NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA February 2020

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira April 6–May 3, 2020.

Atate Wathu Yehova Amatikonda Kwambiri

Tisamakayikire kuti Atate wathu Yehova amatikonda komanso kutisamalira ndipo sangatisiye.

Timakonda Kwambiri Atate Wathu Yehova

Onani zinthu zimene tingachite posonyeza kuti timakonda kwambiri Atate wathu Yehova.

Muzipewa Nsanje Kuti Muzikhala Mwamtendere

Nthawi zina tikhoza kumavutika ndi mtima wa nsanje. Onani zimene tingachite kuti tipewe nsanje n’kumakhala mwamtendere ndi anzathu.

Muzilola Kuti Yehova Azikutonthozani

Hana, mtumwi Paulo ndi Mfumu Davide ankavutika ndi nkhawa. Kodi tingaphunzire chiyani tikaganizira mmene Yehova anawatonthozera?