Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Chidani Chikadzatheratu?

Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Chidani Chikadzatheratu?

Ngakhale kuti tingayesetse kuthetsa chidani mumtima mwathu, sitingathe kuchititsa anthu ena kusiya kudana ndi anzawo. Zili choncho chifukwa chakuti anthu akupitirizabe kudana ndi anthu osalakwa. Ndiye kodi ndi ndani amene angathetseretu chidani?

Yehova Mulungu yekha ndi amene adzathetseretu chidani. N’zimenenso Baibulo limalonjeza kuti iye adzachita.​—Miyambo 20:22.

MULUNGU ADZATHETSA ZONSE ZIMENE ZIMAYAMBITSA CHIDANI

  1. 1. SATANA MDYEREKEZI. Satana, yemwe ndi mngelo wopanduka, ndi amene amachititsa kuti anthu azidana padzikoli. Mulungu adzawononga Satana ndi anthu onse amene amatengera zochita zake n’kumadana ndi anthu ena.​—Salimo 37:38; Aroma 16:20.

  2. 2. DZIKO LA SATANA LODZADZA NDI CHIDANI. Mulungu adzathetsa zoipa zonse padzikoli kuphatikizapo anthu okonda ziphuphu monga andale komanso atsogoleri achipembedzo omwe amalimbikitsa chidani. Mulungu adzachotsanso anthu amalonda adyera omwe amachita zachinyengo komanso kudyera anthu masuku pamutu.​—2 Petulo 3:13.

  3. 3. UCHIMO. Baibulo limafotokoza kuti anthu tonse tinatengera uchimo kwa Adamu ndipo chifukwa cha uchimowu, nthawi zambiri timaganiza komanso kuchita zinthu zoipa. (Aroma 5:12) Mwachitsanzo, uchimowu umatichititsa kuti tizisungira ena zifukwa ndiponso kudana nawo. Choncho kuti chidani chidzatheretu padzikoli, Mulungu adzatithandiza kuti tithetse maganizo onse auchimo omwe amatichititsa kuti tizidana ndi ena.​—Yesaya 54:13.

BAIBULO LIMATILONJEZA KUTI CHIDANI CHIDZATHERATU PADZIKOLI

  1. 1. ZINTHU ZOPANDA CHILUNGAMO ZIDZATHA. Ufumu wa Mulungu womwe uli kumwamba udzalamulira dziko lonse lapansi ndipo udzabweretsa chilungamo mpaka kalekale. (Danieli 2:44) Anthu adzasiya kusankhana mitundu ndipo azidzachita zinthu mololerana. Pa nthawiyi, Mulungu adzathetseratu zinthu zonse zopanda chilungamo zimene anthu akukumana nazo panopa.​—Luka 18:7.

  2. 2. ALIYENSE ADZAKHALA MWAMTENDERE. Palibe munthu wina aliyense amene azidzavutika chifukwa cha zinthu zachiwawa kapenanso nkhondo. (Salimo 46:9) Anthu padzikoli azidzakhala motetezeka chifukwa padzakhala anthu okhawo amene amakonda mtendere.​—Salimo 72:7.

  3. 3. ALIYENSE ADZAKHALA NDI MOYO WABWINO KWAMBIRI MPAKA KALEKALE. Anthu onse padzikoli azidzakondana kuchokera pansi pa mtima. (Mateyu 22:39) Palibe amene azidzavutika ndi nkhawa chifukwa chokumbukira zinthu zoipa zimene zinkamuchitikira m’mbuyo. (Yesaya 65:17) Pa nthawi imeneyi, anthu onse okhala padziko lapansi sazidzadananso “ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”​—Salimo 37:11.

Kodi mungakonde kudzakhala m’dziko limeneli? Ngakhale panopa, anthu ambiri akuyesetsa kuthetsa mtima wachidani chifukwa choti amatsatira mfundo za m’Baibulo. (Salimo 37:8) Zimenezi n’zimene a Mboni za Yehova padziko lonse akuyesetsa kuchita. Iwo amakondana komanso kugwirizana ngati anthu am’banja limodzi ngakhale kuti ndi osiyana zikhalidwe ndiponso kochokera.​—Yesaya 2:2-4.

A Mboni za Yehova angasangalale kukambirana nanu zimene anaphunzira zokhudza zimene tingachite anthu ena akamatichitira zinthu zopanda chilungamo kapenanso akamatisala. Zimene mungaphunzire zingakuthandizeni kuti musiye kudana ndi anthu ena n’kuyamba kuwakonda. Mungaphunzirenso mmene mungachitire zinthu mokoma mtima ndi anthu onse ngakhalenso amene akuoneka kuti ndi osayamika kapenanso amene amadana nanu. Mukatero muzikhala osangalala panopa komanso muzigwirizana kwambiri ndi anthu ena. Koposa zonse mudzaphunzira zimene mungachite kuti mudzakhale mu Ufumu wa Mulungu pa nthawi imene chidani chidzatheretu.​—Salimo 37:29.