Kodi Mumaona Akazi Ngati Mmene Yehova Amawaonera?

Kodi Mumaona Akazi Ngati Mmene Yehova Amawaonera?

TILI ndi mwayi wotumikira ndi alongo ambiri okhulupirika ndipo timakonda komanso kuyamikira kwambiri alongo akhamawa. a Choncho abalenu, yesetsani kuti muzichita nawo zinthu mokoma mtima, mwachilungamo komanso mwaulemu. Koma popeza si ife angwiro, nthawi zina kuchita zimenezi kumativuta. Abale ena amakumananso ndi vuto lina pa nkhani imeneyi.

Ambiri anakulira m’zikhalidwe zimene amuna ambiri amaona kuti akazi ndi otsika. Mwachitsanzo, woyang’anira dera wina ku Bolivia dzina lake Hans, ananena kuti: “Amuna ena anakulira m’zikhalidwe zimene zimalimbikitsa amuna kukhala odzikuza. Amuna amenewa amaona kuti akazi ndi otsika ndipo sawalemekeza.” Mkulu wina ku Taiwan, dzina lake Shengxian, ananena kuti: “Kumene ndimakhala, amuna ambiri amaona kuti akazi sayenera kuuza amuna zochita. Mwamuna akapereka maganizo a mkazi pa nkhani inayake, amuna anzake amamunyoza.” Koma amuna ena amaonetsa tsankho kwa akazi m’njira zosaonekera. Mwachitsanzo, iwo anganene nthabwala zosalemekeza akazi.

Chosangalatsa n’chakuti mwamuna aliyense akhoza kusintha zimene anazolowera m’chikhalidwe chake. Angathe kusiya kuona kuti akazi ndi otsika. (Aef. 4:22-24) Zimenezi zingatheke ngati atamatsanzira Yehova. Munkhaniyi, tiona mmene Yehova amaonera akazi, zimene abale angachite potsanzira Yehova komanso mmene akulu angaperekere chitsanzo pa nkhani yolemekeza alongo.

KODI YEHOVA AMAWAONA BWANJI AKAZI?

Yehova amapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya mmene tiyenera kumachitira zinthu ndi akazi. Iye ndi Bambo wachikondi ndipo amakonda kwambiri anthu onse a m’banja lake. (Yoh. 3:16) Komanso alongo okhulupirika ali ngati ana ake a mtengo wapatali. Tiyeni tikambirane njira zimene Yehova anasonyezera kuti amalemekeza akazi.

Amachita nawo zinthu mopanda tsankho. Yehova analenga amuna ndi akazi m’chifaniziro chake. (Gen. 1:27) Iye sanapereke luso kapena nzeru zambiri kwa amuna poyerekeza ndi akazi, komanso sikuti amakonda kwambiri amuna kuposa akazi. (2 Mbiri 19:7) Iye analenga onse m’njira yofanana yoti azitha kuphunzira mfundo za m’Baibulo komanso kusonyeza makhalidwe ake abwino. Iye amaona chikhulupiriro cha onsewa mofanana, kaya ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli mpaka kalekale kapena kukalamulira ndi Yesu monga mafumu ndi ansembe kumwamba. (2 Pet. 1:1) Kunena zoona, Yehova sachita zinthu mwatsankho ndi akazi.

Amawamvetsera. Yehova amaganizira mmene akazi amamvera komanso zimene zikuwadetsa nkhawa. Mwachitsanzo, iye anamvetsera mapemphero a Rakele ndi Hana ndipo anawathandiza. (Gen. 30:22; 1 Sam. 1:10, 11, 19, 20) Yehova anauziranso anthu kuti alembe m’Baibulo nkhani za amuna omwe anamvetsera maganizo a akazi. Mwachitsanzo, Abulahamu anatsatira malangizo a Yehova oti amvetsere maganizo a mkazi wake Sara. (Gen. 21:12-14) Mfumu Davide anamvetsera zimene Abigayeli ananena. Ndipotu Davide ankaona kuti Yehova ndi amene anatumiza Abigayeli kuti adzalankhule naye. (1 Sam. 25:32-35) Yesu, yemwe ankasonyeza bwino makhalidwe a Atate ake, ankamvetsera mayi ake Mariya. (Yoh. 2:3-10) Zitsanzozi zikusonyeza kuti njira imodzi imene Yehova amasonyezera kuti amalemekeza akazi ndi kuwamvetsera.

Amawadalira. Mwachitsanzo, Yehova anasonyeza kuti ankadalira Hava pomupatsa udindo woti athandize kusamalira dziko lonse. (Gen. 1:28) Pamenepa anasonyeza kuti sankaona Hava ngati wotsika pomuyerekezera ndi mwamuna wake Adamu, koma monga mnzake womuyenerera. Yehova anaperekanso udindo kwa aneneri aakazi, Debora komanso Hulida, kuti azilangiza anthu ake kuphatikizapo woweruza komanso mfumu. (Ower. 4:4-9; 2 Maf. 22:14-20) Masiku anonso Yehova anapereka udindo kwa akazi wogwira ntchito yake. Alongo okhulupirikawa amatumikira monga ofalitsa, apainiya komanso amishonale. Amathandiza pokonza mapulani, kumanga ndi kusamalira Nyumba za Ufumu komanso maofesi a nthambi. Ena mwa alongowa amatumikira pa Beteli komanso m’maofesi omasulira mabuku. Alongowa ali ngati gulu lalikulu limene Yehova akuligwiritsa ntchito pokwaniritsa cholinga chake. (Sal. 68:11) Apa n’zoonekeratu kuti Yehova saona kuti akazi ndi otsika kapena ofooka.

KODI ABALE ANGATANI KUTI AZILEMEKEZA AKAZI NGATI MMENE YEHOVA AMACHITIRA?

Abale, kuti tidziwe ngati timalemekeza akazi ngati mmene Yehova amachitira, tiyenera kufufuza maganizo ndi zochita zathu. Koma kuti zimenezi zitheke tiyenera kuthandizidwa. Monga mmene mashini a X-ray amathandizira madokotala kudziwa mmene mtima wa munthu ulili, mnzathu wabwino komanso Mawu a Mulungu angatithandize kudziwa ngati timaona akazi moyenerera. Ndiye kodi tingatani kuti tithandizidwe?

Muzifunsa mnzanu. (Miy. 18:17) Tizifunsa mnzathu wodalirika amene amadziwika kuti ndi wokoma mtima komanso woganiza bwino mafunso monga awa: “Kodi ndimachita bwanji zinthu ndi akazi? Kodi amaona kuti ndimawalemekeza? Kodi pali zinthu zina zomwe ndiyenera kusintha?” Ngati mnzanuyo wakuuzani mbali zimene muyenera kukonza, musamadziikire kumbuyo. M’malomwake muzikhala okonzeka kusintha.

Muziphunzira Mawu a Mulungu. Kodi njira yabwino imene ingatithandize kudziwa ngati timalemekeza akazi ndi iti? Mawu a Mulungu angatithandize kufufuza maganizo ndi zochita zathu. (Aheb. 4:12) Tikamawerenga Baibulo, timaphunzira za amuna amene ankalemekeza akazi komanso amene sankawalemekeza. Ndiye tingayerekezere zimene iwo ankachita ndi zimene ifeyo timachita. Anthu ena amagwiritsa ntchito mavesi ena a m’Baibulo poikira kumbuyo maganizo olakwika omwe ali nawo okhudza akazi. Koma kuyerekezera mavesiwa ndi mavesi ena kungatithandize kupewa zimenezi. Mwachitsanzo, lemba la 1 Petulo 3:7 limanena kuti akazi azipatsidwa ulemu chifukwa ali ngati “chiwiya chosachedwa kusweka.” b Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti akazi ndi otsika, nzeru zawo ndi zochepa komanso alibe luso poyerekeza ndi amuna? Ayi ndithu. Tayerekezerani mawu a Petulowa ndi zimene lemba la Agalatiya 3:26-29 limanena. Lembali limasonyeza kuti Yehova anasankha amuna ndi akazi omwe kuti adzalamulire limodzi ndi Yesu kumwamba. Kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kupempha mnzathu kuti atithandize pa nkhaniyi kungatithandize kuti tizilemekeza akazi.

KODI AKULU ANGASONYEZE BWANJI KUTI AMALEMEKEZA ALONGO?

Abale mumpingo angaphunzire kulemekeza alongo poona chitsanzo cha akulu. Kodi akulu angapereke bwanji chitsanzo pa nkhani yolemekeza alongo? Tiyeni tikambirane njira zingapo.

Amayamikira alongo. Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino chomwe akulu angatengere. M’kalata yomwe analembera Akhristu a ku Roma, iye anatchula mayina angapo a alongo omwe ankawayamikira. (Aroma 16:12) Alongo amenewa ayenera kuti anasangalala kwambiri pamene kalata ya Paulo inkawerengedwa kumpingo. Nawonso akulu amayamikira alongo chifukwa cha makhalidwe awo abwino komanso chifukwa chogwira mwakhama ntchito ya Yehova. Zimenezi zimathandiza alongo kudziwa kuti amalemekezedwa komanso kuyamikiridwa. Mawu omwe akulu angawauze angawalimbikitse kuti apitirize kutumikira Yehova mokhulupirika.​—Miy. 15:23.

Muziwayamikira

Poyamikira alongo, akulu amachita zimenezo mochokera pansi pa mtima komanso kutchula zenizeni zimene alongowo achita bwino. N’chifukwa chiyani ayenera kutero? Mlongo wina dzina lake Jessica ananena kuti: “Zimakhala bwino abale akamauza alongo kuti ‘mwachita bwino.’ Koma timayamikira kwambiri akatchula zenizeni zimene tinachita. Mwachitsanzo, angatiyamikire chifukwa chothandiza ana athu kuti azikhala pansi n’kumamvetsera mwatcheru tikakhala pamisonkhano, kapenanso chifukwa choyesetsa kukatenga munthu amene timaphunzira naye Baibulo pobwera kumisonkhano.” Akulu akamayamikira alongo potchula mwachindunji zimene achita bwino, alongowo amadzimva kuti ndi ofunika mumpingo.

Amamvetsera maganizo a alongo. Akulu odzichepetsa amazindikira kuti si iwo okha amene amakhala ndi mfundo zabwino. Akulu oterowo amapempha alongo kuti apereke maganizo awo ndipo amawamvetsera mwatcheru akamalankhula. Akamachita zimenezi amalimbikitsa alongo ndipo iwonso amapindula. Mkulu wina yemwe amatumikira pa Beteli dzina lake Gerardo ananena kuti: “Ndinaona kuti kufunsa alongo kuti apereke maganizo awo kumandithandiza kuti ndizigwira bwino ntchito yanga. Nthawi zambiri zimakhala kuti iwo akhala akugwira ntchitoyo kwa zaka zambiri kuposa abale ena.” Mumpingo, alongo ambiri ndi apainiya choncho amadziwa zambiri zokhudza anthu a m’dera limene amakhala. Mkulu wina dzina lake Brian ananena kuti: “Alongo athu akhoza kuthandiza kwambiri gulu la Yehova m’njira zambiri. Choncho muzilola kuti akuthandizeni chifukwa amadziwa zambiri.”

Muziwamvetsera

Akulu ozindikira safulumira kunyalanyaza maganizo a alongo. N’chifukwa chiyani tikutero? Mkulu wina dzina lake Edward ananena kuti: “Maganizo a alongo komanso zimene akudziwa zingamuthandize m’bale kudziwa mbali zonse zokhudza nkhani inayake ndipo zingamuthandizenso kukhala wachifundo.” (Miy. 1:5) Ngakhale mkulu atadziwa kuti sagwiritsa ntchito maganizo amene mlongo wapereka, ayenera kumuyamikira chifukwa choti wapereka maganizo ake komanso wasonyeza nzeru.

Amaphunzitsa alongo. Akulu ozindikira amafunafuna mipata yoti aphunzitse alongo. Mwachitsanzo, iwo amaphunzitsa alongo mmene angachititsire misonkhano yokonzekera utumiki ngati palibe m’bale wobatizidwa. Angawaphunzitse mmene angagwiritsire ntchito zipangizo zosiyanasiyana komanso mashini kuti azithandiza pa ntchito zomangamanga m’gulu lathu. Pa Beteli, abale oyang’anira madipatimenti amaphunzitsa alongo ntchito zosiyanasiyana monga kukonza zinthu, kugula zinthu, kuwerengetsera ndalama, zamakompyuta ndi ntchito zina. Akulu akamaphunzitsa alongo amawasonyeza kuti ndi odalirika komanso kuti amawakhulupirira.

Muziwaphunzitsa

Alongo ambiri amagwiritsa ntchito zimene akulu anawaphunzitsa pothandizanso ena. Mwachitsanzo, alongo ena omwe anaphunzitsidwa ntchito zomangamanga amathandiza kukonza nyumba za anzawo pakachitika ngozi. Alongo omwe anaphunzitsidwa mmene angachitire ulaliki wa m’malo opezeka anthu ambiri amaphunzitsanso alongo ena ambiri mmene angachitire ulalikiwu. Kodi alongo amamva bwanji akaganizira za akulu omwe anawaphunzitsa? Mlongo wina dzina lake Jennifer ananena kuti: “Pamene ndinkagwira nawo ntchito yamanga Nyumba ya Ufumu ina, m’bale yemwe ankayang’anira anandiphunzitsa zambiri. Ankandiyamikira chifukwa cha zimene ndakwanitsa kuchita. Ndinkasangalala kugwira naye ntchito chifukwa ndinkadziona kuti ndine wofunika komanso ndimadaliridwa.”

UBWINO WOLEMEKEZA ALONGO MUMPINGO

Timakonda kwambiri alongo athu okhulupirika ngati mmene Yehova amachitira, choncho timawaona ngati anthu a m’banja lathu. (1 Tim. 5:1, 2) Timaona kuti kugwira nawo ntchito limodzi ndi mwayi waukulu ndipo timasangalala akazindikira kuti timawakonda komanso kuwathandiza. Mlongo wina dzina lake Vanessa ananena kuti: “Ndimayamikira kukhala m’gulu la Yehova, lomwe muli abale amene amandilimbikitsa kwambiri.” Mlongo wina wa ku Taiwan ananena kuti: “Ndimayamikira kwambiri Yehova ndi gulu lake chifukwa amatilemekeza kwambiri akazife komanso amaganizira mmene timamvera. Zimenezi zimalimbitsa chikhulupiriro changa ndipo zimandichititsa kuyamikira mwayi wokhala m’gulu la Yehova.”

Yehova amasangalala kwambiri akamaona amuna a Chikhristu akuyesetsa kuona alongo ngati mmene iye amachitira. (Miy. 27:11) Mkulu wina wa ku Scotland, dzina lake Benjamin, ananena kuti: “M’dzikoli anthu ambiri amanyoza akazi, choncho timafuna kuti akazi akafika m’Nyumba ya Ufumu aziona kusiyana.” Choncho tiyeni tizichita zonse zomwe tingathe n’kumatsanzira Yehova pokonda komanso kulemekeza alongo athu okondedwa.​—Aroma 12:10.

a Munkhaniyi, mawu akuti “alongo” akunena za akazi a Chikhristu, osati mchemwali wake wa munthu.

b Kuti mumve zambiri pa mawu akuti “chiwiya chosachedwa kusweka,” onani nkhani yakuti “Mtengo wa ‘Chotengera Chochepa Mphamvu’” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2006, komanso yakuti “Malangizo Anzeru kwa Okwatirana” mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 2005.