Aliyense Amafuna Kukhala Ndi Tsogolo Labwino YAMBANI Aliyense Amafuna Kukhala Ndi Tsogolo Labwino Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Kodi inuyo mumafuna kukhala ndi tsogolo lotani? Mofanana ndi anthu ambiri, sitikukayikira kuti inunso mumafuna kukhala ndi tsogolo labwino limodzi ndi banja lanu. Mumafuna mutakhala osangalala, athanzi, kukhala moyo wamtendere komanso wosasowa chilichonse. Komabe, anthu ambiri amakayikira kuti angakhale ndi tsogolo labwino. Mwachitsanzo, mliri wa COVID-19, womwe anthu sankauyembekezera, wakhudza miyoyo ya anthu ambiri, wayambitsa umphawi ngakhalenso kupha anthu ambirimbiri. Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri amaona kuti n’zosatheka kukhala ndi tsogolo labwino. Popeza kuti sakudziwa zokhudza tsogolo lawo, anthu akufunafuna zinthu zimene zingawathandize kuti akhale ndi tsogolo labwino. Ena amakhulupirira kuti pali mphamvu zinazake zosaoneka zimene zingathe kuwabweretsera tsoka kapena mwayi pa moyo wawo. Anthu ambiri amaganiza kuti maphunziro ndi chuma, ndi zimene zingawathandize kuti adzakhale ndi tsogolo labwino. Pomwe ena amaona kuti akungofunika kukhala munthu wabwino n’cholinga choti akhale ndi moyo wabwino. Kodi zinthu zimenezi zingakuthandizenidi kukhala ndi tsogolo labwino? Kuti mudziwe zoona zake, ganizirani mafunso awa: Kodi tsogolo lanu mungalidziwe bwanji? Kodi maphunziro ndi ndalama, n’zimene zingatithandize kukhala ndi moyo wabwino? Kodi kungokhala munthu wabwino n’kumene kungachititse kuti mukhale ndi tsogolo labwino? Kodi mungapeze kuti malangizo odalirika omwe angakuthandizeni kukhala ndi tsogolo labwino? Magaziniyi ikuthandizani kupeza mayankho a mafunso amenewa. Yam'mbuyo Yotsatira Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi ESSENTIAL BIBLE TEACHINGS Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? Ali padziko lapansi, Yesu anafotokoza kwambiri za Ufumu wa Mulungu kuposa nkhani ina iliyonse. Kwa zaka zambiri otsatira ake akhala akupempherera Ufumu umenewu kuti ubwere. ESSENTIAL BIBLE TEACHINGS Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona? Ngati Baibulo linachokeradi kwa Mulungu, ndiye kuti liyenera kukhala losiyana kwambiri ndi mabuku ena onse. ZOKHUDZA IFEYO Pemphani Kuti Tidzakuyendereni Mutha kukhala ndi mwayi wokambirana nkhani inayake ya m’Baibulo kapena kudziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova. Sindikizani Patsani ena Patsani ena Aliyense Amafuna Kukhala Ndi Tsogolo Labwino NSANJA YA OLONDA Aliyense Amafuna Kukhala Ndi Tsogolo Labwino Chinenero Chamanja cha ku Malawi Aliyense Amafuna Kukhala Ndi Tsogolo Labwino https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/2021163/univ/art/2021163_univ_sqr_xl.jpg wp21.3 1