Mulungu Amasamala za Inu

Mulungu Amasamala za Inu

M’BAIBULO muli malangizo abwino kwambiri amene angakuthandizeni chifukwa ndi buku lochokera kwa Mulungu. Ngakhale zili choncho, si buku la zachipatala. Komabe lingakuthandizeni kuthana ndi mavuto osiyanasiyana pa moyo wanu monga kuvutika ndi nkhawa, kumva kupweteka m’thupi komanso ngati mukudwala matenda ovutika maganizo.

Chofunika kwambiri n’chakuti Baibulo limatitsimikizira kuti mlengi wathu Yehova Mulungu, a amadziwa bwino mmene timaganizira komanso mmene timamvera kuposa wina aliyense. Iye ndi wofunitsitsa kutithandiza kuthana ndi mavuto aliwonse amene tikukumana nawo. Mwachitsanzo, taonani malemba awiri a m’Baibulo otsatirawa amene angakulimbikitseni:

“Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”​—SALIMO 34:18.

“Pakuti ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’”—YESAYA 41:13.

Koma kodi Yehova amatithandiza bwanji kuthana ndi mavuto obwera chifukwa cha matenda ovutika maganizo? Monga mmene muonere munkhani zotsatirazi, muona zimene Yehova amachita posonyeza kuti amasamaladi za ife komanso mmene amatithandizira m’njira zosiyanasiyana.

a Yehova ndi dzina la Mulungu.​—Salimo 83:18.