NKHANI YOPHUNZIRA 6

Zimene Baibulo Limatiuza Zokhudza Mlembi Wake

Zimene Baibulo Limatiuza Zokhudza Mlembi Wake

Lemba m’buku mawu onse amene ndidzalankhula nawe.”—YER. 30:2.

NYIMBO NA. 96 Buku la Mulungu Ndi Chuma

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. N’chifukwa chiyani mumayamikira Mulungu pokupatsani Baibulo?

 TIMAYAMIKIRA kwambiri Yehova chifukwa chotipatsa Baibulo. Kudzera m’bukuli, iye amatipatsa malangizo anzeru amene angatithandize kudziwa zomwe tingachite polimbana ndi mavuto omwe timakumana nawo masiku ano. Amatipatsanso chiyembekezo chosangalatsa cha m’tsogolo. Koposa zonse, kudzera m’Baibulo Yehova watidziwitsa zambiri zokhudza makhalidwe ake. Tikamaganizira makhalidwe ake abwinowa, timakhudzidwa mtima ndipo izi zimachititsa kuti tiyambe kukhala naye pa ubwenzi wolimba.​—Sal. 25:14.

2. Kodi Yehova anadzidziwikitsa kwa anthu pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana ziti?

2 Yehova amafuna kuti anthu amudziwe. M’mbuyomu, iye anadzidziwikitsa kwa anthu kudzera mwa angelo, m’maloto komanso m’masomphenya. (Num. 12:6; Mac. 10:3, 4) Koma kodi tikanadziwa bwanji zokhudza maloto, masomphenya kapena mauthenga ochokera kwa angelowa zikanakhala kuti sizinalembedwe penapake? Choncho pa chifukwa chabwino, Yehova anauza amuna kuti ‘alembe m’buku’ zimene ankafuna kuti tizidziwe. (Yer. 30:2) Popeza kuti “njira ya Mulungu woona ndi yangwiro,” sitikayikira kuti njira imene anagwiritsa ntchito polankhula nafeyi ndi yabwino kwambiri komanso yothandiza.​—Sal. 18:30.

3. Kodi Yehova anatani pofuna kuonetsetsa kuti Baibulo latetezedwa? (Yesaya 40:8)

3 Werengani Yesaya 40:8. Kwa zaka zambiri, Mawu a Mulungu akhala akupereka malangizo abwino kwa amuna ndi akazi okhulupirika. Kodi zimenezi zatheka bwanji? Funso limenelitu ndi labwino chifukwa Malembawa analembedwa kalekale pa zinthu zoti zitha kuwonongeka. Choncho masiku ano zolemba zoyambirira sizipezekanso. Koma Yehova anaonetsetsa kuti anthu akopera Malemba opatulika. Ngakhale kuti okoperawa sanali angwiro, anayesetsa kuchita zinthu mosamala kwambiri. Mwachitsanzo, ponena za Malemba a Chiheberi katswiri wina analemba kuti: “Tinganene motsimikiza kuti palibe buku lina lakale lomwe linakoperedwa molondola kwambiri ngati Malembawa.” Choncho ngakhale kuti zinthu zomwe analembapo zinali zoti zimawonongeka, okopera ake sanali angwiro komanso kuti padutsa nthawi yaitali, tingakhalebe otsimikiza kuti zimene timawerenga m’Baibulo masiku ano ndi maganizo a Mlembi wake, Yehova.

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Yehova ndi amene amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Yak. 1:17) Baibulo ndi imodzi mwa mphatso zabwino kwambiri zimene iye anatipatsa. Mphatso imatiuza zambiri zokhudza woperekayo kuti amatidziwa bwino komanso amadziwa zimene timafunikira. Ndi mmenenso zilili ndi Mulungu yemwe anatipatsa Baibulo. Timaphunzira zambiri zokhudza Yehova kudzera mu mphatsoyi. Timaphunziramonso kuti iye amatidziwa bwino kwambiri komanso amadziwa zimene timafunikira. Munkhaniyi, tikambirana mmene Baibulo limasonyezera atatu mwa makhalidwe a Yehova omwe ndi nzeru, chilungamo komanso chikondi. Choyamba, tiyeni tikambirane mmene Baibulo limasonyezera nzeru za Mulungu.

BAIBULO LIMASONYEZA NZERU ZA MULUNGU

5. Kodi ndi njira imodzi iti yomwe Baibulo limasonyezera nzeru za Mulungu?

5 Yehova amadziwa kuti timafunikira malangizo ake anzeru. Choncho mphatso ya Baibulo imene anatipatsa ndi yodzaza ndi malangizo anzeruwa ndipo amathandiza kwambiri anthu. Baibulo limasintha anthu. Mabuku oyambirira a Baibulo atalembedwa, Mose anauza Aisiraeli kuti: “Amenewa si mawu opanda pake kwa inu, chifukwa mawu amenewa ndiwo moyo wanu.” (Deut. 32:47) Anthu omwe ankatsatira malangizo a m’Malemba ankakhala moyo wabwino komanso wosangalala. (Sal. 1:2, 3) Ngakhale kuti Mawu a Mulungu analembedwa kalekale, adakali ndi mphamvu yosintha moyo wa anthu. Mwachitsanzo, munkhani zakuti “Baibulo Limasintha Anthu,” za pa jw.org, mungapezemo zitsanzo zoposa 50, zosonyeza mmene mfundo za m’Baibulo ‘zikugwiriranso ntchito mwa okhulupirira’ masiku ano.​—1 Ates. 2:13.

6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti palibe buku lofanana ndi Baibulo?

6 Palibe buku lililonse lomwe lingafanane ndi Mawu a Mulungu. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Mlembi wa bukuli, Yehova Mulungu, ndi Wamphamvuyonse, wamuyaya komanso nzeru zake ndi zosayerekezeka. Pali mabuku ambiri omwe anthu amawawerengabe ngakhale kuti olemba ake anamwalira. Komabe m’kupita kwa nthawi malangizo ake sakhalanso othandiza. Koma malangizo anzeru a m’Baibulo amakhala othandiza nthawi zonse ndipo amathandiza anthu a mibadwo yonse. Tikamawerenga buku lopatulikali komanso kuganizira zimene tikuphunzirazo, Mlembi wake amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera kutithandiza kuona mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu. (Sal. 119:27; Mal. 3:16; Aheb. 4:12) Choncho Mlembi wa Baibulo yemwe ndi wamoyo, ndi wofunitsitsa kutithandiza. Zimenezitu ziyenera kutilimbikitsa kuti tiziwerenga Baibulo nthawi zonse.

Kodi Baibulo lathandiza bwanji anthu a Yehova kukhala ogwirizana m’mbuyomu komanso masiku ano? (Onani ndime 7-8)

7. Kodi m’mbuyomu Baibulo linathandiza bwanji anthu a Mulungu kukhala ogwirizana?

7 Njira ina imene Baibulo limasonyezera nzeru za Mulungu ndi mmene limathandizira anthu a Mulungu kukhala ogwirizana. Pamene Aisiraeli analowa m’Dziko Lolonjezedwa, anakhazikika m’madera osiyanasiyana. Ena anakhala asodzi, ena ankaweta ng’ombe ndipo ena anali alimi. Aisiraeli omwe ankakhala dera lina akanatha kusiya kuganizira za Aisiraeli anzawo omwe ankakhala mbali ina m’dzikolo. Koma Yehova anakonza zoti nthawi zambiri Aisiraeli azikumana pamodzi n’cholinga choti amvetsere Mawu ake akamawerengedwa ndiponso kufotokozedwa. (Deut. 31:10-13; Neh. 8:2, 8, 18) Tangoganizani mmene Mwisiraeli wokhulupirika ankamvera akafika ku Yerusalemu n’kuona mamiliyoni a olambira anzake ochokera m’madera onse. Mwanjira imeneyi, Yehova ankathandiza anthu ake kukhala ogwirizana. M’kupita kwa nthawi, mpingo wa Chikhristu unakhazikitsidwa ndipo munali amuna ndi akazi olankhula zilankhulo zambiri. Ena anali olemera ndi otchuka ndipo ena anali osauka. Koma chifukwa chakuti ankakonda Malemba, onse anali ogwirizana polambira Mulungu woona. Anthu ena omwe anakhala okhulupirira akanatha kumvetsa Mawu a Mulungu pokhapokha ngati akanathandizidwa ndi olambira anzawo komanso kusonkhana nawo limodzi.​—Mac. 2:42; 8:30, 31.

8. Kodi Baibulo limathandiza bwanji anthu a Mulungu masiku ano kukhala ogwirizana?

8 Mulungu wathu wanzeru akupitiriza kuphunzitsa komanso kugwirizanitsa anthu ake pogwiritsa ntchito Baibulo. M’Baibulo muli choonadi chonse chokhudza Yehova chomwe timafunika kuchidziwa. Nthawi zonse timasonkhana pamodzi pamisonkhano ya mpingo, yadera komanso yachigawo kuti timvetsere Malemba akamawerengedwa komanso kufotokozedwa. Choncho Baibulo ndi lofunika kwambiri pokwaniritsa cholinga cha Yehova choti atumiki ake ‘azimutumikira mogwirizana.’​—Zef. 3:9.

9. Kodi ndi khalidwe lofunika liti lomwe tiyenera kukhala nalo kuti timvetse uthenga wa m’Baibulo? (Luka 10:21)

9 Tiyeni tione umboni wina wosonyeza nzeru za Yehova. Malemba ambiri analembedwa m’njira yakuti anthu odzichepetsa okha ndi omwe amatha kuwamvetsa mosavuta. (Werengani Luka 10:21.) Kulikonse anthu amawerenga Baibulo. Ponena za Baibulo, katswiri wina ananena kuti “anthu ambiri amakonda kuliwerenga kuposa buku lililonse, ndipo ndi buku limene amaliwerenga mosamala kwambiri.” Komatu ndi odzichepetsa okha omwe amamvetsa komanso kutsatira zimene limanena.​—2 Akor. 3:15, 16.

10. Kodi ndi njira ina iti imene Baibulo limasonyezera nzeru za Yehova?

10 Baibulo limatithandiza kuona nzeru za Yehova m’njira inanso. Yehova amagwiritsa ntchito Malemba pophunzitsa anthu ake onse monga gulu. Koma amaphunzitsanso ndi kulimbikitsa aliyense payekha. Tikamawerenga Mawu ake timaona kuti Yehova amachita chidwi ndi aliyense payekha. (Yes. 30:21) Pamene munakumana ndi mavuto, n’kutheka kuti kangapo munawerengapo mavesi omwe ankangooneka ngati alembedwera inuyo. Komatu Baibulo limathandiza anthu ambiri. Kodi zinatheka bwanji kuti likhale ndi mfundo zomwe zikugwirizana ndi zomwe inuyo mukufunikira? Zili choncho chifukwa Baibulo linalembedwa ndi Mlengi wanzeru kwambiri m’chilengedwe chonse.​—2 Tim. 3:16, 17.

BAIBULO LIMASONYEZA CHILUNGAMO CHA MULUNGU

11. Kodi Mulungu anasonyeza bwanji kupanda tsankho pamene Baibulo linkalembedwa?

11 Chilungamo ndi khalidwe lina la Yehova. (Deut. 32:4) Chilungamo chimayendera limodzi ndi kupanda tsankho ndipo Yehova ndi wopanda tsankho. (Mac. 10:34, 35; Aroma 2:11) Zimenezi zinaonekera bwino pomwe analola kuti Baibulo lilembedwe m’zilankhulo zosiyanasiyana. Mabuku 39 oyambirira a Baibulo analembedwa m’Chiheberi, chomwe anthu a Mulungu pa nthawiyo ankachimva mosavuta. Komabe pofika m’nthawi ya Akhristu oyambirira anthu ambiri ankalankhula Chigiriki. Choncho mabuku 27 omalizira a Baibulo analembedwa m’chilankhulochi. Yehova sanafune kuti Mawu ake apezeke m’chilankhulo chimodzi chokha. Masiku ano anthu pafupifupi 8 biliyoni padziko lonse amalankhula zilankhulo zambiri. Ndiye kodi zingatheke bwanji kuti anthu ambiri aphunzire za Yehova?

12. Kodi ndi njira imodzi iti yomwe lemba la Danieli 12:4, lakhala likukwaniritsidwira masiku otsiriza ano?

12 Kudzera mwa mneneri Danieli, Yehova analonjeza kuti m’nthawi ya mapeto, anthu “adzadziwa zinthu zambiri zoona” zopezeka m’Baibulo ndipo ambiri adzazimvetsa. (Werengani Danieli 12:4.) Chinthu chimodzi chimene chathandiza kuti anthu alimvetse ndi chakuti Baibulo komanso mabuku ofotokoza Baibulo zamasuliridwa, kufalitsidwa komanso kugawidwa kwa anthu ambiri. Baibulo ndi buku lomwe lamasuliridwa komanso kufalitsidwa kwambiri padziko lonse. Nthawi zambiri Mabaibulo omwe amasuliridwa komanso kusindikizidwa ndi amalonda amakhala odula kwambiri. Pofika pano, anthu a Yehova amasulira Baibulo lathunthu kapena mbali yake m’zilankhulo zoposa 240, ndipo aliyense akhoza kulipeza kwaulere. Zimenezi zikuthandiza kuti anthu amitundu yonse amve ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ mapeto asanafike. (Mat. 24:14) Mulungu wathu wachilungamo amafuna kuti anthu ambiri akhale ndi mwayi womudziwa powerenga Mawu ake. Izi zili choncho chifukwa chakuti iye amatikonda kwambiri tonsefe.

BAIBULO LIMASONYEZA CHIKONDI CHA MULUNGU

13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo limasonyeza chikondi cha Yehova? (Yohane 21:25)

13 Baibulo limatithandiza kumvetsa kuti khalidwe lalikulu la Mulungu ndi chikondi. (1 Yoh. 4:8) Taganizirani zimene iye analola kuti zilembedwe komanso zisalembedwe m’Baibulo. Iye anangotipatsa zomwe timafunikira kuti tikhale naye pa ubwenzi, tizikhala ndi moyo wosangalala panopa komanso kuti tidzapeze moyo wosatha. Choncho chifukwa choti Yehova amatikonda, sanatipatse malangizo ambirimbiri omwe ndi osafunika kwenikweni pa nkhani yomutumikira.​—Werengani Yohane 21:25.

14. Kodi zimene zili m’Baibulo zimasonyeza m’njira inanso iti kuti Mulungu amatikonda?

14 Yehova anasonyezanso kuti amatikonda polankhula nafe m’njira yotilemekeza. M’Baibulo, iye sanatipatse malamulo ambirimbiri otiuza zoyenera kuchita m’mbali iliyonse ya moyo wathu. M’malomwake, amatithandiza kuti tiziganiza komanso kusankha tokha zochita potifotokozera nkhani zochitikira anthu ena, maulosi ochititsa chidwi komanso malangizo othandiza. Mwa njira zimenezi, Mawu a Mulungu amatithandiza kuti tizimukonda komanso kumumvera kuchokera pansi pa mtima.

N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mmene Yehova anachitira zinthu ndi atumiki ake m’mbuyomu? (Onani ndime 15)

15. (a) Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amachita chidwi ndi anthu amene amawerenga Mawu ake? (b) Pachithunzichi, kodi mtsikana, m’bale wachinyamata komanso mlongo wachikulire akuganizira za anthu ati otchulidwa m’Baibulo? (Gen. 39:1, 10-12; 2 Maf. 5:1-3; Luka 2:25-38)

15 Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amachita nafe chidwi kwambiri. Motani? M’Mawu ake muli nkhani zambiri zosonyeza mmene anthu amamvera. Tingathe kumvetsa mmene anthu otchulidwa m’Baibulo ankamvera chifukwa iwo anali anthu “monga ife tomwe.” (Yak. 5:17) Chofunika kwambiri n’chakuti tikamaganizira mmene Mulungu anachitira zinthu ndi anthu ngati ife, timafika pomvetsa bwino kuti “Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.”​—Yak. 5:11.

16. Kodi timaphunzira chiyani zokhudza Yehova tikamawerenga m’Baibulo nkhani za anthu omwe analakwitsa zinthu zina? (Yesaya 55:7)

16 Palinso njira ina imene Baibulo limasonyezera kuti Yehova amatikonda. Malemba amatitsimikizira kuti Mulungu sadzatisiya ngakhale pamene talakwitsa zinthu. Aisiraeli ankachimwira Yehova mobwerezabwereza komabe akalapa kuchokera pansi pa mtima, iye ankawakhululukira. (Werengani Yesaya 55:7.) Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankadziwanso kuti Yehova ankawakonda kwambiri. Mouziridwa, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti ‘akhululukire ndi mtima wonse ndi kutonthoza’ munthu yemwe ankachita tchimo lalikulu koma kenako analapa. (2 Akor. 2:6, 7; 1 Akor. 5:1-5) N’zochititsa chidwi kuti Yehova sankasiya atumiki ake chifukwa choti amuchimwira. M’malomwake, ankawathandiza mwachikondi, kuwawongolera komanso kuwapempha kuti abwerere kwa iye. Masiku anonso iye amalonjeza kuti adzachita zimenezi kwa anthu onse omwe alapa.​—Yak. 4:8-10.

MUZIYAMIKIRA ‘MPHATSO YABWINO’ YA MAWU A MULUNGU

17. N’chifukwa chiyani Baibulo lili mphatso yabwino kwambiri?

17 Yehova watipatsa mphatso yabwino kwambiri. N’chifukwa chiyani Mawu ake ali mphatso yapadera? Monga mmene taphunzirira, Baibulo limatiuza za nzeru, chilungamo komanso chikondi cha Mulungu. Bukuli limatitsimikizira kuti Yehova amafuna kuti timudziwe komanso tikhale anzake.

18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova potipatsa ‘mphatso yabwino’ ya Baibulo?

18 Timaona kuti ‘mphatso yabwino’ ya Mawu a Mulungu ndi yamtengo wapatali. (Yak. 1:17) Choncho tiyeni tipitirize kusonyeza kuti timaiyamikira. Tingachite zimenezi popemphera tikamawerenga Mawu opatulikawa komanso kuwaganizira mozama. Tikamachita zimenezi, tingakhale otsimikiza kuti Mlembi wamkulu wa Baibulo adzadalitsa khama lathu ndipo ‘tidzamudziwadi Mulungu.’​—Miy. 2:5.

NYIMBO NA. 98 Malemba Anauziridwa ndi Mulungu

a Baibulo limatithandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Kodi tingaphunzire chiyani m’buku lopatulikali zokhudza nzeru, chilungamo komanso chikondi cha Mulungu? Zimene timaphunzira zingatithandize kuti tiziyamikira kwambiri Mawu a Mulungu n’kumawaona mmene alilidi, monga mphatso yochokera kwa Atate wathu wakumwamba.