu watipatsa anthufe.”​—ARNE.

María, Raúl, Arne komanso anthu ena ambiri amaona kuti pemphero ndi mphatso yapadera. Iwo amaona kuti akamapemphera amatha kulankhula ndi Mulungu, kumuthokoza komanso kumupempha kuti awathandize. Amakhulupirira ndi mtima wonse lonjezo la m’Baibulo lokhudza pemphero lakuti: “Ifetu timamudalira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.”​—1 Yohane 5:14.

Koma anthu ambiri sakhulupirira kwenikweni zimene Baibulo limanena pa nkhani ya pemphero. Mwachitsanzo, munthu wina dzina lake Steve ananena kuti: “Pamene ndinali ndi zaka 17, anzanga atatu anafa pa ngozi. Mmodzi anafa pa ngozi ya galimoto pomwe awiri enawo anamira m’nyanja.” Kodi Steve anatani? Iye anati: “Ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kumvetsa zimene zinachitikazi, koma sanandiyankhe. Ndiye ndinaona kuti palibe chifukwa chopempherera.” Anthu ambiri amene amaona kuti mapemphero awo sanayankhidwe amayamba kuganiza kuti kupemphera n’kosathandiza.

Anthu enanso ali ndi zifukwa zina zowachititsa kuganiza kuti kupemphera n’kosathandiza. Mwachitsanzo, ena amanena kuti Mulungu amadziwa zonse choncho amadziwa kale zimene timafunikira komanso mavuto athu ndiye palibe chifukwa chomuuzira m’pemphero.

Pomwe ena amakhulupirira kuti Mulungu samvetsera mapemphero awo chifukwa cha zimene analakwitsa m’mbuyomu. Munthu wina dzina lake Jenny anati: “Vuto langa n’lakuti ndinachita zinthu zimene ndimanong’oneza nazo bondo ndipo ndimadziona kuti ndine wachabechabe. Ndiye ndimadziuza kuti si ine woyenera kuti Mulungu azimvetsera mapemphero anga.”

Kodi inuyo mumaona bwanji nkhani ya kupemphera? Ngati inunso munaganizapo mofanana ndi anthuwa zokhudza pemphero, mungasangalale kudziwa kuti Baibulo limapereka mayankho othandiza pa nkhaniyi. Baibulo limafotokoza mfundo zodalirika zokhudza pemphero * ndipo lingakuthandizeni kupeza mayankho a mafunso monga awa:

  • Kodi Mulungu amamvadi mapemphero athu?

  • N’chifukwa chiyani mapemphero ena sayankhidwa?

  • Kodi mungatani kuti Mulungu azimva mapemphero anu?

  • Kodi kupemphera kungakuthandizeni bwanji?

^ ndime 9 M’Baibulo muli mapemphero a atumiki ambiri a Mulungu, kuphatikizapo a Yesu Khristu. M’Malemba Achiheberi, omwe anthu ambiri amati Chipangano Chakale, muli mapemphero oposa 150.