Valani Umunthu Watsopano Ndipo Musauvulenso
“Muvale umunthu watsopano.”—AKOL. 3:10.
NYIMBO: 43, 106
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti n’zotheka kuvala umunthu watsopano? (b) Kodi lemba la Akolose 3:10-14 limatchula makhalidwe ati omwe amapanga umunthu watsopano?
MAWU akuti “umunthu watsopano” amapezeka maulendo awiri mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika. (Aef. 4:24; Akol. 3:10) Umunthuwu ‘umagwirizana ndi chifuniro cha Mulungu’ ndipo n’zotheka kukhala nawo. Tikutero chifukwa chakuti Mulungu analenga anthu m’chifaniziro chake choncho n’zotheka kusonyeza makhalidwe ake abwino.—Gen. 1:26, 27; Aef. 5:1.
2 N’zoona kuti uchimo umene tinatengera kwa makolo athu oyambirira ungachititse kuti tizilakalaka zinthu zolakwika. N’kuthekanso kuti timasokonezedwa ndi dziko limene tikukhalamoli. Koma Yehova akhoza kutithandiza mwachifundo kuti tikhale ndi makhalidwe amene amafuna. Munkhaniyi tikambirana mbali zosiyanasiyana za umunthu watsopano zimene Paulo analemba ndipo zimenezi zitilimbikitsa kuti tiziyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene amasangalatsa Mulungu. (Werengani Akolose 3:10-14.) Tionanso mmene tingasonyezere makhalidwewa tikamalalikira.
NDIFE ANTHU OFANANA
3. Tchulani khalidwe lina lomwe limapanga umunthu watsopano.
3 Paulo atanena kuti tiyenera kuvala umunthu watsopano, anafotokoza kufunika kokhala opanda tsankho. Khalidweli ndi mbali ina yofunika ya umunthu watsopano. Iye anati: “Sipadzakhala Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti, kapolo, kapena mfulu.” a N’chifukwa chiyani Akhristufe sitiyenera kusankha anthu chifukwa cha mtundu wawo, dziko lawo kapena chuma chawo? Zili choncho chifukwa Baibulo limanena kuti tili ngati “munthu mmodzi,” kutanthauza kuti ndife ofanana.—Akol. 3:11; Agal. 3:28.
4. (a) Kodi atumiki a Yehova ayenera kuchita bwanji zinthu ndi anthu ena? (b) Kodi n’chiyani chikhoza kusokoneza mgwirizano wa Akhristu?
4 Akhristu amene avala umunthu watsopano amalemekeza Akhristu anzawo komanso anthu ena mosaganizira mtundu wawo kapena chikhalidwe chawo. (Aroma 2:11) M’mayiko ena kuchita zimenezi ndi kovuta. Mwachitsanzo, kale ku South Africa, kunali lamulo loti kumadera ena kuzingokhala anthu akuda okhaokha, kwina azungu okhaokha ndipo kwina anthu a mitundu ina. A Mboni ambiri akukhalabe m’madera oterewa. Choncho mu October 2013, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti pakhale pulogalamu yothandiza abale kuti ‘afutukule mitima yawo’ n’kuyamba kudziwana ndi abale osiyanasiyana. (2 Akor. 6:13) Kodi pulogalamuyi ndi yotani?
5, 6. (a) Kodi panakonzedwa zotani kuti anthu a Mulungu a m’dziko lina azigwirizana kwambiri? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Kodi pulogalamuyi yathandiza bwanji?
5 Panakonzedwa kuti mipingo iwiri ya zilankhulo zosiyana kapena ya mitundu yosiyana izichitira limodzi zinthu masiku ena. Abale ndi alongo a mipingo yonse iwiri ankalalikira limodzi, kusonkhana limodzi komanso kuitanirana kunyumba zawo. Mipingo yambiri inayamba kuchita zimenezi ndipo ofesi ya nthambi inamva anthu ambiri akuyamikira pulogalamuyi ndipo ena si a Mboni. Mwachitsanzo, m’busa wina ananena kuti: “Si ine wa Mboni, koma ndinganene kuti a Mboninu mumagwira ntchito yolalikira mwadongosolo kwambiri ndipo simusankhana mitundu.” Kodi pulogalamuyi yathandiza bwanji abale ndi alongo?
6 Mlongo wina wachikhosa dzina lake Noma ankaopa kuti aitane abale achizungu kunyumba yake yaing’ono. Koma atalalikira limodzi ndi abalewa komanso kucheza kunyumba zawo, ananena kuti: “Anthuwa ndi ife sitikusiyana.” Choncho itafika nthawi yoti mpingo wachikhosa ulandire anthu amumpingo wachingelezi, iye anakonza chakudya n’kuitana abale ena. Pa abale amene anawaitanawo panali mkulu wina wachizungu. Noma anati: “Ndinasangalala kuona kuti analolera kukhala pakireti.” Pulogalamu imeneyi yathandiza kuti abale ndi alongo a mitundu yosiyana ayambe kugwirizana ndipo akupitiriza kuchita zimenezi.
‘VALANI CHIFUNDO CHACHIKULU NDI KUKOMA MTIMA’
7. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala achifundo?
7 Anthufe tizikumanabe ndi mavuto mpaka dziko la Satanali litawonongedwa. Tikhoza kuvutika ndi matenda, kuzunzidwa, ngozi zadzidzidzi, kusowa ntchito, kuberedwa komanso mavuto ena. Kuti tikwanitse kuthandizana pa mavuto ngati amenewa, tiyenera kukhala anthu achifundo. Chifundo chachikulu chingatilimbikitse kuti tikhale anthu okoma mtima. (Aef. 4:32) Makhalidwe awiriwa angatithandize kuti tizitsanzira Mulungu komanso tizilimbikitsa anthu ena.—2 Akor. 1:3, 4.
8. Kodi chingachitike n’chiyani tikamasonyeza chifundo komanso kukoma mtima kwa anthu onse mumpingo? Perekani chitsanzo.
8 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaganizira anthu ochokera m’mayiko ena kapena anthu ovutika mumpingo? Tiyenera kucheza nawo ndiponso kuwathandiza kuona kuti ndi ofunika kwambiri mumpingo. (1 Akor. 12:22, 25) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira m’bale wina dzina lake Dannykarl. M’baleyu anasamuka ku Philippines kupita ku Japan. Kuntchito kwake anthu sankamulemekeza ngati mmene ankachitira ndi anthu akomweko. Koma atapita kumisonkhano ya Mboni za Yehova anaona kusiyana kwambiri. Iye anati: “Anthu onse anali a ku Japan koma anandilandira bwino ngati tinkadziwana kale.” Abalewo ankamusonyeza kukoma mtima ndipo izi zinamuthandiza kuti apitirize kuphunzira za Yehova. Iye anabatizidwa ndipo panopa ndi mkulu. Akulu anzake amaona kuti iye ndi mkazi wake Jennifer amathandiza kwambiri mumpingo. Akuluwo anati: “Moyo wa m’bale ndi mlongoyu ndi wosalira zambiri ndipo akuchita upainiya. Iwo amapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yoika patsogolo zinthu za Ufumu.”—Luka 12:31.
9, 10. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti tikamachitira ena chifundo mu utumiki timadalitsidwa.
9 Tikamalalikira uthenga wa Ufumu, timakhalanso ndi mwayi ‘wochitira anthu onse zabwino.’ (Agal. 6:10) Abale ndi alongo ambiri amachitira chifundo anthu ochokera m’mayiko ena moti amaphunzira chilankhulo chawo ndipo zotsatira zake ndi zabwino kwambiri. (1 Akor. 9:23) Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Tiffany, amene akuchita upainiya ku Australia, anaphunzira Chiswahili n’cholinga choti azikathandiza mumpingo wachilankhulochi mumzinda wa Brisbane. N’zoona kuti kuphunzira chilankhulochi kunali kovuta koma Tiffany wadalitsidwa kwambiri. Iye anati: “Ngati mukufuna kuti muzisangalala ndi utumiki, mungachite bwino kutumikira mumpingo wachilankhulo china. Zimakhala ngati wakaona dziko lina popanda kuchoka kwanu. Umaoneratu kuti anthufe tili pa ubale wapadziko lonse ndipo timagwirizana.”
10 Chitsanzo china ndi cha banja lina la ku Japan. Mwana wamkazi wa m’banjali dzina lake Sakiko ananena kuti: “Cha m’ma 1990, tinkakumana ndi anthu ochokera ku Brazil tikamalalikira. Tinkagwiritsa ntchito Baibulo lachipwitikizi powawerengera malemba monga Chivumbulutso 21:3, 4 kapena Salimo 37:10, 11, 29. Iwo ankamvetsera mwachidwi ndipo nthawi zina ankafika polira chifukwa chokhudzidwa ndi lembalo.” Banjali linkawachitira chifundo kwambiri anthuwa moti Sakiko ananena kuti: “Titaona kuti anthuwa akufunitsitsa kuphunzira za Mulungu, banja lathu linayamba kuphunzira Chipwitikizi.” Patapita nthawi, banjali linathandiza kuyambitsa mpingo wachipwitikizi ndipo lathandiza anthu ambiri amene asamukira m’dzikoli kuti ayambe kutumikira Yehova. Sakiko ananenanso kuti: “Kuphunzira Chipwitikizi sikunali kophweka, koma talandira madalitso ambiri chifukwa chochita zimenezi. Tikuthokoza kwambiri Yehova.”—Werengani Machitidwe 10:34, 35.
‘VALANI KUDZICHEPETSA’
11, 12. (a) Kodi tiyenera kukhala ndi cholinga chiti povala umunthu watsopano, nanga tiyenera kukumbukira mfundo iti? (b) N’chiyani chingatithandize kukhala odzichepetsa?
11 Cholinga chathu povala umunthu watsopano chiyenera kukhala kulemekeza Yehova osati kuti anthu azitilemekeza. Tizikumbukira kuti mngelo wina, yemwe poyamba anali wangwiro, anachimwa chifukwa chakuti anayamba kudzikuza. (Yerekezerani ndi Ezekieli 28:17.) Ngati mngelo wangwiro anayamba kudzikuza kuli bwanji anthu ochimwafe? Ngakhale zili choncho, n’zotheka kuti tivale kudzichepetsa. N’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi?
12 Kuti tikhale odzichepetsa tiyenera kupeza nthawi tsiku lililonse yoti tiwerenge Mawu a Mulungu ndiponso kusinkhasinkha zimene tawerengazo. (Deut. 17:18-20) Tingachite bwino kwambiri kuganizira zimene Yesu ankaphunzitsa ndiponso zimene ankachita potumikira ena modzichepetsa. (Mat. 20:28) Mwachitsanzo, Yesu anasambitsa mapazi a atumwi ake. (Yoh. 13:12-17) Tizipemphanso mzimu wa Mulungu kuti uzitithandiza kupewa mtima wodziona kuti ndife apamwamba kuposa ena.—Agal. 6:3, 4; Afil. 2:3.
13. Kodi timadalitsidwa bwanji tikamakhala odzichepetsa?
13 Werengani Miyambo 22:4. Atumiki onse a Yehova ayenera kukhala odzichepetsa ndipo akamachita zimenezi amadalitsidwa. Tikamakhala odzichepetsa timathandiza kuti mumpingo mukhale mtendere komanso mgwirizano. Tikamayesetsa kukhala odzichepetsa Mulungu amatisonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu. Paja mtumwi Petulo ananena kuti: “Nonsenu muzichitirana zinthu modzichepetsa, chifukwa Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”—1 Pet. 5:5.
‘VALANI KUFATSA NDI KULEZA MTIMA’
14. Kodi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kufatsa ndi kuleza mtima ndi ndani?
14 Masiku ano, anthu ofatsa komanso oleza mtima amaonedwa kuti ndi opepera. Koma maganizo amenewa ndi olakwika kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti makhalidwe awiriwa amachokera kwa Mulungu yemwe ndi wamphamvu kuposa aliyense m’chilengedwe chonse. Yehova Mulungu ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kufatsa komanso kuleza mtima. (2 Pet. 3:9) Mwachitsanzo, taganizirani zimene anachita kudzera mwa angelo ake pamene Abulahamu komanso Loti ankamufunsa mafunso. (Gen. 18:22-33; 19:18-21) Komanso kwa zaka zoposa 1,500, Yehova ankalezera mtima Aisiraeli omwe ankavuta kwambiri.—Ezek. 33:11.
15. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani ya kufatsa komanso kuleza mtima?
15 Nayenso Yesu anali “wofatsa.” (Mat. 11:29) Iye ankalezera mtima kwambiri otsatira ake pamene ankalakwitsa zinthu. Komanso ali padzikoli, ankatsutsidwa kwambiri ndi atsogoleri achipembedzo. Komabe sanasiye kukhala wofatsa ndiponso woleza mtima mpaka pamene anaphedwa. Ali pamtengo wozunzikirapo, iye anapemphera kuti Atate wake akhululukire anthu amene amukhomera pamtengowo ndipo ananena kuti “sakudziwa chimene akuchita.” (Luka 23:34) Apatu Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kufatsa komanso kuleza mtima ngakhale zinthu zitavuta kwambiri.—Werengani 1 Petulo 2:21-23.
16. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ofatsa komanso oleza mtima?
16 Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ofatsa komanso oleza mtima? Paulo ananena njira imodzi imene tingachitire zimenezi pamene anauza Akhristu anzake kuti: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.” (Akol. 3:13) Kunena zoona, pamafunika kufatsa komanso kuleza mtima kuti titsatire lamulo limeneli. Koma tikamakhululukira anzathu timathandiza kuti mumpingo mukhale mgwirizano.
17. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kufatsa ndi kuleza mtima ndi makhalidwe ofunika kwambiri?
17 Mkhristu aliyense ayenera kukhala wofatsa komanso woleza mtima. Zili choncho chifukwa chakuti popanda kuchita zimenezi sangadzapulumuke. (Mat. 5:5; Yak. 1:21) Koma chofunika kwambiri n’chakuti tikakhala ndi makhalidwe amenewa timalemekeza Yehova komanso timathandiza ena kuti azitsatira malangizo a m’Baibulo.—Agal. 6:1; 2 Tim. 2:24, 25.
“VALANI CHIKONDI”
18. Kodi kupanda tsankho kumagwirizana bwanji ndi chikondi?
18 Makhalidwe abwino onse amene takambiranawa amagwirizana kwambiri ndi chikondi. Mwachitsanzo, Yakobo analangiza abale ake kuti asamakondere anthu achuma. Iye ananena kuti khalidwe lokonderalo limaphwanya lamulo lachifumu lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” Kenako ananena kuti: “Mukapitiriza kukhala okondera, mukuchita tchimo.” (Yak. 2:8, 9) Chikondi chimatithandiza kuti tisamakondere anthu chifukwa cha maphunziro awo, mtundu wawo kapena chuma chawo. Koma munthu ayenera kukhala wopanda tsankho kuchokera mumtima osati kungodzionetsera kuti alibe tsankho.
19. N’chifukwa chiyani tiyenera kuvala chikondi?
19 Baibulo limanenanso kuti ‘chikondi n’choleza mtima, n’chokoma mtima komanso sichidzikuza.’ (1 Akor. 13:4) N’zosatheka kupitiriza kulalikira uthenga wa Ufumu ngati munthu si woleza mtima, wokoma mtima komanso wodzichepetsa. (Mat. 28:19) Makhalidwe amenewa amathandizanso kuti tizikhala bwinobwino ndi abale ndi alongo onse mumpingo. Kodi chimachitika n’chiyani tikamasonyeza chikondi m’njira imeneyi? Mipingo imakhala yogwirizana kwambiri ndipo izi zimalemekeza Yehova komanso kuthandiza kuti anthu ena ayambe kumutumikira. M’pomveka kuti Baibulo likamafotokoza za umunthu watsopano limamaliza ndi mfundo yamphamvu yakuti: “Kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.”—Akol. 3:14.
PITIRIZANI ‘KUPHUNZITSIDWA KUTI MUKHALE ATSOPANO’
20. (a) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi? (b) Kodi tonsefe tikuyembekezera nthawi iti?
20 Aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndi zinthu zina ziti zimene ndiyenera kuchita kuti ndivule umunthu wakale ndipo ndisauvalenso?’ Tiyenera kupemphera kuchokera pansi pa mtima kuti Mulungu atithandize. Tiziyesetsanso kuchotsa maganizo oipa alionse komanso kusiyiratu makhalidwe alionse amene angatilepheretse kulowa mu Ufumu wa Mulungu. (Agal. 5:19-21) Tiyeneranso kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikupitiriza kuphunzira kuti ndikhale watsopano “mu mphamvu yoyendetsa maganizo” anga?’ (Aef. 4:23, 24) Mkhristu aliyense ayenera kuvala umunthu watsopano n’kumayesetsa kuti asauvulenso. Ayenera kuchita zimenezi mpaka nthawi imene tonse tidzatha kusonyeza bwinobwino umunthuwu. Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri ikadzafika nthawi imene aliyense padzikoli adzakhale wangwiro n’kumasonyeza bwinobwino umunthu watsopano.
a Kale Asukuti ankanyozedwa chifukwa ankaonedwa kuti anali anthu osaphunzira.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA