Anthu Akuvutika Ndi Chidani Padziko Lonse YAMBANI Anthu Akuvutika Ndi Chidani Padziko Lonse Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Anthu akuvutika kwambiri ndi chidani chomwe chili ponseponse padzikoli. Nkhani zambiri zimene zikumafalitsidwa pa intaneti zikumasonyeza kuti anthu sakukondana. Mwachitsanzo, amatumizirana maimelo, makalata ngakhalenso mauthenga oipa osonyeza chidani. Taganiziraninso zinthu zambirimbiri zoipa zimene anthu amachitira ena monga kuwasala, kuwanyoza chifukwa cha mtundu wawo, kuwanenera mawu achipongwe, kuwaopseza komanso kuwawonongera zinthu zawo. Padzikoli anthu ambiri akusalidwa ndiponso kudedwa. Magaziniyi ikufotokoza mmene chidani chingathere. Sikuti amenewa ndi maganizo ongolakalaka zinthu zabwino basi koma ndi zenizeni zomwe zayamba kale kuchitika padziko lonse lapansi. Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Anthu Akuvutika Ndi Chidani Padziko Lonse NSANJA YA OLONDA Anthu Akuvutika Ndi Chidani Padziko Lonse Chinenero Chamanja cha ku Malawi Anthu Akuvutika Ndi Chidani Padziko Lonse https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/2022007/univ/art/2022007_univ_sqr_xl.jpg wp22.1 10