Ufulu Wosankha Zochita Ndi Mphatso Yapadera

Ufulu Wosankha Zochita Ndi Mphatso Yapadera

“Pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.”—2 AKOR. 3:17.

NYIMBO: 62, 65

1, 2. (a) Kodi anthu ali ndi maganizo osiyana ati pa nkhani ya ufulu wosankha zochita? (b) Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhani ya ufulu wosankha zochita? (c) Kodi m’nkhaniyi tikambirana mafunso ati?

 MAYI wina ankafunika kusankha zochita pa nkhani inayake. Ndiye anauza mnzake kuti: “Ingondiuza zoti ndichite osati zoti ndiganizire.” Mayiyu ankafuna kuti angouzidwa zochita m’malo mogwiritsa ntchito mphatso yapadera imene Yehova anatipatsa. Kodi inuyo mumatani ngati mukufunika kusankha zochita? Kodi mumasankha nokha kapena mumafuna kuti ena akusankhireni? Nanga kodi mumayamikira mphatso ya ufulu wosankha imene Yehova anatipatsa?

2 Anthu amasiyana maganizo pa nkhani ya ufulu wosankhayi. Ena amaona kuti anthufe tilibe ufulu wosakha chifukwa Yehova analemberatu zonse zimene zidzachitike pa moyo wathu. Pamene ena amati munthu angakhale ndi ufulu wosankha pokhapokha zitakhala kuti angathe kuchita chilichonse chimene akufuna. Koma Mawu a Mulungu angatithandize kudziwa zoona pa nkhaniyi. Baibulo limanena kuti Yehova anatipatsa ufulu wosankha zochita. (Werengani Yoswa 24:15.) Baibulo lingatithandizenso kupeza mayankho a mafunso otsatirawa: Kodi munthu angagwiritse ntchito bwanji ufulu wake wosankha zochita? Kodi kukhala ndi ufulu wosankha kukutanthauza kuti tingathe kumangochita chilichonse? N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene timasankha zimasonyeza ngati timakonda kwambiri Yehova kapena ayi? Nanga tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza ufulu wa ena wosankha zochita?

KODI TINGAPHUNZIRE CHIYANI KWA YEHOVA NDI YESU?

3. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji ufulu wake wosankha zochita?

3 Yehova yekha ndi amene ali ndi ufulu wochita chilichonse. Komabe iye ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yogwiritsa ntchito bwino ufulu wosankha zochita. Mwachitsanzo, anasankha Aisiraeli kuti akhale anthu odziwika ndi dzina lake komanso “chuma chake chapadera.” (Deut. 7:6-8) Sikuti Yehova anangosankha mtunduwu popanda chifukwa. Anachita zimenezi pofuna kukwaniritsa lonjezo limene anapangana ndi bwenzi lake Abulahamu. (Gen. 22:15-18) Komanso nthawi zonse Yehova amagwiritsa ntchito ufulu wake wosankha mogwirizana ndi makhalidwe ake ena monga chikondi ndi chilungamo. Umboni wa izi ndi zimene ankachita ndi Aisiraeli. Iwo mobwerezabwereza ankasiya kulambira koona. Koma akalapa, Yehova ankawasonyeza chifundo ndipo ankayambiranso kuwakonda. Iye anati: “Ndidzathetsa kusakhulupirika kwawo. Ndidzawakonda mwa kufuna kwanga.” (Hos. 14:4) Apatu Yehova ankagwiritsa ntchito ufulu wake wosankha zochita pothandiza ena.

4, 5. (a) Kodi ndani anali woyamba kupatsidwa ufulu wosankha zochita, nanga anagwiritsa ntchito bwanji ufuluwo? (b) Kodi tonsefe tiyenera kudzifunsa funso liti?

4 Yehova atayamba ntchito yolenga, anasankha kuti apatse angelo ake ufulu wosankha zochita. Mngelo woyamba kulandira ufulu umenewu anali Mwana wake amenenso ndi “chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo.” (Akol. 1:15) Kodi Yesu amagwiritsa ntchito bwanji ufuluwu? Asanabwere padzikoli anasankha kukhalabe wokhulupirika kwa Atate wake ndipo sanakhale kumbali ya Satana. Atabwera padzikoli, anakananso mayesero a Satana. (Mat. 4:10) Komanso atatsala pang’ono kuperekedwa, iye anapemphera kwa Atate wake ndipo anasonyeza kuti ankafunitsitsa kukhalabe wokhulupirika. Anati: “Atate, ngati mukufuna, ndichotsereni kapu iyi. Komatu chifuniro chanu chichitike, osati changa.” (Luka 22:42) Tiyeni tizitsanzira Yesu ndipo nafenso tizigwiritsa ntchito bwino ufulu wathu wosankha, pochita chifuniro cha Yehova. Koma kodi n’zothekadi kuchita zimenezi?

5 Inde n’zotheka, popeza nafenso tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu. (Gen. 1:26) Komabe kwa ifeyo, kukhala ndi ufulu wosankha sikukutanthauza kuti tingathe kumangochita chilichonse. Paja Yehova yekha ndi amene ali ndi ufulu wochita chilichonse. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti pali zinthu zina zimene sitiyenera kuchita ndipo tiyenera kutsatira zimene Mulungu amafuna. Mwachitsanzo, akazi ayenera kugonjera amuna awo ndipo ana ayenera kumvera makolo. (Aef. 5:22; 6:1) Kodi mfundo yoti pali zina zimene sitiyenera kuchita imakhudza bwanji ufulu wathu wosankha zochita? Funso limeneli ndi lofunika kwambiri chifukwa zimene timasankha zingachititse kuti tidzapeze moyo kapena ayi.

KUGWIRITSA NTCHITO UFULU WOSANKHA ZOCHITA MOYENERA NDI MOLAKWIKA

6. Fotokozani chitsanzo chosonyeza kuti malamulo otiletsa kuchita zinthu zina amatithandiza.

6 Kodi munthu amene sakuyenera kuchita zinazake tinganene kuti alidi ndi ufulu? Inde. N’chifukwa chiyani tikutero? Malamulo oletsa anthu kuchita zinthu zinazake amatiteteza. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mwasankha kuti mupite kwinakwake kutali pagalimoto. Koma kumene mukupitako kulibe malamulo a pamsewu ndipo aliyense amangoyenda mbali imene akufuna komanso amathamangitsa galimoto mmene akufunira. Kodi mungamve kuti ndinu wotetezeka? Yankho ndi lodziwikiratu. Choncho malamulo amathandiza kuti anthu azisangalala ndi ufulu wawo moyenera. Kuti timvetse bwino mfundoyi tiyeni tikambirane zitsanzo za m’Baibulo zosonyeza kuti malamulo a Yehova otiletsa kuchita zinthu zina amatithandiza.

7. (a) Kodi Adamu anali wosiyana bwanji ndi zinyama? (b) Kodi Adamu anagwiritsa ntchito bwanji moyenera ufulu wake wosankha zochita?

7 Mulungu anapatsa Adamu mphatso ya ufulu wosankha zochita ngati imene anapatsa angelo. Zimenezi zinachititsa kuti Adamu akhale wosiyana ndi zinyama. Poyamba Adamu anagwiritsira ntchito ufulu umenewu moyenera. Mulungu anayamba kulenga zinyama asanalenge munthu. Koma iye anapatsa Adamu mwayi woti atchule mayina nyamazo. Baibulo limanena kuti Mulungu “anayamba kuzibweretsa kwa munthuyo, kuti chilichonse achitche dzina.” Adamu atasankha mayina oti apatse nyamazo, Yehova sanasinthe mayina amene anaperekedwawo. Choncho “dzina lililonse limene munthuyo anatchula chamoyo chilichonse, limenelo linakhaladi dzina lake.”—Gen. 2:19.

8. Kodi Adamu anagwiritsa ntchito bwanji molakwika ufulu wake wosankha zochita, nanga zotsatira zake zinali zotani?

8 Yehova anapatsanso Adamu ntchito yoti asandutse dziko lonse lapansi kukhala Paradaiso. Anamuuza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire. Muyang’anirenso nsomba . . . zolengedwa zouluka, . . . komanso cholengedwa chilichonse chokwawa padziko lapansi.” (Gen. 1:28) Koma m’malo mokhutira ndi ntchito imene anapatsidwayi, Adamu anasankha kuswa lamulo la Mulungu ndipo anadya chipatso chimene Mulunguyo anamuletsa. Apatu Adamu anagwiritsa ntchito molakwika ufulu wake wosankha zochita. Zimene anachitazi zinabweretsa mavuto aakulu kwa anthu onse. (Aroma 5:12) Kuganizira mfundo imeneyi kungatithandize kuti tizigwiritsa ntchito moyenera ufulu wathu n’kumapewa kuswa malamulo a Mulungu.

9. Kodi Yehova anapatsa Aisiraeli mwayi wotani, ndipo iwo anatani?

9 Anthu onse anatengera uchimo ndi imfa kwa Adamu ndi Hava. Ngakhale zili choncho, iwo ali ndi ufulu wosankha zochita. Umboni wa zimenezi ndi mmene Mulungu ankachitira zinthu ndi mtundu wa Isiraeli. Kudzera mwa Mose, Yehova anapatsa Aisiraeli mwayi wosankha kukhala anthu ake apadera kapena ayi. (Eks. 19:3-6) Ndiye kodi iwo anatani? Anasankha kukhala anthu a Mulungu ndipo anavomera kuti azimvera malamulo ake. Iwo anati: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo.” (Eks. 19:8) Koma n’zomvetsa chisoni kuti patapita nthawi Aisiraeli anayamba kugwiritsa ntchito molakwika ufulu wawo wosankha zochita ndipo sanatsatire mawu awowa. Tingaphunzire zambiri kwa Aisiraeliwa. Tiyeni tiziyamikira mphatso ya ufulu wosankha imene Yehova anatipatsa. Tiziyesetsa kukhalabe naye pa ubwenzi komanso kumumvera.—1 Akor. 10:11.

10. Tchulani zitsanzo zosonyeza kuti anthu ochimwafe tingathe kugwiritsa ntchito moyenera ufulu wathu wosankha zochita. (Onani chithunzi patsamba 12.)

10 Mu chaputala 11 cha Aheberi muli mayina a atumiki a Mulungu 16 amene anasankha kumvera Yehova. Izi zinachititsa kuti apeze madalitso ambiri. Komanso anthuwa adzakhala ndi moyo wosatha. Mwachitsanzo, Nowa anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba. Iye anasankha kumvera Mulungu ndipo anamanga chingalawa chomwe anapulumukiramo limodzi ndi banja lake. Izi zinathandiza kuti mtundu wa anthu usathe padzikoli. (Aheb. 11:7) Abulahamu ndi Sara anamvera Mulungu ndipo anapita kudziko limene iye anawalonjeza. Pa nthawi ina anali ndi “mpata wobwerera” ku Uri koma sanabwerere. Iwo ankaganizira kwambiri za ‘kukwaniritsidwa kwa malonjezo’ a Mulungu ndipo ‘ankafunitsitsa malo abwino koposa.’ (Aheb. 11:8, 13, 15, 16) Mose anasiya chuma cha ku Iguputo ndipo “anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu, m’malo mochita zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo.” (Aheb. 11:24-26) Tiyeni tizitsanzira chikhulupiriro cha anthu amenewa. Tizigwiritsa ntchito moyenera ufulu wathu wosankha, pochita chifuniro cha Mulungu. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tikuyamikira mphatsoyi.

11. (a) Kodi tingagwiritse ntchito ufulu wathu wosankha zochita posankha zinthu ziti? (b) N’chiyani chimakupangitsani kuti muzigwiritsa ntchito moyenera ufulu wanu wosankha zochita?

11 Anthu ena amaona kuti zimakhala zophweka kuti wina azingowasankhira zochita. Koma tikamachita zimenezi tingalephere kugwiritsa ntchito mphatso ya mtengo wapatali imeneyi posankha zinthu zofunika kwambiri. Zinthu zake zafotokozedwa palemba la Deuteronomo 30:19, 20. (Werengani.) Vesi 19 likusonyeza kuti Mulungu anapatsa Aisiraeli ufulu woti asankhe zimene ankafuna kuchita. Pamene vesi 20 likusonyeza kuti Yehova anawapatsa mwayi woti asonyeze zimene zinali mumtima mwawo. Ifenso tingasankhe kuti tizilambira Yehova. Tingathenso kusankha kuti tizigwiritsa ntchito ufulu wathu wosankha potamanda Yehova komanso posonyeza zimene zili mumtima mwathu.

TISAMAGWIRITSE NTCHITO MOLAKWIKA UFULU WATHU WOSANKHA ZOCHITA

12. Kodi tizipewa kuchita chiyani ndi mphatso yathu ya ufulu wosankha zochita?

12 Tiyerekeze kuti mwapatsa mnzanu mphatso yamtengo wapatali. Kodi mungamve bwanji mutaona kuti mnzanuyo wataya mphatsoyo kapena akuigwiritsa ntchito povulaza ena? Ndiye kodi mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji akaona anthu ambiri akugwiritsa ntchito molakwika ufulu wawo wosankha, mwina pochitira ena zoipa? Baibulo linaneneratu kuti ‘m’masiku otsiriza’ ano anthu ambiri adzakhala “osayamika.” (2 Tim. 3:1, 2) Koma ifeyo tiziyamikira mphatso imeneyi ndipo tizipewa kuigwiritsa ntchito molakwika. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?

13. Kodi tingapewe bwanji kugwiritsa ntchito molakwika ufulu wathu wosankha zochita?

13 Tonsefe tili ndi ufulu wosankha pa nkhani ya anthu ocheza nawo, zovala, kudzikongoletsa komanso zosangalatsa. Koma ngati titasankha kumangotsatira zofuna zathu kapena ngati timatengeka kwambiri ndi dzikoli, ufulu wathuwu ungakhale ngati “chophimbira zoipa.” (Werengani 1 Petulo 2:16.) Si bwino kugwiritsa ntchito ufulu wathu “polimbikitsira zilakolako za thupi.” M’malomwake tiyeni tiziyesetsa kusankha zochita zimene zingatithandize kutsatira malangizo akuti: “Chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.”—Agal. 5:13; 1 Akor. 10:31.

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira Yehova tikamagwiritsa ntchito ufulu wathu wosankha zochita?

14 Chinthu china chimene chingatithandize kugwiritsa ntchito bwino ufulu wathu wosankha zochita ndi kudalira Yehova kuti azititsogolera. Iye yekha ndi amene ‘amatiphunzitsa kuti zinthu zitiyendere bwino komanso amatichititsa kuti tiyende m’njira imene tiyenera kuyendamo.’ (Yes. 48:17) Tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumavomereza mfundo yakuti: “Munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yer. 10:23) Tizipewa msampha wodzidalira ndipo tisakhale ngati Adamu ndi Aisiraeli osamvera aja. Koma tiyeni ‘tizikhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse.’—Miy. 3:5.

TIZILEMEKEZA UFULU WA ENA WOSANKHA ZOCHITA

15. Kodi tikuphunzira chiyani pa mfundo yopezeka pa Agalatiya 6:5?

15 Tiyeneranso kulemekeza ufulu wa anthu ena wosankha zochita. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi? Popeza aliyense ali ndi mphatsoyi, sizingatheke kuti nthawi zonse tizisankha zinthu zofanana. Akhristu angasankhe zosiyana ngakhale pa nkhani zokhudza kulambira. Tisamaiwale mfundo yopezeka pa Agalatiya 6:5. (Werengani.) Kukumbukira kuti Mkhristu aliyense ayenera “kunyamula katundu wake,” kungatithandize kuti tizilemekeza ufulu wa ena wosankha zochita.

Tisamaumirize ena kuti nawonso achite zimene ifeyo tasankha (Onani ndime 15)

16, 17. (a) Kodi mumpingo wa ku Korinto munayambika nkhani yotani yokhudza ufulu wosankha? (b) Kodi Paulo anawathandiza bwanji kuthetsa nkhaniyi, nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani?

16 Tiyeni tione chitsanzo cha m’Baibulo chosonyeza kufunika kolemekeza zimene ena asankha mogwirizana ndi chikumbumtima chawo. Akhristu a ku Korinto ankasiyana maganizo pa nkhani yokhudza kudya nyama yoperekedwa nsembe kwa mafano, imene inkagulitsidwa pamsika. Ena ankaganiza kuti: ‘Popeza mafano alibe ntchito, palibe vuto kudya nyamayi.’ Komabe ena amene poyamba ankalambira mafano ankaona kuti kudya nyamayo kunali ngati kulambira mafano. (1 Akor. 8:4, 7) Nkhaniyi inali yovuta ndipo ikanatha kuyambitsa magawano mumpingo. Ndiye kodi Paulo anathandiza bwanji Akhristu a ku Korinto kudziwa mmene Yehova ankaionera nkhaniyo?

17 Choyamba, iye anawakumbutsa kuti chakudya sichingathandize munthu kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. (1 Akor. 8:8) Kenako anawachenjeza kuti asamalole kuti ‘ufulu wawo’ wosankha ukhale “chopunthwitsa kwa ofooka.” (1 Akor. 8:9) Iye analangizanso anthu amene chikumbumtima chawo chinkawaletsa kudya nyamayo kuti asamaweruze anzawo amene anasankha kuti azidya. (1 Akor. 10:25, 29, 30) Izi zikusonyeza kuti pa nkhani yokhudza kulambirayi, Mkhristu aliyense ankayenera kusankha zochita mogwirizana ndi chikumbumtima chake. Choncho tiyenera kulemekeza zimene ena asankha ngakhale pa nkhani zing’onozing’ono.—1 Akor. 10:32, 33.

18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mphatso ya ufulu wosankha?

18 Yehova anatipatsa mphatso ya ufulu wosankha zochita ndipo izi zimachititsa kuti tikhale ndi ufulu weniweni. (2 Akor. 3:17) Timayamikira mphatsoyi chifukwa imatithandiza kuti tizitha kusankha zinthu zimene zimasonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova. Tiyeni tipitirize kuyamikira mphatso yamtengo wapataliyi polemekeza Mulungu komanso polemekeza zimene anthu ena asankha.