NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA August 2017

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa September 25 mpaka October 22, 2017.

Kodi Mukhoza Kuyembekezera Moleza Mtima?

Atumiki okhulupirika a Yehova akale anafunsa kuti ayenera kupirira mavuto mpaka liti. Koma Mulungu sanawadzudzule chifukwa chofunsa zimenezi.

‘Mtendere wa Mulungu Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse’

Kodi munadzifunsapo chifukwa chimene Mulungu analolera kuti mukumane ndi mavuto enaake? Ngati ndi choncho, n’chiyani chingakuthandizeni kupirira mavuto uku mukukhulupirirabe Mulungu ndi mtima wonse?

Vulani Umunthu Wakale Ndipo Musauvalenso

Tiyenera kuvula umunthu wakale ndipo tisauvalenso. Kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi ngakhale kuti kale tinkachita zinthu zoipa kwambiri?

Valani Umunthu Watsopano Ndipo Musauvulenso

Yehova angakuthandizeni kuti mukhale ndi makhalidwe amene amamusangalatsa. Werengani kuti mudziwe njira zina zimene mungasonyezere chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa komanso kufatsa.