N’zotheka Kukhala Ndi Tsogolo Labwino

N’zotheka Kukhala Ndi Tsogolo Labwino

KODI MUKUGANIZA KUTI N’CHIYANI CHINGAKUTHANDIZENI KUTI MUKHALE NDI TSOGOLO LABWINO? KODI NDI:

  • Maphunziro akuyunivesite?

  • Chuma?

  • Kungokhala munthu wabwino?

  • Kapena zinthu zina?

Malemba Opatulika amati:

“Dziwa nzeru kuti upindule. Ukazipeza, udzakhala ndi tsogolo labwino.”​—MIYAMBO 24:14.

M’Malemba Opatulika mungapezemo mawu anzeru omwe angakuthandizeni kukhala ndi tsogolo labwino.