Kwa zaka zambiri, anthu akhala akuona kuti kukhala munthu wabwino kungathandize kuti munthu akhale ndi tsogolo labwino. Mwachitsanzo, anthu ambiri ku Asia ankagwirizana ndi zimene wafilosofe wina wotchuka dzina lake Confucius ananena. Iye anati: “Zimene simukufuna kuti anthu ena akuchitireni, inunso musamawachitire.”*
ZIMENE ANTHU AMBIRI AMACHITA
Anthu ambiri amakhulupirira kuti kukhala ndi makhalidwe abwino n’kumene kungawathandize kukhala ndi tsogolo labwino. Iwo amayesetsa kuchita zinthu mwaulemu, kukhala ndi makhalidwe abwino, amayesetsa kukwaniritsa maudindo awo ndiponso amayesetsa kukhala ndi chikumbumtima chabwino. Mayi wina wa ku Vietnam dzina lake Linh, anati: “Ndakhala ndikukhulupirira kuti ndingadzakhale ndi tsogolo labwino ndikamachita zinthu moona mtima ndiponso mwachilungamo.”
Anthu ena amachita zinthu zabwino chifukwa cha zimene amakhulupirira kuchipembedzo chawo. Bambo wina wa ku Taiwan dzina lake Hsu-Yun, anati: “Ndinaphunzitsidwa kuti zimene munthu amachita ali moyo zingachititse kuti akadzamwalira adzasangalale ndi moyo kwamuyaya kapena kuzunzidwa kwamuyaya.”
KODI ZOTSATIRA ZAKE ZIMAKHALA ZOTANI?
N’zoona kuti timakhala osangalala tikamachitira anthu ena zabwino. Komabe, anthu ambiri omwe amayesetsa kuchitira anthu ena zabwino ndi mtima wawo wonse amaona kuti si nthawi zonse pamene anthu enawonso amawachitira zabwino. Mayi wina yemwe amakhala ku Hong Kong, dzina lake Shiu Ping, anati: “Zimene zinandichitikira zinandithandiza kuzindikira kuti si nthawi zonse pamene anthu amene unawachitira zabwino angadzakuchitirenso zabwino. Ndinkayesetsa kusamalira bwino banja langa komanso kulichitira zabwino. Koma banja langa linasokonekera ndipo mwamuna wanga anachoka n’kundisiya ndekha ndi mwana wanga.”
Anthu ambiri amaona kuti si nthawi zonse pamene anthu omwe ali m’chipembedzo amakhala abwino. Mayi wina wa ku Japan dzina lake Etsuko, anati: “Ndinalowa m’kagulu kenakake kachipembedzo, kenako ndinakhala mtsogoleri wa achinyamata. Ndinadabwa kuona kuti anthu ena m’chipembedzo changa anali ndi makhalidwe oipa, ankalimbirana maudindo komanso ankagwiritsa ntchito molakwika ndalama zampingo.”
“Ndinkayesetsa kusamalira bwino banja langa komanso kulichitira zabwino. Koma banja langa linasokonekera ndipo mwamuna wanga anachoka n’kundisiya ndekha ndi mwana wanga.”—SHIU PING, wa ku HONG KONG
Anthu ena omwe amadzipereka kwambiri kuchipembedzo chawo komanso amayesetsa kuchita zabwino, amakhumudwa akaona zinthu zoipa zikuwachitikira pa moyo wawo. Zimenezi n’zimene zinachitikira mayi wina wa ku Vietnam dzina lake Van. Iye anati: “Tsiku lililonse ndinkagula zipatso, maluwa komanso zakudya n’kumazipereka nsembe kwa makolo anga omwe anamwalira ndipo ndinkaganiza kuti zinthu zizindiyendera bwino komanso ndikhala ndi tsogolo labwino. Ngakhale kuti ndinkayesetsa kuchita zabwino komanso kutsatira miyambo yachipembedzo chathu kwa zaka zambiri, mwamuna wanga anadwala kwambiri. Kenako mwana wanga wamkazi yemwe ankaphunzira kudziko lina anamwalira ali ndi zaka 20 zokha.”