NKHANI YOPHUNZIRA 3

Khamu Lalikulu la Nkhosa Zina Likutamanda Mulungu ndi Khristu

Khamu Lalikulu la Nkhosa Zina Likutamanda Mulungu ndi Khristu

“Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwana wa nkhosa.”​—CHIV. 7:10.

NYIMBO NA. 14 Tamandani Mfumu Yatsopano Yolamulira Dziko Lapansi

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi nkhani imene inakambidwa pamsonkhano wachigawo mu 1935, inathandiza bwanji wachinyamata wina?

BANJA lina la Ophunzira Baibulo, lomwe ndi dzina limene a Mboni za Yehova ankadziwika nalo pa nthawiyo, linali ndi ana aamuna atatu komanso aakazi awiri. Banjali linaphunzitsa ana awo kuti azitumikira Yehova Mulungu komanso kutsanzira Yesu Khristu. Mwana wawo wina wamwamuna anabatizidwa mu 1926 ali ndi zaka 18. Mofanana ndi mmene ankachitira Ophunzira Baibulo onse pa nthawiyo, wachinyamatayo ankadya nawo mkate komanso kumwa vinyo chaka chilichonse pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Komabe chiyembekezo chake chinasintha chifukwa cha nkhani yosaiwalika yamutu wakuti “Khamu Lalikulu.” Nkhaniyi inakambidwa ndi M’bale J. F. Rutherford pamsonkhano wachigawo womwe unachitika ku Washington, D.C. ku America mu 1935. Kodi Ophunzira Baibulo anaphunzira chiyani pamsonkhano umenewu?

2. Kodi ndi mfundo yosangalatsa iti yachoonadi imene M’bale Rutherford anafotokoza munkhani yake?

2 Munkhani yake M’bale Rutherford anafotokoza za “khamu lalikulu la anthu” lotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9. Pa nthawi imeneyo Ophunzira Baibulo ankaganiza kuti khamu lalikulu ndi gulu la anthu amene sanali okhulupirika kwenikweni poyerekeza ndi Akhristu odzozedwa koma nawonso adzapita kumwamba. M’bale Rutherford anagwiritsa ntchito malemba pofotokoza kuti a khamu lalikulu sadzapita kumwamba, koma ndi nkhosa zina za Khristu, * omwe ndi anthu amene adzapulumuke pa ‘chisautso chachikulu’ n’kudzakhala padzikoli mpaka kalekale. (Chiv. 7:14) Yesu analonjeza kuti: “Ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za khola ili, zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa. Zidzamva mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.” (Yoh. 10:16) Nkhosa zina zimenezi ndi a Mboni za Yehova okhulupirika amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. (Mat. 25:31-33, 46) Tiyeni tione mmene kumvetsa mfundo ya m’Baibulo imeneyi kunathandizira atumiki ambiri a Yehova kuphatikizapo m’bale wachinyamata tamutchula uja.​—Sal. 97:11; Miy. 4:18.

KUMVETSA MFUNDO YATSOPANO KUNATHANDIZA ANTHU AMBIRI

3-4. Pamsonkhano wachigawo wa mu 1935, kodi anthu ambiri anazindikira kuti ali ndi chiyembekezo chotani, nanga n’chifukwa chiyani?

3 Nthawi yosangalatsa inafika pamene M’bale Rutherford anapempha anthu omwe anasonkhanawo kuti: “Onse amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padzikoli aimirire.” M’bale wina yemwe analipo pamsonkhanowu ananena kuti pa anthu 20,000 omwe anasonkhanawo, anthu oposa 10,000 anaimirira. Kenako M’bale Rutherford anati: “Taonani, khamu lalikulu!” Atangotero, anthu onse pamsonkhanowo anafuula mosangalala. Anthu amene anaimirirawo anazindikira kuti Yehova sanawasankhe kuti adzapite kumwamba. Iwo anadziwa kuti sanadzozedwe ndi mzimu woyera wa Mulungu. Patsiku lotsatira la msonkhanowu, anthu 840 anabatizidwa ndipo ambiri mwa iwo anali a nkhosa zina.

4 Pambuyo pa nkhaniyi, wachinyamata tamutchula kumayambiriro uja ndi enanso ambiri anasiya kudya mkate komanso kumwa vinyo pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Ambiri anamva mofanana ndi mmene m’bale wina anafotokozera modzichepetsa kuti: “Ulendo womaliza umene ndinadya zizindikiro panali pa Chikumbutso cha mu 1935. Nkhani ya pamsonkhano uja inandithandiza kuzindikira kuti sindinadzozedwe ndi mzimu woyera wa Yehova kuti ndidzapite kumwamba. M’malomwake ndinkayembekezera kudzakhala padziko lapansi n’kudzagwira nawo ntchito yolikonza kuti likhale paradaiso.” (Aroma 8:16, 17; 2 Akor. 1:21, 22) Kuchokera nthawi imeneyo, khamu lalikulu likuwonjezereka, ndipo lakhala likugwira ntchito ndi Akhristu odzozedwa omwe adakali padzikoli.

5. Kodi Yehova amaona bwanji anthu amene amasiya kudya zizindikiro za pa Chikumbutso?

5 Kodi Yehova amaona bwanji anthu amene anasiya kudya zizindikiro za pa Chikumbutso pambuyo pa 1935? Nanga amaona bwanji Mkhristu wobatizidwa masiku ano amene amadya mkate komanso kumwa vinyo pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, koma kenako n’kuzindikira kuti sanadzozedwe ndi mzimu woyera? (1 Akor. 11:28) Ena amayamba kudya zizindikirozi chifukwa choti sakudziwa bwinobwino chiyembekezo chawo. Koma moona mtima akavomereza kuti amalakwitsa n’kusiya kudya komanso kupitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika, iye amawawerengera monga a nkhosa zina. Koma ngakhale kuti amasiya kudya mkate komanso kumwa vinyo, iwo amapezekabe pa Chikumbutso chifukwa amayamikira kwambiri zimene Yehova ndi Yesu anawachitira.

CHIYEMBEKEZO CHOSANGALATSA

6. Kodi Yesu analamula angelo kuti achite chiyani?

6 Popeza chisautso chachikulu chayandikira, zingakhale zolimbikitsa kuonanso zimene lemba la Chivumbulutso chaputala 7 limanena pankhani ya Akhristu odzozedwa komanso khamu lalikulu la nkhosa zina. Yohane anaona Yesu akulamula angelo kuti apitirize kugwira mphepo zinayi zoononga. Iwo ankafunika kugwira mphepozi kuti zisaombe padziko lapansi kufikira Akhristu onse odzozedwa atadindidwa chidindo, kutanthauza kuvomerezedwa komaliza ndi Yehova. (Chiv. 7:1-4) Yohane anaona abale ake a Khristu odzozedwawa akulandira mphoto chifukwa cha kukhulupirika kwawo n’kukhala mafumu ndi ansembe limodzi ndi Yesu kumwamba. (Chiv. 20:6) Yehova, Yesu komanso angelo onse adzasangalala kuona Akhristu odzozedwa okwana 144,000 akulandira mphoto yawo kumwamba.

A khamu lalikulu avala mikanjo yoyera, anyamula nthambi za kanjedza m’manja mwawo ndipo aimirira pamaso pa mpando wachifumu wa ulemelero wa Mulungu komanso pamaso pa Mwanawankhosa (Onani ndime 7)

7. Mogwirizana ndi Chivumbulutso 7:9, 10, kodi Yohane anaona ndani m’masomphenya, nanga ankachita chiyani? (Onani chithunzi chapachikuto.)

7 Pambuyo pofotokoza za mafumu ndi ansembe 144,000 amenewa, Yohane anaona chinthu china chosangalatsa. Iye anaona “khamu lalikulu” lomwe lidzapulumuke pa Aramagedo. Mosiyana ndi gulu loyamba lija, gulu lachiwirili linali ndi anthu ambiri komanso osawerengeka. (Werengani Chivumbulutso 7:9, 10.) Iwo anali “atavala mikanjo yoyera,” kutanthauza kuti anali ‘opanda banga’ m’dziko la Satanali ndipo anali okhulupirika kwa Mulungu ndi Khristu. (Yak. 1:27) Anthuwa ankafuula kuti apulumutsidwa chifukwa cha zimene Yehova ndi Yesu, yemwe ndi Mwanawankhosa wa Mulungu, anachita. Komanso iwo anali atanyamula nthambi za kanjedza m’manja mwawo, kutanthauza kuti amavomereza mosangalala kuti Yesu ndi Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu.​—Yerekezerani ndi Yohane 12:12, 13.

8. Kodi lemba la Chivumbulutso 7:11, 12, limatiuza chiyani za banja la Yehova la kumwamba?

8 Werengani Chivumbulutso 7:11, 12. Kodi angelo anatani ataona khamu lalikulu? Yohane anaona banja lakumwamba la Yehovali likusangalala komanso likutamanda Mulungu. Yehova, Yesu, angelo komanso Akhristu odzozedwa adzasangalala kwambiri kuona masomphenyawa akukwaniritsidwa pamene khamu lalikulu lidzapulumuke pa chisautso chachikulu.

9. Mogwirizana ndi Chivumbulutso 7:13-15, kodi a khamu lalikulu akuchita chiyani panopa?

9 Werengani Chivumbulutso 7:13-15. Yohane analemba kuti a khamu lalikulu anali ‘atachapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.’ Zimenezi zikutanthauza kuti iwo ali ndi chikumbumtima choyera komanso Yehova amasangalala nawo. (Yes. 1:18) Iwowa ndi Akhristu odzipereka omwe anabatizidwa komanso amakhulupirira kwambiri nsembe ya Yesu ndipo ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Yoh. 3:36; 1 Pet. 3:21) N’chifukwa chake Yehova amasangalala nawo ndipo iwo amamuchitira “utumiki wopatulika usana ndi usiku” pano padziko lapansi. Panopa iwo amagwira mwakhama ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa za Ufumu chifukwa amaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri.​—Mat. 6:33; 24:14; 28:19, 20.

A nkhosa zina akusangalala atapulumuka pa chisautso chachikulu (Onani ndime 10)

10. Kodi a khamu lalikulu ndi otsimikiza za chiyani, nanga ndi lonjezo liti limene adzaone likukwaniritsidwa?

10 A khamu lalikulu omwe adzapulumuke pa chisautso chachikulu, ndi otsimikiza kuti Mulungu adzapitiriza kuwasamalira chifukwa “wokhala pampando wachifumuyo, adzatambasulira hema wake pamwamba pawo kuti awateteze.” Lonjezo la Mulungu limene takhala tikuliyembekezera kwa nthawi yaitali lidzakwaniritsidwa. Lonjezoli limati: Iye “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”​—Chiv. 21:3, 4.

11-12. (a) Mogwirizana ndi Chivumbulutso 7:16, 17, kodi a khamu lalikulu akuyembekezera madalitso otani? (b) Kodi a nkhosa zina amachita chiyani pa Chikumbutso, nanga n’chifukwa chiyani?

11 Werengani Chivumbulutso 7:16, 17. Panopa atumiki ena a Yehova akuvutika ndi njala chifukwa chosowa ndalama zogulira chakudya. Akuvutikanso ndi ziwawa zimene zikuchitika m’mayiko awo komanso nkhondo. Ndiponso ena ali m’ndende chifukwa cha zimene amakhulupirira. Komabe a khamu lalikulu amasangalala chifukwa chodziwa kuti akadzapulumuka, adzakhala ndi chakudya cha mwanaalirenji komanso azidzalandira malangizo ambiri kuchokera kwa Yehova. Yehova akamadzawononga dziko loipa la Satanali, adzateteza a khamu lalikulu ku mkwiyo wake wotentha womwe adzausonyeze pamitundu ya anthu. Chisautso chachikulu chikadzatha, Yesu adzatsogolera onse opulumuka ku “madzi a moyo” wosatha. Tangoganizani, a khamu lalikulu akuyembekezera zinthu zosangalatsa kwambiri. Pa anthu mabiliyoni omwe akhalapo ndi moyo padzikoli, anthu amene adzapulumuke pa chisautso chachikuluwa akhoza kudzakhala ndi moyo mpaka kalekale.​—Yoh. 11:26.

12 A nkhosa zina akuyembekezera zinthu zabwino kwambiri ndipo amathokoza Yehova ndi Yesu chifukwa cha zimenezi. Ngakhale kuti Yehova sanawasankhe kuti akakhale ndi moyo kumwamba, iye amawakonda monga mmene amakondera Akhristu odzozedwa. Magulu onse awiriwa amatamanda Mulungu ndi Khristu. Njira imodzi imene amachitira zimenezi ndi kupezeka pa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye.

MUZITAMANDA MULUNGU NDI KHRISTU PA CHIKUMBUTSO

Mkate ndi vinyo zimene zimayendetsedwa pa Chikumbutso zimatikumbutsa kuti Yesu anatifera kuti tidzapeze moyo (Onani ndime 13-15)

13-14. N’chifukwa chiyani tonsefe tiyenera kupezeka pamwambo wokumbukira imfa ya Khristu?

13 M’zaka zaposachedwapa m’mipingo yambiri, pa anthu 1,000 alionse amene apezeka pa Chikumbutso, pamakhala munthu mmodzi kapenanso sipakhala aliyense wodya mkate kapena kumwa vinyo. Izi zikusonyeza kuti anthu ambiri amene amapezeka pa Chikumbutso ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi. Ndiye n’chifukwa chiyani anthu amenewa amapezeka pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye? Chifukwa chimene amapezekera pamwambowu n’chofanana ndi chimene anthu amapezekera paukwati wa mnzawo. Anthu amapezeka paukwati chifukwa chofuna kuthandiza komanso kusonyeza kuti amakonda anthu amene akukwatiranawo. Mofanana ndi zimenezi, a nkhosa zina amapezeka pa Chikumbutso chifukwa chofuna kuthandiza komanso kusonyeza kuti amakonda Khristu ndi odzozedwa. Iwo amapezekanso pamwambowu posonyeza kuti amayamikira kwambiri nsembe ya Yesu yomwe inathandiza kuti adzakhale ndi moyo wosatha padzikoli.

14 Chifukwa china chimene chimapangitsa a nkhosa zina kupezeka pamwambo wa Chikumbutso ndi chakuti amafuna kumvera lamulo la Yesu. Pamene Yesu ankayambitsa mwambo wapaderawu limodzi ndi atumwi ake okhulupirika, anawauza kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (1 Akor. 11:23-26) Choncho a nkhosa zina adzapitirizabe kuchita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye pa nthawi yonse imene odzozedwa adzakhale adakali ndi moyo padzikoli. Ndipotu iwo amaitanira ena kuti adzakhale nawo pamwambo wa Chikumbutso.

15. Kodi tingatamande bwanji Mulungu ndi Khristu pamwambo wa Chikumbutso?

15 Pamwambo wa Chikumbutso timakhala ndi mwayi wotamanda Mulungu ndi Khristu poimba nyimbo komanso kupemphera. Chaka chino, nkhani ya Chikumbutso ili ndi mutu wakuti “Muziyamikira Zimene Mulungu ndi Khristu Akuchitirani.” Nkhaniyi idzatithandiza kuti tiziyamikira kwambiri Yehova ndi Khristu. Mkate ndi vinyo zikamadzayendetsedwa zidzatithandiza kuganizira zimene zizindikirozi zimaimira, zomwe ndi thupi komanso magazi a Yesu. Zidzatithandiza kukumbukira kuti Yehova analola kuti Mwana wake atifere n’cholinga choti tidzapeze moyo. (Mat. 20:28) Aliyense amene amakonda Atate wathu wakumwamba limodzi ndi Mwana wake, adzayesetsa kuti apezeka pamwambo wa Chikumbutsowu.

MUZIYAMIKIRA YEHOVA CHIFUKWA CHA CHIYEMBEKEZO CHIMENE ANAKUPATSANI

16. Kodi odzozedwa ndi a nkhosa zina amafanana munjira ziti?

16 Si kuti Mulungu amaona kuti odzozedwa ndi osiyana ndi a nkhosa zina. Iye amawakonda onsewa ndipo amaona kuti ndi amtengo wapatali. Ndipotu iye anawagula onsewo pamtengo wofanana, womwe ndi moyo wa Mwana wake wokondedwa. Kusiyana kumene kulipo pakati pa magulu awiriwa ndi kwakuti ali ndi chiyembekezo chosiyana. Koma onse amafunika kupitirizabe kukhala okhulupirika kwa Mulungu ndi Khristu. (Sal. 31:23) Ndipo tizikumbukira kuti mzimu woyera wa Mulungu umagwira ntchito mofanana kwa tonsefe. Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova amapereka mzimu wake woyera kwa aliyense mogwirizana ndi mmene akufunikira.

17. Kodi odzozedwa omwe adakali padziko lapansi akuyembekezera chiyani?

17 Akhristu odzozedwa sabadwa ali ndi chiyembekezo chopita kumwamba. Mulungu ndi amene amawapatsa chiyembekezochi. Iwo amaganizira za chiyembekezo chawochi, kuchipempherera, komanso amakhala ofunitsitsa kukalandira mphoto yawo kumwamba. Iwo sadziwa n’komwe kuti adzakhala ndi matupi otani akadzapita kumwambako. (Afil. 3:20, 21; 1 Yoh. 3:2) Ngakhale zili choncho, amayembekezera kudzakumana ndi Yehova, Yesu, angelo komanso odzozedwa onse n’kukakhala nawo limodzi mu Ufumu wakumwamba.

18. Kodi a nkhosa zina akuyembekezera chiyani?

18 A nkhosa zina mwachibadwa amasangalala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padzikoli. (Mlal. 3:11) Iwo amayembekezera mwachidwi nthawi imene adzathandize kukonza dziko lonse lapansi kukhala paradaiso. Amalakalaka nthawi imene adzamange nyumba, kulima minda komanso kulera ana awo ali angwiro. (Yes. 65:21-23) Akuyembekezeranso kudzapita malo osiyanasiyana padzikoli kukaona mapiri, nkhalango, nyanja komanso kuphunzira zinthu zonse zimene Yehova analenga. Koposa zonse, a nkhosa zina amasangalala kwambiri kudziwa kuti adzapitirizabe kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.

19. Kodi mwambo wa Chikumbutso umatipatsa mwayi wochita chiyani, nanga uchitika liti chaka chino?

19 Yehova wapereka chiyembekezo chabwino cham’tsogolo kwa mtumiki wake aliyense wodzipereka. (Yer. 29:11) Mwambo wokumbukira imfa ya Khristu umatipatsa tonsefe mwayi waukulu wotamanda Mulungu ndi Khristu chifukwa cha zimene anatichitira n’cholinga choti tidzasangalale ndi moyo wosatha. Mpake kuti mwambo wa Chikumbutso umakhala wapadera kwambiri kwa Akhristu chaka chilichonse. Chaka chino mwambowu udzachitika Loweruka pa 27 March 2021, dzuwa litalowa. Anthu ambiri akukhala m’madera amene kuli mtendere ndipo n’zosavuta kupezeka pamwambo wofunikawu. Pomwe ena adzapezeka pamwambowu ngakhale kuti amatsutsidwa. Ndiponso ena adzachita mwambo umenewu ali m’ndende. Pamene Yehova, Yesu, angelo ndi odzozedwa omwe ali kumwamba azidzaonerera, tikukufunirani zabwino zonse monga mpingo, kagulu komanso aliyense payekhapayekha pamene mukuchita mwambo wa Chikumbutsowu.

NYIMBO NA. 150 Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke

^ ndime 5 Tsiku la 27 March 2021, lidzakhala lapadera kwambiri kwa Mboni za Yehova. Madzulo a tsiku limeneli tidzachita mwambo wokumbukira imfa ya Khristu. Anthu ambiri amene adzapezeke pamwambowu ndi amene Yesu anawatchula kuti a “nkhosa zina.” Kodi mu 1935, a Mboni za Yehova anadziwa mfundo yachoonadi iti? Kodi a nkhosa zina akuyembekezera kudzasangalala ndi zinthu ziti pambuyo pa chisautso chachikulu? Nanga amatamanda bwanji Mulungu ndi Khristu akapezeka pamwambo wa Chikumbutso?

^ ndime 2 MATANTHAUZO A MAWU ENA: Nkhosa zina ndi anthu omwe amatsatira Khristu ndipo akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padzikoli. Ena mwa anthu amenewa anayamba kutumikira Mulungu m’masiku otsiriza. Khamu lalikulu ndi a nkhosa zina amene adzakhale ndi moyo pa nthawi imene Khristu azidzaweruza anthu pa chisautso chachikulu. Ndipo anthu amenewa adzapulumuka pa chisautso chachikulucho.