Nkhani Yophunzira 4
‘Mzimu Umachitira Umboni’
“Mzimuwo umachitira umboni limodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu.”—AROMA 8:16.
NYIMBO NA. 25 Chuma Chapadera
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1-2. Kodi pa Pentekosite mu 33 C.E. panachitika zinthu zodabwitsa ziti?
LAMLUNGU m’mawa pa Pentekosite wa mu 33 C.E., ophunzira a Yesu pafupifupi 120 anasonkhana m’chipinda cham’mwamba ku Yerusalemu. (Mac. 1:13-15; 2:1) Masiku angapo izi zisanachitike, Yesu anauza ophunzira akewo kuti akhalebe ku Yerusalemu n’cholinga choti alandire mphatso yapadera. (Mac. 1:4, 5) Ndiye kodi chinachitika n’chiyani?
2 “Mwadzidzidzi kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu.” Phokoso lake linadzaza m’nyumba yonseyo. Kenako, “malawi amoto ooneka ngati malilime” anaoneka pamwamba pa mitu ya ophunzirawo. Ndiyeno onsewo “anadzazidwa ndi mzimu woyera.” (Mac. 2:2-4) Yehova anagwiritsa ntchito njira yodabwitsayi podzoza anthuwo ndi mzimu wake. (Mac. 1:8) Ophunzirawo anali anthu oyamba kudzozedwa ndi mzimu woyera * n’kupatsidwa chiyembekezo chokalamulira ndi Yesu kumwamba.
N’CHIYANI CHIMACHITIKA MUNTHU AKADZOZEDWA?
3. N’chifukwa chiyani anthu pa Pentekosite sanakayikire kuti adzozedwa?
3 Mukanakhala kuti munalipo m’chipinda cham’mwambacho pa tsikulo, simukanaiwala pa moyo wanu wonse zimene zinachitika. Pamutu panu pakanaima chinthu chooneka ngati lilime lamoto, inu n’kuyamba kulankhula m’chilankhulo china. (Mac. 2:5-12) Simukanakayikiranso zoti mwadzozedwa ndi mzimu woyera. Koma kodi anthu onse amadzozedwa m’njira yodabwitsa komanso pa nthawi yofanana? Ayi. N’chifukwa chiyani tikutero?
4. Kodi Akhristu onse oyambirira anadzozedwa pa nthawi yofanana? Fotokozani.
4 Tiyeni tikambirane za nthawi imene anthu amadzozedwa. Anthu amene anadzozedwa pa Pentekosite mu 33 C.E. sanali 120 okha. Pa nthawi ina tsiku lomwelo, anthu ena 3,000 analandiranso mzimu woyera pa nthawi imene anabatizidwa. (Mac. 2:37, 38, 41) Koma pa zaka zotsatira, si Akhristu onse amene ankadzozedwa pa nthawi ya ubatizo. Anthu ena a ku Samariya analandira mzimu woyera patapita nthawi kuchokera pamene anabatizidwa. (Mac. 8:14-17) Pomwe Koneliyo ndi banja lake analandira mzimu woyera pa nthawi yosiyana ndi anthu ena chifukwa anaulandira asanabatizidwe n’komwe.—Mac. 10:44-48.
5. Malinga ndi 2 Akorinto 1:21, 22, kodi chimachitika n’chiyani munthu akadzozedwa?
5 Tiyeni tsopano tikambirane zimene zimachitika munthu akadzozedwa ndi mzimu woyera. Poyamba, anthu ena amene adzozedwa angavutike kuvomereza kuti Yehova wawasankha. Mwina angadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu wasankha ineyo?’ Pomwe anthu ena savutika ndi zimenezi. Koma mtumwi Paulo ananena zimene zimachitika kwa Mkhristu aliyense amene wadzozedwa. Iye anati: “Mutakhulupirira munaikidwa chidindo * cha mzimu woyera wolonjezedwawo, umene ndi chikole cha cholowa chathu cham’tsogolo.” (Aef. 1:13, 14) Choncho Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake potsimikizira Akhristuwo kuti wawasankha. Apa tingati mzimuwo umakhala “chikole,” kapena kuti lonjezo, powatsimikizira kuti adzalandira moyo wosatha kumwamba osati padzikoli.—Werengani 2 Akorinto 1:21, 22.
6. Kodi odzozedwa ayenera kuchita chiyani kuti adzalandire mphoto yawo kumwamba?
6 Kodi munthu akangodzozedwa ndiye kuti basi adzapita kumwamba? Ayi. N’zoona kuti sakayikira zoti anasankhidwa kuti adzapite kumwamba. Koma ayenera kukumbukira malangizo akuti: “Abale, chitani chilichonse chotheka kuti mukhalebe okhulupirika, n’cholinga choti mupitirizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana ndi kuwasankha, pakuti mukapitiriza kuchita zinthu zimenezi simudzalephera ngakhale pang’ono.” (2 Pet. 1:10) Choncho ngakhale kuti munthu wodzozedwa amasankhidwa kuti apite kumwamba, iye amafunika kukhalabe wokhulupirika kuti adzalandire mphotoyo.—Afil. 3:12-14; Aheb. 3:1; Chiv. 2:10.
KODI MUNTHU AMADZIWA BWANJI KUTI WADZOZEDWA?
7. Kodi Akhristu odzozedwa amadziwa bwanji kuti asankhidwa kupita kumwamba?
7 Koma kodi munthu amadziwa bwanji kuti wasankhidwa kupita kumwamba? Tingapeze yankho la funsoli pa mawu amene Paulo anauza Akhristu a ku Roma omwe anali “oitanidwa kukhala oyera.” Iye anati: “Popeza simunalandire mzimu wa ukapolo woyambitsanso mantha, koma munalandira mzimu wakuti mukhale ana, umene timafuula nawo kuti: ‘Abba, Atate!’ Pakuti mzimuwo umachitira umboni limodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu.” (Aroma 1:7; 8:15, 16) Choncho Mulungu amagwiritsa ntchito mzimu wake potsimikizira odzozedwa kuti asankhidwa kupita kumwamba.—1 Ates. 2:12.
8. Kodi lemba la 1 Yohane 2:20, 27 limasonyeza bwanji kuti odzozedwa sadalira anthu ena kuti awatsimikizire zoti adzozedwa?
8 Yehova amathandiza anthu odzozedwa kuti asamakayikire ngakhale pang’ono kuti asankhidwa kupita kumwamba. (Werengani 1 Yohane 2:20, 27.) N’zoona kuti Akhristu odzozedwa amafunika kuphunzitsidwa ndi Yehova mumpingo wake mofanana ndi Mkhristu wina aliyense. Koma sadalira anthu ena kuti awatsimikizire zoti adzozedwa. Zili choncho chifukwa Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake, womwe ndi wamphamvu kwambiri, kuti awatsimikizire kuti ndi odzozedwa.
‘AMABADWANSO’
9. Malinga ndi Aefeso 1:18, kodi chimasintha n’chiyani munthu akadzozedwa?
9 Atumiki a Yehova ambiri sangamvetse bwinobwino zimene zimachitika munthu akadzozedwa. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa iwo amakhala kuti sanadzozedwepo. Cholinga cha Mulungu polenga anthu chinali choti azikhala padzikoli osati kumwamba. (Gen. 1:28; Sal. 37:29) Koma wasankha anthu ena kuti adzakhale kumwamba. Choncho akadzoza munthu, amamusinthanso kwambiri maganizo ake moti munthuyo amayamba kuyembekezera kukakhala kumwamba.—Werengani Aefeso 1:18.
10. Kodi kubadwanso kumatanthauza chiyani? (Onani mawu am’munsi.)
10 Choncho munthu akadzozedwa ndi mzimu, ‘amabadwanso’ kapena kuti ‘amabadwa kuchokera kumwamba.’ * Yesu anasonyezanso kuti n’zovuta kufotokozera munthu amene sanadzozedwe zimene zimachitika munthu ‘akabadwanso’ kapena kuti ‘akabadwa mwa mzimu.’—Yoh. 3:3-8.
11. Kodi maganizo a munthu amasintha bwanji akadzozedwa?
11 Kodi munthu akadzozedwa maganizo ake amasintha bwanji? Yehova asanadzoze munthu, munthuyo amayembekezera ndi mtima wonse kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Amayembekezera kudzaona Mulungu atachotsa zoipa zonse n’kusintha dzikoli kuti likhale lokongola kwambiri. Mwina amayembekezeranso kudzaonana ndi anzake kapena achibale ake amene anamwalira. Koma akadzozedwa, maganizo ake amasinthiratu. Sikuti amangoyamba kuganiza kuti moyo wosatha padziko lapansi sungakhale wosangalatsa. Sasinthanso chifukwa chopanikizika ndi mavuto kapena nkhawa. Sikutinso amangoyamba kuganiza kuti moyo wapadzikoli udzakhala wotopetsa. M’malomwake, Yehova ndi amene amagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti asinthe maganizo a munthuyo komanso zimene amayembekezera.
12. Malinga ndi 1 Petulo 1:3, 4, kodi munthu akadzozedwa amamva bwanji?
12 Munthu amene wadzozedwa akhoza kuganiza kuti si woyenera kupatsidwa mwayi umenewu. Koma sakayikira ngakhale pang’ono zoti Mulungu wamusankha. Iye amasangalala kwambiri akaganizira zimene akuyembekezera ndipo amayamikira.—Werengani 1 Petulo 1:3, 4.
13. Kodi odzozedwa amamva bwanji akaganizira za moyo wawo padzikoli?
13 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti odzozedwawo amalakalaka atafa? Mtumwi Paulo anayankha funso limeneli. Iye anayerekezera thupi la munthu ndi msasa ndipo ananena kuti: “Ndipotu, ife amene tili mumsasa uno tikubuula chifukwa cholemedwa. Kwenikweni si chifukwa chofuna kuuvula, koma kuti tivale nyumba inayo, kuti chokhoza kufachi chilowedwe m’malo ndi moyo.” (2 Akor. 5:4) Akhristuwo sanyansidwa ndi moyo m’dzikoli n’kumafuna kufa msanga. Iwo amasangalala ndi moyo ndipo amafuna kuti tsiku lililonse azitumikira Yehova limodzi ndi mabanja awo komanso anzawo. Koma kaya akuchita zotani, saiwala zoti akuyembekezera zinthu zabwino kwambiri kumwamba.—1 Akor. 15:53; 2 Pet. 1:4; 1 Yoh. 3:2, 3; Chiv. 20:6.
KODI INUYO MWADZOZEDWA?
14. Kodi ndi zinthu ziti zimene sizisonyeza kuti munthu wadzozedwa?
14 Mwina mumadzifunsa ngati munadzozedwa kapena ayi. Ngati ndi choncho, mungachite bwino kuganizira mafunso ofunikawa: Kodi muli ndi mtima wofunitsitsa kutumikira Yehova? Kodi mumaona kuti mumachita khama kwambiri mu utumiki? Kodi mumaphunzira mwakhama Mawu a Mulungu ndipo mumakonda kwambiri kuphunzira “zinthu zozama za Mulungu”? (1 Akor. 2:10) Kodi mumaona kuti Yehova wakudalitsani kwambiri pa ntchito yolalikira? Kodi mumafunitsitsa kuthandiza ena kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova? Nanga kodi mwaona kuti Yehova wakuthandizani m’njira zosiyanasiyana pa moyo wanu? Ngati mwayankha kuti inde pa mafunso onsewa, kodi zimenezi zikusonyeza kuti ndinu wodzozedwa? Ayi. Zili choncho chifukwa zimenezi zikhoza kuchitikira atumiki a Mulungu onse, kaya ndi odzozedwa kapena ayi. Komanso Mulungu angapatse mtumiki wake aliyense mphamvu zofanana pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera, mosaganizira chiyembekezo chake. Ndipotu mukamakayikira ngati mwadzozedwa kapena ayi, kukayikirako ndi umboni wakuti simunadzozedwe. Anthu amene Yehova wawasankha sakayikira ngakhale pang’ono. Iwo amangodziwiratu kuti adzozedwa.
15. Kodi tikudziwa bwanji kuti si anthu onse amene anapatsidwa mzimu woyera omwe adzapite kumwamba?
15 M’Baibulo muli zitsanzo za anthu ambiri okhulupirika omwe anapatsidwa mzimu woyera, koma sankayembekezera kupita kumwamba. Mwachitsanzo, Davide ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera. (1 Sam. 16:13) Mzimuwo unkamuthandiza kumvetsa zinthu zozama zokhudza Yehova komanso kumutsogolera polemba mbali zina za Baibulo. (Maliko 12:36) Ngakhale zili choncho, mtumwi Petulo ananena kuti Davide “sanakwere kumwamba.” (Mac. 2:34) Nayenso Yohane M’batizi ‘anadzazidwa ndi mzimu woyera.’ (Luka 1:13-16) Yesu ananena kuti panalibe wamkulu kuposa Yohane koma iye sadzapita kumwamba. (Mat. 11:10, 11) Yehova anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera pothandiza anthuwo kuchita zinthu zikuluzikulu, koma sanagwiritse ntchito mzimu wake kuti awasankhe kupita kumwamba. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti sanali okhulupirika kwambiri poyerekezera ndi amene anasankhidwa kuti akalamulire kumwamba? Ayi. Zikungotanthauza kuti Yehova adzawaukitsa kuti adzakhale ndi moyo padzikoli.—Yoh. 5:28, 29; Mac. 24:15.
16. Kodi atumiki ambiri a Mulungu amasiku ano akuyembekezera zotani?
16 Atumiki a Yehova ambiri padzikoli sakuyembekezera kupita kumwamba. Mofanana ndi Abulahamu, Sara, Davide, Yohane M’batizi ndi enanso otchulidwa m’Baibulo, iwo amayembekezera kudzakhala padzikoli Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira.—Aheb. 11:10.
17. Kodi tidzakambirana mafunso ati munkhani yotsatira?
17 Popeza odzozedwa ena adakali padzikoli, tikhoza kukhala ndi mafunso ena. (Chiv. 12:17) Mwachitsanzo, kodi Akhristu odzozedwa ayenera kudziona bwanji? Ngati munthu wina mumpingo mwanu wayamba kudya zizindikiro pa Chikumbutso, kodi muyenera kutani? Nanga muyenera kudandaula ngati chiwerengero cha anthu amene amanena kuti ndi odzozedwa chikuwonjezekabe? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso amenewa.
^ ndime 5 Kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E., Yehova wakhala akupatsa Akhristu ena chiyembekezo chapadera chokalamulira ndi Mwana wake kumwamba. Koma kodi Akhristu amenewa amadziwa bwanji kuti apatsidwa mwayi woti adzapite kumwamba? Nanga chimachitika n’chiyani munthu akapatsidwa mwayi wapaderawu? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa ndipo mfundo zake zikugwirizana ndi zamunkhani imene inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya January 2016.
^ ndime 2 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Kudzozedwa ndi mzimu woyera: Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera kusankha munthu kuti akalamulire ndi Yesu kumwamba. Pogwiritsa ntchito mzimu wake, Mulungu amapatsa munthuyo “chikole” kapena kuti kumulonjeza zinthu zam’tsogolo. (Aef. 1:13, 14) Akhristu amenewa anganene kuti mzimu woyera “umachitira umboni,” kapena kuti kuwatsimikizira kuti mphoto yawo ili kumwamba.—Aroma 8:16.
^ ndime 5 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Chidindo. Munthu sadindidwa chidindo chomaliza mpaka atatsala pang’ono kufa adakali wokhulupirika kapena chisautso chachikulu chitatsala pang’ono kuyamba.—Aef. 4:30; Chiv. 7:2-4; onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya April 2016.
^ ndime 10 Kuti mumvetse tanthauzo la “kubadwanso,” onani Nsanja ya Olonda ya April 1, 2009, tsa. 3-12.
NYIMBO NA. 27 Ulemerero wa Ana a Mulungu Udzaonekera
^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Akhristu amene ali m’ndende chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira komanso amene amalalikira ndi kuphunzitsa anthu mwaufulu, amayembekezera kudzakhala padziko lapansi Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA