MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA

Mfundo Zothandiza Pophunzira

Mfundo Zothandiza Pophunzira

Sikuti timangolambira Yehova tikakhala pagulu lalikulu ngati pamisonkhano yampingo, yadera kapena yachigawo koma timamulambiranso monga banja komanso patokha. Izi ndi zina zomwe mungachite mukamaphunzira panokha kapena pa kulambira kwa pabanja:

  • Kukonzekera misonkhano yampingo. Mungaphatikizepo kuphunzira nyimbo komanso kuthandiza onse a m’banja lanu kuti akayankhe.

  • Kuwerenga nkhani ya m’Baibulo. Pambuyo pake mungajambule chithunzi cha nkhani yomwe mwawerengayo kapena kulemba zimene mwaphunzirapo.

  • Kuwerenga pemphero linalake lopezeka m’Baibulo kenako kukambirana mmene lingakuthandizireni kuti mapemphero anu azikhala abwino.

  • Kuonera imodzi mwa mavidiyo athu kenako kukambirana kapena kulemba zimene mwaphunzirapo.

  • Kukonzekera ulaliki, mwinanso kuyeserera zimene mungakachite.

  • Kufufuza zokhudza chilengedwe komanso kuganizira kapena kukambirana zimene mukuphunzirapo zokhudza Yehova. a

a Onani nkhani yakuti “Muziphunzira Zambiri Zokhudza Yehova Poona Chilengedwe Chake” mu Nsanja ya Olonda ya March 2023.