NKHANI YOPHUNZIRA 1
‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzira Anga’
LEMBA LA CHAKA CHA 2020: “Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza.”—MAT. 28:19.
NYIMBO NA. 79 Athandizeni Kukhala Olimba
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1-2. Kodi mngelo anauza azimayi ena kuti chiyani, nanga Yesu anawauza kuti chiyani?
M’MAWA wa pa Nisani 16 mu 33 C.E., azimayi ena oopa Mulungu anapita kumanda amene anaikamo thupi la Yesu Khristu. Limeneli linali tsiku lachiwiri chiikireni thupilo m’manda. Pa nthawiyi anali ndi chisoni ndipo anapita kuti akapake thupilo zonunkhiritsa. Koma atafika anadabwa kuona kuti m’mandamo munalibe thupi la Yesu. Ndiyeno mngelo ananena kuti Yesu wauka ndipo anawauza kuti: “Watsogola kupita ku Galileya. Kumeneko mukamuona.”—Mat. 28:1-7; Luka 23:56; 24:10.
2 Atangochoka kumandako, Yesu anawapeza n’kuwauza kuti: “Pitani, kauzeni abale anga, kuti apite ku Galileya ndipo akandiona kumeneko.” (Mat. 28:10) Chinthu choyamba chimene Yesu anachita atangoukitsidwa chinali kukonza zoti akumane ndi ophunzira ake. Apa n’zodziwikiratu kuti ankafuna kuwapatsa malangizo ofunika kwambiri.
KODI LAMULOLI ANALIPEREKA KWA NDANI?
3-4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu sanapereke lamulo la pa Mateyu 28:19, 20 kwa atumwi ake okha? (Onani chithunzi chapachikuto.)
3 Werengani Mateyu 28:16-20. Pamsonkhano umene Yesu anachita ndi ophunzira ake, iye ananena za ntchito yofunika imene ophunzirawo ankafunika kugwira, yomwe tikuigwiranso masiku ano. Iye anati: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”
4 Yesu amafuna kuti otsatira ake onse azilalikira. Lamuloli sanalipereke kwa atumwi ake okhulupirika 11 okha. Tikutero chifukwa chakuti pa nthawi imene Yesu ankapereka lamuloli paphiri lina la ku Galileya panalinso anthu ena osati atumwi okha. Paja mngelo anawauza azimayi aja kuti: “Mukamuona [ku Galileya].” Zimenezi zikusonyeza kuti azimayi okhulupirika analiponso pamsonkhanowo. Komanso mtumwi Paulo ananena kuti Yesu “anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi.” (1 Akor. 15:6) Kodi zimenezi zinachitika kuti?
5. Kodi tikuphunzira chiyani pa 1 Akorinto 15:6?
5 Pali zifukwa zomveka zotichititsa kuganiza kuti Paulo ankanena za msonkhano wa ku Galileya umene unatchulidwa m’chaputala 28 cha buku la Mateyu. Chifukwa choyamba n’chakuti ophunzira ambiri a Yesu anali ochokera ku Galileya. Choncho paphiri linalake la ku Galileya panali pabwino kuchitira msonkhano wa anthu ambiri kusiyana ndi kuchitira m’nyumba ya munthu ku Yerusalemu. Chifukwa chachiwiri n’chakuti Yesu ataukitsidwa, anali ataonekera kale kwa atumwi ake 11 m’nyumba ina ku Yerusalemu. Ngati iye akanafuna kuuza atumwi ake okha kuti azilalikira komanso kuphunzitsa anthu, akanachita zimenezi ku Yerusalemuko. Sakanawauza kuti akakumane ku Galileya limodzi ndi azimayi aja komanso anthu ena.—Luka 24:33, 36.
6. Kodi lemba la Mateyu 28:20 limasonyeza bwanji kuti lamulo loti tiziphunzitsa anthu limatikhudza masiku ano, nanga Akhristu akulitsatira bwanji?
6 Chifukwa chachitatu n’chakuti Yesu sanangopereka lamulo lija kwa Akhristu a m’nthawi ya atumwi okha. Tikutero chifukwa chakuti iye atapereka lamuloli, anamaliza ndi mawu akuti: “Ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Mogwirizana ndi mawu a Yesuwa, ntchito yophunzitsa anthu ikuyenda bwino kwambiri masiku ano. Tikutero chifukwa chakuti chaka chilichonse anthu pafupifupi 300,000 amabatizidwa n’kukhala ophunzira a Yesu Khristu.
7. Kodi tikambirana chiyani panopa, nanga n’chifukwa chiyani?
7 Anthu ambiri amene amaphunzira Baibulo amafika pobatizidwa. Koma zikuoneka kuti anthu ena amene timaphunzira nawo amachita mantha kuti akhale ophunzira a Yesu. Iwo amasangalala kuphunzira koma sasintha kuti afike pobatizidwa. Ngati mukuphunzira ndi munthu, n’zosachita kufunsa kuti mumafuna kumuthandiza kuti azitsatira zimene akuphunzirazo kuti akhale wophunzira wa Khristu. Munkhaniyi, tikambirana zimene tingachite kuti tizifika anthu pamtima n’kuwathandiza kuti akhale ophunzira a Yesu. N’chifukwa chiyani tiyenera kukambirana zimenezi? Zili choncho chifukwa mwina tingafunike kusankha kupitiriza kuphunzira ndi munthu kapena ayi.
MUZIYESETSA KUFIKA ANTHU PAMTIMA
8. N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta kuti tiwafike anthu pamtima?
8 Yehova amafuna kuti anthu azimutumikira chifukwa chomukonda. Choncho cholinga chathu n’chothandiza anthu kuzindikira kuti Yehova amawakonda kwambiri komanso amawafunira zabwino. Timafuna kuwathandiza kuzindikira kuti Yehova ndi “tate wa ana amasiye ndi woweruzira akazi amasiye milandu.” (Sal. 68:5) Anthu akazindikira kuti Yehova amawakonda akhoza kumva bwino ndipo angayambenso kumukonda kwambiri. Anthu ena zimawavuta kuona kuti Yehova ndi Bambo wawo wachikondi chifukwa chakuti sanasonyezedwe chikondi ndi bambo awo. (2 Tim. 3:1, 3) Choncho mukamaphunzira ndi anthu muzitsindika makhalidwe abwino a Yehova. Muziwathandiza kuzindikira kuti Mulungu amafuna kuti iwo adzapeze moyo wosatha ndipo angawathandize kuti zimenezi zitheke. Kodi tingachitenso chiyani powathandiza?
9-10. Kodi tizigwiritsa ntchito mabuku ati pophunzira ndi anthu, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito mabukuwo?
9 Muzigwiritsa ntchito buku lakuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa” ndi lakuti “Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?” Mabuku amenewa anakonzedwa m’njira yoti azitithandiza kuwafika pamtima anthu amene tikuphunzira nawo. Mwachitsanzo, mutu 1 m’buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa uli ndi mfundo izi: Kodi Mulungu amatiganizira kapena ndi wopanda chisoni?, Kodi Mulungu amamva bwanji akaona anthu akuvutika? ndiponso yakuti Yehova akhoza kukhala mnzanu. Pomwe buku lakuti Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani limathandiza munthu kudziwa kuti akamayendera mfundo za m’Baibulo pa moyo wake zinthu zimamuyendera bwino komanso amalimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova. Mwina munaphunzirapo mabukuwa ndi anthu ena, koma mungachite bwino kukonzekera musanakaphunzire ndi munthu aliyense n’kuganizira mmene mfundo zake zingamuthandizire.
10 Kodi mungatani ngati munthu akufuna kudziwa nkhani inayake imene imafotokozedwa bwino m’buku lina lomwe silili m’gulu la Zinthu Zophunzitsira? Mwina mungamuuze kuti akawerenge payekha bukulo n’cholinga choti mupitirize kuphunzira pogwiritsa ntchito mabuku amene tatchula aja.
11. Kodi tiyenera kuyamba liti kutsegula komanso kutseka phunziro ndi pemphero, nanga tingafotokozere bwanji munthu zimenezi?
11 Muziyamba phunziro ndi pemphero. Ngati n’zotheka, musamadikire kuti muphunzire kaye ndi munthu maulendo ambiri musanayambe kutsegula ndiponso kutseka phunziro ndi pemphero. Tiyenera kuthandiza anthu kuzindikira kuti timafunika mzimu wa Yehova kuti tizimvetsa Mawu ake. Abale ndi alongo ena amafotokoza kufunika kwa pemphero powerenga lemba la Yakobo 1:5 lomwe limati: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu.” Kenako amafunsa munthu amene akuphunzira naye kuti, “Kodi tingapemphe bwanji Mulungu kuti atipatse nzeru?” Anthu ambiri angayankhe kuti tiyenera kupemphera kwa iye.
12. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji Salimo 139:2-4 pothandiza munthu kuti azipemphera kuchokera mumtima?
12 Muziphunzitsa anthu kupemphera. Muziuza anthu kuti Yehova amafuna kumva mapemphero awo ochokera mumtima. Afotokozereni kuti tikamapemphera patokha tikhoza kuuza Yehova momasuka zimene zili mumtima mwathu zomwe sitingamasuke kuuza munthu wina. Paja Yehova amadziwa kale zonse zimene zili mumtima mwathu. (Werengani Salimo 139:2-4.) Tingauzenso munthu amene tikuphunzira naye kuti azipempha Yehova kuti amuthandize kusintha maganizo kapena makhalidwe olakwika. Tiyerekeze kuti munthu amene wakhala akuphunzira kwa nthawi yaitali akukondabe holide inayake imene Akhristu sayenera kukondwerera. Amadziwa kuti si yabwino koma pali zinthu zina zokhudza holideyo zimene zimamusangalatsa. Ndi bwino kumulimbikitsa kuti auze Yehova mmene akumvera komanso kumupempha kuti amuthandize kukonda zimene iye amakonda.—Sal. 97:10.
13. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuitanira anthu kumisonkhano mwamsanga? (b) Kodi tingathandize bwanji munthu kuti asachite chilendo kwambiri ku Nyumba ya Ufumu?
13 Muziwaitanira kumisonkhano mwamsanga. Zinthu zimene munthu angamve kapena kuona kumisonkhano yathu zikhoza kumuthandiza kwambiri. Mungamuonetse vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? kenako n’kumuitanira kumisonkhano. Ngati n’zotheka muuzeni kuti mudzapita kukamutenga. Zimakhala bwinonso kupita ndi ofalitsa osiyanasiyana pokaphunzira ndi munthuyo. Izi zimathandiza kuti adziwane ndi anthu amumpingo, moti sangachite chilendo kwambiri akafika kumisonkhano.
MUZITHANDIZA ANTHU KUTI AKULE MWAUZIMU
14. N’chiyani chingathandize munthu kuti akule mwauzimu?
14 Cholinga chathu ndi kuthandiza anthu kuti akule mwauzimu. (Aef. 4:13) Munthu akavomera kuphunzira, nthawi zambiri amaganizira mmene zinthu zimene akuphunzirazo zingamuthandizire iyeyo. Koma akayamba kukonda kwambiri Yehova, amayambanso kuganizira mmene angathandizire anthu ena, kuphatikizapo amumpingo. (Mat. 22:37-39) Pa nthawi yoyenera, tingamufotokozere kuti tili ndi mwayi wopereka ndalama zothandiza pa ntchito za Ufumu.
15. Kodi tingathandize bwanji munthu kudziwa zochita akakumana ndi mavuto?
15 Muzithandiza anthu kudziwa zimene angachite akakumana ndi mavuto. Tiyerekeze kuti mumaphunzira ndi wofalitsa wosabatizidwa ndipo wakuuzani kuti munthu wina mumpingo wamukhumudwitsa. M’malo moikira kumbuyo munthu mmodzi, mungachite bwino kumufotokozera zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. Paja limasonyeza kuti iye akhoza kungomukhululukira munthuyo, koma ngati sangakwanitse, akhoza kukambirana naye mwachikondi n’cholinga choti agwirizane. (Yerekezerani ndi Mateyu 18:15.) Muzimuthandiza kuti akonzekere zimene angakanene pokambirana ndi munthuyo. Muzimusonyeza mmene angagwiritsire ntchito JW Library®, Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani komanso jw.org® kuti apeze mfundo zothandiza. Akamaphunzira zambiri asanabatizidwe sadzavutika kugwirizana ndi anthu mumpingo akadzabatizidwa.
16. N’chifukwa chiyani tingachite bwino kutenga ofalitsa ena pokaphunzira ndi munthu?
16 Muzipempha anthu ena mumpingo, kuphatikizapo woyang’anira dera, kuti akhale nanu pa phunzirolo. Kuwonjezera pa zifukwa zimene tatchula kale, ofalitsa ena akhoza kuthandiza munthu amene mukuphunzira naye pa zinthu zimene inuyo simungakwanitse. Mwachitsanzo, mwina munthuyo wakhala akuyesetsa kuti asiye kusuta koma zikumuvuta. Mwina mungapite ndi wofalitsa amene anavutikanso kusiya koma anakwanitsa. N’kutheka kuti wofalitsayo angapereke malangizo omwe angathandize wophunzirayo. Ngati simungamasuke kuchititsa phunziro pali wofalitsa waluso mungamupemphe kuti achititse iyeyo. Mfundo ndi yakuti muzilola abale ndi alongo ena kuti azithandizanso munthuyo. Tizikumbukira kuti cholinga chathu ndi kuthandiza anthu kuti akule mwauzimu.
KODI NDISIYE KUPHUNZIRA NAYE?
17-18. Kodi muyenera kuganizira mfundo ziti musanasiye kuphunzira ndi munthu?
17 Ngati munthu amene tikuphunzira naye sakusintha moyo wake, tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndipitirize kuphunzira naye kapena ndimusiye?’ Musanasankhe zochita pa nkhaniyi muyenera kuganizira zimene munthuyo angakwanitse. Anthu ena amatenga nthawi yaitali kuti asinthe kusiyana ndi ena. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi munthuyu akuyesetsa kuchita zimene angathe? Kodi wayamba “kusunga,” kapena kuti kutsatira, zimene akuphunzira?’ (Mat. 28:20) N’zoona kuti anthu ena sangasinthe mwamsanga koma ayenera kusonyeza kuti akusintha.
18 Koma bwanji ngati munthu amene taphunzira naye kwa nthawi yaitali sakusonyeza kwenikweni kuti akuyamikira zimene amaphunzira? Tiyerekeze kuti munthu wamaliza kuphunzira buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa ndipo mwina wayamba kuphunzira buku la Mulungu Azikukondani koma sanapezekepo kumisonkhano kapena ku Chikumbutso. Komanso amakonda kupereka zifukwa zosamveka kuti musaphunzire. Zikatero, ndi bwino kukambirana naye mosapita m’mbali. *
19. Kodi mungakambirane bwanji ndi munthu amene akuoneka kuti sayamikira zimene akuphunzira, nanga zimenezi zingathandize bwanji?
19 Mungayambe ndi kumufunsa kuti, ‘Kodi kwenikweni chimene chingakulepheretseni kudzakhala wa Mboni za Yehova n’chiyani?’ Mwina angayankhe kuti, ‘Inetu kuphunzira ndilibe nako vuto, koma zoti ndingadzakhale wa Mboni za Yehova ndiye ayi.’ Ngati taphunzira ndi munthuyo kwa nthawi yaitali ndipo ali ndi maganizo amenewa, kodi ndi nzeru kupitiriza kuphunzira naye? Koma nthawi zina, munthu akhoza kutchula vuto linalake limene likumudetsa nkhawa. Mwachitsanzo, mwina amaona kuti sangakwanitse kulalikira kunyumba ndi nyumba. Mukadziwa zinthu ngati zimenezi mukhoza kumuthandiza moyenera.
20. Kodi lemba la Machitidwe 13:48 lingatithandize bwanji kudziwa ngati tiyenera kupitiriza kuphunzira ndi munthu kapena ayi?
20 N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena ali ngati Aisiraeli a m’nthawi ya Ezekieli. Yehova anauza Ezekieli kuti: “Kwa iwo uli ngati munthu woimba nyimbo zachikondi. Uli ngati munthu wa mawu anthetemya komanso wodziwa kuimba choimbira cha zingwe. Iwo adzamva ndithu mawu ako, koma palibe amene adzawatsatire.” (Ezek. 33:32) N’zoona kuti zimakhala zovuta kuuza munthu kuti tisiya kuphunzira naye. Koma tizikumbukira kuti “nthawi yotsalayi yafupika.” (1 Akor. 7:29) M’malo mokakamira kuphunzira ndi munthu amene sakusintha, ndi bwino kufufuza anthu ena amene akusonyeza kuti ‘ali ndi maganizo abwino owathandiza kukapeza moyo wosatha.’—Werengani Machitidwe 13:48.
21. Kodi lemba la chaka cha 2020 ndi liti, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti ndi loyenera
21 Lemba la chaka cha 2020 litithandiza kuti tiziyesetsa kuwonjezera luso lathu pophunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Lembali lili ndi mawu amene Yesu ananena pamsonkhano umene anachititsa paphiri lina ku Galileya akuti: “Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza.”—Mat. 28:19.
NYIMBO NA. 70 Fufuzani Anthu Oyenerera
^ ndime 5 Lemba la chaka cha 2020 likutilimbikitsa kuti ‘tiziphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira.’ Lamulo limeneli linaperekedwa kwa atumiki a Yehova onse. Koma kodi tingatani kuti tiziwafika pamtima anthu n’cholinga choti akhale ophunzira a Khristu? Nkhaniyi ifotokoza zimene tingachite kuti tithandize anthu amene timaphunzira nawo kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Tionanso zimene zingatithandize kudziwa ngati m’poyenera kupitiriza kuphunzira ndi munthu kapena ayi.
^ ndime 18 Onerani vidiyo ya pa JW Library® yakuti Kusiya Kuphunzira ndi Munthu Yemwe Sakupita Patsogolo.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA