NKHANI YOPHUNZIRA 3

NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse

Yehova Adzakuthandizani pa Nthawi Yovuta

Yehova Adzakuthandizani pa Nthawi Yovuta

“M’masiku anu, [Yehova] adzachititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka (osagwedezeka).​—YES. 33:6.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona zimene tingachite kuti Yehova azitithandiza tikakumana ndi mavuto.

1-2. Kodi atumiki a Yehova okhulupirika angakumane ndi mavuto ati?

 MAVUTO aakulu angasinthe moyo wathu mwadzidzidzi. Mwachitsanzo, m’bale wina wokhulupirika dzina lake Luis a anapezeka ndi khansa yoopsa. Adokotala anamuuza kuti akhala ndi moyo kwa miyezi yochepa yokha. Monika ndi mwamuna wake ankatumikira Yehova limodzi. Kenako tsiku lina anadziwa kuti mwamuna wake yemwe anali mkulu, ankachita machimo aakulu mobisa kwa zaka zambiri. Mlongo wina wosakwatiwa dzina lake Olivia ankafunika kuchoka kunyumba kwake chifukwa mphepo yamkuntho inali itatsala pang’ono kufika m’dera lawo. Atabwerera, anapeza kuti mphepoyo inawonongeratu nyumba yake. M’kanthawi kochepa, moyo wa anthu tatchulawa unasintha kwambiri. Kodi inunso munayamba mwakumanapo ndi mavuto ngati amenewa? Kodi munakumana ndi mavuto omwe anachititsa kuti moyo wanu usinthe?

2 Ngakhale kuti ndife atumiki okhulupirika a Yehova, mofanana ndi anthu onse, timakumana ndi mavuto komanso matenda. Nthawi zinanso timatsutsidwa kapena kuzunzidwa ndi anthu odana ndi anthu a Mulungu. Yehova samatiteteza kuti tisakumane ndi mavuto, koma amatilonjeza kuti adzatithandiza. (Yes. 41:10) Iye akatithandiza timapitirizabe kukhala osangalala, timasankha zinthu mwanzeru komanso timakhalabe okhulupirika kwa iye ngakhale pamene zili zovuta kutero. Munkhaniyi, tikambirana njira 4 zimene Yehova amagwiritsa ntchito potithandiza tikakumana ndi mavuto aakulu pa moyo wathu. Tionanso zimene tingachite kuti azitithandiza.

YEHOVA ADZAKUTETEZANI

3. Kodi tikakumana ndi mavuto aakulu zimakhala zovuta kuchita chiyani?

3 Vuto limene tingakumane nalo. Tikakumana ndi vuto lalikulu, zingakhale zovuta kuti tiziganiza bwino komanso kusankha zochita mwanzeru. Chifukwa chiyani? Zimakhala zikutipweteka kwambiri mumtima ndipo tikhoza kumada nkhawa kwambiri. Zingakhale ngati tikuyenda kunja kutachita nkhungu moti sitikuona komwe tikulowera. Taganizirani mmene alongo awiri omwe tawatchula aja anamvera atakumana ndi mavuto aakulu. Olivia ananena kuti: “Mphepo yamkuntho itawononga nyumba yanga ndinasokonezeka kwambiri.” Pofotokoza za zimene mwamuna wake anachita, Monika anati: “Ndinakhumudwa kwambiri. Ndinamva ngati kuti wina wandibaya mumtimamu. Sindinkathanso kuchita zinthu bwinobwino. Sindinkakhulupirira zomwe zinandichitikirazo.” Kodi Yehova amatilonjeza kuti adzatithandiza bwanji tikakhala ndi nkhawa?

4. Kodi Yehova akulonjeza chiyani pa Afilipi 4:6, 7?

4 Zimene Yehova amachita. Iye amatilonjeza kuti atipatsa “mtendere wa Mulungu” wotchulidwa m’Baibulo. (Werengani Afilipi 4:6, 7.) Munthu akakhala ndi mtendere umenewu, mtima ndi maganizo ake zimakhala m’malo chifukwa choti ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Mtenderewu ndi woti “anthu sangathe kuumvetsa” ndipo ndi wodabwitsa kuposa mmene tingaganizire. Kodi inunso mtima wanu unayamba wakhalapo m’malo mutapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima? Munamva choncho chifukwa cha “mtendere wa Mulungu.”

5. Kodi mtendere wa Mulungu umateteza bwanji maganizo ndi mitima yathu?

5 Lemba lija limanenanso kuti mtendere wa Mulungu “udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.” Mawu omwe anawamasulira kuti “udzateteza” amanena za asilikali omwe ankalondera mzinda kuti usaukiridwe ndi adani. Anthu a mumzindawo ankagona mwamtendere podziwa kuti asilikali akulondera pageti. Mtendere wa Mulungu ukamateteza mtima ndi maganizo athu, ifenso timakhala mosatekeseka podziwa kuti ndife otetezeka. (Sal. 4:8) Mofanana ndi Hana, timakhalabe ndi mtendere wa mumtima ngakhale zitakhala kuti zinthu sizinasinthe nthawi yomweyo. (1 Sam. 1:16-18) Ndipo tikakhala osatekeseka, nthawi zambiri zimakhala zosavuta kuti tiziganiza bwino komanso tizisankha zochita mwanzeru.

Muzipemphera mpaka mutaona kuti “mtendere wa Mulungu” ukuteteza mtima ndi maganizo anu (Onani ndime 4-6)


6. Kodi tingatani kuti mtendere wa Mulungu utithandize? (Onaninso chithunzi.)

6 Zimene tiyenera kuchita. Mukapanikizika ndi mavuto muziitana asilikali, titero kunena kwake, kuti akutetezeni. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Muzipemphera mpaka mutamva kuti muli ndi mtendere wa Mulungu. (Luka 11:9; 1 Ates. 5:17) Luis yemwe tamutchula uja anafotokoza zimene iye ndi mkazi wake Ana, anachita kuti apirire atadziwa kuti watsala ndi miyezi yochepa kuti akhale ndi moyo. Iye anati: “Pa nthawi ngati imeneyi, zimakhala zovuta kwambiri kusankha zochita pa nkhani ya thandizo la mankhwala komanso nkhani zina. Koma kupemphera kwatithandiza kuti tikhale ndi mtendere pa nthawi yovutayi.” Luis ndi mkazi wake ananena kuti ankapemphera mochokera pansi pa mtima ndiponso mobwerezabwereza kuti Yehova awapatse mtendere wa mumtima ndi m’maganizo komanso nzeru kuti azitha kusankha bwino zochita ndipo anaona kuti anawathandiza. Inunso mukakumana ndi mavuto muzilimbikira kupemphera ndipo mudzaona mtendere wa Yehova ukuteteza mtima ndi maganizo anu.​—Aroma 12:12

YEHOVA ADZAKUTHANDIZANI KUTI MUSAGWEDEZEKE

7. Kodi tingamamve bwanji tikakumana ndi mavuto aakulu?

7 Vuto limene tingakumane nalo. Tikakumana ndi mavuto aakulu timamva kupweteka mumtima, maganizo athu amasokonezeka ndipo sitingachite zinthu ngati mmene timachitira nthawi zonse. Tingakhale ngati sitima yomwe ikukankhidwira uku ndi uku ndi mphepo yamphamvu. Ana yemwe tamutchula kale uja ananena kuti Luis atamwalira ankaganiza zambiri. Iye anati: “Nthawi zina ndinkangodziona ngati wachabechabe ndipo ndinkangodzimvera chisoni. Koma kenako ndinkakwiya kwambiri ndikaganizira zoti wapita.” Kuwonjezera pamenepo, Ana ankangodziona kuti ali yekhayekha komanso ankakhala wokhumudwa chifukwa ankafunika kusankha zochita pa nkhani zimene Luis sankavutika nazo. Nthawi zina ankangodzimva ngati ali panyanja pomwe pali chimphepo chamkuntho. Kodi Yehova amatithandiza bwanji tikamamva chonchi?

8. Kodi Yehova akutitsimikizira chiyani pa Yesaya 33:6?

8 Zimene Yehova amachita. Iye amatitsimikizira kuti adzatithandiza kuti tisagwedezeke. (Werengani Yesaya 33:6.) Sitima ikakumana ndi mphepo yamphamvu panyanja, imayamba kukankhidwira uku ndi uku ndipo zimakhala zoopsa. Koma sitima zina zimakhala ndi zinthu zina m’mbali mwake zomwe zimathandiza kuti sitima ikhazikike pamadzi. Zinthu zimenezi zimathandiza kuti sitimayo isamatengeketengeke, zomwe zimachititsa kuti anthu omwe akwera akhale otetezeka. Koma zinthu zambiri zomwe zimathandiza kuti sitima isamagwedezeke zimagwira bwino ntchito sitimayo ikamayenda. Mofanana ndi zimenezi, Yehova adzatithandiza kuti tisagwedezeke ngati tikupitirizabe kumutumikira mokhulupirika pamene tikukumana ndi mavuto.

Muzigwiritsa ntchito zinthu zofufuzira kuti musagwedezeke (Onani ndime 8-9)


9. Kodi zinthu zogwiritsa ntchito pofufuza zingatithandize bwanji kuti tiziganiza bwino? (Onaninso chithunzi.)

9 Zimene tiyenera kuchita. Mukakumana ndi mavuto muziyesetsabe kuchita zinthu zokhudza kulambira. N’zoona kuti simungamachite ngati poyamba, koma Yehova amamvetsa. (Yerekezerani ndi Luka 21:1-4.) Zinthu zina zomwe muyenera kuchita ndi kuphunzira panokha komanso kuganizira mozama zimene mwaphunzirazo. Chifukwa chiyani? Yehova amagwiritsa ntchito gulu lake potipatsa mfundo za m’Malemba zomwe zingatithandize kuti tiziganiza bwino. Kuti mupeze zimene zingakuthandizeni, mungagwiritse ntchito zinthu zothandiza pofufuza monga pulogalamu ya JW Library, buku la Watch Tower Publications Index komanso Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani. Monika yemwe tamutchula uja ananena kuti ankagwiritsa ntchito zinthu zofufuzirazi akaona kuti wapanikizika ndi mavuto enaake. Mwachitsanzo, iye anafufuza mawu akuti “kukwiya.” Nthawi zinanso ankafufuza mawu akuti “kusakhulupirika” kapena “kukhulupirika.” Kenako ankawerenga mpaka atayambiranso kumva bwino. Iye anati: “Ndikamayamba kufufuza ndinkakhala ndi nkhawa koma ndikapitiriza kuwerengako zinkangokhala ngati Yehova wandikumbatira. Ndikamawerenga ndinkazindikira kuti Yehova akumvetsa mmene ndikumvera ndiponso kuti akundithandiza.” Inunso Yehova akhoza kukuthandizani mpaka mutayambiranso kumva bwino.​—Sal. 119:143, 144.

YEHOVA ADZAKUTHANDIZANI

10. Kodi tingamve bwanji tikakumana ndi mavuto aakulu?

10 Vuto limene tingakumane nalo. Pakachitika vuto linalake lalikulu, masiku ena mukhoza kumakhala wofooka komanso ndi nkhawa. Mukhoza kumamva ngati katswiri wothamanga yemwe wavulala ndipo akutsimphina. Mukhoza kumavutika kugwira ntchito zina zomwe poyamba sizinkakuvutani kapenanso simungafune kuchita zimene poyamba zinkakusangalatsani. Mofanana ndi Eliya, mungamafune kuti muzingogona osadzuka. (1 Maf. 19:5-7) Kodi Yehova akulonjeza kuti adzachita chiyani tikafooka?

11. Kodi Yehova amatithandizanso pogwiritsa ntchito njira iti? (Salimo 94:18)

11 Zimene Yehova amachita. Iye amatilonjeza kuti adzatithandiza. (Werengani Salimo 94:18.) Munthu wothamanga yemwe wavulala amafunika kuthandizidwa kuti ayende. Ifenso tingafunike kuthandizidwa kuti tipitirize kutumikira Yehova. Pa nthawi ngati imeneyi, Yehova amatitsimikizira kuti: “Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja, Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’” (Yes. 41:13) Mfumu Davide anaona Yehova akumuthandiza mwa njira imeneyi. Iye atakumana ndi mavuto komanso kuopsezedwa ndi adani, anauza Yehova kuti: “Dzanja lanu lamanja limandithandiza.” (Sal. 18:35) Koma kodi Yehova amatithandiza bwanji?

Muzilola kuti anthu a m’banja lanu, anzanu komanso akulu akuthandizeni (Onani ndime 11-13)


12. Kodi Yehova angagwiritse ntchito ndani kuti atithandize pamene tafooka?

12 Nthawi zambiri Yehova amatithandiza polimbikitsa anthu ena kuti atithandize. Mwachitsanzo, Davide atafooka, Yonatani yemwe anali mnzake anabwera kudzamuthandiza komanso kumuuza mawu olimbikitsa. (1 Sam. 23:16, 17) Yehova anasankhanso Elisa kuti akalimbikitse Eliya. (1 Maf. 19:16, 21; 2 Maf. 2:2) Masiku anonso Yehova angagwiritse ntchito anthu a m’banja lathu, anzathu kapenanso akulu kuti atithandize. Komabe zinazake zikatipweteka sitimafuna kucheza ndi anthu, timangofuna kukhala patokha. Zimenezi sizachilendo. Koma kodi tingatani kuti Yehova atithandize?

13. Kodi tiyenera kutani kuti Yehova atithandize? (Onaninso chithunzi.)

13 Zimene tiyenera kuchita. Muzipewa mtima wosafuna kucheza ndi anthu. Nthawi zambiri munthu akakhala payekha saganiza bwino chifukwa amangoganizira za iyeyo ndi mavuto amene akukumana nawo. Kaganizidwe kameneka kangachititse kuti asasankhe bwino zochita. (Miy. 18:1) N’zoona tonsefe timafunika kukhala patokha makamaka tikakumana ndi mavuto aakulu. Komabe tikakhala kwatokha kwa nthawi yaitali, timatalikirana ndi anthu amene Yehova angawagwiritse ntchito kuti atithandize. Choncho muzilola kuti anthu a m’banja lanu, anzanu komanso akulu akuthandizeni ngakhale kuti nthawi zina zimenezi zimakhala zovuta tikakumana ndi mavuto. Muziona kuti anthu amenewa ndi njira imene Yehova angagwiritse ntchito kuti akuthandizeni.​—Miy. 17:17; Yes. 32:1, 2.

YEHOVA ADZAKUTONTHOZANI

14. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatichititse mantha?

14 Vuto limene tingakumane nalo. Nthawi zina tikhoza kuchita mantha ndi zinthu zina. Atumiki ena okhulupirika a Mulungu ananenapo za nthawi imene anada nkhawa kapena kunjenjemera chifukwa cha adani awo kapena mavuto ena. (Sal. 18:4; 55:1, 5) Nafenso tikhoza kutsutsidwa kusukulu, kuntchito, ndi anthu a m’banja lathu kapenanso ndi boma. Apo ayi tikhoza kudwala mwakayakaya. Pa nthawi ngati imeneyi tikhoza kukhala ngati kamwana kamene kakusowa mtengo wogwira. Kodi Yehova amatithandiza bwanji pa nthawi ngati imeneyi?

15. Kodi mawu a pa Salimo 94:19 angatilimbikitse bwanji?

15 Zimene Yehova amachita. Iye amatitonthoza komanso kutilimbikitsa. (Werengani Salimo 94:19.) Salimoli lingatichititse kuganizira za kamtsikana kamene kakulephera kugona chifukwa choopa mabingu. Kenako bambo ake akubwera n’kukanyamula mpaka kakugona. Ngakhale kuti mvula yamabinguyo ikugwabe, mwanayo akuona kuti ndi wotetezeka chifukwa choti bambo ake amunyamula. Ifenso ngati tikuchita mantha chifukwa cha mayesero enaake, timafuna kuti Atate wathu wakumwamba akhale ngati watinyamula mpaka manthawo atatha. Ndiye kodi tingatani kuti Yehova atitonthoze

Muzilola kuti Atate wanu wakumwamba akutonthozeni kudzera m’Malemba (Onani ndime 15-16)


16. Kodi tingatani kuti Yehova azititonthoza? (Onaninso chithunzi.)

16 Zimene tiyenera kuchita. Tizilankhula ndi Yehova pafupipafupi popemphera kwa iye komanso kuwerenga Mawu ake. (Sal. 77:1, 12-14) Choncho tikadzakumana ndi mavuto, choyambirira kuchita chidzakhala kupemphera kwa Atate wathu wakumwamba. Muzimufotokozera Yehova zimene zikukuchititsani mantha komanso kukudetsani nkhawa. Muzimulola kuti akulankhuleni komanso kukutonthozani kudzera m’Malemba. (Sal. 119:28) Mudzaona kuti malemba ena m’Baibulo amatilimbikitsa makamaka tikakhala ndi mantha. Mwachitsanzo, mukhoza kupeza mawu olimbikitsa m’mabuku a Yobu, Masalimo, Miyambo komanso m’mawu a Yesu opezeka m’chaputala 6 cha buku la Mateyu. Mukamapemphera kwa Yehova komanso kuwerenga Mawu ake, iye adzakutonthozani.

17. Kodi sitiyenera kukayikira chiyani?

17 Tisamakayikire kuti Yehova adzatithandiza pa nthawi imene takumana ndi mavuto aakulu. Sadzatisiya tokha. (Sal. 23:4; 94:14) Yehova akulonjeza kuti adzatiteteza, kutithandiza kuti tisagwedezeke, kutilimbikitsa komanso kutitonthoza. Ponena za Yehova, lemba la Yesaya 26:3 limati: “Anthu amene amakudalirani ndi mtima wonse mudzawateteza. Mudzawapatsa mtendere wosatha, chifukwa amadalira inu.” Choncho muzidalira Yehova ndipo muzilola kuti akuthandizeni pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. Mukatero mudzapeza mphamvu ngakhale pa nthawi imene mukukumana ndi mavuto aakulu.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi ndi pa nthawi iti pomwe tingafune kuti Yehova atithandize?

  • Kodi Yehova amatithandiza pogwiritsa ntchito njira 4 ziti tikakumana ndi mavuto?

  • Kodi tingatani kuti Yehova atithandize?

NYIMBO NA. 12 Yehova ndi Mulungu Wamkulu

a Mayina ena asinthidwa.