NKHANI YOPHUNZIRA 8

NYIMBO NA. 123 Tizigonjera Mulungu Mokhulupirika

Pitirizani Kutsatira Malangizo a Yehova

Pitirizani Kutsatira Malangizo a Yehova

“Ine Yehova ndine amene . . . ndimakutsogolerani.”​—YES. 48:17.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Nkhaniyi itithandiza kuona mmene Yehova amatsogolerera anthu ake masiku ano komanso madalitso omwe timapeza chifukwa chotsatira malangizo ake.

1. Perekani chitsanzo chosonyeza chifukwa chake tiyenera kutsatira Yehova, yemwe ndi Wotitsogolera.

 YEREKEZERANI kuti mwasochera munkhalango. M’nkhalangomo muli zoopsa zambiri monga nyama zolusa, tizilombo tomwe tingakupatseni matenda, zomera zapoizoni komanso maenje omwe mutha kugweramo. Mungayamikiretu kwambiri kukhala ndi wokutsogolerani yemwe akudziwa bwino malowo n’cholinga choti mupewe zoopsazi. Dzikoli lili ngati nkhalango imeneyi. Muli zoopsa zambiri zomwe zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Koma tili ndi Wotitsogolera wabwino, yemwe ndi Yehova. Iye amatitsogolera kuti tidutse m’njira yabwino mpaka tikafike komwe tikupita, kumene ndi m’dziko latsopano, komwe tidzalandire moyo wosatha.

2. Kodi Yehova amatitsogolera bwanji?

2 Kodi Yehova amatitsogolera bwanji? Njira yaikulu ndi kudzera m’Mawu ake, Baibulo. Komanso iye amagwiritsa ntchito anthu. Mwachitsanzo, amagwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” potipatsa chakudya chauzimu chomwe chimatithandiza kuti tizisankha zochita mwanzeru. (Mat. 24:45) Yehova amagwiritsanso ntchito amuna ena oyenerera kuti azititsogolera. Oyang’anira madera komanso akulu, amatilimbikitsa ndiponso kutipatsa malangizo omwe amatithandiza kupirira m’nthawi yovutayi. Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa chotipatsa malangizo odalirika m’masiku otsiriza ano. Malangizowa amatithandiza kuti tizichita zimene iye amasangalala nazo komanso tipitirize kuyenda panjira ya kumoyo.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Komabe, nthawi zina zingamativute kutsatira malangizo a Yehova, makamaka akamaperekedwa ndi anthu omwe si angwiro. Chifukwa chiyani? Chifukwa mwina malangizowo sangagwirizane ndi zimene timakonda. Kapenanso tingaone kuti malangizowo si anzeru ndipo tingamaganize kuti sanachokere kwa Yehova. Pa nthawi ngati imeneyi, tingafunike kukhulupirira kwambiri kuti Yehova ndi amene akutsogolera anthu ake ndiponso kuti kutsatira malangizowo kungachititse kuti tipeze madalitso. Pofuna kutithandiza kuti tizidalira kwambiri malangizo a Yehova, nkhaniyi ifotokoza (1) mmene kale Yehova ankatsogolerera anthu ake, (2) mmene amatitsogolerera masiku ano, komanso (3) madalitso omwe timapeza tikamatsatira malangizo ake nthawi zonse.

Kuyambira kale, Yehova wakhala akugwiritsa ntchito anthu omuimira potsogolera anthu ake (Onani ndime 3)



MMENE YEHOVA ANKATSOGOLERERA AISIRAELI

4-5. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ankagwiritsa ntchito Mose potsogolera Aisiraeli? (Onani chithunzi chapachikuto.)

4 Yehova anasankha Mose kuti atsogolere Aisiraeli potuluka ku Iguputo. Ndipo anawapatsa umboni wooneka, wosonyeza kuti iye ndi amene ankawatsogolera pogwiritsa ntchito Mose. Mwachitsanzo, masana ankawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha mtambo ndipo usiku pogwiritsa ntchito chipilala cha moto. (Eks. 13:21) Mose ankatsatira chipilalacho chomwe chinatsogolera iyeyo ndi Aisiraeli ku Nyanja Yofiira. Anthuwo anachita mantha kwambiri poganiza kuti asowa kolowera chifukwa kutsogolo kwawo kunali nyanja ndipo kumbuyo kunali asilikali a Iguputo. Iwo ankaganiza kuti Mose analakwitsa powabweretsa ku Nyanja Yofiira. Koma sikuti analakwitsa. Yehova ndi amene anatsogolera anthu akewo kumeneko pogwiritsa ntchito Mose. (Eks. 14:2) Kenako iye anawapulumutsa m’njira yodabwitsa kwambiri.​—Eks. 14:26-28.

Mose ankadalira chipilala cha mtambo potsogolera anthu a Mulungu m’chipululu (Onani ndime 4-5)



5 Pa zaka 40 zotsatira, Mose anapitiriza kudalira chipilala cha mtambo potsogolera anthu a Mulungu m’chipululu. a Kwa kanthawi, Yehova anachititsa kuti chipilala cha mtambo chiime pamwamba pa chihema cha Mose, pomwe Aisiraeli onse ankatha kuchiona. (Eks. 33:7, 9, 10) Yehova ankalankhula ndi Mose kudzera m’chipilalacho ndipo Mose ankapereka malangizo a Yehovawo kwa anthu. (Sal. 99:7) Aisiraeli anali ndi umboni wokwanira wosonyeza kuti Yehova ankagwiritsa ntchito Mose powatsogolera.

Mose ndi Yoswa, yemwe anamulowa m’malo (Onani ndime 5, 7)



6. Kodi Aisiraeli ambiri anatani pamene Yehova ankawatsogolera? (Numeri 14:2, 10, 11)

6 N’zomvetsa chisoni kuti Aisiraeli ambiri sanavomereze umboni woti Yehova ankagwiritsa ntchito Mose ngati womuimira wake. (Werengani Numeri 14:2, 10, 11.) Mobwerezabwereza, iwo ankakana zoti Mose anatumidwa ndi Yehova. Pa chifukwa chimenechi, Yehova sanalole kuti Aisiraeli amenewa akalowe m’Dziko Lolonjezedwa.​—Num. 14:30.

7. Tchulani zitsanzo za anthu amene anatsatira malangizo a Yehova. (Numeri 14:24) (Onaninso chithunzi.)

7 Komabe, panali Aisiraeli ena omwe ankatsatira malangizo a Yehova. Mwachitsanzo, nthawi ina Yehova anati: “Kalebe . . . wakhala akunditsatira ndi mtima wonse.” (Werengani Numeri 14:24.) Mulungu anadalitsa Kalebe ndipo atafika m’dziko la Kanani, amamulola kusankha dera lomwe ankafuna kukhala. (Yos. 14:12-14) Aisiraeli amene analoledwa kulowa m’Dziko Lolonjezedwalo, anaperekanso chitsanzo chabwino potsatira malangizo a Yehova. Pamene Yoswa anasankhidwa kuti alowe m’malo mwa Mose, kuti aziwatsogolera, iwo ‘ankamulemekeza kwambiri masiku onse a moyo wake.’ (Yos. 4:14) Zotsatira zake n’zakuti, Yehova anawadalitsa powapatsa dziko limene anawalonjeza.​—Yos. 21:43, 44.

8. Fotokozani mmene Yehova ankatsogolera anthu ake m’nthawi ya mafumu. (Onaninso chithunzi.)

8 Patapita zaka, Yehova anasankha oweruza kuti azitsogolera anthu ake. Kenako, m’nthawi ya mafumu, Yehova ankasankha aneneri kuti azipereka malangizo kwa anthu ake. Mafumu okhulupirika ankatsatira malangizo a aneneriwa. Mwachitsanzo, Davide anamvera modzichepetsa atadzudzulidwa ndi mneneri Natani. (2 Sam. 12:7, 13; 1 Mbiri 17:3, 4) Mfumu Yehosafati inkadalira malangizo a mneneri Yahazieli ndipo inalimbikitsa anthu a ku Yuda kuti ‘azikhulupirira aneneri a [Mulungu].’ (2 Mbiri 20:14, 15, 20) Atathedwa nzeru, Mfumu Hezekiya anapempha malangizo kwa mneneri Yesaya. (Yes. 37:1-6) Nthawi zonse mafumu akamatsatira malangizo a Yehova, ankadalitsidwa ndipo mtundu wonse unkakhala wotetezeka. (2 Mbiri 20:29, 30; 32:22) Apa aliyense akanatha kuona kuti Yehova ankagwiritsa ntchito aneneriwo potsogolera anthu ake. Komabe mafumu ambiri komanso anthu, sankamvera aneneri a Yehova.​—Yer. 35:12-15.

Mfumu Hezekiya ndi mneneri Yesaya (Onani ndime 8)



MMENE YEHOVA ANKATSOGOLERERA ANTHU AKE M’NTHAWI YA ATUMWI

9. Kodi Yehova anasankha ndani kuti azitsogolera Akhristu m’nthawi ya atumwi? (Onaninso chithunzi.)

9 Pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Yehova anakhazikitsa mpingo wa Chikhristu. Kodi ankatsogolera bwanji Akhristu amenewo? Iye anasankha Yesu kuti akhale mutu wa mpingo. (Aef. 5:23) Koma sikuti Yesu ankatsogolera wophunzira aliyense payekha. M’malomwake ankagwiritsa ntchito atumwi ndi akulu ku Yerusalemu kuti azitsogolera. (Mac. 15:1, 2) Pankasankhidwanso akulu kuti azitsogolera mipingo.​—1 Ates. 5:12; Tito 1:5.

Atumwi ndi akulu ku Yerusalemu (Onani ndime 9)



10. (a) Kodi Akhristu ambiri a m’nthawi ya atumwi ankatani akapatsidwa malangizo? (Mac. 15:30, 31) (b) N’chifukwa chiyani kale ena sankamvera anthu omwe Yehova ankawagwiritsa ntchito? (Onani bokosi lakuti “ Chifukwa Chake Ena Amakana Kuvomereza.”)

10 Kodi Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankatsatira malangizo? Ambiri ankamvera komanso kutsatira malangizo. Ndipotu ‘ankasangalala chifukwa cha mawu olimbikitsa’ omwe ankalandira. (Werengani Machitidwe 15:30, 31.) Ndiye kodi Yehova akutsogolera bwanji anthu ake masiku ano?

MMENE YEHOVA AMATITSOGOLERERA MASIKU ANO

11. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene Yehova wakhala akuthandizira anthu omuimira m’masiku athu ano.

11 Yehova akupitiriza kutsogolera anthu ake masiku ano. Iye amachita zimenezi pogwiritsa ntchito Mawu ake komanso Mwana wake, yemwe ndi mutu wa mpingo. Kodi pali umboni wosonyeza kuti m’masiku athu anonso, Yehova amagwiritsa ntchito anthu omuimira? Inde. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika m’zaka za m’ma 1800. Charles Taze Russell ndi anzake anayamba kuzindikira kuti chaka cha 1914 chidzakhala chofunika chifukwa ndi nthawi yomwe Ufumu wa Mulungu udzakhazikitsidwe. (Dan. 4:25, 26) Maulosi a m’Baibulo ndi omwe anawathandiza kudziwa zimenezi. Kodi Yehova ankawatsogolera pamene iwo ankafufuza m’Baibulo? Mosakayikira ankawathandiza. Zimene zinachitika mu 1914, zinatsimikizira kuti Ufumu wa Mulungu unali utayamba kulamulira. M’chakachi, nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayambika, ndipo kunali miliri, zivomerezi komanso njala. (Luka 21:10, 11) Yehova ankagwiritsadi ntchito amuna a mitima yabwinowa kuti athandize anthu ake.

12-13. Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, kodi abale otsogolera anakonza zotani pa nkhani yolalikira ndi kuphunzitsa?

12 Taganiziraninso zimene zinachitika pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Pambuyo pomvetsa lemba la Chivumbulutso 17:8, abale otsogolera kulikulu lathu, anazindikira kuti nkhondoyo siinali chiyambi cha Aramagedo. M’malomwake pambuyo pa nkhondoyo pakhala nthawi ya mtendere, zomwe zithandize kuti ntchito yolalikira iwonjezereke. Choncho gulu la Yehova linakonza zoti pakhale Sukulu ya Giliyadi, zomwe zinkaoneka ngati zosathandiza pa nthawiyo. Cholinga cha Sukuluyi chinali kuthandiza amishonale kuti azilalikira komanso kuphunzitsa anthu padziko lonse. Amishonalewo ankatumizidwa m’madera osiyanasiyana ngakhale pa nthawi yankhondo. Kuwonjezera apo, kapolo anakonza zoti pakhale Sukulu ya Utumiki wa Mulungu b n’cholinga chofuna kuthandiza onse mumpingo kuti azilalikira komanso kuphunzitsa bwino Mawu a Mulungu. Zimenezi zinathandiza anthu a Mulungu kukonzekera bwino ntchito yolalikira yomwe ankafunika kugwira.

13 Masiku ano, timaona umboni woti Yehova ankatsogolera anthu ake pa nthawi yovutayo. Kungoyambira pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, anthu a Yehova m’mayiko ambiri akhala akugwira ntchito yolalikira popanda kusokonezedwa. Ndipotu ntchitoyi yakhala ikuyenda bwino kwambiri.

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira malangizo ochokera kugulu la Yehova komanso kwa akulu? (Chivumbulutso 2:1) (Onaninso chithunzi.)

14 Masiku ano, abale a m’Bungwe Lolamulira akupitirizabe kudalira malangizo ochokera kwa Khristu. Iwo amafuna kuti malangizo omwe amapereka kwa abale azikhala ogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Ndipo amagwiritsa ntchito oyang’anira madera komanso akulu kuti azipereka malangizowo kumipingo. c Akulu odzozedwa ali ‘m’dzanja lamanja’ la Khristu. (Werengani Chivumbulutso 2:1.) N’zoona kuti akulu onse si angwiro ndipo amalakwitsa zinthu. Mose ndi Yoswa, nawonso nthawi zina ankalakwitsa zinthu, ngatinso mmene ankachitira atumwi. (Num. 20:12; Yos. 9:14, 15; Aroma 3:23) Komabe Khristu akutsogolera kapolo wokhulupirika komanso akulu, ndipo apitiriza kuchita zimenezi “masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Choncho, tili ndi zifukwa zokwanira zotichititsa kukhulupirira malangizo omwe Yesu amatipatsa kudzera mwa anthu omwe wasankha kuti azititsogolera.

Bungwe Lolamulira la masiku ano (Onani ndime 14)



TIMAPINDULA TIKAPITIRIZA KUTSATIRA MALANGIZO A YEHOVA

15-16. Kodi mwaphunzira chiyani kwa anthu omwe anatsatira malangizo a Yehova?

15 Tikamatsatira malangizo a Yehova, timapeza madalitso ngakhale panopa. Mwachitsanzo, Andy ndi Robyn anatsatira malangizo a kapolo otilimbikitsa kuti tizikhala moyo wosalira zambiri. (Mat. 6:22) Zotsatira zake n’zakuti, iwo anadzipereka kukagwira nawo ntchito zomangamanga. Robyn anati: “Nthawi zambiri tinkakhala m’nyumba zazing’ono, ndipo zinanso zinkakhala zopanda khitchini. Ndinkafunikanso kugulitsa zinthu zambiri zomwe ndinkazikonda kuphatikizapo makamera ndi zinthu zina zogwiritsa ntchito pojambula. Ndinkalira pogulitsa zinthuzi. Koma mofanana ndi Sara, mkazi wa Abulahamu, ndinali nditatsimikiza kuti ndizingoyang’ana kutsogolo osayang’ana m’mbuyo.” (Aheb. 11:15) Kodi banjali linapindula bwanji chifukwa cha zimene anasankhazi? Robyn anati: “Timasangalala kwambiri podziwa kuti timapatsa Yehova zonse zomwe tili nazo. Tikamagwira ntchito zomwe Yehova watipatsa, timaona mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano.” Andy anawonjezera kuti: “Timasangalala chifukwa chogwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zathu pothandiza pa ntchito ya Ufumu.”

16 Kodi timapindulanso bwanji tikamatsatira malangizo a Yehova? Atamaliza maphunziro ake a kusekondale, Marcia ankafunitsitsa kutsatira malangizo omwe amatilimbikitsa kuti tizichita zambiri potumikira Yehova. (Mat. 6:33; Aroma 12:11) Iye anati: “Ndinapatsidwa mwayi wokachita maphunziro kuyunivesite kwa zaka 4. Koma ine ndinkafuna nditachita zambiri potumikira Yehova. Choncho ndinasankha zopita kusukulu yophunzitsa ntchito zamanja n’cholinga choti ndingopeza luso lomwe lingadzandithandize pa utumiki wanga. Ichi ndi chimodzi mwa zosankha zabwino kwambiri zomwe ndinapanga. Panopa ndikusangalala kuchita upainiya wokhazikika ndipo ntchito imene ndimagwira imandipatsa mpata woti masiku ena ndizikatumikira ku Beteli komanso kuchita zinthu zina zambiri potumikira Yehova.”

17. Kodi timapeza madalitso enanso ati tikamatsatira malangizo a Yehova? (Yesaya 48:17, 18)

17 Nthawi zina timalandira malangizo omwe amatiteteza ku zinthu monga kukonda chuma komanso zinthu zina zomwe zingatichititse kuswa malamulo a Mulungu. Apanso zinthu zimatiyendera bwino chifukwa chotsatira malangizo omwe Yehova amatipatsa. Timakhala ndi chikumbumtima chabwino ndipo timapewa mavuto ambiri. (1 Tim. 6:9, 10) Zotsatira zake n’zakuti timatumikira Yehova ndi mtima wathu wonse ndipo timapeza mtendere ndi chimwemwe chochuluka.​—Werengani Yesaya 48:17, 18.

18. N’chifukwa chiyani muyenera kukhala otsimikiza kutsatira malangizo a Yehova?

18 Mosakayikira, Yehova apitiriza kugwiritsa ntchito anthu kuti adzatipatse malangizo pa chisautso chachikulu komanso mpaka mu Ulamuliro wa Zaka 1.000. (Sal. 45:16) Tiyeni tipitirize kutsatira malangizo ngakhale kuti nthawi zina kuchita zimenezi kungachititse kuti tisiye zinthu zomwe zimatisangalatsa. Zimenezi zidzakhala zosavuta ngati panopa timatsatira malangizo a Yehova. Choncho, tiyeni nthawi zonse tizitsatira malangizo a Yehova kuphatikizapo omwe timapatsidwa kudzera mwa amuna amene asankhidwa kuti azititsogolera. (Yes. 32:1, 2; Aheb. 13:17) Tikamatero, tingakhale ndi zifukwa zabwino zokhulupirira Yehova, yemwe ndi Wotitsogolera. Iye amatithandiza kuti tipewe zinthu zomwe zingawononge ubwenzi wathu ndi iyeyo, mpaka tikafike m’dziko latsopano mmene tidzalandire moyo wosatha.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Yehova ankatsogolera bwanji Aisiraeli?

  • Kodi Yehova ankatsogolera bwanji Akhristu a m’nthawi ya atumwi?

  • Kodi timapindula bwanji chifukwa chotsatira malangizo a Yehova masiku ano?

NYIMBO NA. 48 Tiziyenda ndi Yehova Tsiku Lililonse

a Yehova anasankhanso mngelo amene “ankayenda patsogolo pa Aisiraeli” powatsogolera ku Dziko Lolonjezedwa. N’zodziwikiratu kuti ameneyu ndi Mikayeli, lomwe ndi dzina limene Yesu amadziwika nalo kumwamba.​—Eks. 14:19; 32:34.

b Masiku ano maphunziro a m’Sukuluyi amachitika pamisonkhano ya mkati mwa mlungu.

c Onani bokosi lakuti “Udindo wa Bungwe Lolamulira” mu Nsanja ya Olonda ya February 2021, tsamba 18.