4 | Baibulo Lingakupatseni Malangizo Othandiza
BAIBULO LIMATI: “Malemba onse . . . ndi opindulitsa.”—2 TIMOTEYO 3:16.
Tanthauzo Lake
Ngakhale kuti Baibulo si buku la zachipatala, komabe lingakupatseni malangizo abwino komanso opindulitsa. Malangizo amenewa angathandize munthu amene akuvutika ndi matenda amaganizo.
Mmene Mfundo Zimenezi Zingakuthandizireni
“Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.”—MATEYU 9:12.
Baibulo limatilimbikitsa kuti timafunika kupeza thandizo lachipatala. Anthu amene akudwala matenda amaganizo athandizidwa kudziwa zolondola zokhudza vuto lawolo komanso athandizidwa ndi madokotala.
“Kulimbitsa thupi kuli ndi phindu ndithu.”—1 TIMOTEYO 4:8, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.
Kuchita zinthu zimene zingalimbitse thupi kungachepetse vuto la matenda amaganizo. Zinthu zake ndi monga, kukhala ndi chizolowezi chochita masewera olimbitsa thupi, kudya zakudya zopatsa thanzi komanso kugona mokwanira.
“Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.”—MIYAMBO 17:22.
Kuwerenga nkhani zolimbikitsa za m’Baibulo komanso kukhala ndi zolinga zomwe mungazikwaniritsedi, kungakuthandizeni kuti muzikhala osangalala. Tikamaganizira zinthu zabwino pa moyo wathu komanso kukhulupirira kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo, zidzatithandiza kuti tipitirizebe kupirira matenda amaganizo.
“Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.”—MIYAMBO 11:2.
Nthawi zina sitingakwanitse kuchita zonse zimene tikufuna patokha, choncho tizivomereza anthu ena akafuna kutithandiza. Achibale komanso anzathu angafune kuti atithandize, koma mwina sangadziwe zomwe tikufunikira. Ndiye muziwafotokozera zinthu zimene zingakhaledi zothandiza kwa inu. Musamayembekezere kuti azikuchitirani zinthu zoposa zimene angakwanitse ndipo nthawi zonse muziwathokoza akakuthandizani.
Mmene Malangizo a M’Baibulo Akuthandizira Anthu Odwala Matendawa
“Ndinapita kukakumana ndi dokotala nditaona kuti sindikumva bwino. Choncho atandiyeza anapeza vuto limene ndinali nalo. Zimenezi zinandithandiza kuti ndivomereze vuto langalo komanso kulandira thandizo lachipatala kuti ndizisamalira bwino thanzi langa.”—Nicole, a yemwe ali ndi matenda amaganizo (bipolar disorder).
“Ndaona kuti kuphunzira Baibulo mokhazikika ndi mkazi wanga kumandithandiza kuti ndiyambe tsiku ndili ndi maganizo abwino. Ndipo nthawi zambiri pa masiku amene ndikulimbana ndi nkhawa, ndimakumbukira vesi linalake limene limandilimbikitsa.”—Peter, yemwe amadwala matenda ovutika maganizo.
“Zinali zovuta kwambiri kuuza anzanga za vuto langali chifukwa ndinkachita manyazi. Koma nditafotokozera mnzanga amene ndinkacheza naye kwambiri anandimvetsera mokoma mtima ndipo anamvetsa mmene ndinkamvera. Iye anandithandiza kwambiri kuti ndiyambirenso kumva bwino komanso kuti ndisamadzimve kuti ndili ndekhandekha.”—Ji-yoo, amene ali ndi matenda ovutika kudya.
“Baibulo landithandiza kuti ndiziona zinthu moyenera, ndizipuma mokwanira komanso kuti ndisamadzipanikize ndi ntchito. Mfundo za m’Baibulo zandithandiza kuti ndizilimbana ndi mavuto obwera chifukwa cha nkhawa.”—Timothy, yemwe ali ndi matenda amaganizo (obsessive compulsive disorder).
a Mayina ena asinthidwa.
Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA
Yambani kuphunzira Baibulo
Phunzirani Baibulo kwaulere, mochita kukambirana ndi mphunzitsi wanu.
NSANJA YA OLONDA