NKHANI YOPHUNZIRA 4

NYIMBO NA. 30 Atate Wanga, Mulungu Wanga Ndiponso Bwenzi Langa

Yehova Amakukondani Kwambiri

Yehova Amakukondani Kwambiri

“Yehova ndi wachikondi chachikulu.”​—YAK. 5:11.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona mmene chikondi cha Yehova chimatithandizira kuti tikhale naye pa ubwenzi, tizidziona kuti ndife otetezeka, timasamaliridwa ndiponso timalimbikitsidwa.

1. N’chiyani chimabwera m’maganizo mwanu mukaganizira za Yehova?

 KODI munayamba mwaganizirapo kuti Yehova ndi wotani? N’chiyani chimabwera m’maganizo mwanu mukamayankhula naye m’pemphero? Ngakhale kuti sitingathe kumuona, Baibulo limamufotokoza m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, Yehova amatchedwa “dzuwa ndiponso chishango” komanso “moto wowononga.” (Sal. 84:11; Aheb. 12:29) Amafotokozedwanso kuti ali ngati mwala wa safiro, chitsulo chowala komanso utawaleza. (Ezek. 1:26-28) Zina zokhudza Yehova zomwe zafotokozedwazi zingatidabwitse kwambiri kapenanso kutichititsa mantha.

2. Kodi n’chiyani chimachititsa ena kuti aziona kuti Yehova sangawakonde?

2 Popeza kuti sitingathe kuona Yehova, mwina zingativute kukhulupirira kuti amatikonda. Ena amaganiza kuti Yehova samawakonda chifukwa cha zinthu zoipa zomwe zinawachitikira m’mbuyomu. Mwinanso ena sanasonyezedwepo chikondi ndi bambo awo. Yehova amamvetsa mmene timamvera ndipo amadziwa mmene zimenezi zimachititsira kuti zikhale zovuta kuti tikhale naye pa ubwenzi. Choncho pofuna kutithandiza, iye amatifotokozera makhalidwe ake osangalatsa kudzera m’Mawu ake.

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira zokhudza chikondi cha Yehova?

3 Mawu amodzi omwe amafotokoza bwino Yehova ndi chikondi. (1 Yoh. 4:8) Baibulo limati Mulungu ndiye chikondi. Zilizonse zimene amachita, amazichita chifukwa cha chikondi. Chikondi chake ndi champhamvu kwambiri moti amachisonyeza ngakhale kwa anthu omwe samukonda. (Mat. 5:44, 45) Munkhaniyi tikambirana za Yehova ndi chikondi chake. Tikamaphunzira kwambiri zokhudza Mulungu, m’pamenenso timayamba kumukonda kwambiri.

YEHOVA AMATIKONDA KWAMBIRI

4. Kodi mumamva bwanji chifukwa cha chikondi chachikulu cha Yehova? (Onaninso chithunzi.)

4 Baibulo limati “Yehova ndi wachikondi chachikulu.” (Yak. 5:11) Iye amadziyerekezera ndi mayi wachikondi. (Yes. 66:12, 13) Taganizirani za mayi yemwe amasamalira mwana wake mwachikondi. Amamunyamula m’manja mwake n’kumamulankhula mwachikondi komanso mokoma mtima. Akamalira kapenanso kumva ululu amaonetsetsa kuti wamupatsa zimene akufunikira. Ifenso tikamamva ululu sitikayikira kuti Yehova amatisonyeza chikondi. Wolemba masalimo anati: “Nkhawa zitandichulukira, munanditonthoza komanso kundisangalatsa.”​—Sal. 94:19.

“Mofanana ndi mayi amene amatonthoza mwana wake, inenso ndidzapitiriza kukutonthozani” (Onani ndime 4)


5. Kodi mumalimbikitsidwa bwanji mukaganizira za chikondi chokhulupirika cha Yehova?

5 Yehova ndi wokhulupirika. (Sal. 103:8) Iye sasiya kutikonda tikalakwitsa zinazake. Aisiraeli ankakhumudwitsa Yehova mobwerezabwereza. Koma iye anasonyeza kuti ankakonda kwambiri anthu osalapawa powauza kuti: “Ndinayamba kukuona kuti ndiwe wamtengo wapatali, unalemekezedwa ndipo ndimakukonda.” (Yes. 43:4, 5) Chikondi cha Yehova sichinasinthe. Nthawi zonse tisamakayikire kuti amatikonda. Ngakhale tilakwitse kwambiri zinthu, Yehova sasiya kutikonda. Tikalapa n’kubwerera kwa iye, tidzaona kuti amatikondabe. Iye amatilonjeza kuti ‘adzatikhululukira ndi mtima wonse.’ (Yes. 55:7) Baibulo limafotokoza kuti akakhululuka zimakhala kuti ‘nyengo zotsitsimutsa zabwera kuchokera kwa Yehova.’​—Mac. 3:19.

6. Kodi lemba la Zekariya 2:8 likutiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova?

6 Werengani Zekariya 2:8. Popeza kuti Yehova amatikonda amamvetsa mmene timamvera ndipo amakhala wokonzeka kutiteteza. Tikamamva kupweteka nayenso amamva kupweteka. Choncho mpake kuti tingapemphere kwa iye kuti: “Nditetezeni ngati mwana wa diso lanu.” (Salimo 17:8) Diso ndi lamtengo wapatali komanso chimodzi mwa ziwalo zofunika kutetezedwa kwambiri. Choncho Yehova akamatiyerekezera ndi mwana wa diso lake, zimakhala ngati akunena kuti, ‘Aliyense wofuna kukuvulazani akuvulaza chinthu chamtengo wapatali kwa ine.’

7. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira zoti Yehova amatikonda?

7 Yehova amafuna tizidziwa kuti amakonda munthu aliyense payekha. Koma amadziwa kuti chifukwa cha zimene zinatichitikirapo m’mbuyomu, mwina tingamakayikire ngati amatikonda. Mwinanso tikukumana ndi mavuto amene angatichititse kukayikira kuti Yehova amatikonda. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamakayikire zimenezi? Chimene chingatithandize ndi kuphunzira mmene amasonyezera chikondi kwa Yesu, odzozedwa komanso kwa tonsefe.

MMENE YEHOVA AMASONYEZERA CHIKONDI CHAKE

8. N’chifukwa chiyani Yesu sankakayikira kuti Atate wake amamukonda?

8 Yehova ndi Mwana wake akhala ali limodzi kwa zaka zambirimbiri ndipo izi zachititsa kuti azikondananso kwambiri. Ubwenzi wawowu ndi wakale kwambiri kuposa ubwenzi wina uliwonse. Pa Mateyu 17:5, Yehova anafotokoza mmene amakondera Yesu. Yehova akanatha kungonena kuti, ‘Uyu ndi amene amandisangalatsa.’ Koma pofuna kutisonyeza mmene amakondera Yesu, ananena kuti “uyu ndi Mwana wanga wokondedwa.” Yehova ankasangalala kwambiri ndi Yesu komanso ndi zimene Yesuyo anali atatsala pang’ono kuchita (Aef. 1:7) Ndipo Yesu sankakayikira kuti Atate wake amamukonda. Ankaona kuti chikondi cha Yehova ndi chenicheni ndipo ankachimva mumtima mwake. Iye anafotokoza mobwerezabwereza kuchokera pansi pa mtima kuti Atate wake amamukonda.​—Yoh. 3:35; 10:17; 17:24.

9. Kodi ndi mawu ati omwe amasonyeza kuti Yehova amakonda odzozedwa? Fotokozani. (Aroma 5:5)

9 Yehova amasonyezanso kuti amakonda odzozedwa. (Werengani Aroma 5:5.) Mawu amene anamasuliridwa kuti “amasonyeza kuti amatikonda” angamasuliridwenso kuti “amatikhuthulira chikondi chake.” Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo limanena kuti chikondichi chimabwera ngati mtsinje. Mawu amenewa ndi amphamvu ndipo amasonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri odzozedwa. Odzozedwa amadziwa kuti “[Mulungu] amawakonda.” (Yuda 1) Mtumwi Yohane anafotokoza mmene iwo amamvera polemba kuti: “Taganizirani za chikondi chachikulu chimene Atate watisonyeza potitchula kuti ana ake.” (1 Yoh. 3:1) Kodi Yehova amakonda odzozedwa okha? Ayi, iye amatikonda tonsefe.

10. Kodi ndi njira yaikulu iti yomwe Yehova anasonyezera kuti amatikonda?

10 Kodi njira yaikulu kwambiri imene Yehova wasonyezera kuti amatikonda ndi iti? Dipo ndi njira yaikulu kwambiri imene wasonyezera chikondi kuposa wina aliyense. (Yoh. 3:16; Aroma 5:8) Yehova analola kuti Mwana wake wamtengo wapatali afe n’cholinga choti anthu onse akhululukidwe machimo awo komanso akhale anzake. (1 Yoh. 4:10) Tikamaganizira kwambiri mtengo umene Yehova ndi Yesu anapereka m’pamene timamvetsa mmene iwo amakondera munthu aliyense payekha. (Agal. 2:20) Sikuti dipo linangoperekedwa chifukwa linkafunika mogwirizana ndi chilungamo cha Yehova, koma ndi mphatso imene anapereka chifukwa cha chikondi chawo. Yehova wasonyeza kuti amatikonda popereka nsembe Yesu, yemwe ndi wamtengo wapatali kwambiri kwa iye. Iye analola kuti Mwana wake avutike komanso aphedwe chifukwa cha ifeyo.

11. Kodi tikuphunzira chiyani pa Yeremiya 31:3?

11 Malinga ndi zimene takambiranazi, Yehova samangomva mumtima mwake kuti amatikonda koma amatiuzanso mmene amatikondera. (Werengani Yeremiya 31:3.) Yehova anatikokera kwa iye chifukwa chakuti amatikonda. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 7:7, 8.) Palibe chinthu chilichonse kapena munthu aliyense amene angatisiyanitse ndi chikondi chake. (Aroma 8:38, 39) Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira za chikondichi? Werengani Salimo 23 kuti muone mmene Davide anamvera chifukwa cha chikondi cha Yehova komanso mmene inuyo mungamvere.

KODI MUMAMVA BWANJI MUKAGANIZIRA CHIKONDI CHA YEHOVA?

12. Kodi mungafotokoze bwanji mwachidule mfundo za mu Salimo 23?

12 Werengani Salimo 23:1-6 Davide, yemwe analemba Salimo 23, anasonyeza kuti sankakayikira kuti Yehova amamukonda kwambiri. Iye anafotokoza zokhudza ubwenzi wolimba womwe unalipo pakati pa iyeyo ndi Yehova, yemwe anali M’busa wake. Davide ankamva kuti anali wotetezeka chifukwa ankalola kuti Yehova azimutsogolera ndipo ankamudalira pa chilichonse. Ankadziwa kuti Yehova azimusonyeza chikondi kwa moyo wake wonse. N’chifukwa chiyani iye sankakayikira zimenezi ngakhale pang’ono?

13. N’chifukwa chiyani Davide sankakayikira kuti Yehova amamukonda?

13 “Sindidzasowa kanthu.” Davide ankaona kuti Yehova amamusamalira chifukwa nthawi zonse ankamupatsa zimene ankafunikira. Ankadziwanso kuti Yehova ndi mnzake ndipo amasangalala naye. N’chifukwa chake sankakayikira kuti kaya akumana ndi zotani Yehova adzapitiriza kumusamalira. Popeza Davide ankakhulupirira kuti Yehova amamukonda komanso adzamusamalira, zinamuthandiza kuti asamade nkhawa, m’malomwake azisangalala.​—Sal. 16:11.

14. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amatisamalira mwachikondi?

14 Yehova amatisamalira mwachikondi makamaka pamene takumana ndi mavuto. Claire, a yemwe wakhala akutumikira pa Beteli kwa zaka zoposa 20 anasowa zochita pamene anthu a m’banja lake anakumana ndi mavuto aakulu motsatizanatsatizana. Bambo ake anadwala matenda opha ziwalo, mng’ono wake anachotsedwa komanso bizinesi ya banja lawo inatha moti banjalo linalibe pokhala. Ndiye kodi Yehova anawasonyeza bwanji chikondi? Claire ananena kuti: “Yehova anaonetsetsa kuti anthu a m’banja langa akupeza zofunikira tsiku lililonse. Nthawi zambiri Yehova ankatipatsa zinthu zochuluka kuposa zimene timayembekezera. Ndimakonda kuganizira za nthawi imene Yehova anatisonyeza chikondi ndipo sindidzaiwala. Kuganizira zimenezi kwandithandiza kuti ndizipirira mavuto ena.”

15. Kodi Yehova anatsitsimula bwanji Davide? (Onaninso chithunzi.)

15 “Amanditsitsimula.” Nthawi zina Davide ankada nkhawa kwambiri chifukwa cha mavuto amene ankakumana nawo. (Sal. 18:4-6) Koma ankatsitsimulidwa chifukwa Yehova ankamusonyeza chikondi komanso kumusamalira. Pa nthawi imeneyi, Yehova ankatsogolera mnzakeyu kumalo “a msipu wambiri” komanso “kumalo opumira a madzi ambiri.” Zimenezi zinathandiza Davide kupezanso mphamvu ndipo anapitiriza kutumikira Mulungu.​—Sal. 18:28-32.

Ngakhale kuti Davide ankakhala moyo wothawathawa, Yehova ankamukonda, kumusamalira komanso kumutsitsimula (Onani ndime 15)


16. Kodi chikondi cha Yehova chimatitsitsimula bwanji?

16 Masiku anonso Yehova amatisonyeza chikondi chokhulupirika ndipo ngakhale kuti timakumana ndi mavuto ambiri, “sitinatheretu.” (Maliro 3:22; Akol. 1:11) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Rachel. Pa nthawi ya mliri wa COVID-19 zinamupweteka kwambiri pamene mwamuna wake anamusiya n’kusiyanso Yehova. Kodi Yehova anamuthandiza bwanji? Iye anati: “Yehova anandithandiza kuti ndizimva kuti ndimakondedwa. Panali anzanga amene ankacheza nane, kundibweretsera chakudya, kunditumizira mameseji ndi malemba olimbikitsa, kuseka nane ndiponso ankandikumbutsa kuti Yehova amandikonda. Nthawi zonse ndimayamikira Yehova chifukwa chondipatsa banja lalikulu la anthu okondana.”

17. N’chifukwa chiyani Davide ‘sankaopa kanthu’?

17 “Sindikuopa kanthu chifukwa inu muli ndi ine.” Nthawi zambiri moyo wa Davide unkakhala pangozi ndipo adani ake ankakhala amphamvu. Komabe chikondi cha Yehova chinkamuthandiza kuti azimva kuti ndi wotetezeka. Nthawi zonse Davide ankaona kuti Yehova anali naye ndipo zimenezi zinkamulimbikitsa. Choncho iye anaimba kuti: “[Yehova] anandipulumutsa ku zinthu zonse zomwe zimandichititsa mantha.” (Sal. 34:4) Ngakhale kuti nthawi zina Davide ankachita mantha kwambiri, ankakhalabe wolimba mtima chifukwa chodziwa kuti Yehova amamukonda.

18. Kodi kusakayikira kuti Yehova amatikonda kungatilimbikitse bwanji tikamachita mantha?

18 Kodi kudziwa kuti Yehova amatikonda kumatipatsa bwanji mphamvu tikakumana ndi zinthu zochititsa mantha? Mpainiya wina dzina lake Susi anafotokoza mmene iye ndi mwamuna wake anamvera, mwana wawo atadzipha. Iye anati: “Zinthu zina zoopsa zikachitika, umasokonezeka maganizo ndipo umasowa chochita. Koma kudziwa kuti Yehova amatikonda kwambiri kwatithandiza kumva kuti ndife otetezeka.” Rachel yemwe tamutchula kale uja anati: “Tsiku lina usiku zitayamba kundipweteka kwambiri mumtima, ndinada nkhawa ndipo ndinkachita mantha. Ndiyeno ndinapemphera mokweza kwa Yehova ndikulira. Nthawi yomweyo ndinamva kuti iye anakhazika mtima wanga pansi ngati mmene mayi amatonthozera mwana wake ndipo ndinagona tulo. Sindidzaiwala nthawi imeneyi.” Mkulu wina dzina lake Tasos anakhala m’ndende zaka 4 chifukwa chokana kulowa usilikali. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti amamukonda komanso kumusamalira? Iye anati: “Yehova anandipatsa zinthu zoposa zimene ndinkafunikira. Izi zinandithandiza kuti ndizimukhulupirira kwambiri. Komanso Yehova anagwiritsa ntchito mzimu wake womwe unandithandiza kuti ndizisangalala ngakhale kuti ndinali kumalo ovuta. Zimenezi zinandithandiza kuona kuti ndikamadalira kwambiri Yehova m’pamenenso ndingamamve kuti amandikonda kwambiri. Choncho ndinayamba kuchita upainiya wokhazikika ndili kundende komweko.”

PITIRIZANI KUKHALA PA UBWENZI NDI MULUNGU YEMWE NDI WACHIKONDI

19. (a) Kodi kudziwa kuti Yehova amatikonda kungatithandize bwanji kudziwa zoyenera kutchula m’mapemphero athu? (b) Kodi ndi mfundo iti yokhudza chikondi cha Yehova yomwe imakulimbikitsani inuyo? (Onani bokosi lakuti “ Mawu Omwe Amatithandiza Kudziwa Kuti Yehova Amatikonda Kwambiri.”)

19 Zitsanzo zimene takambiranazi zikusonyeza kuti Yehova “Mulungu amene ndi wachikondi,” ali nafe. (2 Akor. 13:11) Iye amakonda munthu aliyense payekha. Sitimakayikira kuti nthawi zonse amatisonyeza “chikondi chake chokhulupirika.” (Sal. 32:10) Tikamaganizira kwambiri mmene amasonyezera chikondi chake kwa ife, m’pamenenso timakhala naye pa ubwenzi wolimba kwambiri. Tingathe kupemphera kwa iye momasuka ndi kumufotokozera mmene timayamikirira chikondi chake. Tingamamufotokozerenso zonse zimene zikutidetsa nkhawa n’kumakhulupirira kuti amatimvetsa ndiponso ndi wofunitsitsa kutithandiza.​—Sal. 145:18, 19.

20. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kuti tikhale naye pa ubwenzi?

20 Tonsefe timakopeka ndi chikondi cha Yehova ngati mmene timachitira ndi moto pa tsiku limene kukuzizira. Chikondi cha Yehova ndi champhamvu koma amachisonyezanso mokoma mtima. Choncho muzisangalala chifukwa Yehova amakukondani. Zimenezi zizitichititsa tonsefe kunena mosangalala kuti: “Ndimakonda Yehova.”​—Sal. 116:1.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi mungachifotokoze bwanji chikondi cha Yehova?

  • N’chifukwa chiyani simuyenera kukayikira kuti Yehova amakukondani kwambiri?

  • Kodi mumamva bwanji mukaganizira za chikondi cha Yehova?

NYIMBO NA. 108 Chikondi Chosatha cha Mulungu

a Mayina ena asinthidwa.