Kodi Maphunziro Ndi Ndalama Zingatithandize Kukhala Ndi Tsogolo Labwino?
Anthu ambiri amaganiza kuti anthu ophunzira kwambiri komanso olemera ndi amene ali ndi tsogolo labwino. Iwo amakhulupirira kuti maphunziro akuyunivesite angawathandize kukhala munthu wabwino kuntchito, m’banja, m’dera lawo komanso m’dziko lawo. Iwo amaona kuti maphunziro oterewa angathandize munthu kuti apeze ntchito yabwino yoti azilandira ndalama zambiri n’kumakhala wosangalala.
ZIMENE ANTHU AMBIRI AMASANKHA
Taganizirani zimene ananena Zhang Chen, yemwe amakhala ku China. Iye anati: “Ndinkakhulupirira kuti ndikufunikira kukhala ndi digirii kuti ndisakhale wosauka komanso kuti ndipeze ntchito yandalama zambiri zomwe zingandithandize kukhala ndi moyo wosangalala komanso wabwino kwambiri.”
Pofuna kukhala ndi tsogolo labwino, ambiri amayesetsa kupita kumayunivesite otchuka, mwinanso kumayiko ena. Anthu ambiri akhala akuchita zimenezi mpaka pamene mliri wa COVID-19 unachititsa kuti anthu asamapite kwambiri m’mayiko ena. Lipoti la mu 2012 la bungwe lina loona za chuma ndi chitukuko, linanena kuti: “52 peresenti ya ophunzira ochokera kumayiko ena inali ya anthu a ku Asia.”
Nthawi zambiri, makolo ena amalolera kudzimana zinthu zambiri n’cholinga choti atumize ana awo kumayunivesite am’mayiko ena. Qixiang, wa ku Taiwan, anati: “Ngakhale kuti makolo anga ndi osauka, anakwanitsa kutumiza ana tonse 4 ku United States kuti tikachite maphunziro akukoleji.” Kuti akwanitse kulipira maphunziro amenewa, makolo ake ankafunika kutenga ngongole ngati mmene makolo ambiri amachitira.
KODI ZOTSATIRA ZAKE ZIMAKHALA ZOTANI?
Maphunziro amathandiza anthu m’njira zina. Koma si nthawi zonse pamene ana asukulu amapeza zomwe ankayembekezera. Mwachitsanzo, pambuyo pogwira ntchito mwakhama kwa zaka zambiri komanso kubwereka ndalama zolipirira sukulu, anthu ambiri sapeza ntchito yomwe ankafuna. Lipoti la nyuzipepala ina ya ku Singapore, lomwe analemba Rachel Mui, linati: “Zikuoneka kuti anthu ambiri amene anamaliza maphunziro akuyunivesite sakupeza ntchito.” (Business Times) Jianjie, wa ku Taiwan yemwe ndi wophunzira kwambiri, anati: “Anthu ambiri amakakamizika kugwira ntchito yosagwirizana ndi maphunziro awo.”
Anthu omwe apeza ntchito yogwirizana ndi maphunziro awo amaona kuti zomwe zikuchitika pa moyo wawo si zomwe ankayembekezera. Niran wa ku Thailand, yemwe anakachita maphunziro akuyunivesite ku United Kingdom, anapeza ntchito yogwirizana ndi maphunziro ake. Iye anati: “Digirii inandithandiza kupeza ntchito ya ndalama zambiri monga mmene ndinkayembekezera. Komabe, kuti ndizilandira ndalama zambiri ndinkafunika kugwira ntchito mwakhama kwambiri komanso kwa maola ambiri. Koma kenako kampaniyo inachotsa ntchito anthu ambiri, kuphatikizapo ineyo. Apatu ndinazindikira kuti palibe ntchito iliyonse yomwe ingathandize munthu kukhala ndi tsogolo labwino.”
Ngakhale anthu omwe ndi olemera kapena amaoneka ngati zikuwayendera, amakumana ndi mavuto am’banja, matenda komanso amangokhalira kudandaula zokhudza ndalama. Katsutoshi, wa ku Japan, anati: “Ngakhale kuti ndinali ndi ndalama zambiri, sindinkakhala mosangalala chifukwa anthu ankachita zinthu mopikisana nane, kundichitira nsanje ndi zinthu zina zoipa.” Mayi wina dzina lake Lam, yemwe amakhala ku Vietnam, anati: “Ndaonapo anthu ambiri akufunafuna ntchito yandalama zambiri n’cholinga choti akhale ndi tsogolo labwino, koma zoona zake n’zakuti sapeza zomwe amafunazo. M’malomwake amangokhalira kuda nkhawa, kudwala komanso kuvutika maganizo.”
Mofanana ndi Franklin, anthu ambiri aona kuti pali zinthu zambiri zofunika zomwe munthu angachite pa moyo kuposa maphunziro akuyunivesite kapena kufunafuna chuma. M’malo momangofunafuna chuma, anthu ena aona kuti akhoza kukhala ndi tsogolo labwino pokhala munthu wabwino komanso kuchitira ena zabwino. Koma kodi kuchita zimenezi kungathandizedi kuti munthu akhale ndi tsogolo labwino? Nkhani yotsatira iyankha funso limeneli.