1924—Zaka 100 Zapitazo
UTUMIKI WA UFUMU a wa January 1924 unanena kuti: “Kumayambiriro kwa chaka, Mkhristu aliyense wobatizidwa amafunafuna mipata yoti awonjezere utumiki wake.” M’chaka chimenechi, Ophunzira Baibulo anatsatira malangizowa m’njira ziwiri. Iwo ankalalikira molimba mtima komanso kugwiritsa ntchito njira zatsopano.
KULALIKIRA MOLIMBA MTIMA KUDZERA PA WAILESI
Kwa nthawi yoposa chaka, abale ku Beteli anagwira ntchito yokonza malo oti padzakhale wailesi ya WBBR pachilumba cha Staten ku New York City. Atadula mitengo pamalopo, anamanga nyumba yoti ogwira ntchito azikhalamo komanso nyumba ina kuti ikhale youlutsira mawu. Atamaliza kugwira ntchitoyi, anayamba kusonkhanitsa zipangizo zogwiritsa ntchito poulutsa mawu. Koma panali mavuto angapo.
Ntchito yovuta kwambiri imene abalewa anagwira inali yoika tawa. Ankafunika kuimika tawa yaitali mamita 91 n’kuika matabwa awiri olimbitsira, aatali mamita 61. Ulendo woyamba umene anayesa kuchita zimenezi analephera. Koma chifukwa chodalira Yehova iwo anakwanitsa kugwira ntchitoyi. M’bale Calvin Prosser, yemwe anagwira nawo ntchitoyi ananena kuti: “Zikanatheka ulendo woyamba uja bwenzi tikudzitamandira n’kumanena kuti, ‘Taonani zimene takwanitsa kuchita!’” Zimenezi zinachititsa kuti abalewa alemekeze Yehova. Koma mavuto awo sanathere pomwepo.
Kuulutsa mawu pa wailesi kunali kutangoyamba kumene ndipo zipangizo zoulutsira mawu sizinkapezekapezeka. Choncho abale anagula chipangizo chotumiza mawu chomwe anthu ena ankagwiritsa ntchito. M’malo mogula maikolofoni, ankagwiritsa ntchito cholankhulira pa telefoni. Tsiku lina usiku mu February, abale anaganiza zoyeserera mashini amene ankakonzawa. Iwo ankafunika pulogalamu yoti aulutse, choncho anaimba nyimbo za Ufumu. M’bale Ernest Lowe amakumbukira zinthu zoseketsa zomwe zinachitika pamene abalewa ankaimba. Iwo analandira foni kuchokera kwa M’bale Rutherford, b yemwe anali ku Brooklyn, womwe unali mtunda wa makilomita 25. M’baleyu anawamva akuimba pa wailesi yake.
M’bale Rutherford anati: “Siyani zimenezo. Zikungomveka ngati kulira kwa amphaka.” Abalewo anachita manyazi n’kuthimitsa, koma anadziwa kuti tsopano anali okonzeka kuulutsa mawu pa wailesi.
Pa 24 February 1924, pamene anaulutsa koyamba mawu pa wailesiyi, M’bale Rutherford ananena kuti wailesiyi inali yoti “izithandiza pa zinthu zokhudza Ufumu wa Mesiya.” Iye ananena kuti, “Cholinga cha wailesiyi ndi kuthandiza anthu kumvetsa mfundo za m’Baibulo zokhudza nthawi imene tikukhalamoyi, posatengera zimene amakhulupirira kapena chipembedzo chawo.”
Zimene zinachitika patsikuli zinali ndi zotsatirapo zabwino. Wailesi ya WBBR inakhala ikuulutsa mawu kwa zaka 33 zotsatira.
KUTSUTSA MOLIMBA MTIMA ATSOGOLERI A ZIPEMBEDZO
Mu July 1924, Ophunzira Baibulo anali ndi msonkhano ku Columbus ku Ohio. Alendo anachokera m’madera osiyanasiyana padziko lonse, ndipo anamvetsera nkhani zomwe zinakambidwa mu Chiarabu, Chingelezi, Chifulenchi, Chijeremani, Chigiriki, Chihangare, Chitaliyana, Chilithuaniya, Chipolishi, Chirasha, zilankhulo za ku Scandinavia, komanso Chiyukireniya. Mbali zina za pulogalamuyi zinaulutsidwa pa wailesi komanso panakonzedwa zoti nyuzipepala ina ya m’dzikolo (Ohio State Journal) izilemba zomwe zikuchitika pa tsiku lililonse la msonkhanowo.
Lachinayi pa 24 July abale ndi alongo oposa 5,000 omwe anapezeka pamsonkhanowu anakalalikira mumzindawu. Iwo anagawira mabuku pafupifupi 30,000 komanso kuyambitsa maphunziro a Baibulo ambiri. Nsanja ya Olonda inanena kuti limeneli linali “tsiku losangalatsa kwambiri pamsonkhanowu.”
Chinthu china chapadera pamsonkhanowu chinachitika Lachisanu pa 25 July, pomwe M’bale Rutherford anawerenga molimba mtima chilengezo chomwe chinkatsutsa atsogoleri a chipembedzo. Iye ananena kuti: “Atsogoleri andale, achipembedzo komanso amalonda ankaletsa anthu kudziwa choonadi chokhudza Ufumu wa Mulungu womwe Mulungu adzagwiritse ntchito podalitsa anthu.” Ananenanso kuti anthuwa “ankalakwitsa kwambiri chifukwa ankathandiza bungwe la League of Nations n’kumanena kuti ‘ndi njira imene Mulungu akugwiritsa ntchito polamulira dziko lapansi.’” Ophunzira Baibulo ankafunika kulimba mtima kwambiri kuti alalikire uthenga umenewu kwa anthu.
Pofotokoza za msonkhanowu, nkhani ina ya mu Nsanja ya Olonda inanena kuti: “Anthu amene anapezeka pamsonkhano ku Columbus anabwerera kwawo chikhulupiriro chitalimba . . . , sankaopa chilichonse, ndipo anali okonzeka kulalikira molimba mtima ngakhale azitsutsidwa.” M’bale Leo Claus, yemwe anapezeka pamsonkhanowu ananena kuti: “Tinachoka pamsonkhanowu tili okonzeka kukagawa timapepala tokhala ndi uthenga umenewu kwa anthu a m’gawo lathu.”
Mu October, Ophunzira Baibulo anayamba kugwira ntchito yogawira timapepala mamiliyoni tokhala ndi uthenga womwe M’bale Rutherford analengeza munkhani yake. Ku tauni ya Cleveland, ku Oklahoma, Frank Johnson anamaliza kugawira timapepala m’gawo limene anapatsidwa, kutatsala maminitsi 20 kuti ofalitsa anzake abwere kudzamutenga. Podikira anzakewo, iye sakanatha kuima pamalo oonekera chifukwa anthu a m’tauniyo omwe anakwiya chifukwa cha ntchito yolalikirayi ankamufunafuna. Choncho m’baleyu anaganiza zokabisala m’tchalitchi china chomwe chinali pafupi. Atapeza kuti mulibe anthu, iye anasiya timapepala tija m’Baibulo la m’busa wa tchalitchicho komanso pampando uliwonse. Atatero, iye anatuluka mwamsanga. Popeza kuti nthawi inali idakalipobe, anachitanso chimodzimodzi m’matchalitchi ena awiri.
Kenako anapita mwamsanga pamalo pamene anagwirizana kuti akakumane ndi ofalitsa anzake aja. Iye anabisala kuseli kwa malo ogulitsira mafuta a galimoto kuti anthu omwe ankamufunafuna aja asamuone. Anthuwo anadutsadi pamalowo ali pagalimoto koma sanamuone. Anthu aja atapita, ofalitsa anzake omwe ankalalikira chapafupi anafika kudzamutenga pa galimoto.
M’bale wina ananena kuti “tikutuluka m’tauniyo tinadutsa matchalitchi atatu aja. Pa tchalitchi chilichonse tinapeza pataima anthu pafupifupi 50. Anthu ena ankawerenga kapepalako pomwe ena ankakaimika m’mwamba pomusonyeza m’busa wawo. Tinachoka mwamsanga m’deralo kuti tisakumane ndi mavuto. Koma timathokoza Mulungu wathu Yehova chifukwa chotiteteza komanso kutipatsa nzeru kuti adani a Ufumu asatilepheretse kugawa timapepalati.”
KULIKONSE OPHUNZIRA BAIBULO ANKALALIKIRA MOLIMBA MTIMA
M’mayiko enanso, Ophunzira Baibulo ankalalikira molimba mtima. Kumpoto kwa dziko la France, M’bale Józef Krett ankalalikira kwa anthu ochokera kudziko la Poland omwe ankagwira ntchito m’migodi. Panakonzedwa zoti iye akakambe nkhani ya mutu wakuti “Posachedwapa Akufa Adzaukitsidwa.” Abale ndi alongo atagawa timapepala toitanira anthu kuti adzamvetsere nkhaniyo, wansembe wina anachenjeza anthu a m’tchalitchi chake kuti asapite. Komabe si zomwe zinachitika. Anthu oposa 5,000 anamvetsera nkhaniyo kuphatikizaponso wansembeyo. M’bale Krett anapempha wansembeyo kuti afotokoze zimene amakhulupirira koma anakana. M’bale Krett anagawira anthuwo mabuku onse amene anali nawo ataona kuti iwo ankafuna kudziwa zambiri zokhudza Mawu a Mulungu.—Amosi 8:11.
Ku Africa, M’bale Claude Brown ndi amene anapita ndi uthenga wabwino ku Gold Coast, komwe panopa ndi ku Ghana. Nkhani zomwe ankakamba komanso mabuku omwe ankagawira zinathandiza kuti choonadi chifalikire mofulumira m’dzikolo. John Blankson, yemwe ankachita maphunziro okhudzana ndi zamankhwala anamvetsera imodzi mwa nkhani za M’bale Brown. Nthawi yomweyo anazindikira kuti wapeza choonadi. Iye ananena kuti: “Choonadi chinandisangalatsa kwambiri, moti ndinkauza aliyense za choonadichi kusukulu.”
Tsiku lina John anapita kutchalitchi cha Anglican kuti akafunse wansembe zokhudza Utatu chifukwa anali atamvetsa bwino kuti mfundo imeneyi si ya m’Malemba. Wansembeyo anamuthamangitsa kwinaku akufuula kuti: “Choka! Si iwe Mkhristu koma ndiwe wa Mdyerekezi!”
Atafika kunyumba, John analembera kalata wansembeyo yomupempha kuti adzakambirane zokhudza Utatu pagulu la anthu. Wansembeyo anamuyankha pomuitanitsa kuti akakumane naye ku ofesi ya mphunzitsi wamkulu wa pasukulu ya zamankhwala imene ankaphunzirapo ija. Mphunzitsi wamkuluyo anamufunsa ngati analemberadi kalata wansembeyo.
John anayankha kuti “Ee ndinalembadi.”
Mphunzitsiyo analamula John kuti alembere kalata wansembeyo yomupepesa. Ndiye John analemba kuti:
“Aphunzitsi anga andiuza kuti ndilembe kalata yokupepesani ndipo ndine wokonzeka kulemba kalatayo ngati mungavomereze kuti mumaphunzitsa zabodza.”
Modabwa kwambiri mphunzitsiyo anamufunsa John kuti, “Zoona zimenezi ndi zimene ukufunadi kulemba?”
Iye anayankha kuti, “Inde ndi zimene ndikufuna ndilembe.”
“Uchotsedwa sukulu. Sungakhale pasukuluyi n’kumanyoza wansembe wa tchalitchi chomwe ndi chodziwika ndi boma.”
Ndiyeno John anafunsa kuti, “Aphunzitsi . . . mukamaphunzitsa ndiye pakakhala mfundo zimene sitikumvetsa, kodi sitimakufunsani mafunso?”
Mphunzitsiyo anayankha kuti, “Mumatha kufunsa.”
John anayankha kuti: “Zimenezotu ndi zimene zinachitika. Iwo aja ankaphunzitsa Baibulo ndiye ine ndinawafunsa funso. Ndiye atalephera kuyankha funsolo n’chifukwa chiyani ndikufunika kulemba kalata yowapepesa?”
Pamapeto pake, John sanachotsedwe sukulu ndipo sanalembenso kalata yopepesa.
OPHUNZIRA BAIBULO ANALI OFUNITSITSA KUCHITA ZAMBIRI
Pofotokoza zimene zinachitika m’chakachi, Nsanja ya Olonda inanena kuti: “Tsopano tingathe kunena ngati Davide kuti: ‘Inu mudzandipatsa mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo. Mudzachititsa kuti adani anga agonje.’ (Salimo 18:39) Zimene zachitika m’chakachi ndi zolimbikitsa kwambiri chifukwa takhala tikuona dzanja la Ambuye likutithandiza . . . Atumiki ake okhulupirika . . . akhala akuchitira umboni mosangalala.”
Chakumapeto kwa chakacho, abale anakonza zoti pakhale wailesi inanso youlutsa mawu. Nyumba youlutsira mawuyi inamangidwa ku Chicago. Wailesi yatsopanoyi inkadziwika ndi dzina lakuti MAWU. Wailesiyi inkagwiritsa ntchito zipangizo zamphamvu. Moti anthu amene anali kutali, ngakhale kumpoto kwa dziko la Canada ankatha kumva uthenga wa Ufumu.
Mu 1925 munachitikanso zinthu zosangalatsa chifukwa Ophunzira Baibulo anamvetsa bwino mfundo za mu Chivumbulutso chaputala 12. Kwa ena, zimenezo zinachititsa kuti asiye kutumikira Yehova. Koma ambiri anasangalala kumvetsa mfundo zimene anaphunzira, zokhudza zimene zinachitika kumwamba komanso mmene zimenezo zinakhudzira anthu padzikoli.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA