NKHANI YOPHUNZIRA 43

Kodi Tingatani Kuti Tisiye Kukayikira?

Kodi Tingatani Kuti Tisiye Kukayikira?

“Muzifufuza zinthu zonse n’kutsimikizira.”1 ATES. 5:21.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite ngati timakayikira zinthu zina zomwe zikhoza kusokoneza utumiki wathu kwa Yehova.

1-2. (a) Kodi atumiki a Yehova ena amakayikira zinthu ziti? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

 MUNTHU aliyense nthawi zina amakayikira a zinthu zina. Mwachitsanzo, wachinyamata wa Mboni angamakayikire ngati Yehova amamukonda. Choncho angamakayikirenso zoti abatizidwe. Chitsanzo china chingakhale cha bambo amene ali wachinyamata, anasankha kuti azitumikira Yehova m’malo mopeza ntchito ya ndalama zambiri. Pambuyo pokumana ndi mavuto a zachuma, angamakayikire ngati anasankha bwino. Taganiziraninso za mlongo wachikulire yemwe alibe mphamvu zokwanira. Iye angamakhumudwe chifukwa sangathe kuchita zambiri ngati poyamba. Kodi inuyo munayamba mwadzifunsapo kuti: ‘Kodi Yehova amandikonda? Kodi ndinachita bwino kusankha kuti ndizimutumikira? Kodi iye amaona kuti ndine wofunikabe?’

2 Ngati sitingapeze mayankho a mafunso ngati amenewa, tikhoza kusiya kukhulupirira Yehova ndipo mwinanso tingasiye kumulambira. Munkhaniyi tikambirana mmene mfundo za m’Baibulo zingatithandizire ngati tikukayikira zoti (1) Yehova amatikonda, (2) tinasankha bwino, komanso (3) Yehova amaonabe kuti ndife ofunika.

ZIMENE TINGACHITE KUTI TISIYE KUKAYIKIRA

3. N’chiyani chingatithandize ngati tikukayikira zinthu zina?

3 Chinthu china chimene chingatithandize ngati tikukayikira zinthu zina ndi kuwerenga Mawu a Mulungu kuti tipeze mayankho a mafunso athu. Tikatero tidzapeza mphamvu, tidzakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso ‘tidzakhala ndi chikhulupiriro cholimba.’—1 Akor. 16:13.

4. Kodi tingatani kuti ‘tizifufuza zinthu zonse n’kutsimikizira’? (1 Atesalonika 5:21)

4 Werengani 1 Atesalonika 5:21. Palembali, Baibulo likutilimbikitsa kuti ‘tizifufuza zinthu zonse, n’kutsimikizira.’ Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kutsimikizira kuti zimene timakhulupirira ndi zoona poziyerekezera ndi zimene Baibulo limanena. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti wachinyamata akukayikira zoti Yehova amamukonda. Kodi iye ayenera kungokhulupirira kuti basi samukondadi? Ayi, m’malomwake ayenera kufufuza maganizo a Yehova pa nkhaniyo kuti atsimikizire.

5. Kodi Yehova angatithandize bwanji kupeza mayankho pa mafunso athu?

5 Tikamawerenga Mawu a Mulungu zimakhala ngati tikumva Yehova akutilankhula. Koma timafunika kuchita khama kuti tipeze maganizo a Yehova pa funso limene tili nalo. Tikamawerenga, tiyenera kuganizira kwambiri zimene zikutidetsa nkhawazo. Tingafufuze zambiri pa nkhaniyo pogwiritsa ntchito zinthu zothandiza pophunzira zimene gulu la Yehova latipatsa. (Miy. 2:​3-6) Tingapemphe Yehova kuti atithandize pa nthawi imene tikufufuzayo kuti tidziwe maganizo ake. Kenako tingafufuze mfundo za m’Baibulo zomwe zingatithandize pa nkhani yathuyo. Tingachite bwinonso kuganizira nkhani za m’Baibulo za anthu amene anakumana ndi vuto ngati lathulo.

6. Kodi misonkhano ingatithandize bwanji kuti tisiye kukayikira?

6 Pamisonkhano yathu timakhalanso ngati tikumva Yehova akutilankhula. Ngati nthawi zonse timapezeka pamisonkhano, tikhoza kumva mfundo inayake munkhani kapena ndemanga imene wina wapereka yomwe ingatithandize kuti tisiye kukayikira. (Miy. 27:17) Tsopano tiyeni tikambirane zimene tingachite kuti tisiye kukayikira pa mfundo zitatu zija.

MUKAMAKAYIKIRA ZOTI YEHOVA AMAKUKONDANI

7. Kodi anthu ena amadzifunsa funso liti?

7 Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti, ‘Kodi Yehova amandikonda?’ Ngati mumadziona kuti ndinu wosafunika, mukhoza kumaganiza kuti n’zosatheka kukhala pa ubwenzi ndi Mlengi wa chilengedwe chonse. Mfumu Davide ayenera kuti analinso ndi maganizo amenewa. Ankadabwa ndi mfundo yakuti Yehova amachita chidwi ndi anthu moti ananena kuti: “Inu Yehova, munthu ndi ndani kuti muzimuganizira, kodi mwana wa munthu ndi ndani kuti muzimuwerengera?” (Sal. 144:3) Kodi tingapeze kuti yankho la funso limeneli?

8. Mogwirizana ndi 1 Samueli 16:​6, 7, 10-12, kodi Yehova amaona chiyani mwa anthu?

8 Baibulo limasonyeza kuti Yehova amaganizira anthu amene amaoneka ngati osafunika kwa anthu ena. Mwachitsanzo, Yehova anatuma Samueli kuti akadzoze mmodzi mwa ana a Jese kuti akhale mfumu ya Isiraeli. Jese anaitana ana ake 7 kuti akakumane ndi Samueli koma sanaitane Davide, yemwe anali wamng’ono kwambiri. b Koma Davideyo ndi amene Yehova anamusankha. (Werengani 1 Samueli 16:​6, 7, 10-12.) Yehova anaona zimene zinali mumtima mwa Davide ndipo anazindikira kuti anali munthu wokonda Mulungu.

9. N’chifukwa chiyani simuyenera kukayikira kuti Yehova amakuganizirani? (Onaninso chithunzi.)

9 Yehova wasonyeza kale kuti amakuganizirani. Mwachitsanzo, amakupatsani malangizo ogwirizana ndi zimene mukufunikira. (Sal. 32:8) Zimenezi sizikanatheka akanakhala kuti samakudziwani bwino. (Sal. 139:1) Mukayamba kugwiritsira ntchito malangizo a Yehova n’kuona mmene akukuthandizirani, simukayikira kuti iye amakukondani. (1 Mbiri 28:9; Mac. 17:​26, 27) Yehova amaona zonse zomwe mumachita kuti muzimutumikira. Amaonanso makhalidwe abwino omwe muli nawo ndipo amafuna kuti mukhale mnzake. (Yer. 17:10) Ndiponso amafuna kuti muvomere kukhala mnzake.—1 Yoh. 4:19.

“Ukamufunafuna [Yehova], adzalola kuti umupeze.”—1 Mbiri 28:9 (Onani ndime 9) c


MUKAMAKAYIKIRA ZIMENE MUNASANKHA

10. Kodi nthawi zina tingamakayikire chiyani tikaganizira zimene tinasankha?

10 Nthawi ikamapita, anthu ena amayamba kukayikira ngati anasankha bwino pa zinthu zina. Mwina anasankha kusiya bizinezi kapena ntchito yabwino n’cholinga choti azichita zambiri potumikira Yehova. Panopa mwina papita zaka zambiri ndipo amaona kuti anzawo amene anasankha zinthu zina sakukumana ndi mavuto a zachuma. Choncho angamadzifunse kuti: ‘Kodi ndinasankha bwino kuti ndizitumikira Yehova, kapena ndinataya mwayi?’

11. Kodi amene analemba Salimo 73 ankavutika ndi maganizo ati?

11 Ngati inunso munadzifunsapo mafunso amenewa, chitsanzo cha amene analemba Salimo 73 chingakuthandizeni. Iye ankaona anthu ena omwe ankaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino ndipo sankada nkhawa. (Sal. 73:​3-5, 12) Akaganizira zimenezo, ankangoona kuti kutumikira Yehova ndi kutaya nthawi. Maganizo amenewa ankachititsa kuti ‘azivutika tsiku lonse.’ (Sal. 73:​13, 14) Ndiye kodi iye anatani?

12. Mogwirizana ndi Salimo 73:​16-18, kodi n’chiyani chinathandiza wolemba Salimoli kuti asiye kukayikira?

12 Werengani Salimo 73:​16-18. Wolemba Salimoli anapita pamalo abata kukachisi wa Yehova. Atafika kumeneko anayamba kuganiza bwino. Iye anazindikira kuti ngakhale kuti anthu ena ankaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino, tsogolo lawo silinali labwino. Ataganizira zimenezi mtima wake unakhala m’malo ndipo anaona kuti anasankha bwino kuti azitumikira Yehova. Zimenezi zinamupatsa mphamvu kuti azipitiriza kutumikira Yehova.—Sal. 73:​23-28.

13. Kodi mungatani kuti mtima wanu ukhale m’malo ngati mukukayikira zoti munasankha bwino? (Onaninso chithunzi.)

13 Kodi Mawu a Mulungu angakuthandizeni bwanji kuti mtima wanu ukhale m’malo? Muziganizira zinthu zabwino zimene mwapeza. Mwachitsanzo, muziyerekezera madalitso amene Yehova wakulonjezani ndi zinthu zimene dzikoli lingakupatseni panopa. Anthu enawo angamadalire zimene akwanitsa kupeza m’dzikoli chifukwa chakuti alibe chiyembekezo chilichonse m’tsogolo. Koma inuyo Yehova wakulonjezani zinthu zabwino kwambiri kuposa zimene mungaziganizire. (Sal. 145:16) Taganiziraninso funso ili: Kodi tinganene motsimikiza mmene moyo wathu ukanakhalira zikanakhala kuti tinasankha zinthu zina? Chomwe muyenera kudziwa ndi chakuti amene amasankha zochita chifukwa chokonda Mulungu ndi anthu, nthawi zonse amapezabe zinthu zowathandiza kukhala osangalala.

Tiziyembekezera madalitso amene Yehova watilonjeza (Onani ndime 13) d


TIKAMAKAYIKIRA ZOTI YEHOVA AMAONABE KUTI NDIFE OFUNIKA

14. N’chifukwa chiyani anthu ena amadzikayikira, nanga ndi funso liti limene limawavutitsa?

14 Atumiki a Yehova ena amavutika chifukwa cha matenda, ukalamba kapena mavuto ena okhudza thanzi lawo. Izi zingachititse kuti azikayikira ngati Yehova amawaonabe kuti ndi amtengo wapatali. Angamadzifunse kuti, ‘Kodi Yehova amaonabe kuti ndine wofunika?’

15. Kodi wolemba Salimo 71 sankakayikira za chiyani?

15 Wolemba Salimo 71 ankakayikiranso ngati Yehova amamuona kuti ndi wofunika. Iye anapemphera kuti: “Musandisiye pa nthawi imene mphamvu zanga zatha.” (Sal. 71:​9, 18) Koma iye sankakayikira kuti ngati angapitirize kutumikira Mulungu mokhulupirika, Yehova adzamutsogolera komanso kumuthandiza. Wolemba Salimoyu anazindikira kuti Yehova amasangalala ndi anthu amene amapitiriza kumutumikira ngakhale pamene sakutha kuchita zambiri.—Sal. 37:​23-25.

16. Kodi achikulire ndi ofunika kwa Yehova m’njira ziti? (Salimo 92:​12-15)

16 Ngati ndinu wachikulire, muyenera kuganizira mmene Yehova amakuonerani. Ngakhale kuti mphamvu zanu zikuchepa iye angakuthandizeni kuti mukhale amphamvu mwauzimu. (Werengani Salimo 92:​12-15.) M’malo moganizira zimene simungathe kuchita, muziganizira zimene mungakwanitse. Mwachitsanzo, zimene mumachita komanso mtima wanu wokonda anthu zikhoza kulimbikitsa anthu ena. Mukhoza kufotokozera ena mmene Yehova wakhala akukuthandizirani kwa zaka zambiri komanso malonjezo a m’Baibulo amene mukuwayembekezera kwambiri. Musamakayikirenso kuti mapemphero anu ochokera pansi pa mtima akhoza kuthandiza anthu ena. (1 Pet. 3:12) Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tonsefe tikhoza kupereka kanthu kenakake kwa Yehova komanso kwa anthu ena.

17. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudziyerekezera ndi anthu ena?

17 Ngati mukuona kuti simukuchita zambiri potumikira Yehova, dziwani kuti iye amayamikira kwambiri zimene mumakwanitsa kuchita. Nthawi zina mungayambe kuyerekezera zimene mumachita ndi zimene ena amachita. N’chifukwa chiyani muyenera kupewa zimenezi? Chifukwa chakuti Yehova samakuyerekezerani ndi ena. (Agal. 6:4) Mwachitsanzo, Mariya anapatsa Yesu mphatso ya mafuta amtengo wapatali. (Yoh. 12:​3-5) Koma mkazi wina wamasiye anapereka kukachisi tindalama tiwiri tochepa mphamvu. (Luka 21:​1-4) Koma Yesu anaona kuti akazi onsewa anasonyeza chikhulupiriro. Ndipo Atate wake Yehova, amayamikira zilizonse zimene mumachita chifukwa choti munadzipereka kwa iye ndipo mumamukonda, kaya zikhale zochepa bwanji.

18. N’chiyani chingatithandize kuti tisiye kukayikira? (Onaninso bokosi lakuti “ Mawu a Yehova Angatithandize Kuti Tisiye Kukayikira.”)

18 Tonsefe nthawi zina timakayikira zinthu zina. Koma munkhaniyi taona kuti Mawu a Mulungu angatithandize kuti tisiye kukayikira. Choncho muzichita zonse zimene mungathe kuti musiye kukayikira ndipo mukatero mtima wanu udzakhala m’malo. Yehova amaona kuti inuyo panokha ndinu ofunika. Iye amayamikira zonse zimene mumachita kuti muzimutumikira ndipo adzakupatsani mphoto. Musamakayikire kuti Yehova amakonda komanso kuganizira atumiki ake onse okhulupirika.

NYIMBO NA. 111 Tili ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala

a MATANTHAUZO A MAWU ENA: Munkhaniyi tikukambirana za kukayikira ngati Yehova amatikonda kapenanso ngati tinasankha bwino. Sitikukambirana za kukayikira kumene Baibulo limasonyeza kuti ndi umboni wakuti sitikukhulupirira Yehova kapena malonjezo ake.

b Baibulo silitiuza zaka zimene Davide anali nazo pamene Yehova anamusankha, koma ayenera kuti anali asanakwanitse zaka 20.—Onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 2011, tsamba 29, ndime 2.

c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Wachinyamata wa Mboni akufufuza m’Malemba kuti adziwe maganizo a Yehova.

d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akugwira ntchito kuti apezere banja lake zinthu zofunika, koma akuganiziranso kwambiri zimene zidzachitike m’Paradaiso.