Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi nyimbo zinali zofunika bwanji m’nthawi ya Aisiraeli?

NYIMBO zinali zofunika kwambiri pa chikhalidwe cha Aisiraeli. Baibulo limasonyeza kuti nyimbo zina zinkaimbidwa ndi zida pomwe zina zinkaimbidwa ndi pakamwa. Ndipotu mbali ina ya Malemba ndi nyimbo, monga buku la Masalimo, Nyimbo ya Solomo komanso Maliro. Buku lina linanena kuti Baibulo limasonyeza kuti “kalelo anthu ankaimba nyimbo pa zochitika zosiyanasiyana.”—Music in Biblical Life.

Ankaimba nyimbo pa zochitika za tsiku ndi tsiku. Aisiraeli ankaimba nyimbo posonyeza mmene ankamvera. (Yes. 30:29) Akazi ankagwiritsa ntchito maseche kwinaku akuimba mosangalala komanso kuvina pa mwambo woveka ufumu, pa zikondwerero komanso ngati apambana nkhondo. (Owe. 11:34; 1 Sam. 18:​6, 7; 1 Maf. 1:​39, 40) Aisiraeli ankaimbanso nyimbo zokhudza mtima pa nthawi ya maliro. (2 Mbiri 35:25) Buku lina linanena kuti n’zoonekeratu “kuti Aisiraeli ankakonda nyimbo.”—McClintock and Strong’s Cyclopedia.

Ankaimba nyimbo m’nyumba yachifumu. Mafumu a Aisiraeli ankasangalala kwambiri ndi nyimbo. Mwachitsanzo, Mfumu Sauli anaitana Davide ku nyumba yachifumu kuti azikaimba nyimbo. (1 Sam. 16:​18, 23) Ndipo pambuyo pake Davide atakhala mfumu anakonza zipangizo zoimbira, anapeka nyimbo zabwino komanso anakonza zoti pakhale gulu loimba nyimbo pakachisi wa Yehova. (2 Mbiri 7:6; Amosi 6:5) Mfumu Solomo analinso ndi oimba aamuna ndi aakazi.—Mla. 2:8.

Ankaimba polambira. Chofunika kwambiri ndi chakuti Aisiraeli ankaimba nyimbo polambira Yehova. Mwachitsanzo, pakachisi ku Yerusalemu panali oimba 4,000. (1 Mbiri 23:5) Iwo ankaimba pogwiritsa ntchito zinganga, zoimbira za zingwe, azeze komanso malipenga. (2 Mbiri 5:12) Koma sikuti anthu amene ankaimba polambira Yehova anali akatswiri okhaokha. Zikuoneka kuti Aisiraeli ambiri ankaimba Nyimbo Zokwerera Kumzinda akamapita ku zikondwerero ku Yerusalemu. (Sal. 120-134) Ndipo zolemba za Ayuda zimasonyeza kuti Aisiraeli ankaimba nyimbo zokhala ndi mawu akuti Tamandani Ya, a pa mwambo wa Pasika.

Nyimbo ndi zofunikabe kwa anthu a Mulungu masiku ano. (Yak. 5:13) Timaimba tikamalambira Mulungu. (Aef. 5:19) Ndipo nyimbo zimatithandiza kuti tizigwirizana ndi Akhristu anzathu. (Akol. 3:16) Zimatilimbikitsanso tikamakumana ndi mavuto. (Mac 16:25) Nyimbo zimatithandiza kwambiri kusonyeza kuti timakhulupirira Yehova komanso timamukonda.

a Ayuda ankaimba nyimbo zokhala ndi mawu akuti Tamandani Ya, zopezeka mu Salimo 113 mpaka 118 potamanda Yehova.