NKHANI YOPHUNZIRA 7

Timakonda Kwambiri Atate Wathu Yehova

Timakonda Kwambiri Atate Wathu Yehova

“Timasonyeza chikondi, chifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.”​—1 YOH. 4:19.

NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. N’chifukwa chiyani Yehova anatipatsa mwayi wokhala m’banja lake, nanga anachita bwanji zimenezi?

YEHOVA watilola kuti tikhale m’banja la atumiki ake. Uwutu ndi mwayi waukulu kwambiri. M’banja lathuli muli anthu amene adzipereka kwa Mulungu ndipo amasonyeza kuti amakhulupirira nsembe ya dipo ya Mwana wake. Banja lathu ndi losangalala kwambiri. Zili choncho chifukwa timakhala ndi moyo wabwino panopa komanso tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha, kaya kumwamba kapena padzikoli.

2 Chifukwa chotikonda, Yehova anakonza zoti tikhale m’banja lake ngakhale kuti zinali zovuta kwambiri. (Yoh. 3:16) Paja iye ‘anatigula pa mtengo wokwera.’ (1 Akor. 6:20) Yehova anakonza zoti dipo liperekedwe kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. Choncho tili ndi mwayi woti Munthu wamkulu kwambiri m’chilengedwe chonse akhale Atate wathu. Malinga ndi zimene tinaphunzira munkhani yapita ija, Yehova ndi Atate wabwino kwambiri.

3. Kodi tingadzifunse mafunso ati? (Onani bokosi lakuti, “ Kodi Yehova Amandiwerengera?”)

3 Mofanana ndi wolemba Baibulo wina, tingadzifunse kuti: “Yehova ndidzamubwezera chiyani pa zabwino zonse zimene wandichitira?” (Sal. 116:12) Yankho la funsoli ndi lakuti palibe chimene tingamubwezere. Koma chikondi chake chimatichititsa kuti nafenso tizimukonda. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ife timasonyeza chikondi, chifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.” (1 Yoh. 4:19) Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Atate wathu wakumwamba?

MUZILIMBITSA UBWENZI WANU NDI YEHOVA

Timasonyeza kuti timakonda kwambiri Atate wathu Yehova tikamakonda kupemphera, tikamamumvera komanso tikamathandiza ena kuti azimukonda (Onani ndime 4-14)

4. Malinga ndi Yakobo 4:8, n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita khama kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

4 Yehova amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba komanso tizilankhulana naye. (Werengani Yakobo 4:8.) Amatilimbikitsa kuti ‘tizilimbikira kupemphera’ ndipo nthawi zonse amakhala wokonzeka kumva mapemphero athu. (Aroma 12:12) Iye sangatope kapena kutanganidwa kwambiri moti sangatimvetsere. Ifenso timamumvetsera tikamawerenga Baibulo komanso mabuku otithandiza kulimvetsa. Timamvanso mawu ake tikamamvetsera pamisonkhano. Tikamalankhula ndi Yehova komanso kumumvetsera nthawi zonse ubwenzi wathu umalimba ngati mmene zimakhalira makolo akamalankhulana pafupipafupi ndi ana awo.

Onani ndime 5

5. Kodi tingatani kuti mapemphero athu azikhala ochokera pansi pa mtima?

5 Kodi mapemphero anu amakhala otani? Yehova amafuna kuti tikamapemphera tizikhuthula zamumtima mwathu. (Sal. 62:8) Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi mapemphero anga amakhala ngati uthenga umene ndangokopera? Kapena amakhala ngati uthenga umene ndaulemba mochokera mumtima?’ N’zosachita kufunsa kuti mumakonda kwambiri Yehova ndipo mumafuna kukhala naye pa ubwenzi wolimba. Kuti zimenezi zitheke, muyenera kumalankhula naye pafupipafupi. Muzimuuza zakukhosi kwanu, zimene zikukusangalatsani komanso zimene zikukudetsani nkhawa. Ndipo musamakayikire kuti iye adzakuthandizani mukamupempha kuti akuthandizeni.

6. Kodi tingatani kuti tikhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Atate wathu wakumwamba?

6 Kuti tikhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Atate wathu wakumwamba, tiyenera kukhala ndi mtima woyamikira. Tizikhala ngati wolemba masalimo yemwe anati: “Inu Yehova Mulungu wanga, mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa, ndipo mumatiganizira. Palibe angafanane ndi inu. Ndikafuna kulankhula ndi kunena za zodabwitsazo, zimachuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.” (Sal. 40:5) Sikuti tizingokhala oyamikira mumtima mwathu, koma mawu ndi zochita zathu zizisonyeza kuti timayamikira Yehova. Izi zimachititsa kuti tizikhala osiyana kwambiri ndi anthu am’dzikoli. Anthu ambiri masiku ano sayamikira zimene Yehova amawachitira. Ndipo chizindikiro china chakuti tili ‘m’masiku otsiriza’ n’chakuti anthu ambiri ndi osayamika. (2 Tim. 3:1, 2) Tiyenera kupeweratu mtima umenewu.

7. Kodi Yehova amafuna kuti tizikhala bwanji ndi anzathu, nanga n’chifukwa chiyani?

7 Makolo amafuna kuti ana awo azigwirizana osati kukanganakangana. Nayenso Yehova amafuna kuti ana ake azigwirizana. Ndipo chikondi chimene timasonyezana n’chimene chimathandiza anthu kudziwa kuti ndife Akhristu enieni. (Yoh. 13:35) Tiyenera kukhala ngati wolemba masalimo amene analemba kuti: “Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!” (Sal. 133:1) Tikamakonda abale athu timasonyeza kuti timakondanso Yehova. (1 Yoh. 4:20) Timayamikira kwambiri kukhala m’banja la abale ndi alongo amene amakhala ‘okomerana mtima komanso achifundo chachikulu.’​—Aef. 4:32.

MUZISONYEZA KUTI MUMAKONDA YEHOVA POMUMVERA

Onani ndime 8

8. Malinga ndi 1 Yohane 5:3, kodi chifukwa chachikulu chotichititsa kumvera Yehova n’chiyani?

8 Yehova amafuna kuti ana azimvera makolo awo ndipo amafuna kuti ifeyo tizimumvera iyeyo. (Aef. 6:1) Tiyenera kumumveradi chifukwa ndi amene anatilenga, ndi amene amatipatsa zofunika pa moyo komanso ndi wanzeru kuposa makolo onse. Koma chifukwa chachikulu chotilimbikitsa kumvera Yehova n’chakuti timamukonda. (Werengani 1 Yohane 5:3.) Ngakhale kuti pali zifukwa zambiri zotichititsa kumumvera, iye satikakamiza kuchita zimenezi. Iye anatipatsa ufulu wosankha ndipo amasangalala tikamamumvera mwa kufuna kwathu.

9-10. Kodi kudziwa komanso kutsatira mfundo za Yehova n’kofunika bwanji?

9 Makolo amafuna kuti ana awo akhale otetezeka. N’chifukwa chake amawaphunzitsa makhalidwe abwino pofuna kuwateteza. Ana akamatsatira malangizo a makolo awo amasonyeza kuti amawadalira komanso kuwalemekeza. Ngati zili choncho ndi makolo, kuli bwanji Atate wathu wakumwamba? Kudziwa komanso kutsatira mfundo zake n’kofunika kwambiri. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timakonda Atate wathu komanso kumulemekeza ndipo zinthu zimatiyendera bwino. (Yes. 48:17, 18) Koma anthu amene amakana Yehova komanso mfundo zake amakumana ndi mavuto.​—Agal. 6:7, 8.

10 Tikamatsatira malangizo a Yehova timateteza thupi lathu, maganizo athu komanso moyo wathu wauzimu. Yehova amadziwa zinthu zimene zingatithandize kwambiri. Mlongo wina wa ku United States dzina lake Aurora anati: “Ndimadziwa kuti tikamamvera Yehova moyo wathu umakhala wabwino kwambiri.” Mfundo imeneyitu ndi yoona. Kodi inuyo kumvera Yehova kwakuthandizani bwanji?

11. Kodi pemphero limatithandiza bwanji?

11 Pemphero limatithandiza kuti tizikhala omvera ngakhale pamene kuchita zimenezi n’kovuta. Nthawi zina timavutika kumvera Yehova koma tiyenera kuyesetsa kulimbana ndi mtima wofuna kuchita zoipa. Wolemba masalimo anapempha Mulungu kuti: “Ndithandizeni kukhala wozindikira kuti nditsatire chilamulo chanu, ndiponso kuti ndichisunge ndi mtima wonse.” (Sal. 119:34) Mlongo wina dzina lake Denise, yemwe ndi mpainiya wokhazikika, ananena kuti: “Ndikamavutika kutsatira lamulo lina la Yehova ndimamupempha kuti andipatse mphamvu kuti ndichite zinthu zoyenera.” Tisamakayikire kuti Yehova adzayankha mapemphero ngati amenewa.​—Luka 11:9-13.

MUZITHANDIZA ANTHU ENA KUTI AZIKONDA ATATE WATHU

12. Mogwirizana ndi Aefeso 5:1, kodi tiyenera kuchita chiyani?

12 Werengani Aefeso 5:1. Popeza ndife ‘ana okondedwa’ a Yehova, timayesetsa kumutsanzira. Timatsanzira makhalidwe ake tikamachitira ena zinthu mwachikondi, mwachifundo komanso kuwakhululukira. Anthu amene sadziwa Mulungu akamaona makhalidwe athu abwino, zingawachititse kufuna kuti amudziwe bwino. (1 Pet. 2:12) Makolo achikhristu ayenera kutsanzira Yehova pochita zinthu ndi ana awo. Akamachita zimenezi, anawo angakhale ndi mtima wofuna kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Atate wathu wachikondi.

Onani ndime 13

13. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani?

13 Ana aang’ono amanyadira bambo awo ndipo amasangalala kuuza ena za bambo awowo. Nafenso timanyadira kwambiri Atate wathu wakumwamba Yehova ndipo timafuna kuti ena amudziwe. Timamva ngati mmene Mfumu Davide ankamvera. Iye analemba kuti: “Ndidzadzitamandira mwa Yehova.” (Sal. 34:2) Koma ngati ndife amanyazi, kodi tingatani kuti tikhale olimba mtima? Timalimba mtima tikamakumbukira kuti Yehova amasangalala tikamalalikira komanso kuti anthu amene angatimvetsere adzapeza madalitso. Yehova adzatithandiza kukhala olimba mtima. Iye anathandiza Akhristu oyambirira kulimba mtima ndipo adzatithandizanso ifeyo.​—1 Ates. 2:2.

14. N’chifukwa chiyani kugwira nawo ntchito yolalikira n’kofunika?

14 Yehova alibe tsankho ndipo amasangalala akaona kuti nafenso timakonda anthu amtundu uliwonse. (Mac. 10:34, 35) Njira yabwino kwambiri imene tingasonyezere kuti timakonda ena ndi kuwauza uthenga wabwino. (Mat. 28:19, 20) Kodi ntchito imeneyi ndi yothandiza bwanji? Anthu amene angatimvere angakhale ndi moyo wabwino panopa komanso angadzapeze moyo wosatha m’tsogolo.​—1 Tim. 4:16.

MUZIKONDA ATATE WATHU KUTI MUZISANGALALA

15-16. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatichititse kukhala osangalala?

15 Yehova ndi bambo wachikondi choncho amafuna kuti ana ake azikhala osangalala. (Yes. 65:14) Pali zinthu zambiri zotichititsa kukhala osangalala panopa ngakhale tikukumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, sitikayikira kuti Atate wathu wakumwamba amatikonda kwambiri. Timadziwanso mfundo zolondola za m’Mawu a Mulungu. (Yer. 15:16) Ndipo tili m’banja lapadera kwambiri la anthu amene amakonda Yehova ndi mfundo zake zapamwamba komanso amene amakondana.​—Sal. 106:4, 5.

16 Timakhalabe osangalala chifukwa sitikayikira kuti zinthu zidzakhala bwino kwambiri m’tsogolo. Tikudziwa kuti posachedwapa Yehova adzachotsa anthu onse oipa ndipo adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pokonza dzikoli kuti likhale labwino kwambiri. Tilinso ndi chiyembekezo chakuti amene anamwalira adzaukitsidwa n’kumakhalanso limodzi ndi anzawo. (Yoh. 5:28, 29) Zimenezitu zidzakhala zosangalatsa. Chofunika kwambiri n’chakuti posachedwapa, aliyense kumwamba komanso padziko lapansi adzakhala wodzipereka kwa Atate wathu wachikondi ndipo azidzamupatsa ulemu ndi ulemerero womuyenera.

NYIMBO NA. 12 Yehova Ndi Mulungu Wamkulu

^ ndime 5 Timadziwa kuti Atate wathu Yehova amatikonda kwambiri ndipo watithandiza kuti tikhale m’banja la atumiki ake. Izi zimachititsa kuti tizimukonda. Koma kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Atate wathu wachikondi? Munkhaniyi tikambirana zinthu zingapo zimene zingatithandize.