‘Zinthu Zimenezo Uziziphunzitsa kwa Anthu Okhulupirika’

‘Zinthu Zimenezo Uziziphunzitsa kwa Anthu Okhulupirika’

“Zimenezo uziphunzitse kwa anthu okhulupirika amene nawonso, adzakhala oyenerera bwino kuphunzitsa ena.”2 TIM. 2:2.

NYIMBO: 123, 53

1, 2. Kodi anthu ambiri amaona bwanji ntchito yawo?

 ANTHU ena amaganiza kuti ntchito imene amagwira imawachititsa kukhala ofunika kapena osafunika. Ndipo m’madera ena, anthu akayamba kucheza ndi munthu koyamba amamufunsa kuti: “Kodi mumagwira ntchito yanji?”

2 Nthawi zina Baibulo limatchulanso ntchito zimene anthu ena ankagwira. Mwachitsanzo, limanena za “Mateyu wokhometsa msonkho,” ‘Simoni wofufuta zikopa’ komanso “Luka, dokotala wokondedwa.” (Mat. 10:3; Mac. 10:6; Akol. 4:14) Enanso ankadziwika ndi udindo umene Mulungu anawapatsa. Mwachitsanzo panali Mfumu Davide, mneneri Eliya komanso mtumwi Paulo. Anthu amenewa ankaona kuti udindo wawowo ndi wofunika kwambiri. Ifenso ngati tili ndi udindo m’gululi, tiyenera kuuona kuti ndi wofunika kwambiri.

3. N’chifukwa chiyani achikulire ayenera kuphunzitsa achinyamata? (Onani chithunzi pamwambapa.)

3 Ambirife timakonda kutumikira Yehova komanso timakonda udindo umene tili nawo m’gululi. Koma vuto ndi lakuti munthu akamakalamba sakwanitsa kuchita zambiri ngati poyamba. (Mlal. 1:4) Masiku ano, zimenezi zimabweretsa mavuto ena kwa Akhristu. Panopa, ntchito m’gulu la Yehova yakula kwambiri ndipo ikufuna zambiri. Ntchito zatsopano zachititsa kuti papezeke njira zatsopano zogwirira ntchitozo ndipo njira zambiri ndi zamakono. Ndiyeno achikulire ena amavutika kuzolowera njira zatsopanozo. (Luka 5:39) Ngakhale zitakhala kuti achikulirewo sakuvutika, achinyamata amakhala ndi mphamvu zambiri kuposa achikulire. (Miy. 20:29) Choncho ndi bwino kuti achikulire aziphunzitsa achinyamata kuti akhale ndi maudindo akuluakulu.—Werengani Salimo 71:18.

4. N’chifukwa chiyani ena zimawavuta kuphunzitsa ena? (Onani bokosi lakuti,  “N’chifukwa Chiyani Anthu Ena Amaopa Kupatsa Ena Udindo?”)

4 Akhristu ena amene ali ndi maudindo zimawavuta kuphunzitsa achinyamata. Ena amaopa kuti alandidwa udindo umene amaukonda. Pomwe ena amakayikira achinyamatawo ndipo amaganiza kuti sangachite bwino zinthu. Ndiye pali enanso amene amaganiza kuti alibe nthawi yophunzitsa munthu wina. Koma nawonso abale achinyamata ayenera kukhala odekha akaona kuti sakupatsidwa udindo winawake.

5. Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhaniyi?

5 Tiyeni tsopano tikambirane bwinobwino nkhani yopatsa ena udindoyi. Tiona mbali ziwiri. Choyamba, kodi abale achikulire angathandize bwanji achinyamata kuti agwire bwino ntchito imene apatsidwa, ndipo ubwino wochita zimenezi ndi wotani? (2 Tim. 2:2) Chachiwiri, n’chifukwa chiyani abale achinyamata ayenera kukhala ndi maganizo oyenera akamagwira ntchito ndi achikulire komanso akamaphunzira zinthu kwa iwo? Tiyeni tiyambe ndi kukambirana mmene Davide anathandizira mwana wake kuti agwire ntchito yaikulu kwambiri.

DAVIDE ANATHANDIZA SOLOMO

6. Kodi Davide ankafuna kuchita chiyani, nanga Yehova anati bwanji?

6 Davide anakhala moyo wothawathawa kwa zaka zambiri. Koma kenako anakhala mfumu ndipo anali ndi nyumba yabwino kwambiri. Komabe anakhumudwa poona kuti panalibe kachisi wa Yehova choncho anaganiza zoti amange kachisiyo. Ndiyeno anauza mneneri Natani kuti: “Ine ndikukhala m’nyumba ya mitengo ya mkungudza, koma likasa la pangano la Yehova likukhala m’chihema chansalu.” Natani anati: “Chitani chilichonse chimene chili mumtima mwanu, chifukwa Mulungu woona ali nanu.” Koma maganizo a Yehova anali osiyana ndi amenewa. Anauza Natani kuti akauze Davide kuti: “Si iwe amene udzandimangira nyumba yokhalamo.” Ngakhale kuti Yehova analonjeza kuti adzapitiriza kudalitsa Davide, ananena kuti Solomo ndi amene adzamange kachisi. Ndiye kodi Davide anatani atamva zimenezi?—1 Mbiri 17:1-4, 8, 11, 12; 29:1.

7. Kodi Davide anatani Yehova atamuuza kuti samanga kachisi?

7 Davide akanatha kukhumudwa kwambiri chifukwa choti ankafunitsitsa kumanga kachisi wa Yehova. Koma anathandiza kwambiri pokonzekera ntchito imene Solomo adzagwireyo. Anapeza zitsulo, mkuwa, siliva, golide matabwa komanso anthu oti adzagwire ntchitoyo. Iyeyo sanadandaule kuti akapanda kumanga kachisiyo sadzatamandidwa. Ndipotu atamangidwa ankatchedwa kachisi wa Solomo. M’malomwake analimbikitsa Solomo kuti: “Tsopano mwana wanga, Yehova akhale nawe, ndipo zinthu zikuyendere bwino kuti umange nyumba ya Yehova Mulungu wako, monga mmene iye analankhulira za iwe.”—1 Mbiri 22:11, 14-16.

8. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zikanachititsa Davide kuganiza kuti Solomo sangakwanitse ntchito yomanga kachisi? (b) Koma kodi Davide anatani?

8 Werengani 1 Mbiri 22:5. Davide akanatha kuganiza kuti Solomo wachepa nayo ntchitoyo. Pajatu kachisiyo anafunika kukhala ‘wokongola ndiponso waulemerero wosaneneka.’ Kuwonjezera pamenepo, Solomo anali adakali “wamng’ono komanso wosakhwima.” Koma Davide ankadziwa kuti Yehova adzathandiza Solomo kuti agwire bwino ntchitoyo. Choncho Davide anangochita zimene akanatha ndipo anamuthandiza kukonzekera ntchito yaikuluyo.

MUZISANGALALA KUPHUNZITSA ENA

Zimasangalatsa kwambiri kuona abale achinyamata akuchita zambiri m’gulu la Yehova (Onani ndime 9)

9. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti abale achikulire ayenera kusangalala akasiyira achinyamata maudindo ena.

9 Abale achikulire asamakhumudwe pakafunika kuti apatse abale achinyamata ntchito imene iwo ankagwira. Ayenera kudziwa kuti achinyamata akaphunzitsidwa bwino n’kutenga udindo zimathandiza kuti ntchito iziyenda bwino. Abale achikululire ayenera kusangalala akaona kuti achinyamata amene anawaphunzitsa akuyenerera udindo. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti pali bambo ndi mwana wake. Mwanayo ali wamng’ono ankangoyang’ana pamene bambo ake ankayendetsa galimoto. Koma atakula, bambowo anayamba kumamufotokozera zimene akuchita akamayendetsa galimotoyo. Kenako mwanayo atafika msinkhu woyendetsa galimoto anayamba kuphunzira kuyendetsa ndipo bambo akewo ankamupatsa malangizo. Nthawi zina ankasinthana kuyendetsa. Koma patapita nthawi, mwanayo ndi amene amawayendetsa nthawi zonse chifukwa tsopano bambo akewo ndi achikulire. Bambowo amasangalala ndi zimenezi ndipo saganiza kuti ndi osafunika chifukwa sayendetsanso galimoto. N’chimodzimodzinso ndi abale achikulire. Iwo ayenera kusangalala akaona achinyamata amene anawaphunzitsa ali ndi udindo m’gulu la Yehova.

10. N’chiyani chikusonyeza kuti Mose sankadera nkhawa za udindo kapena ulemerero wake?

10 Komanso abale achikulire ayenera kupewa mtima wansanje. Tingaphunzire zambiri kuchokera pa zimene Mose anachita pamene Aisiraeli ena anayamba kuchita zinthu ngati aneneri. (Werengani Numeri 11:24-29.) Pa nthawiyo Yoswa anali mtumiki wa Mose ndipo ankafuna kuwaletsa. Mwina iye ankafuna kuwaletsa poganiza kuti iwo alanda udindo komanso ulemerero wa Mose. Koma Mose anamuuza kuti: “Kodi ukuchita nsanje chifukwa chondidera nkhawa? Ayi usatero. Ndikanakonda anthu onse a Yehova akanakhala aneneri, chifukwa Yehova akanaika mzimu wake pa iwo!” Mose ankaona kuti Yehova ndi amene akuthandiza anthu ake. N’chifukwa chake sanafune ulemerero, koma anati akanakonda kuti anthu onse a Mulungu akhale ndi udindo wonenera. Kodi nafenso timasangalala anthu ena akapatsidwa udindo m’gululi?

11. Fotokozani zimene m’bale wina ananena m’bale wachinyamata atayamba kugwira ntchito imene iye ankagwira poyamba.

11 Masiku ano pali abale ambiri amene atumikira mwakhama kwa nthawi yaitali ndipo aphunzitsa abale achinyamata kuti azigwira ntchito zambiri. Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Peter wachita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 74. Iye wakhala akutumikira panthambi ya ku Europe kwa zaka 35. M’baleyu anakhalapo woyang’anira Dipatimenti ya Utumiki ndipo anagwira ntchito kwa nthawi yaitali ndi m’bale wina wachinyamata dzina lake Paul. Panopa M’bale Paul ndi amene akuyang’anira Dipatimenti ya Utumiki. M’bale Peter atafunsidwa mmene amamvera akaganiza za kusinthaku, anati: “Ndikusangalala kwambiri kuona kuti pali abale amene aphunzitsidwa omwe panopa ali ndi udindo waukulu ndipo akugwira bwino ntchito yawo.”

MUZIONA KUTI ACHIKULIRE NDI OFUNIKA KWAMBIRI

12. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Rehobowamu?

12 Solomo atamwalira, mwana wake dzina lake Rehobowamu anakhala mfumu. Pa nthawi ina, iye ankafuna malangizo okhudza udindo wake. Choyamba anapita kwa achikulire koma ananyalanyaza zimene anamuuza. Kenako anafunsa anyamata anzake amene ankamutumikira ndipo anatsatira malangizo awo. Zotsatira zake zinali zoipa kwambiri. (2 Mbiri 10:6-11, 19) Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Ndi bwino kufunsa malangizo kwa achikulire chifukwa amadziwa zambiri. N’zoona kuti achinyamata sayenera kumangotsatira njira zakale, koma si bwinonso kuganiza kuti achikulire sangawathandize.

13. Kodi abale achinyamata angatani kuti azigwira ntchito bwino ndi achikulire?

13 Masiku ano, pali abale achinyamata amene akuyang’anira ntchito zimene zikugwiridwa ndi achikulire. Zikatere, abale achinyamatawo ayenera kufunsira nzeru kwa achikulirewo asanasankhe zochita. M’bale Paul uja ananena kuti: “Ndinkafunsa malangizo kwa M’bale Peter ndipo ndinalimbikitsa aliyense mudipatimenti kuti azichita chimodzimodzi.”

14. Kodi tingaphunzire chiyani pa mgwirizano womwe unali pakati pa Timoteyo ndi mtumwi Paulo?

14 Timoteyo ali wachinyamata anatumikira ndi mtumwi Paulo kwa zaka zambiri. (Werengani Afilipi 2:20-22.) Paulo analembera Akorinto kuti: “Ndikukutumizirani Timoteyo, popeza iye ndi mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Iye adzakukumbutsani mmene ndimachitira zinthu potumikira Khristu Yesu, monga mmenenso ineyo ndikuphunzitsira kulikonse, mumpingo uliwonse.” (1 Akor. 4:17) Mawu amenewa akusonyeza kuti Paulo ndi Timoteyo ankagwira ntchito limodzi mogwirizana. Paulo anayesetsa kupeza nthawi yophunzitsa Timoteyo ‘mmene ankachitira zinthu potumikira Khristu.’ Timoteyo anaphunzira zambiri ndipo Paulo ankamukonda kwabasi. Ndipotu Paulo ankakhulupirira kuti Timoteyo angathe kuthandiza Akorinto. Zimene Paulo anachita ndi chitsanzo chabwino kwa akulu akamaphunzitsa ena kuti akhale oyang’anira.

TONSE TIYENERA KUCHITA MBALI YATHU

15. Kodi malangizo amene Paulo analembera Akhristu a ku Roma angatithandize bwanji zinthu zikasintha?

15 Masiku ano mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova ikukula ndipo izi n’zosangalatsa kwambiri. Koma zimenezi zikupangitsa kuti pazifunika kusintha zinthu zina m’gululi. Choncho kusintha kukatikhudza ifeyo tiyenera kukhala odzichepetsa. Tiziganizira kwambiri zimene Yehova akufuna osati zofuna zathu. Tikatero tidzakhala ogwirizana. Paulo analembera Akhristu a ku Roma kuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira. Koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino, malinga ndi chikhulupiriro chimene Mulungu wamupatsa. Pakuti monga tilili ndi ziwalo zambiri m’thupi limodzi, koma ziwalozo sizigwira ntchito yofanana, momwemonso ifeyo, ngakhale kuti ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu.”—Aroma 12:3-5.

16. Kodi achikulire, achinyamata komanso akazi ayenera kuchita chiyani kuti m’gulu la Yehova mukhale mtendere ndi mgwirizano?

16 Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tiyeni tizichita zimene tingathe potumikira Yehova. Ngati ndinu wachikulire, yesetsani kuphunzitsa achinyamata ntchito zanu. Nanunso achinyamata muyenera kuvomera mukapatsidwa udindo ndipo muzikhala odzichepetsa komanso muzilemekeza achikulire. Akazi nawonso ayenera kutsanzira Purisikila amene ankathandiza mwamuna wake mokhulupirika ngakhale kuti zinthu zinkasintha pa moyo wawo.—Mac. 18:2.

17. Kodi Yesu ankakhulupirira kuti ophunzira ake adzakwanitsa kuchita chiyani, nanga anawaphunzitsa ntchito iti?

17 Yesu ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yophunzitsa ena kuti atenge maudindo. Iye ankadziwa kuti adzachoka padzikoli ndipo padzafunika anthu ena oti azigwira ntchito imene ankagwira. Ophunzira ake anali ochimwa koma iye ankawakhulupirira ndipo anawauza kuti adzachita zambiri kuposa zimene iyeyo anachita. (Yoh. 14:12) Iye anawaphunzitsa bwino moti anakwanitsa kulalikira uthenga wabwino “m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.”—Akol. 1:23.

18. Kodi tikuyembekezera zinthu ziti, nanga panopa tiyenera kuchita chiyani?

18 Yesu atafa anaukitsidwa n’kupita kumwamba. Kumwambako, anapatsidwa udindo waukulu kwambiri kuposa ‘boma lililonse, ulamuliro uliwonse, amphamvu onse komanso ambuye onse.’ (Aef. 1:19-21) Tikakhalabe okhulupirika n’kumwalira Aramagedo isanafike, tidzaukitsidwa m’dziko latsopano ndipo tidzakhala ndi ntchito zambiri zosangalatsa. Koma panopa ntchito yofunika kwambiri imene tiyenera kugwira ndi yolalikira uthenga wabwino ndi kuphunzitsa anthu. Choncho kaya ndife achikulire kapena achinyamata, tiyeni tiziyesetsa kukhala ndi ‘zochita zambiri mu ntchito ya Ambuye.’—1 Akor. 15:58.