NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA April 2020
M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira June 1–July 5, 2020.
Gulu Lankhondo Lochokera Kumpoto
Nkhani yophunzira 14: mlungu wa June 1-7, 2020. Kodi pali zifukwa 4 ziti zochititsa kuti tisinthe kafotokozedwe ka ulosi wa m’chaputala 1 ndi 2 cha buku la Yoweli?
Kodi Anthu Am’gawo Lanu Mumawaona Bwanji?
Nkhani yophunzira 15: Mlungu wa June 8-14, 2020. Onani zimene mungachite kuti muzitsanzira Yesu komanso Paulo poganizira zimene anthu amene mumakumana nawo amakhulupirira, amakonda komanso powaona kuti akhoza kukhala ophunzira a Khristu.
Tizimvetsera Anthu, Kuwadziwa Komanso Kuwachitira Chifundo
Nkhani yophunzira 16: June 15-21, 2020. Yehova anathandiza Yona, Eliya, Hagara komanso Loti. Phunzirani nkhaniyi kuti muone zomwe mungachite potsanzira Yehova pa nkhani yochita zinthu ndi anthu ena.
“Ndakutchani Mabwenzi”
Nkhani yophunzira 17: Mlungu wa June 22-28, 2020. Timakumana ndi mavuto ambiri pamene tikuyesetsa kuti tikhale anzake a Yesu. Komabe ndi zotheka kuthana nawo.
‘Tizithamanga Panjirayo Mpaka pa Mapeto’
Nkhani yophunzira 18: Mlungu wa June 29–July 5, 2020. Kodi tingatani kuti tipambane pampikisano wokapeza moyo ngakhale kuti tikulimbana ndi ukalamba kapena matenda aakulu?