NKHANI YOPHUNZIRA 4

Chifukwa Chake Timapezeka pa Chikumbutso

Chifukwa Chake Timapezeka pa Chikumbutso

“Muzichita zimenezi pondikumbukira.”​—LUKA 22:19.

NYIMBO NA. 20 Munapereka Mwana Wanu Wobadwa Yekha

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. (a) Kodi ndi pa nthawi iti pamene timakumbukira kwambiri wokondedwa wathu amene anamwalira? (b) Kodi Yesu anayambitsa chiyani pa usiku wake womaliza asanaphedwe?

 KAYA patenga nthawi yaitali bwanji kuchokera pamene munthu amene tinkamukonda anamwalira, timamukumbukirabe. Timakumbukira zinthu zabwino zokhudza wokondedwa wathuyo, makamaka tsiku limene anamwalira likafika.

2 Chaka chilichonse timakhala m’gulu la anthu mamiliyoni padzikoli omwe amasonkhana kuti akumbukire imfa ya munthu wina amene timamukonda kwambiri, yemwe ndi Yesu Khristu. (1 Pet. 1:8) Timachita zimenezi kuti tizikumbukira munthu amene anapereka moyo wake monga nsembe kuti atipulumutse ku uchimo ndi imfa. (Mat. 20:28) Ndipotu Yesu ankafuna kuti otsatira ake azikumbukira imfa yake. Pa usiku wake womaliza asanaphedwe, Yesu anayambitsa mwambo wapadera wa chakudya chamadzulo ndipo analamula kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.”​—Luka 22:19.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Ochepa mwa anthu amene amapezeka pamwambo wokumbukira imfa ya Khristu, ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba. Komabe anthu mamiliyoni ambiri omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli, amapezekanso pamwambowu. Munkhaniyi tikambirana zimene zimachititsa magulu awiri onsewa kukhala ofunitsitsa kupezeka pamwambowu chaka chilichonse. Tionanso mmene kupezeka pamwambowu kumatithandizira. Poyamba tiyeni tikambirane zifukwa zina zimene zimachititsa odzozedwa kupezeka pamwambowu.

CHIFUKWA CHAKE ODZOZEDWA AMAPEZEKA PAMWAMBOWU

4. N’chifukwa chiyani odzozedwa amadya mkate komanso kumwa vinyo pa Chikumbutso?

4 Chaka chilichonse, odzozedwa amayembekezera kupezeka pa Chikumbutso monga odya zizindikiro. N’chifukwa chiyani iwo amadya mkate komanso kumwa vinyo pamwambowu? Kuti tiyankhe funsoli, taganizirani zimene zinachitika pa usiku womaliza wa moyo wa Yesu padzikoli. Atachita mwambo wa Pasika, Yesu anayambitsa mwambo umene umadziwika kuti mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Anapereka mkate ndi vinyo kwa atumwi ake 11 okhulupirika n’kuwauza kuti adye ndi kumwa. Iye anawafotokozera zokhudza mapangano awiri, omwe ndi pangano latsopano komanso pangano la Ufumu. * (Luka 22:19, 20, 28-30) Mapanganowa anatsegula mwayi woti atumwi ndi anthu ena owerengeka adzakhale mafumu komanso ansembe kumwamba. (Chiv. 5:10; 14:1) Odzozedwa amene adakali padzikoli, omwe ali m’mapangano awiriwa, ndi amene ayenera kudya mkate ndi kumwa vinyo pa Chikumbutso.

5. Kodi odzozedwa amazindikira chiyani zokhudza chiyembekezo chimene anapatsidwa?

5 Palinso chifukwa china chimene chimachititsa odzozedwa kukhala ofunitsitsa kupezeka pa Chikumbutso. Kupezeka pamwambowu kumawapatsa mwayi woti aziganizira za chiyembekezo chawo. Yehova wawapatsa chiyembekezo chabwino kwambiri, chomwe ndi kudzakhala ndi moyo umene sungafe kumwamba limodzi ndi anzawo a m’gulu la 144,000 komanso kukatumikira ndi Yesu Khristu, yemwe anapatsidwa ulemerero. Koposa zonse, iwo adzapatsidwa mwayi wokakhala ndi Yehova Mulungu. (1 Akor. 15:51-53; 1 Yoh. 3:2) Odzozedwa amazindikira kuti apatsidwa mwayi woti akasangalale ndi zinthu zimenezi kumwamba. Koma kuti adzaloledwe kupita kumwamba, iwo ayenera kukhala okhulupirika mpaka imfa yawo. (2 Tim. 4:7, 8) Odzozedwa amasangalala kwambiri akamaganizira za chiyembekezo chawochi. (Tito 2:13) Nanga bwanji a “nkhosa zina”? (Yoh. 10:16) Kodi ndi zifukwa zina ziti zimene zimawachititsa kupezeka pa Chikumbutso?

CHIFUKWA CHAKE A NKHOSA ZINA AMAPEZEKA PA CHIKUMBUTSO

6. N’chifukwa chiyani a nkhosa zina amapezeka pa Chikumbutso chaka chilichonse?

6 A nkhosa zina amapezeka pa Chikumbutso monga oonerera osati odya zizindikiro. Mu 1938, omwe anali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli anaitanidwa mwachindunji kwa nthawi yoyamba kuti apezeke pa Chikumbutso. Nsanja ya Olonda ya March 1, 1938, inanena kuti: “N’koyenera kuti [a nkhosa zina] azipezeka pamwambowu n’kuonerera zimene zikuchitika. . . . Imeneyi ndi nthawi yoti iwonso azisangalala.” Mofanana ndi alendo amene amasangalala kupezeka pa ukwati, a nkhosa zina nawonso amasangalala kupezeka pa Chikumbutso monga oonerera.

7. N’chifukwa chiyani a nkhosa zina amayembekezera mwachidwi kumvetsera nkhani ya Chikumbutso?

7 Kupezeka pa Chikumbutso kumathandizanso a nkhosa zina kuganizira za chiyembekezo chawo. Iwo amayembekezera mwachidwi kumvetsera nkhani ya Chikumbutso yomwe imafotokoza kwambiri zimene Khristu ndi olamulira anzake okwana 144,000 adzachitire anthu okhulupirika mu Ulamuliro wa Zaka 1,000. Motsogoleredwa ndi Mfumu Yesu Khristu, olamulira anzakewa adzathandiza kusintha dzikoli kukhala Paradaiso komanso anthu omvera kuti akhale angwiro. Zimakhalatu zosangalatsa kwa anthu mamiliyoni ambiri omwe amapezeka pa Chikumbutso akamaganizira maulosi a m’Baibulo omwe adzakwaniritsidwe m’tsogolo, monga opezeka pa Yesaya 35:5, 6; 65:21-23 ndi Chivumbulutso 21:3, 4. Akamadziyerekezera ali m’dziko latsopano limodzi ndi okondedwa awo, chiyembekezo chawo cham’tsogolo chimalimba ndipo amatsimikiza mtima kuti asasiye kutumikira Yehova.​—Mat. 24:13; Agal. 6:9.

8. Kodi ndi chifukwa china chiti chimene chimachititsa a nkhosa zina kupezeka pa Chikumbutso?

8 Taganizirani chifukwa chinanso chimene chimachititsa a nkhosa zina kupezeka pa Chikumbutso. Iwo amafuna kusonyeza chikondi komanso kuthandiza odzozedwa. Mawu a Mulungu ananeneratu kuti odzozedwa azidzagwirizana kwambiri ndi amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli. Motani? Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo.

9. Kodi ulosi wa pa Zekariya 8:23, ukusonyeza bwanji mmene a nkhosa zina amamvera ponena za odzozedwa?

9 Werengani Zekariya 8:23. Ulosiwu ukusonyeza bwino mmene a nkhosa zina amamvera akaganizira za abale ndi alongo awo odzozedwa. Mawu akuti “Myuda” komanso “anthu inu,” akunena za gulu limodzi la anthu lomwe ndi odzozedwa omwe adakali padzikoli. (Aroma 2:28, 29) “Amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina” akuimira a nkhosa zina. Iwo “adzagwira,” kapena kuti kukhalabe okhulupirika kwa odzozedwa, n’kumalambira limodzi Yehova movomerezeka. Choncho pa usiku wa pa Chikumbutso, a nkhosa zina amasonyeza kuti ndi ogwirizana kwambiri ndi odzozedwa akapezekapo pamwambowu.

10. Kodi Yehova wachita zotani pokwaniritsa ulosi wa pa Ezekieli 37:15-19, 24, 25?

10 Werengani Ezekieli 37:15-19. Pokwaniritsa ulosiwu, Yehova wathandiza kuti odzozedwa ndi a nkhosa zina azigwira ntchito limodzi mogwirizana kwambiri. Ulosiwu umatchula za ndodo ziwiri. Amene ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba, ali ngati ndodo “ya Yuda,” fuko limene munkachokera mafumu a Isiraeli. Ndipo amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli ali ngati ndodo “ya Efuraimu.” * Yehova anati adzagwirizanitsa magulu awiriwa kuti akhale “ndodo imodzi.” Zimenezi zikutanthauza kuti iwo amatumikira mogwirizana motsogoleredwa ndi Mfumu imodzi, Khristu Yesu. Chaka chilichonse odzozedwa ndi a nkhosa zina amapezeka pa Chikumbutso osati monga magulu awiri osiyana koma “gulu limodzi” lokhala ndi “m’busa mmodzi.”​—Yoh. 10:16.

11. Kodi “nkhosa” zotchulidwa pa Mateyu 25:31-36, 40, zimasonyeza bwanji kuti zimathandiza abale ake a Khristu?

11 Werengani Mateyu 25:31-36, 40. “Nkhosa” zotchulidwa mufanizoli, zikuimira olungama mu nthawi ya mapeto ino omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli kapena kuti a nkhosa zina. Iwo amathandiza mokhulupirika abale ake a Khristu odzozedwa pokwaniritsa udindo waukulu umene ali nawo, wolalikira ndi kuphunzitsa anthu padziko lonse.​—Mat. 24:14; 28:19, 20.

12-13. Kodi a nkhosa zina amasonyeza kuti amathandiza abale ake a Khristu m’njira zina ziti?

12 Chaka chilichonse kutatsala milungu ingapo kuti tsiku la Chikumbutso lifike, a nkhosa zina amasonyeza kuti amathandiza abale ake a Khristu pogwira nawo ntchito yapadera yomwe imachitika padziko lonse yoitanira anthu achidwi ku Chikumbutso. (Onani bokosi lakuti, “ Kodi Mukukonzekera Chikumbutso?”) Iwo amayesetsanso kuthandiza pokonzekera kuti Chikumbutso chichitike mumpingo uliwonse ngakhale kuti m’mipingo yambiri mulibe amene amadya zizindikiro. A nkhosa zina amasangalala kuthandiza abale ake a Khristu m’njira zimenezi. Iwo amadziwa kuti Yesu amaona zimene amachita pothandiza abale ake odzozedwa ngati kuti akuchitira iyeyo.​—Mat. 25:37-40.

13 Posatengera chiyembekezo chathu, kodi ndi zifukwa zinanso ziti zimene zimachititsa tonsefe kupezeka pa Chikumbutso?

CHIFUKWA CHAKE TONSE TIMAPEZEKA PA CHIKUMBUTSO

14. Kodi Yehova ndi Yesu anatisonyeza bwanji chikondi chachikulu?

14 Timayamikira kwambiri Yehova ndi Yesu chifukwa cha chikondi chimene anatisonyeza. Yehova watisonyeza chikondi m’njira zambiri. Koma njira yapadera imene anatisonyezera chikondi ndi kutumiza Mwana wake wokondedwa kuti adzavutike n’kutifera. (Yoh. 3:16) Timazindikira kuti nayenso Yesu anatisonyeza chikondi chachikulu pololera kupereka moyo wake chifukwa cha ife. (Yoh. 15:13) Sitingathe kubwezera Yehova ndi Yesu pa chikondi chimene anatisonyeza. Komabe tingasonyeze kuyamikira ndi zimene timachita pa moyo wathu tsiku lililonse. (Akol. 3:15) Ndipo timapezeka pa Chikumbutso kuti tizikumbukira chikondi chimenechi komanso kusonyeza kuti timawakonda.

15. N’chifukwa chiyani odzozedwa komanso a nkhosa zina amaona kuti dipo ndi mphatso yamtengo wapatali?

15 Timaona kuti mphatso ya dipo ndi yamtengo wapatali kwambiri. (Mat. 20:28) Odzozedwa amaona kuti dipo ndi lamtengo wapatali chifukwa limachititsa kuti chiyembekezo chawo chikhale chotheka. Chifukwa chakuti amakhulupirira nsembe ya Khristu, Yehova amawaona monga olungama komanso ana ake. (Aroma 5:1; 8:15-17, 23) A nkhosa zina nawonso amayamikira dipo. Chifukwa chokhulupirira magazi a Khristu, Mulungu amawaona kuti ndi oyera, akhoza kumuchitira utumiki wopatulika komanso ali ndi chiyembekezo ‘chodzatuluka ‘m’chisautso chachikulu.’ (Chiv. 7:13-15) Njira imodzi imene odzozedwa komanso a nkhosa zina amasonyezera kuti amayamikira dipo, ndi kupezeka pa Chikumbutso chaka chilichonse.

16. Kodi n’chifukwa china chiti chimene chimatichititsa kupezeka pa Chikumbutso?

16 Chifukwa china chimene chimachititsa kuti tizipezeka pa Chikumbutso ndi chakuti timafuna kumvera Yesu. Kaya tili ndi chiyembekezo chotani m’tsogolo, aliyense wa ife amafunitsitsa kumvera lamulo limene Yesu anapereka pamene anayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake lakuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.”​—1 Akor. 11:23, 24.

MMENE KUPEZEKA PA CHIKUMBUTSO KUMATITHANDIZIRA

17. Kodi kupezeka pa Chikumbutso kumatithandiza bwanji kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

17 Timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Yak. 4:8) Kupezeka pa Chikumbutso kumatipatsa mwayi woganizira chiyembekezo chimene Yehova watipatsa komanso chikondi chachikulu chimene anatisonyeza. (Yer. 29:11; 1 Yoh. 4:8-10) Tikamaganizira chiyembekezo chathu cham’tsogolo chomwe ndi chotsimikizika, komanso chikondi chosatha chimene Mulungu anatisonyeza, timayamba kumukonda kwambiri ndipo ubwenzi wathu ndi iye umalimba.​—Aroma 8:38, 39.

18. Kodi kuganizira chitsanzo cha Yesu kumatilimbikitsa kuchita chiyani?

18 Timalimbikitsidwa kutengera chitsanzo cha Yesu. (1 Pet. 2:21) Kutatsala masiku ochepa kuti Chikumbutso chichitike, timaganizira nkhani za m’Baibulo zofotokoza zimene zinachitika pa mlungu womaliza wa moyo wa Yesu padzikoli, imfa yake komanso kuukitsidwa kwake. Kenako pa tsiku la Chikumbutso madzulo, nkhani imene imakambidwa imatikumbutsa chikondi chimene Yesu anatisonyeza. (Aef. 5:2; 1 Yoh. 3:16) Tikamawerenga komanso kuganizira chitsanzo cha Yesu chololera kuvutikira ena, timalimbikitsidwa “kupitiriza kuyenda mmene iyeyo anayendera.”​—1 Yoh. 2:6.

19. Kodi tingatani kuti tipitirizebe kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu?

19 Timakhala otsimikiza kukhalabe mabwenzi a Yehova. (Yuda 20, 21) Timapitiriza kukhalabe pa ubwenzi ndi Mulungu tikamayesetsa kumumvera, kuyeretsa dzina lake komanso kusangalatsa mtima wake. (Miy. 27:11; Mat. 6:9; 1 Yoh. 5:3) Kupezeka pa Chikumbutso kumatichititsa kuti tikhale otsimikiza kuti tsiku lililonse tizichita zinthu zomwe zingakhale ngati tikumuuza Yehova kuti, ‘Ndikufuna kukhala bwenzi lanu mpaka kalekale.’

20. Kodi tili ndi zifukwa zomveka ziti zotichititsa kupezeka pa Chikumbutso?

20 Kaya tikuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padzikoli mpaka kalekale, tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kupezeka pa Chikumbutso. Chaka chilichonse tikasonkhana pa tsikuli, timakumbukira imfa ya Yesu Khristu yemwe timamukonda kwambiri. Koposa zonse timakumbukira za chikondi chachikulu chimene Yehova anatisonyeza potipatsa Mwana wake monga nsembe. Chaka chino Chikumbutso chidzachitika madzulo a Lachisanu pa 15 April, 2022. Timakonda kwambiri Yehova ndi Mwana wake. Choncho pa tsiku lokumbukira imfa ya Yesu, palibe chinthu chimene tiyenera kuchiona kuti ndi chofunika kwambiri chomwe chingatilepheretse kupezeka pamwambo wa Chikumbutso.

NYIMBO NA. 16 Tamandani Yehova Chifukwa cha Mwana Wake Wodzozedwa

^ ndime 5 Kaya tikuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala m’Paradaiso padzikoli, timayembekezera mwachidwi kuchita Chikumbutso chaka chilichonse. Munkhaniyi tikambirana zifukwa zomveka zochokera m’Malemba zotichititsa kupezeka pamwambowu komanso mmene timapindulira tikapezekapo.

^ ndime 4 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya pangano latsopano komanso pangano la Ufumu, onani nkhani yakuti, “Mudzakhala ‘Ufumu wa Ansembe’” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2014, tsamba 15-17.

^ ndime 10 Kuti mudziwe zambiri zokhudza ulosi wonena za ndodo ziwiri wotchulidwa mu Ezekieli chaputala 37, onani nkhani yakuti, “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya July 2016.