2 | ‘Malemba Angakulimbikitseni’

2 | ‘Malemba Angakulimbikitseni’

BAIBULO LIMATI: “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa amatipatsa chiyembekezo chifukwa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.”—AROMA 15:4

Tanthauzo Lake

M’Baibulo muli mfundo zolimbikitsa zimene zingatipatse mphamvu komanso kutithandiza kupirira kuti tithane ndi maganizo olakwika. Baibulo limatipatsanso chiyembekezo chakuti kuvutika maganizo kulikonse kudzatha.

Mmene Mfundo Zimenezi Zingakuthandizireni

Nthawi zina tonsefe timakhala ndi nkhawa koma anthu amene amavutika ndi matenda amaganizo kapena nkhawa, tsiku lililonse angamavutike ndi ululu wamumtima. Ndiye kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji?

  • M’Baibulo muli mfundo zambiri zabwino zimene zingakuthandizeni kuthana ndi maganizo olakwika. (Afilipi 4:8) Kuganizira kwambiri mfundo zimenezi, kungakutonthozeni komanso kungakuthandizeni kukhala odekha ndipo zimenezi zingachititse kuti muziganiza bwino.​—Salimo 94:18, 19.

  • Baibulo lingatithandize kuthana ndi maganizo odziona kuti ndife osafunika.​—Luka 12:6, 7.

  • Malemba osiyanasiyana a m’Baibulo, amatitsimikizira kuti sitili tokha ndipo Mulungu yemwe ndi Mlengi wathu, amamvetsa bwino mmene timamvera mumtima mwathu.​—Salimo 34:18; 1 Yohane 3:19, 20.

  • Baibulo limatilonjeza kuti Mulungu adzathetsa zopweteka za mtundu wina uliwonse ndipo sitidzazikumbukiranso. (Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:4) Lonjezo limeneli limatipatsa mphamvu kuti tipitirizebe kupirira tikamasokonezeka maganizo.