Kodi Tsogolo Lanu Mungalidziwe Bwanji?
Anthu ambiri amakhulupirira kuti pali mphamvu zinazake zosaoneka zomwe zimawathandiza kudziwa tsogolo lawo. Chifukwa cha zikhulupiriro zimenezo, iwo amatsatira miyambo inayake yomwe amakhulupirira kuti ingawathandize kukhala ndi moyo wabwino.
ZIMENE ANTHU AMBIRI AMAKHULUPIRIRA
KUKHULUPIRIRA NYENYEZI: Anthu ena amakhulupirira kuti angathe kudziwa zokhudza tsogolo lawo potengera mmene nyenyezi zinalili pa nthawi yomwe ankabadwa. Iwo amapempha anthu olosera zam’tsogolo pogwiritsa ntchito nyenyezi kuti awathandize kudziwa zinthu zimene zingawachitikire n’cholinga choti apewe zinthu zoopsa kapena apeze mwayi winawake.
FENG SHUI: Anthu amene amakhulupirira feng shui amaona kuti pali mphamvu zinazake zosaoneka zam’chilengedwe zimene zingawathandize kuti zinthu ziziwayendera bwino. Lo Wing, * yemwe amakhala ku Hong Kong, ananena kuti: “Katswiri wina wodziwa za feng shui anandiuza kuti kuika timiyala tinatake tonyezimira pamalo enaake musitolo yanga, kungandithandize kuti ndizipeza ndalama zambiri.”
MIZIMU YAMAKOLO: Anthu enanso amakhulupirira kuti ayenera kulemekeza mizimu yamakolo kapenanso milungu ina yosiyanasiyana n’cholinga choti iwateteze komanso kuwadalitsa. Van, yemwe amakhala ku Vietnam, anati: “Ndinkakhulupirira kuti ndikamalemekeza mizimu yamakolo, ndingakhale ndi moyo wabwino panopa komanso ndingadzakhale ndi tsogolo labwino limodzi ndi ana anga.”
KUKABADWANSO KWINAKWAKE: Anthu ambiri amaona kuti moyo wamunthu sumatha ndipo akabadwa n’kumwalira, amakabadwanso. Iwo amakhulupirira kuti zinthu zabwino kapena zoipa zomwe akukumana nazo panopa zikuchitika chifukwa cha zimene ankachita m’moyo wam’mbuyo asanabadwe.
Komabe, anthu ambiri amaona kuti zikhulupiriro zimenezi ndi zogwirizana ndi kukhulupirira mizimu. Ngakhale kuti anthu ambiri amanena kuti sakhulupirira zimenezi, amachitabe zinthu monga kutanthauzira mizere yam’manja, kukhulupirira nyenyezi, kukhulupirira maloto, kuwombeza, kutsirika, kugwiritsa ntchito zithumwa, ndi zina zambiri. Iwo amaganiza kuti kuchita zimenezi kungawathandize kudziwa zinthu zokhudza tsogolo lawo.
KODI ZIKHULUPIRIROZI N’ZOTHANDIZADI?
Kodi anthu amene amakhulupirira zinthu zimenezi amakhala ndi moyo wabwino komanso tsogolo labwino?
Taganizirani zimene zinachitikira Hào, yemwe amakhala ku Vietnam. Iye anayesera kukhulupirira nyenyezi, feng shui ndi kulambira mizimu yamakolo kuti zimuthandize. Koma kodi zinamuthera bwanji? Iye anati: “Bizinezi yanga inasokonekera, ndinalowa mungongole, tinkangokhalira kukangana m’banja mwathu ndiponso ndinkavutika maganizo kwambiri.”
Nayenso Qiuming wa ku Taiwan ankakhulupirira nyenyezi, ankakhulupirira mwayi, feng shui, ankalambira mizimu yamakolo ndipo ankakhulupiriranso kuti munthu akamwalira amakabadwanso kwinakwake. Komabe, atafufuza zikhulupiriro zimenezi mosamala kwambiri, iye anati: “Ndinazindikira kuti zikhulupiriro ndi miyambo imeneyi n’zosagwirizana ndiponso n’zosokoneza. Ndinapeza kuti zimene okhulupirira nyenyezi ankalosera, nthawi zambiri sizinkakhala zolondola. Ndinaonanso kuti chikhulupiriro chakuti munthu akamwalira amapitiriza kukhala ndi moyo kwinakwake, si cholondola chifukwa ngati sukukumbukira zimene unkachita m’moyo wakumbuyo usanabadwe, sizingatheke kuti usinthe n’kumachita zabwino m’moyo wina.”
“Ndinazindikira kuti zikhulupiriro ndi miyambo imeneyi n’zosagwirizana ndiponso n’zosokoneza.”—QIUMING, wa ku TAIWAN
Monga mmene Hào, Qiuming ndi anthu ena afotokozera, sitingathe kudziwa zokhudza tsogolo lathu chifukwa chokhulupirira mwayi, nyenyezi, mizimu yamakolo kapenanso zoti munthu akamwalira amakabadwanso kwinakwake. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibe zomwe tingachite n’cholinga choti tidzakhale ndi tsogolo labwino?
Anthu ambiri amaona kuti angadzakhale ndi tsogolo labwino ngati angachite maphunziro akuyunivesite komanso akakhala ndi chuma. Koma kodi anthu ena omwe anasankha kuchita zimenezi anakumana ndi zotani?
^ ndime 5 Mayina ena asinthidwa munkhaniyi komanso nkhani zina zotsatira.
^ ndime 16 Mawu amenewa amapezeka m’Baibulo Lopatulika pa Agalatiya 6:7. Anthu akum’mawa kwa dziko lapansi amakonda kufotokoza mfundo yamulembali kuti ukadzala mavwende, udzakololanso mavwende; ukadzala nyemba, udzakololanso nyemba.
Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi
NSANJA YA OLONDA
Kodi Okhulupirira Nyenyezi Komanso Olosera Angatithandizedi Kudziwa Zam’tsogolo?
Kodi muyenera kudalira anthu okhulupirira nyenyezi kuti akuthandizeni kudziwa zam’tsogolo?
NSANJA YA OLONDA