N’zotheka Kuthetsa Chidani

N’zotheka Kuthetsa Chidani

Kodi munayamba mwadedwapo ndi anthu ena?

Ngati simunakumanepo ndi vuto limeneli n’kutheka kuti munaona anthu ena zikuwachitikira. Masiku ano nkhani zambiri zimakhala zokhudza kudana ndi anthu chifukwa cha mtundu wawo, dziko lomwe anachokera kapenanso chifukwa choti amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo. Chifukwa cha zimenezi maboma ambiri akumakhazikitsa malamulo n’cholinga choti amene wapezeka akudana ndi gulu linalake la anthu azipatsidwa chilango chokhwima.

Nthawi zambiri anthu amene amadedwa nawonso amayamba kudana ndi anthu ena. Anthu amene amadedwa amakonda kubwezera ndipo zimenezi zimachititsa kuti vutoli lizingopitirira.

N’kutheka kuti inuyo munakumanapo ndi zinthu monga kusalidwa, kunyozedwa chifukwa cha mtundu wanu, kunenedwa mawu achipongwe kapenanso kuopsezedwa. Komabe, chidani chimachititsa kuti anthu azichitirana zinthu zoopsa kwambiri monga nkhanza, kuwononga zinthu za ena, kugwiririra ngakhalenso kupha mwankhanza anthu amtundu winawake.

Magaziniyi isonyeza mmene tingathetsere chidani komanso iyankha mafunso otsatirawa:

  • N’chifukwa chiyani anthu amadana kwambiri?

  • N’chiyani chingathandize kuti anthu asiye kudana?

  • Kodi n’zotheka kuti chidani chidzatheretu padzikoli?