NKHANI YOPHUNZIRA 8

Muzipewa Nsanje Kuti Muzikhala Mwamtendere

Muzipewa Nsanje Kuti Muzikhala Mwamtendere

“Tiyeni titsatire zinthu zobweretsa mtendere ndiponso zolimbikitsana.”​—AROMA 14:19.

NYIMBO NA. 113 Yehova Amatipatsa Mtendere

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi nsanje inasokoneza bwanji banja la Yosefe?

YAKOBO ankakonda ana ake onse, koma ankakonda kwambiri mwana wake wazaka 17 dzina lake Yosefe. Kodi abale ake a Yosefe anatani? Iwo ankamuchitira nsanje ndipo zimenezi zinachititsa kuti ayambe kumuda. Yosefe sanachite chilichonse chochititsa kuti azidedwa. Koma abale akewo anamugulitsa kuti akhale kapolo n’kukanamiza bambo awo kuti waphedwa ndi chilombo cholusa. Nsanje inawachititsa kuti asokoneze mtendere wa banja lonse komanso amvetse chisoni kwambiri bambo awo.​—Gen. 37:3, 4, 27-34.

2. Malinga ndi Agalatiya 5:19-21, kodi nsanje ndi yoopsa bwanji?

2 Malemba amasonyeza kuti nsanje * ili m’gulu la “ntchito za thupi” zimene zingachititse kuti munthu asadzalowe mu Ufumu wa Mulungu. (Werengani Agalatiya 5:19-21.) Ndipo nsanje ndi imene imayambitsa mavuto ena monga udani, ndewu ndi kupsa mtima.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Zimene abale ake a Yosefe anachita zimasonyeza mmene nsanje ingasokonezere ubwenzi wa anthu komanso mtendere m’banja. N’zoona kuti sitingachite zimene abale ake a Yosefe anachita, koma tonsefe si angwiro ndipo tili ndi mtima wonyenga. (Yer. 17:9) Choncho n’zosadabwitsa kuti nthawi zina tingalimbane ndi kamtima kansanje. Tiyeni tikambirane zitsanzo zina za m’Baibulo zimene zingatithandize kudziwa zinthu zina zimene zingayambitse nsanje. Kenako tikambirana zinthu zimene zingatithandize kupewa nsanje n’kumalimbikitsa mtendere.

ZINTHU ZIMENE ZINGATICHITITSE NSANJE

4. N’chifukwa chiyani Afilisiti ankachitira nsanje Isaki?

4 Chuma. Isaki anali ndi chuma ndipo Afilisiti ankamuchitira nsanje. (Gen. 26:12-14) Iwo anafika pokwirira zitsime zake zomwe ankagwiritsa ntchito pomwetsera ziweto. (Gen. 26:15, 16, 27) Mofanana ndi Afilisiti, anthu ena masiku ano amachitira nsanje anthu amene ali ndi chuma chambiri. Sikuti amangosirira zimene ali nazo koma amafunanso kuti asakhale nazo.

5. N’chifukwa chiyani atsogoleri achipembedzo ankachitira Yesu nsanje?

5 Kukondedwa. Atsogoleri achipembedzo chachiyuda ankachitira Yesu nsanje chifukwa choti anthu ambiri ankamukonda. (Mat. 7:28, 29) Yesu ankaimira Mulungu komanso ankaphunzitsa mfundo zachoonadi. Ngakhale zinali choncho, atsogoleriwo ankafalitsa mabodza okhudza Yesu n’cholinga choti aipitse mbiri yake. (Maliko 15:10; Yoh. 11:47, 48; 12:12, 13, 19) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhaniyi? Tiyenera kupewa kamtima kochitira nsanje anthu amene ali ndi makhalidwe omwe amachititsa anthu ambiri mumpingo kuwakonda. M’malomwake, tiziyesetsa kutsanzira makhalidwe awo abwino.​—1 Akor. 11:1; 3 Yoh. 11.

6. Kodi Diotirefe anasonyeza bwanji kuti ankachita nsanje?

6 Utumiki. Nthawi ya atumwi, Diotirefe ankachitira nsanje anthu amene ankatsogolera mumpingo. Iye ankafuna “kukhala woyamba” pakati pa Akhristu, choncho ankanenera zamwano mtumwi Yohane ndi abale ena amene ankatsogolera n’cholinga choti aipitse mbiri yawo. (3 Yoh. 9, 10) Mwina sitingafike pochita zinthu ngati Diotirefe koma tikhoza kuyamba kuchitira nsanje anthu amene apatsidwa utumiki umene timaulakalaka, makamaka ngati tikuona kuti nafenso ndi oyenera kulandira utumikiwo.

Mtima wathu uli ngati dothi, ndipo makhalidwe athu abwino ali ngati maluwa okongola. Koma nsanje ili ngati chomera choipa kwambiri. Nsanje ingalepheretse munthu kukhala ndi makhalidwe abwino monga chikondi, chifundo ndi kukoma mtima (Onani ndime 7)

7. Kodi nsanje ndi yoopsa bwanji?

7 Nsanje ili ngati chomera choipa kwambiri. Ikangozika mizu mumtima mwathu zimakhala zovuta kwambiri kuti tiichotse. Ndipo imakula chifukwa cha makhalidwe ena oipa monga kusirira, kudzikuza ndi kudzikonda. Nsanje ikhoza kulepheretsa munthu kukhala ndi makhalidwe abwino monga chikondi, chifundo ndi kukoma mtima. Choncho tikangozindikira kuti tayamba kamtima ka nsanje tiyenera kukachotseratu. Kodi tingapewe bwanji mtima wa nsanje?

MUZIYESETSA KUKHALA ODZICHEPETSA KOMANSO KUKHUTIRA NDI ZIMENE MULI NAZO

Kodi tingapewe bwanji nsanje? Mzimu woyera wa Mulungu ungatithandize kuchotsa nsanje n’kuyamba kukhala odzichepetsa komanso okhutira (Onani ndime 8-9)

8. Kodi ndi makhalidwe ati amene angatithandize kupewa nsanje?

8 Kukhala odzichepetsa komanso kukhutira ndi zimene tili nazo kungatithandize kupewa nsanje. Tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino, nsanje singakule mumtima mwathu. Kudzichepetsa kumathandiza munthu kuti azidziona moyenera komanso azipewa kuganiza kuti ndi woyenera kukhala ndi zinthu zabwino kuposa aliyense. (Agal. 6:3, 4) Munthu wokhutira ndi zimene ali nazo sadziyerekezera ndi anthu ena. (1 Tim. 6:7, 8) Munthu wodzichepetsa komanso wokhutira ndi zimene ali nazo amasangalala akaona kuti munthu wina walandira zinthu zabwino.

9. Malinga ndi Agalatiya 5:16 ndi Afilipi 2:3, 4, kodi mzimu woyera ungatithandize bwanji?

9 Tiyenera kuthandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu kuti tipewe nsanje n’kumakhala odzichepetsa ndiponso okhutira ndi zimene tili nazo. (Werengani Agalatiya 5:16; Afilipi 2:3, 4.) Mzimu woyera wa Yehova ungatithandize kudzifufuza kuti tidziwe zonse zimene zili m’maganizo komanso mumtima mwathu. Mulungu angatithandize kuchotsa maganizo oipa n’kukhala ndi maganizo abwino. (Sal. 26:2; 51:10) Tsopano tiyeni tikambirane chitsanzo cha Mose ndi Paulo, omwe ankapewa nsanje.

Mnyamata wina wathamanga kuti akauze Mose ndi Yoswa kuti amuna awiri mumsasamo akuchita zinthu ngati aneneri. Yoswa akupempha Mose kuti awaletse koma Mose akukana. M’malomwake, akuuza Yoswa kuti akusangalala kuti Yehova wapatsa amuna awiriwo mzimu wake. (Onani ndime 10)

10. N’chiyani chikanachititsa kuti Mose achite nsanje? (Onani chithunzi chapachikuto.)

10 Mose ankatsogolera anthu a Mulungu koma sankachitira nsanje anthu ena amene anapatsidwa udindo. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Yehova anachotsa mphamvu ina ya mzimu woyera kwa Mose n’kuipereka kwa akulu ena achiisiraeli omwe ankaima pafupi ndi chihema chokumanako. Kenako Mose anamva kuti akulu awiri amene sanapite kuchihemacho analandiranso mzimu woyera ndipo anayamba kuchita zinthu ngati aneneri. Kodi iye anatani Yoswa atamuuza kuti awaletse akuluwo? Mose ataona kuti Yehova akugwiritsa ntchito akulu awiriwo sanawachitire nsanje. M’malomwake, iye anasonyeza kudzichepetsa ndipo anasangalala nawo chifukwa cha udindo umene anapatsidwa. (Num. 11:24-29) Kodi tikuphunzira chiyani kwa Mose?

Kodi akulu angatsanzire bwanji kudzichepetsa kwa Mose? (Onani ndime 11-12) *

11. Kodi akulu angatsanzire bwanji Mose?

11 Ngati ndinu mkulu, kodi munapemphedwapo kuti muphunzitse munthu wina kuti azichita utumiki umene mumaukonda kwambiri? Mwachitsanzo, mwina mumasangalala ndi udindo wanu wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Koma ngati ndinu wodzichepetsa ngati Mose, simungadandaule ngati mwapemphedwa kuphunzitsa m’bale wina kuti azidzachititsa. M’malomwake, mudzasangalala kuthandiza m’bale wanuyo.

12. Kodi Akhristu ambiri masiku ano akusonyeza bwanji kuti ndi odzichepetsa komanso okhutira ndi zimene ali nazo?

12 Tiyeni tikambirane nkhani ina imene ikukhudza abale ambiri achikulire. Kwa zaka zambiri, abalewo akhala akutumikira monga ogwirizanitsa ntchito za akulu. Koma akafika zaka 80 amalola kuti anthu ena atenge udindowo. Oyang’anira madera amene akwanitsa zaka 70 amasonyezanso kudzichepetsa posiya udindowo n’kuyamba utumiki wina. Komanso anthu ambiri pa Beteli alandira utumiki watsopano. Abale ndi alongo okhulupirikawa sachitira nsanje anthu amene akugwira ntchito zimene iwo ankagwira kale.

13. Kodi n’chiyani chikanachititsa Paulo kuti achitire nsanje atumwi 12?

13 Chitsanzo china pa nkhaniyi ndi Mtumwi Paulo. Iye sanalole kuti nsanje ikule mumtima mwake. Paulo ankachita khama mu utumiki koma ananena modzichepetsa kuti: “Ineyo ndine wamng’ono kwambiri mwa atumwi onse, ndipo si ine woyenera kutchedwa mtumwi.” (1 Akor. 15:9, 10) Atumwi 12 ankayenda ndi Yesu pamene ankatumikira padzikoli, koma Paulo sanakhale Mkhristu mpaka Yesu ataphedwa n’kuukitsidwa. Ngakhale kuti anasankhidwa kukhala ‘mtumwi wotumidwa kwa mitundu ina,’ sanapatsidwe mwayi wokhala mmodzi wa atumwi 12 aja. (Aroma 11:13; Mac. 1:21-26) Koma Paulo ankakhutira ndi zinthu zimene anali nazo ndipo sanachitire nsanje atumwi 12 omwe ankagwirizana kwambiri ndi Yesu aja.

14. Ngati ndife odzichepetsa ndiponso okhutira ndi zimene tili nazo, kodi tidzachita chiyani?

14 Ngati ndife odzichepetsa komanso okhutira ndi zimene tili nazo ngati Paulo, tidzalemekeza anthu amene Yehova wawapatsa udindo. (Mac. 21:20-26) Iye wakonza zoti abale ena azitsogolera mumpingo. Yehova amaona kuti abale amenewa ndi “mphatso za amuna” ngakhale kuti si angwiro. (Aef. 4:8, 11) Tikamalemekeza abalewa komanso kutsatira modzichepetsa malangizo amene amapereka, timakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndiponso timakhala mwamtendere ndi Akhristu anzathu.

“TITSATIRE ZINTHU ZOBWERETSA MTENDERE”

15. Kodi tiyenera kuchita chiyani?

15 Ngati anthu akuchitirana nsanje, mtendere sungakhalepo. Choncho tiyenera kuchotseratu nsanje mumtima mwathu komanso kupewa zinthu zimene zingayambitse nsanje m’mitima ya anthu ena. Tiyenera kuchita zimenezi pomvera lamulo la Yehova lakuti: “Titsatire zinthu zobweretsa mtendere ndiponso zolimbikitsana.” (Aroma 14:19) Kodi tingathandize bwanji anthu ena kuti asayambe mtima wansanje, nanga tingalimbikitse bwanji mtendere?

16. Kodi tingathandize bwanji ena kuti azipewa nsanje?

16 Zochita zathu zimakhudza kwambiri anthu ena. Dzikoli limalimbikitsa mtima ‘wodzionetsera ndi zinthu zimene tili nazo.’ (1 Yoh. 2:16) Koma mtima umenewu ndi umene umalimbikitsa nsanje. Kuti tithandize ena kupewa nsanje, tiyenera kupewa kulankhulalankhula za zinthu zimene tili nazo kapena zimene tikufuna kugula. Tingachitenso bwino kukhala ndi maganizo odzichepetsa pa nkhani ya maudindo amene tili nawo mumpingo. Tikutero chifukwa chakuti tikamadzionetsera pa maudindo amene tili nawo tingachititse anthu ena kuyamba nsanje. Koma tikamasonyeza kuti timaganizira anthu ena komanso kuwayamikira pa zinthu zabwino zimene amachita, timawathandiza kuti azikhala okhutira ndipo timalimbikitsa mgwirizano ndi mtendere mumpingo.

17. Kodi abale ake a Yosefe anathandiza kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

17 Tingakwanitse kupewa nsanje. Tiyeni tiganizirenso chitsanzo cha abale ake a Yosefe. Patapita zaka zambiri kuchokera pamene anagulitsa Yosefe, iwo anakumana naye ku Iguputo. Yosefe asanadziulule kwa abale ake, anawayesa kuti aone ngati asintha. Iye anakonza zoti adyere limodzi ndipo anapatsa Benjamini chakudya chambiri kuposa ena onse. (Gen. 43:33, 34) Koma Baibulo silisonyeza kuti abale ake anamuchitira nsanje. M’malomwake, ankadera nkhawa Benjamini komanso bambo awo kuchokera pansi pamtima. (Gen. 44:30-34) Popeza abale ake a Yosefe anasiya kuchita nsanje, iwo anathandiza kuti m’banja mwawo mukhalenso mtendere. (Gen. 45:4, 15) Ifenso tikamapewa nsanje, tidzathandiza kuti m’banja komanso mumpingo mwathu mukhale mtendere.

18. Malinga ndi Yakobo 3:17, 18, n’chiyani chingachitike tikamayesetsa kukhala mwamtendere?

18 Yehova amafuna kuti tizipewa nsanje n’kumalimbikitsa mtendere. Koma tiyenera kuchita khama kuti zimenezi zitheke. Monga taonera munkhaniyi, anthufe mwachibadwa timakhala ndi kamtima kansanje. (Yak. 4:5) Ndipo anthu ambiri m’dzikoli amalimbikitsa nsanje. Koma tingapewe nsanje tikamayesetsa kukhala odzichepetsa, okhutira ndi zomwe tili nazo komanso oyamikira. Tikamatero tizikhala mwamtendere ndi anzathu ndipo tidzakhala achikondi, okoma mtima komanso achifundo.​—Werengani Yakobo 3:17, 18.

NYIMBO NA. 130 Muzikhululuka

^ ndime 5 M’gulu la Yehova muli mtendere. Koma ngati titayamba mtima wansanje, mtendere umenewu ukhoza kusokonekera. Munkhaniyi tikambirana zinthu zimene zingayambitse nsanje. Kenako tidzakambirana zimene tingachite kuti tipewe mtima umenewu n’kumalimbikitsa mtendere.

^ ndime 2 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Malinga ndi zimene Baibulo limanena, nsanje ingachititse munthu kusirira zinthu za munthu wina mpaka kufika pofuna kuti asakhale nazo.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pamsonkhano wa bungwe la akulu, m’bale wachikulire yemwe amachititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda wapemphedwa kuti aphunzitse mkulu wachinyamata kuti azichititsa phunzirolo. Ngakhale kuti m’bale wachikulireyo amakonda kwambiri udindo wakewu, akuchita zinthu mogwirizana ndi zimene akulu asankha pouza m’bale wachinyamatayo zimene zingamuthandize kuti azichititsa bwino komanso akumuyamikira.