NKHANI YOPHUNZIRA 4

Pitirizani Kusonyezana Chikondi Chenicheni

Pitirizani Kusonyezana Chikondi Chenicheni

“Pokonda abale, khalani ndi chikondi chenicheni.”—AROMA 12:10.

NYIMBO NA. 109 Tizikondana Kwambiri Kuchokera Mumtima

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti m’mabanja ambiri mulibe chikondi?

BAIBULO linaneneratu kuti m’masiku otsiriza, anthu adzakhala “osakonda achibale awo.” (2 Tim. 3:1, 3) Masiku ano timaona ulosi umenewu ukukwaniritsidwa. Mwachitsanzo, anthu ambiri amathetsa mabanja awo ndipo makolo amakwiyirana. Zimenezi zimachititsa kuti ana aziona kuti sakukondedwa. Ngakhale anthu a banja limodzi omwe akukhala nyumba imodzi, nthawi zina akhoza kumaonana ngati alendo. Mlangizi wina wa mabanja ananena kuti: “M’mabanja ambiri amayi, abambo ndi ana sachitira zinthu limodzi. Iwo amathera nthawi yambiri pa kompyuta, tabuleti, foni kapenanso masewera a pakompyuta.” Choncho ngakhale kuti amakhala nyumba imodzi, anthuwa sadziwana bwino.

2-3. (a) Mogwirizana ndi Aroma 12:10, kodi ndi ndani amene tiyenera kuwasonyeza chikondi chenicheni? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Ife sitikufuna kukhala ngati anthu a m’dzikoli omwe alibe chikondi. (Aroma 12:2) M’malomwake, tiyenera kusonyeza chikondi chenicheni osati kwa achibale athu okha, koma tiyenera kumasonyezanso chikondichi kwa abale ndi alongo athu mumpingo. (Werengani Aroma 12:10.) Kodi mawu akuti chikondi chenicheni amatanthauza chiyani? Mawu amenewa amanena za kugwirizana komwe kumakhalapo pakati pa anthu a banja limodzi. Chimenechi ndi chikondi chimene tiyenera kusonyezanso kwa abale ndi alongo athu mumpingo. Tikamasonyeza chikondi chenicheni zimathandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana ndipo timatumikira Yehova limodzi mosangalala.​—Mika 2:12.

3 Kuti tipitirize kusonyeza chikondi chimenechi, tiyeni tione zimene tingaphunzire pa zitsanzo za anthu otchulidwa m’Baibulo.

YEHOVA NDI MULUNGU “WACHIKONDI CHACHIKULU”

4. Kodi lemba la Yakobo 5:11, likutithandiza bwanji kudziwa kuti Yehova amatikonda kwambiri?

4 Baibulo limatifotokozera makhalidwe abwino amene Yehova ali nawo. Mwachitsanzo, limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:8) Kudziwa zimenezi kumatithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi. Koma Baibulo limanenanso kuti Yehova ndi “wachikondi chachikulu.” (Werengani Yakobo 5:11.) Mawu amenewa akutithandiza kudziwa kuti Yehova amatikonda kwambiri.

5. Kodi Yehova amasonyeza bwanji chifundo, nanga tingamutsanzire bwanji?

5 Lemba la Yakobo 5:11, latchula za chikondi chachikulu cha Yehova komanso khalidwe lina limene limatithandiza kukhala naye pa ubwenzi, lomwe ndi chifundo. (Eks. 34:6) Njira imodzi imene Yehova amatisonyezera chifundo ndi kutikhululukira zimene timalakwitsa. (Sal. 51:1) M’Baibulo, kusonyeza chifundo kumaphatikizapo zambiri osati kungokhululukira chabe munthu amene watilakwira. Chifundo ndi khalidwe limene limasonyeza mmene timamvera mumtima tikaona munthu wina akuvutika, ndipo khalidweli limatipangitsa kuti tiyesetse kumuthandiza. Yehova amafotokoza kuti mmene amamvera pofuna kutithandiza zimaposa mmene mayi amamvera pofuna kuthandiza mwana wake. (Yes. 49:15) Tikakhala pa mavuto chifundo cha Yehova chimamuchititsa kuti atithandize. (Sal. 37:39; 1 Akor. 10:13) Tingasonyeze chifundo kwa abale ndi alongo athu tikamawakhululukira komanso tikamapewa kusunga chakukhosi akatilakwira. (Aef. 4:32) Koma njira yaikulu imene tingasonyezere chifundo kwa abale ndi alongo ndi kuwathandiza pamene akumana ndi mavuto. Tikamasonyeza ena chifundo chifukwa chowakonda timakhala tikutsanzira Yehova, yemwe ali ndi chikondi chachikulu kuposa aliyense.​—Aef. 5:1.

“YONATANI ANAGWIRIZANA KWAMBIRI NDI DAVIDE”

6. Kodi Yonatani ndi Davide anasonyeza bwanji kuti ankakondana kwambiri?

6 Baibulo limatifotokozera nkhani za anthu amene ankakondana kwambiri. Taganizirani chitsanzo cha Yonatani ndi Davide. Baibulo limati: “Yonatani anagwirizana kwambiri ndi Davide, moti anayamba kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera yekha.” (1 Sam. 18:1) Yehova anali atasankha Davide kuti adzakhale mfumu m’malo mwa Sauli. Zitatero Sauli anayamba kuchitira nsanje Davide ndipo ankafuna kumupha. Koma Yonatani sanafune kuthandiza bambo ake pofuna kukwaniritsa cholinga chawo chofuna kupha Davide. M’malomwake iye analonjezana ndi Davide kuti adzapitiriza kukhala mabwenzi komanso kuti nthawi zonse azithandizana.​—1 Sam. 20:42.

Yonatani ndi Davide ankakondana kwambiri ngakhale kuti Yonatani anali wamkulu kuposa Davide (Onani ndime 6-9)

7. Kodi ndi chinthu chimodzi chiti chimene chikanalepheretsa Yonatani ndi Davide kuti akhale mabwenzi?

7 N’zochititsa chidwi kuti Yonatani ndi Davide ankagwirizana kwambiri ngakhale kuti panali zinthu zambiri zimene zikanawalepheretsa kuti akhale mabwenzi. Mwachitsanzo, Yonatani ankasiyana ndi Davide ndi zaka pafupipafupi 30. Iye akanatha kuganiza kuti sangakhale mnzake wa munthu amene ndi wamng’ono kwa iye komanso alibe luso lililonse pamoyo. Koma sanaganize zimenezi ndipo ankamulemekeza kwambiri Davide.

8. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Yonatani anali mnzake wabwino wa Davide?

8 Yonatani akanatha kuchitira nsanje Davide. Monga mwana wa Mfumu Sauli, iye akanatha kuganiza kuti ndiye anali woyenerera kukhala mfumu m’malo mwa bambo ake. (1 Sam. 20:31) Koma Yonatani anali wodzichepetsa ndipo anali wokhulupirika kwa Yehova. Iye anagwirizana kwambiri ndi zimene Yehova anasankha kuti Davide adzakhale mfumu. Komanso iye anali wokhulupirika kwa Davide ngakhale kuti zimenezi zinakwiyitsa kwambiri bambo ake Sauli.​—1 Sam. 20:32-34.

9. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yonatani sankachitira nsanje Davide? Fotokozani.

9 Yonatani ankakonda kwambiri Davide ndipo sankamuchitira nsanje. Iye anali katswiri woponya mivi komanso msilikali wolimba mtima. Yonatani ndi bambo ake Sauli ankadziwika kuti “anali aliwiro kuposa chiwombankhanga” komanso “amphamvu kuposa mikango.” (2 Sam. 1:22, 23) Choncho Yonatani akanatha kumadzikweza chifukwa cha luso limene anali nalo. Komabe Yonatani sankachita zinthu mwampikisano kapena kuchita nsanje chifukwa cha zabwino zimene Davide anachita. M’malomwake iye ankasirira kulimba mtima kwa Davide komanso kudalira kwake Yehova. Ndipotu panali pambuyo poti Davide wapha Goliati pamene Yonatani anayamba kumukonda kwambiri. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda abale ndi alongo athu ngati mmene Yonatani ankakondera Davide?

KODI TINGASONYEZE BWANJI CHIKONDI CHENICHENI MASIKU ANO?

10. Kodi mawu akuti ‘kukondana kwambiri kuchokera mumtima’ amatanthauza chiyani?

10 Baibulo limatiuza kuti ‘tizikondana kwambiri kuchokera mumtima.’ (1 Pet. 1:22) Yehova amatipatsa chitsanzo pankhaniyi. Iye amatikonda kwambiri, moti ngati titapitirizabe kukhala okhulupirika palibe chimene chingachititse kuti asiye kutikonda. (Aroma 8:38, 39) Mawu akuti ‘kukondana kwambiri’ akutichititsa kuganiza za munthu amene akuyesetsa kuchita zinthu zosonyeza kuti amakonda ena. Nthawi zina zingamativute kusonyeza chikondi kwa abale ndi alongo athu. Ena akatikhumudwitsa tiyenera kupitirizabe ‘kulolerana m’chikondi, tiziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu pokhala mwamtendere, umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa. Umodziwo timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera.’ (Aef. 4:1-3) Tikamayesetsa ‘kukhala mwamtendere’ ndi abale ndi alongo athu sitidzaganizira kwambiri zimene amalakwitsa. M’malomwake tidzayesetsa kuti tiziwaona mmene Yehova amawaonera.​—1 Sam. 16:7; Sal. 130:3.

Paulo anauza Eodiya ndi Suntuke kuti azigwirizana. Nthawi zina ifenso zingamativute kuti tizigwirizana ndi abale ndi alongo athu (Onani ndime 11)

11. N’chifukwa chiyani nthawi zina zingativute kusonyeza chikondi kwa abale ndi alongo athu?

11 Nthawi zina zimakhala zovuta kusonyeza chikondi chenicheni kwa abale ndi alongo athu makamaka ngati tikudziwa zimene amalakwitsa. Ndipo limeneli ndi vuto limene Akhristu ena anali nalo mu nthawi ya atumwi. Mwachitsanzo, Eodiya ndi Suntuke ayenera kuti sankavutika ‘kugwira ntchito yolengeza uthenga wabwino ndi [Paulo]’. Koma pazifukwa zina awiriwa zinkawavuta kuti azigwirizana. Choncho Paulo anawalimbikitsa “kuti akhale amaganizo amodzi mwa Ambuye.”​—Afil. 4:2, 3.

Akulu achinyamata ndi achikulire angathe kukhala mabwenzi a pamtima (Onani ndime 12)

12. Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri abale ndi alongo athu?

12 Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri abale ndi alongo athu? Tikamawadziwa bwino abale ndi alongo athu, zimakhala zosavuta kuti tiziwamvetsa komanso kuti tiyambe kuwakonda kwambiri. Tikhoza kukhala nawo pa ubwenzi posatengera msinkhu wawo kapena chikhalidwe chawo. Kumbukirani kuti Yonatani ankasiyana ndi Davide ndi zaka pafupifupi 30, komabe iye ankamuona ngati mnzake wa pamtima. Kodi mumpingo mwanu muli wina wake yemwe ndi wamkulu kapena wamng’ono kuposa inuyo amene akhoza kukhala mnzanu? Mukamayesetsa kuti aliyense akhale mnzanu mungasonyeze kuti ‘mumakonda gulu lonse la abale.’​—1 Pet. 2:17.

Onani ndime 12 *

13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti n’zosatheka kuti aliyense mumpingo akhale mnzathu wa pamtima?

13 Tikamayesetsa kukonda abale ndi alongo athu, kodi zikutanthauza kuti aliyense mumpingo adzakhala bwenzi lathu la pamtima? Ayi, zimenezi sizingatheke. Sikulakwa kugwirizana ndi anthu ena kuposa ena chifukwa choti mwina timakonda zinthu zofanana. Yesu anatchula atumwi ake onse kuti “mabwenzi,” koma iye ankakonda kwambiri Yohane. (Yoh. 13:23; 15:15; 20:2) Komabe si kuti Yesu ankachita naye zinthu momukondera. Mwachitsanzo, pamene Yohane ndi m’bale wake Yakobo anapempha kuti akakhale ndi malo apamwamba mu Ufumu wa Mulungu, Yesu anawauza kuti: “Kunena zokhala kudzanja langa lamanja kapena lamanzere, si ine wopereka mwayi umenewo.” (Maliko 10:35-40) Mofanana ndi Yesu ifenso tiyenera kupewa kuchita zinthu mokondera anzathu a pamtima. (Yak. 2:3, 4) Kuchita zinthu mokondera kungachititse kuti anthu mumpingo asamagwirizane.​—Yuda 17-19.

14. Mogwirizana ndi Afilipi 2:3, kodi n’chiyani chingatithandize kupewa mpikisano mumpingo?

14 Tikamakonda kwambiri abale ndi alongo athu timathandiza kuti mumpingo musakhale mpikisano. Kumbukirani kuti Yonatani sanachitire nsanje Davide kapena kumuona monga munthu amene akulimbirana naye mpando wachifumu. Tonsefe tingathe kutsanzira Yonatani. Musamachitire nsanje abale ndi alongo anu chifukwa cha luso limene ali nalo, koma muzichita zinthu modzichepetsa “ndi kuona ena kukhala okuposani.” (Werengani Afilipi 2:3.) Muzikumbukira kuti aliyense wa ife akhoza kuchita zinazake zothandiza mumpingo. Tikakhala odzichepetsa tidzaona zabwino zimene abale ndi alongo athu amachita ndipo tingaphunzire zambiri pa chitsanzo chawo chokhalabe okhulupirika.​—1 Akor. 12:21-25.

15. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Tanya ndi anthu a m’banja lake?

15 Tikakumana ndi mavuto Yehova amatitonthoza komanso kutithandiza mwachikondi pogwiritsa ntchito abale ndi alongo athu. Taganizirani zimene zinachitikira banja lina ku America. Banjali linapita kumsonkhano wa mayiko wa mu 2019 wamutu wakuti “Chikondi Sichitha.” Mayi wa m’banjali dzina lake Tanya anafotokoza zimene zinachitika Loweruka akuchokera kumsonkhanowo. Iye anati: “Tikubwerera ku hotelo komwe tinafikira galimoto ina inachoka kumbali yake n’kubwera kumbali yathu, n’kuwomba galimoto yathu. Palibe anavulala, koma titatsika m’galimoto yathu tinangoima pamsewu titasokonezeka maganizo. Kenako tinaona munthu wina kumbali ina ya msewuwo akutiitana kuti tikalowe m’galimoto yake. Munthuyo anali m’bale ndipo nayenso anali akuchokera kumsonkhano. Koma si m’bale yekhayu amene anaima. Alendo enanso 5 ochokera ku Sweden omwe anabwera pamsonkhanowu nawonso anaima. Alongo anatihaga ndi mwana wanga wamkazi zomwe zinachititsa kuti timveko bwino. Tinawatsimikizira abale ndi alongowa kuti akhoza kumapita koma sanalole kutisiya tokha. Iwo anakhala nafe mpaka pamene achipatala anafika ndipo anaonetsetsa kuti tili ndi zonse zomwe tinkafunikira. Panthawi yonse yovutayi tinaona kuti Yehova amatikonda. Zimene zinachitikazi zinatithandiza kuti tizikonda kwambiri abale ndi alongo athu komanso kuti tizikonda ndi kuyamikira kwambiri Yehova. Kodi inunso mukukumbikira nthawi ina pamene munkafunikira thandizo ndipo abale ndi alongo anakusonyezani chikondi chachikulu?

16. Kodi tili ndi zifukwa ziti zotichititsa kukonda kwambiri abale ndi alongo athu?

16 Taganizirani zinthu zabwino zimene zimachitika tikamakondana kwambiri. Timalimbikitsa abale ndi alongo athu tikamawathandiza akakumana ndi mavuto. Timathandiza abale ndi alongo athu kuti azisangalala potumikira Yehova mogwirizana. Timasonyeza kuti ndife ophunzira a Yesu ndipo zimenezi zimachititsa anthu a maganizo abwino kuti ayambe kutumikira Yehova. Koposa zonse timalemekeza Yehova yemwe ndi “Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” (2 Akor. 1:3) Tiyeni tonse titsimikize mtima kupitirizabe kukonda kwambiri abale ndi alongo athu.

NYIMBO NA. 130 Muzikhululuka

^ ndime 5 Yesu ananena kuti ophunzira ake adzadziwika ngati amasonyezana chikondi pakati pawo. Tonsefe timayesetsa kuti tizisonyeza ena chikondi. Tiyenera kuphunzira kukonda abale ndi alongo athu mmene timakondera achibale athu enieni. Nkhani ino itithandiza kukulitsa komanso kupitirizabe kusonyeza chikondi chenicheni kwa abale ndi alongo athu mumpingo.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mkulu wachinyamata akuphunzira zambiri kuchokera kwa mkulu wachikulire yemwe wamuitanira kunyumba kwake. Mabanja awiriwa akusonyeza kuti amakondana komanso kucherezana.