KODI TINGATHETSE BWANJI CHIDANI?

3 | Yesetsani Kuchotsa Mtima Wachidani M’maganizo Mwanu

3 | Yesetsani Kuchotsa Mtima Wachidani M’maganizo Mwanu

Baibulo Limati:

“Sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.”AROMA 12:2.

Zimene Lembali Limatanthauza:

Mulungu amadziwa bwino zimene timaganiza. (Yeremiya 17:10) Choncho pali zambiri zomwe tiyenera kuchita kuwonjezera pa kupewa kulankhula kapenanso kuchita zinthu zosonyeza kuti tili ndi mtima wachidani. Chidani chimayambira mumtima ndiponso m’maganizo athu ndiye n’chifukwa chake tiyenera kuthetseratu chidani mumtima komanso m’maganizo mwathu. Tikachita zimenezi m’pamenedi ‘tingasandulike’ komanso kuthetsa chidani.

Mmene Lembali Lingakuthandizireni:

Dzifufuzeni moona mtima kuti mudziwe mmene mumaonera anthu ena, makamaka amitundu ina. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimawaona bwanji? Kodi ndimawaona chonchi chifukwa chakuti ndimawadziwa bwino kapena chifukwa choti ndili ndi mtima watsankho?’ Muzipewa mafilimu, kuwerenga kapena kuonera zinthu za pa intaneti ndiponso zosangalatsa zomwe zimalimbikitsa chidani komanso zachiwawa.

Mawu a Mulungu angatithandize kuthetsa chidani mumtima ndi m’maganizo mwathu

Si zophweka kudzifufuza moona mtima ndi cholinga choti tidziwe ngati tili ndi maganizo olakwika. Koma Mawu a Mulungu angatithandize kuti tithe kuzindikira zomwe ‘tikuganiza komanso zolinga za mtima wathu.’ (Aheberi 4:12) Choncho, musasiye kufufuza mfundo za m’Baibulo. Muziyerekezera zimene Baibulo limaphunzitsa ndi zimene mumaganiza kenako muziyesetsa kusintha maganizo anu kuti agwirizane ndi zimene mukuphunzira m’Baibulo. Mawu a Mulungu angatithandize kuthetsa chidani chimene ‘chinazikika molimba’ m’maganizo komanso mumtima mwathu.​—2 Akorinto 10:4, 5.