MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA

Muzibwereza Mfundo Zikuluzikulu

Muzibwereza Mfundo Zikuluzikulu

Kodi nthawi zina mumavutika kukumbukira zimene mwaphunzira? Tonsefe zimenezi zimatichitikira zina. Ndiye kodi chingatithandize n’chiyani? Tizibwereza mfundo zikuluzikulu.

Mukamaphunzira mudziima kaye n’kuona mfundo zofunika kwambiri. Chitsanzo ndi zimene Paulo anachita pothandiza anthu kuona mfundo zikuluzikulu za m’kalata yake. Iye analemba kuti: “Pa zimene tikunenazi, mfundo yaikulu ndi yakuti.” (Aheb. 8:1) Mawu amenewa anathandiza anthu amene ankawerenga kalata yake kutsatira mfundo yake komanso kuona kugwirizana pakati pa mfundo zing’onozing’ono ndi mutu wankhani.

Mukamaliza kuphunzira, mungachite bwino kumakhala ndi nthawi yoganizira mfundo zikuluzikulu zomwe mwaphunzira, mwina kwa maminitsi 10. Ngati simukuzikumbukira, mutha kuona mitu ing’onoing’ono kapena ziganizo zoyambirira za ndime iliyonse. Mukaphunzira mfundo inayake yatsopano muziyesa kuifotokoza m’mawu anuanu. Mukamabwereza mfundo zikuluzikulu, mudzatha kukumbukira mfundozo komanso kuona mmene zikukuthandizirani pa moyo wanu.