NKHANI YOPHUNZIRA 7

Zimene Tingachite Kuti Tizipindula Kwambiri Tikamawerenga Baibulo

Zimene Tingachite Kuti Tizipindula Kwambiri Tikamawerenga Baibulo

“M’Chilamulo, umawerengamo zotani?”​—LUKA 10:26.

NYIMBO NA. 97 Mawu a Mulungu Amatithandiza Kukhala ndi Moyo

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ankaona kuti Malemba ndi ofunika?

 TAGANIZIRANI mmene munthu ankamvera kumva Yesu akuphunzitsa. Nthawi zonse iye ankaphunzitsa kuchokera m’Malemba ndipo ankachita zimenezi kuchokera mumtima. Ndipotu mawu a Yesu oyambirira kulembedwa omwe analankhula atangobatizidwa komanso mawu ake ena omaliza omwe analankhula asanafe, anali ochokera m’Malemba. b (Deut. 8:3; Sal. 31:5; Luka 4:4; 23:46) Ndipo pa zaka zitatu ndi hafu za utumiki wake, nthawi zonse Yesu ankawerenga komanso kufotokoza Malemba.​—Mat. 5:17, 18, 21, 22, 27, 28; Luka 4:16-20.

Pa moyo wake wonse, Yesu anasonyeza kuti ankakonda Malemba ndipo ankalola kuti azimutsogolera (Onani ndime 2)

2. Pamene Yesu ankakula n’chiyani chinamuthandiza kuti adziwe bwino Malemba? (Onani chithunzi chapachikuto.)

2 Kwa zaka zambiri asanayambe utumiki wake, Yesu ankawerenga komanso kumva Mawu a Mulungu kambirimbiri. Akakhala panyumba, mosakaikira ankamva Mariya ndi Yosefe akutchula Malemba akamacheza. c (Deut. 6:6, 7) Sitikukayikiranso kuti Sabata lililonse Yesu ankapita ku sunagoge ndi banja lawo. (Luka 4:16) Kumeneko ayenera kuti ankamvetsera mwatcheru Malemba akamawerengedwa. Patapita nthawi, Yesu anaphunzira kuwerenga payekha Malemba Opatulikawa. Choncho sikuti iye anangofika powadziwa bwino Malemba, koma ankawakondanso n’kumawalola kuti azimutsogolera. Mwachitsanzo, takumbukirani zimene zinachitika m’kachisi pamene Yesu anali ndi zaka 12 zokha. Aphunzitsi omwe anali odziwa bwino Chilamulo cha Mose, “anadabwa kwambiri ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambiri.”​—Luka 2:46, 47, 52.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Ifenso tingafike podziwa komanso kukonda Mawu a Mulungu tikamawawerenga nthawi zonse. Komabe kodi tingatani kuti tizipindula kwambiri ndi zimene timawerenga? Tingaphunzirepo kathu pa zimene Yesu anauza anthu odziwa Chilamulo omwe akuphatikizapo alembi, Afarisi komanso Asaduki. Nthawi zonse atsogoleri achipembedzo amenewa ankawerenga Malemba, koma sankapindula ndi zimene ankawerengazo. Yesu anatchula zinthu zitatu zimene zinkalepheretsa anthu amenewa kuti azipindula ndi Malemba. Zimene anawauza zingatithandize kuti tiwonjezere luso lathu n’cholinga choti (1) tizimvetsa zimene tikuwerenga, (2) tizipeza mfundo zothandiza za choonadi ndiponso (3) tizilola kuti Mawu a Mulungu azititsogolera.

MUZIWERENGA N’CHOLINGA CHOTI MUMVETSE

4. Kodi lemba la Luka 10:25-29, likutiphunzitsa chiyani pankhani yowerenga Mawu a Mulungu?

4 Timafuna kumvetsa tanthauzo la zimene tikuwerenga m’Mawu a Mulungu. Ngati sitingatero sitingapindule mokwanira. Mwachitsanzo, taganizirani zimene Yesu anakambirana ndi “munthu wina wodziwa Chilamulo.” (Werengani Luka 10:25-29.) Pamene munthuyo anamufunsa zimene angachite kuti adzapeze moyo wosatha, Yesu anamuthandiza kupeza yankho m’Mawu a Mulungu pofunsa kuti: “Kodi m’Chilamulo analembamo chiyani? Umawerengamo zotani?” Munthuyo anayankha molondola potchula mawu a m’Malemba omwe amanena za kukonda Mulungu ndi anzathu. (Lev. 19:18; Deut. 6:5) Koma taonani zimene kenako ananena, iye anati: “Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndi ndani kwenikweni?” Munthuyo anasonyeza kuti sankamvetsa tanthauzo la zimene anawerenga. Choncho sankadziwa mmene angagwiritsire ntchito moyenera mfundo za m’Malemba amenewa pa moyo wake.

Kuwerenga kuti timvetse ndi luso lomwe tingathe kuliwonjezera

5. Kodi kupemphera komanso kuwerenga mosathamanga kungakuthandizeni bwanji kumvetsa zomwe mwawerenga?

5 Tingamamvetse kwambiri Mawu a Mulungu ngati titakhala ndi zizolowezi zabwino tikamawawerenga. Zotsatirazi ndi mfundo zina zimene zingakuthandizeni. Muzipemphera musanayambe kuwerenga. Timafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti timvetse Malemba, choncho tingamupemphe mzimu woyera womwe ungatithandize kuika maganizo athu pa zimene tikuwerengazo. Kenako muziwerenga mosathamanga. Zimenezi zingakuthandizeni kumvetsa zomwe mukuwerenga. Zingakhalenso zothandiza ngati mutamawerenga mokweza kapena kumawerenga motsatira Baibulo lochita kujambulidwa. Mukamamvetsera mawu ochita kujambulidwawo komanso kuwaona m’Baibulo lanu, zingakuthandizeni kuti muzimvetsa, kukumbukira komanso kuphunzirapo zambiri. (Yos. 1:8) Mukamaliza kuwerenga, muzipempheranso kwa Yehova n’kumuthokoza chifukwa cha mphatso ya Mawu ake ndipo muzimupempha kuti akuthandizeni kugwiritsa ntchito zimene mwawerenga.

Kodi kulemba mfundo zachidule kungakuthandizeni bwanji kuti muzimvetsa komanso kukumbukira zimene mwawerenga? (Onani ndime 6)

6. Kodi kudzifunsa mafunso komanso kulemba mfundo zachidule kungakuthandizeni bwanji mukamawerenga? (Onaninso chithunzi.)

6 Mfundo zina ziwirizi zingakuthandizeninso kumvetsa zomwe mukuwerenga m’Baibulo. Muzidzifunsa mafunso pa zimene mwawerenga. Mukamawerenga nkhani inayake muzidzifunsa kuti: ‘Kodi nkhaniyi kwenikweni ikunena za ndani? Akulankhula mawuwa ndi ndani? Akulankhula kwa ndani nanga n’chifukwa chiyani? Kodi zikuchitikira kuti ndiponso liti?’ Mafunso amenewa angakuthandizeni kuti muziganizira komanso kutsatira mfundo zikuluzikulu za nkhaniyo. Komanso mukamawerenga muzilemba mfundo zachidule. Mukamalemba zimathandiza kuti maganizo anu onse azikhala pa zimene mukuwerenga ndipo mumazimvetsa kwambiri. Kulemba kumakuthandizaninso kuti muzikumbukira zimene mwawerenga. Mungalembe mafunso, zimene mwapeza pambuyo pofufuza, mfundo zikuluzikulu, mmene mungagwiritsire ntchito zimene mwawerengazo kapenanso mmene mukumvera. Kulemba mfundo ngati zimenezi kungakuthandizeni kumaona kuti Mawu a Mulungu ndi uthenga umene analembera inuyo.

7. Kodi ndi khalidwe liti lomwe timafunikira tikamawerenga, nanga n’chifukwa chiyani? (Mateyu 24:15)

7 Yesu anatchula khalidwe lofunika kwambiri la kuzindikira lomwe lingatithandize kuti tizimvetsa zomwe timawerenga m’Mawu a Mulungu. (Werengani Mateyu 24:15.) Kodi kuzindikira n’kutani? Ndi luso lotha kudziwa kugwirizana pakati pa mfundo ina ndi mfundo ina kapena kusiyana komwe kulipo komanso kumvetsa bwino ngakhale zimene sizinafotokozedwe. Kuwonjezera pamenepo, Yesu anasonyeza kuti timafunika kukhala ozindikira kuti tithe kuona zinthu zimene zikukwaniritsa maulosi a m’Baibulo. Timafunikanso khalidweli kuti tizipindula ndi zonse zomwe timawerenga m’Baibulo.

8. N’chiyani chingatithandize kukhala ozindikira tikamawerenga?

8 Yehova amathandiza atumiki ake kuti akhale ozindikira. Choncho muzipemphera kwa iye ndipo muzimupempha kuti akuthandizeni kukulitsa khalidweli. (Miy. 2:6) Kodi mungatani kuti muzichita zinthu mogwirizana ndi pemphero lanu? Mosamala kwambiri, muziganizira zimene mwawerenga ndipo muziona mmene zikugwirizanira ndi zomwe mukudziwa. Zinthu zothandiza pophunzira zingakuthandizeni kuchita zimenezi. Mwachitsanzo mungagwiritse ntchito Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani. Mabukuwa angakuthandizeni kuti muzimvetsa zomwe mukuwerenga m’Baibulo komanso kuona mmene mungagwiritsire ntchito mfundo zake pa moyo wanu. (Aheb. 5:14) Luso lotha kuzindikira powerenga lidzakuthandizani kuti muzimvetsa bwino Malemba.

MUZIWERENGA KUTI MUPEZE MFUNDO ZOTHANDIZA

9. Kodi ndi mfundo iti yofunika ya choonadi imene Asaduki sankaivomereza?

9 Asaduki ankadziwa bwino mabuku 5 oyambirira a Malemba a Chiheberi koma sankavomereza mfundo za choonadi zofunika za m’mabuku ouziridwawa. Mwachitsanzo, taganizirani mmene Yesu anayankhira Asaduki pamene anamufunsa nkhani yokhudza kuukitsidwa. Yesu anawafunsa kuti: “Kodi inu simunawerenge m’buku la Mose, m’nkhani ya chitsamba chaminga, mmene Mulungu anamuuzira kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’?” (Maliko 12:18, 26) Ngakhale kuti Asaduki ayenera kuti anawerengapo nkhaniyi maulendo ambiri, funso la Yesu linasonyeza kuti iwo sankavomereza mfundo yofunika ya choonadi yonena za kuuka.​—Maliko 12:27; Luka 20:38. d

10. Kodi tiziyesetsa kuchita chiyani tikamawerenga?

10 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tiziyesa kuona zimene tikuphunzira pa mbali zonse za vesi kapena nkhani imene tikuwerengayo. Sitikuyenera kumangoganizira mfundo zokhazo zomwe ndi zosavuta kumvetsa koma tiziganiziranso mfundo zozama za choonadi zomwe zili ngati chuma chobisika.

11. Mogwirizana ndi 2 Timoteyo 3:16, 17, kodi mungatani kuti muzipeza mfundo zothandiza m’Baibulo?

11 Kodi mungatani kuti muzipeza mfundo zothandiza mukamawerenga Baibulo? Taganizirani zimene timawerenga pa 2 Timoteyo 3:16, 17. (Werengani.) Lembali limati, “Malemba onse . . . ndi opindulitsa” pa (1) kuphunzitsa (2) kudzudzula (3) kuwongola zinthu ndiponso (4) kulangiza. Mungapeze mfundo 4 zothandizazi ngakhale m’mabuku a Baibulo amene simuwawerenga kawirikawiri. Mukamawerenga nkhani inayake muziona zimene ikukuphunzitsani zokhudza Yehova, cholinga chake kapena mfundo zake. Muziganizira mmene nkhaniyo ingakhalire yothandiza podzudzula. Muzichita zimenezi poona mmene mavesiwo akukuthandizirani kuzindikira komanso kupewa makhalidwe oipa ndiponso kupitirizabe kukhala okhulupirika kwa Yehova. Muziganizira mmene mungagwiritsire ntchito nkhaniyo powongola kapena kuti pokonza zolakwika mwina zimene munthu amene mukumulalikira wanena. Komanso muzifufuza malangizo omwe angakuthandizeni kuti muziona zinthu mmene Yehova amazionera. Nthawi zonse mukamaganizira zinthu 4 zimenezi, mudzapeza mfundo zothandiza zomwe zingachititse kuti muzipindula kwambiri mukamawerenga Baibulo.

MUZILOLA KUTI ZOMWE MWAWERENGA ZIZIKUSINTHANI

12. N’chifukwa chiyani Yesu anafunsa Afarisi kuti “Kodi simunawerenge?”

12 Yesu anafunsanso funso lakuti “Kodi simunawerenge?” pofuna kusonyeza kuti Afarisi anali ndi maganizo olakwika okhudza zimene ankawerenga m’Malemba. (Mat. 12:1-7) e Pa nthawiyi Afarisi ankanena kuti ophunzira a Yesu sankasunga Sabata. Poyankha Yesu anatchula zitsanzo ziwiri za m’malemba komanso anatchula mawu a m’vesi lina m’buku la Hoseya pofuna kusonyeza kuti Afarisi sankamvetsa bwino lamulo lokhudza Sabata komanso ankalephera kusonyeza chifundo. N’chifukwa chiyani kuwerenga Mawu a Mulungu sikunkawathandiza kusintha? Chifukwa chakuti ankawawerenga ali ndi zolinga zolakwika komanso anali ndi mtima wonyada. Zimenezi zinawalepheretsa kumvetsa zimene ankawerenga.​—Mat. 23:23; Yoh. 5:39, 40.

13. Kodi tiziwerenga Baibulo tili ndi maganizo otani, nanga n’chifukwa chiyani?

13 Timaphunzira kuchokera pa mawu a Yesu kuti tiyenera kumawerenga Baibulo tili ndi maganizo oyenera. Mosiyana ndi Afarisi, tiyenera kukhala odzichepetsa komanso ophunzitsika. Tiyenera ‘kuvomereza mofatsa mawu kuti abzalidwe mwa ife.’ (Yak. 1:21) Tikakhala ofatsa, tidzalola kuti Mawu a Mulungu akhazikike mumtima mwathu. Tikamapewa kukhala ndi maganizo olakwika komanso mtima wonyada, mfundo za m’Baibulo zokhudza chifundo, kukoma mtima komanso chikondi zidzatithandiza kuti tisinthe.

Kodi tingadziwe bwanji ngati tikulola kuti Mawu a Mulungu azitisintha? (Onani ndime 14) f

14. Kodi tingadziwe bwanji ngati timalola kuti Baibulo lizitisintha? (Onaninso zithunzi.)

14 Mmene timachitira zinthu ndi ena zingasonyeze ngati timalola kuti Mawu a Mulungu azitisintha. Afarisi sanalole kuti Mawu a Mulungu aziwafika pamtima ndipo izi zinachititsa kuti ‘aziweruza anthu osalakwa.’ (Mat. 12:7) Mofanana ndi zimenezi mmene timaonera zinthu komanso mmene timachitira zinthu ndi ena, zingasonyeze ngati timalola Mawu a Mulungu kutisintha. Mwachitsanzo, kodi nthawi zambiri timaona zabwino zimene ena amachita kapena timangokhalira kuona zimene amalakwitsa? Kodi ndife achifundo ndiponso timakhala okonzeka kukhululuka kapena timakonda kuweruza ena ndiponso kusunga chakukhosi? Kudzifufuza mwanjira imeneyi kungatithandize kuona ngati timalola zimene timawerenga kuti zisinthe maganizo athu, mmene timamvera komanso zochita zathu.​—1 Tim. 4:12, 15; Aheb. 4:12.

KUWERENGA MAWU A MULUNGU KUMATITHANDIZA KUKHALA OSANGALALA

15. Kodi Yesu ankawaona bwanji Malemba Oyera?

15 Yesu ankakonda Malemba Oyera ndipo lemba la Salimo 40:8, limafotokoza mwaulosi mmene iye ankamvera, kuti: “Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga, ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.” Zimenezi zinachititsa kuti azisangalala potumikira Yehova komanso kuti zinthu zizimuyendera bwino. Ifenso tingamasangalale ndipo zinthu zingamatiyendere bwino tikamayesetsa kuwerenga Mawu a Mulungu komanso kuwakonda.​—Sal. 1:1-3.

16. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tizipindula kwambiri tikamawerenga Mawu a Mulungu? (Onani bokosi lakuti “ Mawu a Yesu Angakuthandizeni Kumvetsa Zimene Mumawerenga.”)

16 Mogwirizana ndi Yesu komanso chitsanzo chake, tingamvetse zimene timawerenga m’Baibulo ngati timapemphera, kuwerenga mosathamanga, kufunsa mafunso komanso kulemba mfundo zachidule. Tingagwiritsenso ntchito luso la kuzindikira tikamafufuza zimene tawerenga pogwiritsa ntchito mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Tingawonjezere luso lathu pogwiritsa ntchito bwino Malemba ngakhale amene sitinawazolowere, pofufuza mfundo zothandiza munkhani zomwe tikuwerenga. Ndipo tingalole kuti Mawu a Mulungu azitisintha tikamayesetsa kukhalabe ndi maganizo oyenera. Tikamachita khama, tidzapindula kwambiri tikamawerenga Baibulo ndipo tidzakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.​—Sal. 119:17, 18; Yak. 4:8.

NYIMBO NA. 95 Kuwala Kukuwonjezerekabe

a Atumiki onse a Yehova amayesetsa kuwerenga Mawu ake tsiku lililonse. Anthu enanso ambiri amawerenga Baibulo koma samvetsa zimene amawerengazo. Ndi mmenenso zinalili ndi anthu ena mu nthawi ya Yesu. Kuona zimene Yesu anauza anthu amene amawerenga Mawu a Mulungu, kungatithandize kuphunzira zinthu zina zomwe zingatithandize kuti tizipindula kwambiri tikamawerenga Baibulo.

b Pa nthawi imene anabatizidwa komanso kudzozedwa ndi mzimu woyera, zikuoneka kuti Yesu anakumbukira mmene analili poyamba asanabwere padzikoli.​—Mat. 3:16.

c Mariya ankadziwa bwino Malemba ndipo ankawafotokoza. (Luka 1:46-55) N’zoonekeratu kuti Yosefe ndi Mariya sakanakwanitsa kukhala ndi buku lawolawo la Malemba. Ayenera kuti ankamvetsera mwatcheru Mawu a Mulungu akamawerengedwa ku sunagoge n’cholinga choti aziwakumbukira pambuyo pake.

d Onani nkhani yakuti “Yandikirani Mulungu​—‘Iye ndi Mulungu . . . wa Anthu Amoyo’” mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2013.

e Onaninso lemba la Mateyu 19:4-6 pomwe Yesu anafunsa Afarisi funso lomweli lakuti: “Kodi simunawerenge?” Ngakhale kuti iwo anali atawerenga nkhani yokhudza mmene Yehova analengera zinthu, ankanyalanyaza zomwe imaphunzitsa pankhani ya mmene Mulungu amaonera ukwati.

f MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pa nthawi ya misonkhano m’Nyumba ya Ufumu, m’bale yemwe akuthandiza kuonetsa mavidiyo walakwitsa zinthu zina koma pambuyo pa misonkhano m’malo mongoyang’ana zimene analakwitsazo abale akumuyamikira chifukwa cha khama lake.